Kodi Mukumbukila?
Kodi munaŵelenga mosamala magazini aposacedwa a Nsanja ya Mlonda? Yesani kuyankha mafunso otsatilawa:
Kodi pali umboni wanji wa m’Malemba woonetsa kuti Mulungu amatimvela cifundo?
Pamene Aisiraeli anali akapolo ku Iguputo, Mulungu anaona mavuto awo, ndipo cinamuŵaŵa mu mtima. (Eks. 3:7; Yes. 63:9) Popeza tinalengedwa m’cifanizilo ca Mulungu, na ise tingaonetse khalidwe la cifundo. Iye amaticitila cifundo ngakhale pamene tidziona kuti ndise osayenelela kusonyezedwa cikondi cake.—wp18.3, mape. 8-9.
Kodi Yesu anaphunzitsa bwanji anthu mmene angathetsele tsankho?
Ayuda ambili m’nthawi ya Yesu anali na tsankho. Khristu anagogomeza kufunika kokhala odzicepetsa, komanso anaphunzitsa anthu kupewa khalidwe lonyadila mtundu wawo. Cinanso, analimbikitsa otsatila ake kuti aziona Akhristu anzawo monga abale na alongo.—w18.06, mape. 9-10.
N’ciani cimene tiphunzilapo tikaganizila cifukwa cake Mulungu sanalole Mose kuloŵa m’Dziko Lolonjezedwa?
Mose anali pa ubwenzi wolimba na Yehova. (Deut. 34:10) Cakumapeto kwa ulendo wa Aisiraeli wa zaka 40 m’cipululu, iwo anayambanso kudandaula cifukwa cosoŵa madzi. Mulungu anauza Mose kuti akambe na thanthwe. Koma iye analimenya thanthwelo. Yehova ayenela kuti anakhumudwa na Mose cifukwa sanatsatile malangizo ake, kapena cifukwa sanam’patse ulemelelo pa cozizwitsa cimeneci. (Num. 20:6-12) Apa tiphunzilapo kuti kumvela Yehova na kum’patsa ulemelelo n’zofunika kwambili.—w18.07, mape. 13-14.
Ngati tiweluza munthu moyang’ana nkhope, tingamuweluze molakwika. Cifukwa ciani?
Pali zinthu zitatu zimene kaŵili-kaŵili anthu amaona monga maziko oweluzilapo ena. Zinthu zake ni mtundu wawo, kulemela kapena kusauka, komanso zaka zakubadwa. Tifunika kuphunzila kuona ena mmene Yehova, Mulungu wopanda tsankho, amawaonela. (Mac. 10:34, 35)—w18.08, mape. 8-12.
Kodi Akhristu acikulile angathandize ena m’njila monga ziti?
Akhristu acikulile amene sakutumikilanso pa udindo umene analipo kale, Mulungu akali kuwakonda. Akhristu amenewa angacite zambili pothandiza ena. Angathandize amuna kapena akazi osakhulupilila amene mnzawo wa m’cikwati ni Mboni. Angathandizenso Akhristu ozilala. Komanso akhoza kumatsogoza maphunzilo a Baibo, kapena angawonjezele zocita pa nchito yolalikila.—w18.09, mape. 8-11.
Ni zida ziti zimene tili nazo mu Thuboksi yathu ya Zida Zophunzitsila?
Tili na tumakadi tongenela pa webusaiti yathu na tumapepa twa ciitanilo. Tilinso na mathilakiti 8 osavuta kuseŵenzetsa, komanso magazini a Nsanja ya Mlonda na Galamuka! Mu Thuboksi imeneyi mulinso mabulosha, mabuku aŵili ophunzitsila, na mavidiyo anayi othandiza kwambili, kuphatikizapo vidiyo yakuti N’cifukwa Ciani Muyenela Kuphunzila Baibulo?—w18.10, peji 16.
Miyambo 23:23 imatilimbikitsa ‘kugula’ coonadi. Kodi tingacite bwanji zimenezi?
Coonadi siticita kugula na ndalama. Komabe, timafunika kucita khama komanso kutayilapo nthawi kuti ticipeze.—w18.11, peji 4.
Kodi tingaphunzilepo ciani tikaganizila mmene Hoseya anacitila zinthu na mkazi wake Gomeri?
Olo kuti Gomeri anacita cigololo mobweleza-bweleza, Hoseya sanam’sudzule, koma anamukhululukila. Ngati Mkhristu wokwatila wacita cigololo, mnzake wosalakwayo angasankhe kumukhululukila. Komanso Mkhristu wosalakwayo akayambanso kukhala malo amodzi na mnzake wolakwayo, sipakhalanso maziko a cisudzulo.—w18.12, peji 13.