ZIMENE ZIKUCITIKA KUTI PA DZIKO PAKHALE MTENDELE
Kuphunzitsa Anthu Makhalidwe Abwino
Anyamata ena acicepele atapita pa ulendo wokonzedwa na sukulu, anagwilila mnyamata mnzawo. Onse anali kuphunzila pa sukulu yapamwamba imene si yaboma ku Canada. Izi zitacitika, mtolankhani wina dzina lake Leonard Stern analemba m’nyuzipepala ina yochedwa Ottawa Citizen kuti: “Kukhala wanzelu ku sukulu, kucita maphunzilo apamwamba, kapena kulemela, sikungapangitse anthu acicepele kupewa kucita zoipa.”
Stern anakambanso kuti: “Timayembekezela makolo kuona kuti kuphunzitsa ana awo makhalidwe abwino, n’cinthu cofunika kwambili kwa iwo. Koma m’malo mwake, iwo amaona kuti cofunika kwambili n’cakuti ana awo aziphasa ku sukulu kuti akapeze nchito zapamwamba, na kukhala olemela.”
N’zoona kuti sukulu ni yofunika. Koma ngakhale maphunzilo akuthupi odalilika kwambili, sangathandize munthu kulimbana na zilakolako zoipa. Nanga kodi tingapeze kuti maphunzilo a makhalidwe abwino amene angatithandize kulimbana na zilakolako zoipa?
MAPHUNZILO OTHANDIZA ANTHU KUKHALA NA MAKHALIDWE ABWINO
Baibo ili monga gilasi. Tikayang’anamo, timaona bwino-bwino zimene sitingakwanitse, komanso zolephela zathu. (Yakobo 1:23-25) Baibo imacitanso zoposa pamenepa. Imatithandiza kusintha umoyo wathu, kuti tikhale na makhalidwe abwino, amene angatithandize kulimbikitsa mtendele komanso mgwilizano weni-weni. Ena mwa makhalidwe amenewa ni ubwino, kukoma mtima, kuleza mtima, kudziletsa, komanso cikondi. Ndipo cikondi “cimagwilizanitsa anthu mwamphamvu kwambili kuposa cinthu cina ciliconse.” (Akolose 3:14) N’cifukwa ciani cikondi n’capadela kwambili? Onani zimene Baibo imakamba za khalidwe limeneli.
-
“Cikondi n’coleza mtima ndiponso n’cokoma mtima. Cikondi sicicita nsanje, sicidzitama, sicidzikuza [kunyada], sicicita zosayenela, sicisamala zofuna zake zokha, sicikwiya. Sicisunga zifukwa. Sicikondwela ndi zosalungama [zoipa], koma cimakondwela ndi coonadi. Cimakwilila zinthu zonse, . . . cimapilila zinthu zonse. Cikondi sicitha.”—1 Akorinto 13:4-8.
-
“Cikondi sicilimbikitsa munthu kucitila zoipa mnzake.”—Aroma 13:10.
-
“Koposa zonse, khalani okondana kwambili, pakuti cikondi cimakwilila macimo oculuka.”—1 Petulo 4:8.
Kodi mumamvela bwanji mukakhala pakati pa anthu amene amakukondani? Kodi simumadzimva wotetezeka ndi womasuka? Inde! Mumadziŵa kuti onse amakufunilani zabwino ndipo sangacite ciliconse cokuvulazani.
Cikondi cingalimbikitsenso anthu kudzimana zinthu zina, komanso kusintha umoyo wawo kuti ena apindule. Mwacitsanzo, a George atakhala ambuye, iwo anali kufunitsitsa kuceza na mdzukulu wawo. Koma panali vuto inayake. A George anali kukoka fodya kwambili, koma mpongozi wawo wamwamuna sanali kufuna kuti azikoka pali mwana. Kodi a George anacita ciani? Ngakhale kuti anakoka fodya kwa zaka 50, iwo analeka fodya
cifukwa cokonda mdzukulu wawo. Zoonadi, cikondi n’camphamvu kwambili!Baibo imatithandiza kukhala na makhalidwe ambili abwino, monga ubwino, kukoma mtima, maka-maka cikondi
Cikondi ni khalidwe limene timacita kuphunzila. Makolo ali na udindo waukulu wophunzitsa ana awo moonetsela ena cikondi. Iwo amapezela ana awo zakudya, kuwateteza, na kuwasamalila akadzicita kapena akadwala. Makolo abwino amakambilana ndi ana awo, komanso amawaphunzitsa. Amapelekanso cilango kwa ana awo, zimene zimaphatikizapo kuwaphunzitsa mfundo zowathandiza kusiyanitsa cabwino na coipa. Ndipo makolo abwino amakhala citsanzo cabwino cimene ana awo angatengele.
N’zacisoni kuti makolo ena amalephela kukwanilitsa udindo wawo. Kodi izi zitanthauza kuti basi n’zosatheka ana awo kusintha kukhala anthu abwino? Kutali-tali! Ngakhale anthu akulu-akulu, kuphatikizapo ena amene anakulila m’banja lovuta kwambili, asintha umoyo wawo modabwitsa kwambili. Iwo akhala anthu oganizila ena, komanso odalilika. Monga mmene tidzaonela m’nkhani yotsatila, ena mwa iwo anali kuonedwa kuti sangasinthe zivute zitani!