Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Acicepele, Mungakhale na Umoyo Wacimwemwe

Acicepele, Mungakhale na Umoyo Wacimwemwe

“Mudzandidziwitsa njila ya moyo.”—SAL. 16:11.

NYIMBO: 133, 89

1, 2. Kodi nkhani ya Tony ionetsa bwanji kuti munthu angathe kusintha?

MNYAMATA wina wamasiye, dzina lake Tony anali kucita maphunzilo ake a ku sekondale. Koma sanali kuikilako nzelu ku sukulu, moti anangotsala pang’ono kuleka. Nthawi zambili kumapeto kwa wiki, anali kupita kukatamba mafilimu kapena kukaceza na anzake. Sikuti anali kucita zaciwawa kapena kuseŵenzetsa am’kolabongo. Kungoti anali kuona kuti moyo wake ulibe phindu. Komanso, anali kukayikila zakuti kuli Mulungu. Ndiyeno tsiku lina, Tony anakumana ndi a Mboni, ndipo anawafunsa mafunso na kuwauza kuti amakayikila zakuti kuli Mulungu. Iwo anam’patsa mabulosha aŵili ofotokoza za ciyambi ca moyo (The Origin of Life—Five Questions Worth Asking ndi kakuti Was Life Created?).

2 A Mboni aja atabwelelako kwa Tony, anam’peza atasintha maganizo. Iye anali ataŵelenga mobweleza-bweleza mabuloshawo cakuti anacita kukwinyika-kwinyika. Tony anawauza kuti: “Zoona, Mulungu alikodi.” Iye anavomela kuyamba kuphunzila Baibo, ndipo m’kupita kwa nthawi anayamba kuona kuti moyo wake uli na phindu. Komanso, anayamba kucita bwino kwambili m’kilasi. Ngakhale a hedi a pa sukulupo, omwe anali kudziŵa kuti Tony anayamba kuphunzila na Mboni, anadabwa na kusintha kwake. Iwo anati: “Tony wasintha kwambili, komanso wayamba kucita bwino m’kilasi, kodi n’cifukwa cakuti unayamba kugwilizana na Mboni za Yehova?” Iye anayankha kuti inde, ndipo anapezelapo mwayi wowalalikila. Tony anaphasa bwino mayeso otsiliza a ku sekondale, ndipo pali pano akutumikila monga mpainiya wanthawi zonse komanso mtumiki wothandiza. Iye amayamikilanso kuti wapeza Tate wabwino, Yehova.—Sal. 68:5.

MUZIMVELA YEHOVA, NDIPO ZINTHU ZIDZAKUYENDELANI BWINO

3. Kodi Yehova wapeleka malangizo anji kwa acicepele?

3 Nkhani ya Tony itiphunzitsa kuti Yehova amakukondani kwambili imwe acicepele. Iye amafuna kuti zinthu zizikuyendelani bwino, komanso kuti mukhale na cimwemwe ceni-ceni. Ndiye cifukwa cake iye amakulangizani kuti: “Kumbukila Mlengi wako Wamkulu masiku a unyamata wako.” (Mlal. 12:1) Kucita zimenezi n’kotheka, olo kuti nthawi zina kumakhala kovuta. Ndipo mwa thandizo la Mulungu, mungakhale na umoyo wacimwemwe, osati cabe pamene muli wacicepele, koma mu umoyo wanu wonse. Kuti tidziŵe mmene tingacitile zimenezi, tiyeni tikambilane zimene zinathandiza Aisiraeli kulanda Dziko Lolonjezedwa, komanso zimene zinathandiza Davide kugonjetsa Goliyati.

4, 5. Ni mfundo yofunika iti imene tiphunzilapo tikaganizila mmene Aisiraeli anagonjetsela Akanani komanso zimene zinathandiza Davide kugonjetsa Goliyati? (Onani mapikica kuciyambi.)

4 Aisiraeli atayandikila Dziko Lolonjezedwa, Mulungu sanawalamule kuti ayambe kuphunzila maluso omenyela nkhondo. (Deut. 28:1, 2) M’malomwake, anangowalangiza kuti amvele malamulo ake na kum’dalila. (Yos. 1:7-9) M’kaonedwe ka umunthu, malangizo amenewa angaoneke ngati osathandiza. Koma anali malangizo abwino koposa, cakuti Yehova anathandiza anthu ake kugonjetsa Akanani. (Yos. 24:11-13) Izi zionetsa kuti kumvela Mulungu kumafuna cikhulupililo. Ndipo munthu akakhala na cikhulupililo, nthawi zonse zinthu zimamuyendela bwino mu umoyo. Ni mmene zinalili kalelo, ndipo masiku anonso zili conco.

5 Goliyati anali ciphona cacitali kwambili kufika mamita 2.9, ndipo anali na zida zoopsa. (1 Sam. 17:4-7) Koma Davide anali cabe na zinthu ziŵili: gulaye, komanso cikhulupililo mwa Yehova Mulungu wake. Mwacionekele, anthu amene analibe cikhulupililo, anaona ngati Davide ni munthu wopanda nzelu. Koma zotulukapo zake zinaonetselatu kuti Goliyati ndiye anali wopanda nzelu.—1 Sam. 17:48-51.

6. N’zinthu ziti zimene tidzakambilana mowonjezeleka m’nkhani ino?

6 M’nkhani yapita, tinakambilana zinthu zinayi zimene zingatipangitse kukhala na umoyo wa phindu komanso wacimwemwe. Zinthu zimenezi ni kudya cakudya cauzimu, kupeza mabwenzi okonda Mulungu, kudziikila zolinga zaphindu, na kuseŵenzetsa ufulu wathu mwanzelu. Tiyeni tsopano tikambilane zinthu zimenezi mowonjezeleka. Ndipo pamene tikambilana, tidzapenda mfundo zina za mu Salimo 16.

YESETSANI KULIMBITSA UBWENZI WANU NA YEHOVA

7. (a) Kodi munthu wauzimu tingam’dziŵe bwanji? (b) Kodi pamene Davide anakamba kuti Yehova ni “gawo” lake anatanthauzanji? Kodi kukhala pa ubwenzi na Mulungu kunam’pangitsa kumvela bwanji?

7 Munthu wauzimu amakhulupilila Mulungu, komanso amaona zinthu mmene iye amazionela. Munthu wotelo amadalila malangizo a Mulungu, ndipo amayesetsa kumumvela. (1 Akor. 2:12, 13) Davide ni citsanzo cabwino pa nkhaniyi. Iye anati: “Yehova ndiye gawo langa, gawo limene ndinapatsidwa, komanso cikho canga.” (Sal. 16:5) Pamene Davide anakamba kuti Yehova ni “gawo” lake, anatanthauza kuti anali pa ubwenzi wabwino na Mulungu, amene analinso malo ake othaŵilako. (Sal. 16:1) Kodi kukhala pa ubwenzi na Mulungu kunam’pangitsa kumvela bwanji? Davide anati: “Moyo wanga ukukondwela.” Inde, kukhala pa ubwenzi wolimba na Mulungu kunam’thandiza Davide kukhala wacimwemwe kwambili mu umoyo wake.—Ŵelengani Salimo 16:9, 11.

8. N’zinthu zina ziti zimene zingakuthandizeni kukhala na cimwemwe ceni-ceni mu umoyo wanu?

8 Anthu amene amakonda zosangalatsa na cuma sangakhale na cimwemwe monga cimene Davide anali naco. (1 Tim. 6:9, 10) M’bale wina wa ku Canada anati: “Cimwemwe ceni-ceni sicidalila pa zinthu zimene timapeza mu umoyo, koma cimadalila pa zimene timapatsa Yehova Mulungu, amene amapeleka mphatso iliyonse yabwino.” (Yak. 1:17) Conco, kulimbitsa cikhulupililo canu mwa Yehova na kum’tumikila kudzakuthandizani kukhala na umoyo wa phindu komanso wacimwemwe. Kodi mungalimbitse bwanji cikhulupililo canu? Muzipatula nthawi yomudziŵa bwino Mulungu. Mungacite izi mwa kuŵelenga Mawu ake, kuyang’ana cilengedwe cake, komanso kusinkha-sinkha za makhalidwe ake, kuphatikizapo cikondi cake pa imwe.—Aroma 1:20; 5:8.

9. Mofanana ndi Davide, mungacite ciani kuti muzilola Mawu a Mulungu kukuwongolelani?

9 Nthawi zina, Mulungu amaonetsa cikondi cake kwa ise mwa kutipatsa uphungu mwacikondi. Pa nthawi ina, Davide anayamikila uphungu wacikondi umene Mulungu anam’patsa. Iye anati: “Ndidzatamanda Yehova amene wandipatsa malangizo. Ndithudi, usiku impso zanga zandiwongolela.” (Sal. 16:7) Davide anali kusinkha-sinkha pa Mawu a Mulungu kuti adziŵe mmene Mulungu amaonela zinthu, na kuyamba kuyendela maganizo ake. Komanso, anali kulola Mawu ake kumuwongolela. Na imwe ngati mucita zimenezi, mudzayamba kukonda kwambili Mulungu, ndipo mudzakhala wofunitsitsa kumumvela. Izi zidzakuthandizaninso kukula mwauzimu na kukhala ozikika mozama m’coonadi. Mlongo wina dzina lake Christin anati: “Pamene niŵelenga nkhani inayake, kufufuza na kuisinkha-sinkha, nimaona ngati kuti Yehova analembela ine nkhaniyo.”

10. Mogwilizana na zimene Yesaya 26:3 imakamba, kodi kukhala munthu wauzimu kungakuthandizeni bwanji?

10 Mukakhala munthu wauzimu, Mulungu amakupatsani nzelu na kukuthandizani kukhala wozindikila. Izi zimakuthandizani kuti muziona dzikoli na tsogolo lake monga mmene iye amalionela. N’cifukwa ciani Mulungu amakupatsani nzelu na kukuthandizani kukhala wozindikila? Cifukwa amafuna kuti muzipanga zosankha mwanzelu. Amafunanso kuti mudziikile zolinga zaphindu mu umoyo wanu, ndi kuti mukhale na ciyembekezo ca tsogolo labwino. (Ŵelengani Yesaya 26:3.) M’bale wina wa ku America, dzina lake Joshua, anati: “Kukhala pa ubwenzi wolimba na Yehova kumanithandiza kudziŵa bwino zinthu zofunika kuika patsogolo mu umoyo.” Kukamba zoona, kukhala munthu wauzimu kumabweletsa cimwemwe coculuka.

PEZANI MABWENZI ABWINO

11. Malinga n’zimene Davide anakamba, kodi mabwenzi abwino tingawapeze bwanji?

11 Ŵelengani Salimo 16:3. Davide anali kudziŵa cisinsi copezela mabwenzi abwino. Iye anali kupeza cimwemwe coculuka mwa kukhala ndi anthu okonda Yehova. Anthu amenewo anali “oyela,” kutanthauza kuti anali na makhalidwe abwino. Wamasalimo wina anakamba mawu ofanana ndi amenewa ponena za mabwenzi ake. Anati: “Ine ndine mnzawo wa anthu okuopani, ndiponso wa anthu osunga malamulo anu.” (Sal. 119:63) Monga tinaphunzilila m’nkhani yapita, na imwe mungathe kupeza mabwenzi abwino ambili pakati pa anthu amene amaopa Yehova na kumumvela. Ndipo mabwenzi amenewo angakhale a misinkhu yosiyana-siyana.

12. N’ciani cinapangitsa kuti ubwenzi wa Davide na Yonatani ukhale wolimba?

12 Davide anali na mabwenzi a misinkhu yosiyana-siyana. Kodi mungakumbukile munthu wa ‘ulemelelo’ amene anali bwenzi lake la pamtima? Anali Yonatani. Ndipo Davide na Yonatani ni ena mwa anthu ochulidwa m’Baibo amene ubwenzi wawo unali wolimba kwambili. Koma kodi mudziŵa kuti Yonatani anali wamkulu kuposa Davide ndi zaka pafupi-fupi 30? Nanga n’ciani cinapangitsa kuti ubwenzi wawo ukhale wolimba? Onse aŵili anali kukhulupilila Mulungu na kulemekezana. Komanso aliyense wa iwo anali kuona makhalidwe abwino a mnzake, monga khalidwe la kulimba mtima pomenyana na adani a Mulungu.—1 Sam. 13:3; 14:13; 17:48-50; 18:1.

13. Mungacite ciani kuti mukhale na mabwenzi osiyana-siyana? Fotokozani citsanzo.

13 Mofanana ndi Davide na Yonatani, na ise ‘timakondwela’ kukhala na mabwenzi amene amakonda Yehova na kum’khulupilila. Kiera, amene watumikila Yehova kwa zaka zambili, anati: “Napeza mabwenzi a zitundu na zikhalidwe zosiyana-siyana, komanso ocokela m’maiko osiyana-siyana.” Ngati na imwe muyesetsa kupeza mabwenzi osiyana-siyana, mudzadzionela mwekha kuti Mawu a Mulungu na mzimu wake zili na mphamvu yogwilizanitsa anthu.

KHALANI NA ZOLINGA ZAPHINDU

14. (a) N’ciani cingakuthandizeni kudziikila zolinga zauzimu? (b) Kodi acicepele ena anakamba ciani pankhani ya kudziikila zolinga zauzimu?

14 Ŵelengani Salimo 16:8. Davide anaona kuti kutumikila Mulungu ndico cinali cinthu cofunika kwambili mu umoyo wake. Na imwe mukamaona kutumikila Yehova kukhala cinthu cofunika kwambili na kudziikila zolinga zimene zingam’kondweletse, mudzakhala na umoyo wacimwemwe. M’bale wina, dzina lake Steven anati: “Nikadziikila zolinga na kuzikwanilitsa, kenako n’kuona mmene napitila patsogolo, nimakhala wacimwemwe.” M’bale wina wacicepele, wocokela ku Germany, amene lomba akutumikila ku dziko lina, anati: “Sinifuna kuti nikadzakalamba, nikadzilinge pokumbukila kuti zonse zimene n’nacita mu umoyo wanga zinali zongofuna kudzikondweletsa nekha.” Tikhulupilila kuti na imwe simufuna kuti zimenezi zikakucitikileni. Conco, mungacite bwino kuseŵenzetsa maluso anu polemekeza Mulungu na kuthandiza ena. (Agal. 6:10) Komanso dziikileni zolinga zauzimu, ndipo muzimupempha Yehova kuti akuthandizeni kuzikwanilitsa. Iye amakondwela kuyankha mapemphelo otelo.—1 Yoh. 3:22; 5:14, 15.

15. Ni zolinga monga ziti zimene mungadziikile? (Onani bokosi yakuti “ Zolinga Zina Zimene Mungadziikile.”)

15 Kodi n’zolinga monga ziti zimene mungadziikile? Mungadziikile zolinga monga ca kupeleka ndemanga m’mawu anu-anu pa misonkhano, kucitako upainiya, kapena kukatumikila pa Beteli. Mwina mungaphunzileko citundu cina, n’colinga cakuti mukatumikile m’gawo la cinenelo cina. Barak, amene ni mtumiki wa nthawi zonse, anati: “Palibe cina ciliconse cimene cimanipatsa cimwemwe coculuka kuposa kuzindikila kuti tsiku lililonse nikucita zonse zimene ningathe potumikila Yehova.”

MUZIYAMIKILA UFULU UMENE MULUNGU WAKUPATSANI

16. Kodi Davide anali kuwaona bwanji malamulo a Yehova na mfundo zake? Nanga n’cifukwa ciani anali kuwaona mwa njila imeneyi?

16 Ŵelengani Salimo 16:2, 4. Monga tinaphunzilila m’nkhani yapita, malamulo a Mulungu na mfundo zake zolungama, zimatipatsa ufulu mwa kutithandiza kuti tiyambe kukonda zabwino na kuzonda zoipa. (Amosi 5:15) Pamene Davide anakamba kuti ubwino wake sukanapindulitsa Yehova, anali kugogomeza mfundo yakuti Yehova ndiye anali Gwelo la khalidwe lake labwino. M’citundu coyambilila ca Baibo, liwu lakuti ubwino limatanthauza makhalidwe abwino. Davide anali kuyesetsa kutengela makhalidwe abwino a Mulungu. Cinanso, iye anali kuzonda makhalidwe amene Mulungu amazonda. Limodzi mwa makhalidwe amenewo ni kulambila mafano. Ili ni khalidwe limene limanyazitsa anthu, komanso kupangitsa kuti ulemelelo umene umafunika kupita kwa Yehova, uzipelekedwa ku zinthu zina kapena kwa anthu ena.—Yes. 2:8, 9; Chiv. 4:11

17, 18. (a) Kodi Davide anakamba kuti anthu opembedza mafano zinthu zimawayendela bwanji mu umoyo? (b) N’ciani cimacititsa anthu kudziculukitsila zopweteka masiku ano?

17 M’nthawi za Baibo, kulambila mafano nthawi zambili kunali kuphatikizapo khalidwe lonyansa la ciwelewele. (Hos. 4:13, 14) N’zoona kuti anthu ambili anali kuona khalidwe limenelo kukhala lokondweletsa. Koma kucita zimenezo sikunawabweletsele cimwemwe cokhalitsa. N’cifukwa cake Davide anati: “Zopweteka zimaculuka kwa anthu amene amati akaona mulungu wina, amamuthamangila.” Kuwonjezela apo, anthu amenewo anapha ana awo ambili-mbili n’kuwapeleka nsembe kwa mafano. (Yes. 57:5) Yehova anali kunyansidwa na mcitidwe wankhanza umenewu. (Yer. 7:31) Yelekezelani kuti munalipo pa nthawiyo, ndipo munali na makolo okhulupilila Yehova na kumumvela. Kodi simukanayamikila kukhala na makolo aconco? Mwacionekele, mukanatelo.

18 N’cimodzi-modzi na masiku ano, zipembedzo zambili zonama zimalekelela khalidwe laciwelewele, kuphatikizapo mathanyula. Koma mofanana ndi kalelo, anthu amene amacita makhalidwe oipa n’kumanamizila kuti ni ufulu wawo, amakumana na mavuto. (1 Akor. 6:18, 19) Mwina na imwe mumaona kuti anthu aconco amadzibweletsela ‘zopweteka zoculuka.’ Conco, imwe acicepele, muzimvela Atate wanu wakumwamba. Muzikhulupilila na mtima wonse kuti kumvela Mulungu kumakutetezani. Muzikumbukila kuti mavuto amene munthu amakumana nawo cifukwa ca khalidwe loipa, amakhala oculuka kwambili poyelekezela na cimwemwe cakanthawi cimene angapeze. (Agal. 6:8) Joshua, amene tam’chula m’nkhani ino, anati: “Tingaseŵenzetse ufulu wathu mmene tifunila, koma ngati tiuseŵenzetsa molakwika, sitingapeze cimwemwe.”

19, 20. Kodi acicepele amene amakhulupilila Yehova na kumumvela akuyembekezela madalitso anji?

19 Yesu anauza otsatila ake kuti: “Mukamasunga mawu anga nthawi zonse, ndiye kuti ndinudi ophunzila anga. Mudzadziwa coonadi, ndipo coonadi cidzakumasulani.” (Yoh. 8:31, 32) Ufulu umenewu umaphatikizapo kumasuka ku cipembedzo conama, umbuli, na zamizimu. Koma umaphatikizaponso zambili. Monga tinaphunzilila, kutsogoloku tidzakhala na “ufulu waulemelelo wa ana a Mulungu.” (Aroma 8:21) Ulaŵeni ufulu umenewu lomba mwa ‘kusunga mawu a Khristu,’ kapena kuti ziphunzitso zake. Mukatelo, “mudzadziŵa coonadi” mwa kuciseŵenzetsa mu umoyo wanu, osati cabe kuciphunzila.

20 Acicepele, muziyamikila ufulu umene Mulungu wakupatsani. Useŵenzetseni mwanzelu. Mukatelo, ndiye kuti mukuyala maziko abwino a tsogolo lanu. M’bale wina wacicepele anati: “Ngati useŵenzetsa ufulu wako mwanzelu ukali wacicepele, zimakuthandiza kwambili kutsogolo popanga zosankha zikulu-zikulu, monga zokhudza kupeza nchito yoyenela, komanso kusankha kuloŵa m’banja kapena kukhala wosakwatila kwa kanthawi.”

21. Mungacite ciani kuti mupitilize kuyenda pa njila yopita ku ‘moyo weni-weni’?

21 M’dziko la Satanali, ngakhale umoyo umene anthu amaona kuti ni wabwino, umakhala waufupi komanso wosapanganika. Sitingadziŵe kuti umoyo wathu udzakhala bwanji maŵa. (Yak. 4:13, 14) Conco, canzelu ni kuyendabe pa njila yopita ku “moyo weniweniwo,” kapena kuti moyo wosatha. (1 Tim. 6:19) Koma Mulungu sacita kutikakamiza kuyenda pa njila imeneyi. Cosankha n’cathu. Cotelo, pangani Yehova kukhala “gawo” lanu, kapena kuti bwenzi lanu. Muziyamikila “zinthu zabwino” zambili zimene iye wakupatsani. (Sal. 103:5) Ndipo khalani na cikhulupililo cakuti iye adzakuthandizani ‘kukondwela mokwanila’ komanso kukhala na “cimwemwe mpaka muyaya.”—Sal. 16:11.