Zimene Baibo Imatiuza
“Iyi ndi nkhani yofotokoza mmene kumwamba ndi dziko lapansi zinalengedwela.” (Genesis 2:4) Umu ni mmene Baibo imafotokozela ciyambi ca dziko lapansi. Kodi zimene Baibo imakamba zimagwilizana na mfundo zotsimikizika za sayansi? Ganizilani zitsanzo zingapo izi.
Kodi cilengedwe cilibe ciyambi?
Genesis 1:1 imati: “Pa ciyambi Mulungu analenga kumwamba na dziko lapansi.”
Caka ca 1950 cisanafike, asayansi ambili ochuka anali kukhulupilila kuti cilengedwe cilibe ciyambi. Koma cifukwa ca zimene atulukila posacedwa, asayansi ambili tsopano amavomeleza kuti cilengedwe cili na ciyambi.
Kodi poyamba dziko lapansi linali kuoneka bwanji?
Genesis 1:2, 9 imati dziko lapansi litangolengedwa, linali “lopanda maonekedwe enieni ndiponso lopanda kanthu,” ndipo paliponse panali madzi okha-okha.
Zimenezi n’zogwilizana na zimene asayansi apeza. Katswili wa maphunzilo a zamoyo, dzina lake Patrick Shih anati, poyamba padziko lapansi “panali mpweya woipa, wopanda oxygen . . . ,” ndipo panalibe camoyo ciliconse. Magazini yochedwa Astronomy imati: “Kafukufuku waposacedwa aonetsa kuti poyamba padziko lapansi panali madzi okha-okha, ndipo mtunda unali kuonekela pang’ono kapena sunali kuoneka n’komwe.”
Kodi cifungadziko cinasintha bwanji m’kupita kwa nthawi?
Genesis 1:3-5 imaonetsa kuti pamene kuwala kunayamba kuonekela padziko lapansi, copangitsa kuwalako sicinali kuonekela padziko. Patapita nthawi, m’pamene dzuŵa na mwezi zinayamba kuonekela bwino padziko lapansi, moti munthu akanakhalapo akanatha kuziona.—Genesis 1:14-18.
Baibo siikamba kuti zamoyo zonse padziko lapansi zinalengedwa m’masiku 6 a maola 24 lililonse
Koleji ina ya kafukufuku wa zacilengedwe yochedwa Smithsonian Environmental Research Center imati, poyamba cifungadziko cinali kulola kuwala kocepa cabe kufika padziko lapansi. Imakambanso kuti: “Dziko lapansi litangokhalapo kumene, paliponse panali nkhungu ya mpweya wa Methane.” Koma patapita nthawi, “nkhunguyo inacoka ndipo kumwamba kunayamba kuoneka buluu.”
Kodi zamoyo zosiyanasiyana zinakhalapo liti padziko lapansi?
Genesis 1:20-27 imati nsomba n’zimene zinali zoyamba, kenako mbalame, nyama za kumtunda, ndipo anthu ndiwo anali othela kulengedwa. Nawonso asayansi amakhulupilila kuti nsomba zinakhalapo kale-kale nyama zakumtunda zisanakhalepo, komanso kuti anthu anakhalapo patapita nthawi yaitali.
Baibo siikamba kuti zamoyo sizingasinthe m’kupita kwa nthawi
Maganizo Olakwika pa Zimene Baibo Imakamba
Anthu ena amakamba kuti zimene Baibo imakamba zimasiyana na zimene asayansi apeza. Koma nthawi zambili anthu amakamba zimenezi cifukwa cosamvetsetsa bwino zimene Baibo imakamba.
Baibo siikamba kuti cilengedwe conse kapena dziko lapansi zangokhalako kwa zaka 6,000. Koma imangokamba kuti kumwamba na dziko lapansi zinalengedwa “paciyambi.” (Genesis 1:1) Baibo siifotokoza kuti ‘paciyambipo’ ni nthawi iti makamaka.
Baibo siikamba kuti zamoyo zonse padziko lapansi zinalengedwa m’masiku 6 a maola 24 lililonse. Koma imaseŵenzetsa mawu akuti “tsiku” pofotokoza za nthawi ya utali wosiyana-siyana. Mwacitsanzo, nthawi imene Mulungu analenga zinthu zonse, kuphatikizapo “masiku” 6 a kulenga ochulidwa mu Genesis caputala 1, nayonso imachedwa “tsiku” limodzi. Baibo imati linali “tsiku limene Yehova a Mulungu anapanga dziko lapansi ndi kumwamba.” (Genesis 2:4) Conco, tsiku lililonse mwa “masiku” 6 akulenga amenewo, pamene Mulungu anakonza dziko lapansi kuti pakhale zamoyo na kulenga zamoyozo, lingakhale kuti limaimila nthawi yaitali kwambili.
Baibo siikamba kuti zamoyo sizingasinthe m’kupita kwa nthawi. Buku la Genesis limakamba kuti nyama zinalengedwa “monga mwa mitundu yawo.” (Genesis 1:24, 25) Liwu la m’Baibo lakuti “mitundu” si liwu la zasayansi, ndipo cioneka kuti limatanthauza magulu akulu-akulu a zamoyo. Conco mu “mtundu” umodzi wa zamoyo mungakhale zamoyo zosiyanasiyana. Mawu amenewa aonetsa kuti zamoyo zosiyana-siyana za mu “mtundu” umodzi komanso zimakhala pamodzi, zingathe kusintha m’kupita kwa nthawi.
Muganiza bwanji?
Monga taonela, Baibo imakamba mosavuta komanso molondola mmene cilengedwe cinayambila, mmene dziko linalili litangopangidwa, komanso mmene moyo unayambila. Ndiye kodi n’kutheka kuti Baibo imakambanso zolondola ponena za amene analenga zinthu zonsezo? Encyclopædia Britannica imati, “Mfundo yakuti zamoyo zinakhalapo cifukwa ca mphamvu inayake yoposa ya munthu ni yogwilizana na zimene sayansi yamakono imakamba.” b