“Iye Amapeleka Mphamvu kwa Munthu Wotopa”
Lemba la caka ca 2018: “Anthu odalila Yehova adzapezanso mphamvu.”—YES. 40:31.
1. Ni mavuto ati amene timakumana nawo? Nanga n’cifukwa ciani Yehova amakondwela na atumiki ake okhulupilika? (Onani mapikica pamwambapa.)
MASIKU ano, timakumana na mavuto oculuka. Ambili a inu abale na alongo okondedwa mukuvutika na matenda aakulu. Ena a inu mumasamalila makolo okalamba olo kuti na imwe ndimwe acikulile. Komanso, ena amavutika ngakhale kupezela mabanja awo zinthu zofunika kwambili pa umoyo. Ndipo tidziŵa kuti ena akukumana ndi mavuto ambili pa nthawi imodzi. Kuti tilimbane na mavuto amenewa, pamafunika nthawi yoculuka, mphamvu, na ndalama zambili. Mosasamala kanthu za mavutowa, muli na cidalilo camphamvu m’malonjezo a Mulungu ndipo cikhulupililo canu ca tsogolo labwino n’cosagwedezeka. Zimenezi zimam’kondweletsa kwambili Yehova.
2 Koma kodi nthawi zina mumaona kuti mavuto anu ni aakulu kwambili cakuti simungathe kuwapilila? Ngati n’conco, si inu nokha. Baibo imaonetsa kuti atumiki ena akale okhulupilika a Mulungu, nthawi zambili anali kuona kuti sakanakwanitsa kupilila mavuto awo. (1 Maf. 19:4; Yobu 7:7) Ngakhale zinali conco, iwo sanataye mtima, koma anadalila thandizo la Yehova. Ndipo iye anawathandizadi, cifukwa Mulungu wathu “amapeleka mphamvu kwa munthu wotopa.” (Yes. 40:29) Koma comvetsa cisoni n’cakuti anthu ena a Mulungu masiku ano afika poganiza kuti njila yabwino yothetsela mavuto ni ‘kucipumulila coonadi,’ titelo kukamba kwake. Iwo amaona ngati kuti kucita zinthu zauzimu ni mtolo osati dalitso. Conco, amaleka kuŵelenga Mau a Mulungu, kupezeka pa misonkhano ya mpingo, na kulalikila. Izi n’zimene Satana amafuna kuti mtumiki wa Mulungu acite akakumana na mavuto.
3. (a) Tingacite ciani kuti Satana asatifooketse? (b) Kodi tidzakambilana ciani m’nkhani ino?
3 Mdyelekezi amadziŵa kuti kucita zinthu zauzimu nthawi zonse kungatithandize kukhala olimba. Koma iye amafuna kutifooketsa. Conco, ngati mwafooka cifukwa ca mavuto ndipo muli na nkhawa, musatalikilane naye Yehova. Koma yesetsani kumuyandikila kwambili, ndipo iye “adzakulimbitsani ndi kukupatsani mphamvu.” (1 Pet. 5:10; Yak. 4:8) M’nkhani ino, tidzakambilana mavuto aŵili amene angacepetse cangu cathu potumikila Mulungu. Tidzakambilananso mmene kuseŵenzetsa mfundo za m’Baibo kungatithandizile kupilila mavuto amenewo. Koma coyamba, tiyeni tikambilane umboni wa pa Yesaya 40:26-31, woonetsa kuti Yehova angakwanitse kutipatsa mphamvu zopilila mavuto.
ODALILA YEHOVA ADZAPEZANSO MPHAMVU
4. Ni mfundo yanji imene tingaphunzilepo pa Yesaya 40:26?
4 Ŵelengani Yesaya 40:26. Palibe munthu amene angakwanitse kuŵelenga nyenyezi zonse kumwamba. Asayansi amakhulupilila kuti mu mlalang’amba wathu cabe, wochedwa Milky Way, muli nyenyezi zokwana 400 biliyoni. Koma Yehova amachula dzina nyenyezi iliyonse. N’ciani cimene tiphunzilapo pamenepa? Ngati Yehova amaona zolengedwa zake zopanda moyo kukhala zofunika, kuli bwanji ise anthu, amene timam’tumikila modzifunila cifukwa com’konda? (Sal. 19:1, 3, 14) Atate wathu wacikondi amatidziŵa bwino kwambili. Baibo imakamba kuti ngakhale ‘tsitsi lenilenilo la m’mutu mwathu amaliŵelenga.’ (Mat. 10:30) Komanso, wamasalimo anati: “Yehova amadziŵa za moyo wa anthu osalakwa.” (Sal. 37:18) Inde, iye amaona mavuto amene timakumana nawo, ndipo angatipatse mphamvu zotithandiza kupilila vuto lililonse.
5. Tidziŵa bwanji kuti Yehova angakwanitse kutipatsa mphamvu zotithandiza kupilila mavuto?
5 Ŵelengani Yesaya 40:28. Yehova ni Gwelo la mphamvu zopanda malile. Mwacitsanzo, ganizilani za dzuŵa limene analenga. Wasayansi wina, dzina lake David Bodanis, anati: “Mphamvu imene dzuŵa limatulutsa pa sekondi imodzi cabe ni yolingana na mphamvu ya mabomba [a nyukiliya mabiliyoni ambili].” Wasayansi winanso anakamba kuti “mphamvu imene [dzuŵa] limatulutsa . . . pa sekondi imodzi cabe ni yokwanila kuthandiza anthu pa moyo wawo kwa zaka 200,000!” Mwa ici, sitiyenela kukayikila ngakhale pang’ono kuti Mulungu, amene analenga dzuŵa lamphamvu conco, angatipatse mphamvu zotithandiza kupilila vuto lililonse limene tingakumane nalo.
6. Kodi goli la Yesu n’lofewa m’lingalilo liti? Ndipo kudziŵa zimenezi kuyenela kutikhudza bwanji?
6 Ŵelengani Yesaya 40:29. Kutumikila Yehova kumabweletsa cimwemwe coculuka. Yesu anauza ophunzila ake kuti: “Senzani goli langa.” Ndipo anapitiliza kuti: “Mudzatsitsimulidwa, pakuti goli langa ndi lofewa ndipo katundu wanga ndi wopepuka.” (Mat. 11:28-30) Mau amenewa ni a zoona. Nthawi zina, timakhala otopa pamene ticoka pa nyumba kupita kumisonkhano kapena mu ulaliki. Koma kodi timamvela bwanji tikabwelako? Timakhala titatsitsimulidwa, ndiponso timakhala na mphamvu zotithandiza kupilila mavuto amene timakumana nawo. Ndithudi, goli la Yesu ni lofewa.
7. Fotokozani citsanzo coonetsa kuti mau a pa Mateyu 11:28-30 ni oona.
7 Mlongo wina, dzina lake Kayla, ali na matenda amene amam’cititsa kuti azikhala wotopa nthawi zonse. Komanso, kaŵili-kaŵili
amadwala mutu ndiponso matenda ovutika maganizo. Conco, n’zosadabwitsa kuti nthawi zina cimamuvuta kupezeka pa misonkhano ya mpingo. Komabe, tsiku lina atadzilimbitsa na kupezeka pa misonkhano, analemba kuti: “Nkhani imene inakambiwa pa tsikulo inali yokhudza zinthu zimene zingatifooketse. Nkhaniyo inakambiwa mogwila mtima na mwaubwenzi cakuti n’nakhudzidwa kwambili mpaka kugwetsa misozi. N’nakumbutsidwa kuti kupezeka pa misonkhano n’kofunika ngako.” Iye anakondwela kwambili kuti anayesetsa kupezeka pa msonkhanowo.8, 9. Kodi mtumwi Paulo anatanthauzanji pamene analemba kuti: “Pamene ndili wofooka, m’pamene ndimakhala wamphamvu”?
8 Ŵelengani Yesaya 40:30. Olo titakhala aluso bwanji, pali zinthu zina zimene sitingakwanitse kucita mwa mphamvu zathu zokha. Tonsefe tiyenela kuivomeleza mfundo imeneyi. Mwacitsanzo, ngakhale kuti mtumwi Paulo anali wocita bwino m’zambili, anali na zofooka zina zimene zinali kumulepheletsa kucita zonse zimene anali kufuna. Pamene iye anafotokozela Mulungu nkhawa yake, Mulunguyo anamuuza kuti: “Mphamvu yanga imakhala yokwanila iweyo ukakhala wofooka.” Paulo anamvetsetsa mfundo imeneyi. N’cifukwa cake anati: “Pamene ndili wofooka, m’pamene ndimakhala wamphamvu.” (2 Akor. 12:7-10) Kodi pamenepa iye anatanthauza ciani?
9 Paulo anadziŵa kuti panali zambili zimene sakanakwanitsa kucita popanda thandizo locokela kwa Mulungu. Koma mzimu woyela wa Mulungu unam’patsa mphamvu. Kuwonjezela apo, unam’thandiza kucita zinthu zimene sakanatha kucita mwa mphamvu zake zokha. N’cimodzi-modzi na ise. Ngati tidalila Yehova, tidzakhala olimba.
10. Kodi Yehova anam’thandiza bwanji Davide kupilila mavuto amene anakumana nawo?
10 Nthawi zambili, wamasalimo Davide anali kuthandizidwa na mzimu woyela wa Mulungu. Iye anaimba kuti: “Ndi thandizo lanu, ndingathamangitse gulu la acifwamba. Ndi thandizo la Mulungu wanga ndingakwele khoma.” (Sal. 18:29) Pali mavuto ena amene sitingawapilile mwa mphamvu zathu zokha. Timafunika thandizo la Yehova.
11. Fotokozani mmene mzimu woyela umatithandizila tikakumana na mavuto.
11 Ŵelengani Yesaya 40:31. Ciwombankhanga cimatha kuuluka mtunda utali popanda kukupiza mapiko. Koma sicicita izi mwa mphamvu zake cabe. Cimadalila mpweya wotentha, umene umacithandiza kuulukila m’mwamba popanda kuwononga mphamvu zambili. Conco, ngati pali zinthu zina zake zovuta zimene mufunika kucita, muzikumbukila ciwombankhanga. Muzipempha Yehova kuti akupatseni thandizo kupitila mwa “mthandizi, amene ndi mzimu woyela.” (Yoh. 14:26) Cokondweletsa n’cakuti tingalandile thandizo limeneli nthawi iliyonse imene tikulifuna. Ndipo timafunikila kwambili thandizo la Mulungu maka-maka ngati tasemphana maganizo na m’bale kapena mlongo wathu mu mpingo. Koma kodi n’cifukwa ciani kusemphana maganizo kumeneku kumacitika?
12, 13. (a) N’cifukwa ciani nthawi zina Akhristu amasemphana maganizo? (b) Kodi nkhani ya Yosefe imatiphunzitsa ciani za Yehova?
12 Timasemphana maganizo na Akhristu anzathu cifukwa tonse ndise opanda ungwilo. Conco, nthawi zina tingakhumudwe na mau kapena zocita za Mkhristu mnzathu, kapena ise tingakhumudwitse mnzathu. Ici cingakhale ciyeso cacikulu. Pa nthawi imeneyi, Yehova amatipatsa mpata woonetsa kukhulupilika kwathu. Ndipo tingaonetse kukhulupilika mwa kuphunzila kucita zinthu mogwilizana ndi atumiki ake odzipeleka, amene iye amawakonda olo kuti amalakwitsa zinthu zina.
13 Yehova amalolela kuti atumiki ake akumane na ziyeso. Umboni wa zimenezi ni nkhani ya Yosefe. Pamene anali wacicepele, abale ake ansanje anam’gulitsa monga kapolo, ndipo om’gulawo anapita naye ku Iguputo. (Gen. 37:28) Yehova anali kuona zonsezi. Mwacionekele, iye anamva cisoni poona zoipa zimene anthu anali kucitila Yosefe, bwenzi lake lolungama. Komabe, Yehova sanaletse zimenezi kucitika. Komanso, nthawi ina mkazi wa Potifara ananamizila Yosefe kuti anafuna kum’gwilila, ndipo anaponyedwa m’ndende. Apanso, Yehova analola kuti zimenezi zim’citikile. Koma kodi Mulungu anam’siya Yosefe? Ayi ndithu. Baibo imati: “Ciliconse cimene iye anali kucita Yehova anali kucidalitsa.”—Gen. 39:21-23.
14. Chulani mapindu a kuuzimu ndi akuthupi amene timapeza ngati tiyesetsa kupewa “kupsa mtima.”
14 Citsanzo cina ni Davide. Iye anacitilidwa zinthu zambili zopanda cilungamo. Komabe, monga bwenzi la Mulungu, sanalole mkwiyo kufooketsa cikhulupililo cake. M’malomwake, analemba kuti: “Usapse mtima ndipo pewa kukwiya. Usapse mtima kuti ungacite coipa.” (Sal. 37:8) Cifukwa cacikulu cimene tiyenela kupewela ‘kupsa mtima’ n’cakuti timafuna kutengela Yehova, amene ‘saticitila mogwilizana ndi macimo athu.’ (Sal. 103:10) Koma pali mapindu ena amene timapeza ngati tipewa ‘kupsa mtima.’ Kupsa mtima kungayambitse matenda monga a BP, a m’mimba, ndi a m’cifuwa. Kungayambitsenso matenda a ciwindi na kalambalala. Cinanso, ngati munthu wapsa mtima, saganiza molongosoka. Ndipo nthawi zina kupsa mtima kungacititse kuti munthu akhale wovutika maganizo kwa nthawi yaitali. Koma Baibo imati: “Mtima wodekha ndiwo moyo wa munthu.” (Miy. 14:30) Nanga bwanji ngati tinakhumudwitsana na m’bale wathu? Tingacite ciani kuti tithetse nkhaniyo na kubweza m’bale wathuyo? Tiyenela kuseŵenzetsa malangizo a m’Baibo.
NGATI ABALE ATHU ATIKHUMUDWITSA
15, 16. Kodi muyenela kucita motani ngati Mkhristu mnzanu wakukhumudwitsani?
15 Ŵelengani Aefeso 4:26. Sitidabwa ngati anthu a m’dzikoli aticitila zinthu zankhanza. Koma cimatiŵaŵa kwambili ngati Mkhristu mnzathu kapena wacibululu wakamba kapena kucita zinthu zotikhumudwitsa. Kodi tingacite bwanji ngati taona kuti sitingathe kungonyalanyaza colakwaco? Kodi tidzasunga mkwiyo kwa nthawi yaitali na kuulekelela kukula? Kapena tidzatsatila malangizo anzelu a m’Baibo akuti tiyenela kuthetsa nkhani mwamsanga? Tikacedwa kuthetsa nkhani, cimakhala covuta kwambili kukhazikitsa mtendele na m’bale wathu.
16 Tiyelekezele kuti Mkhristu mnzanu anakukhumudwitsani, ndipo mukulephela kuiŵalako zimene anakucitilani. N’zinthu ziti zimene mungacite kuti mukhazikitse mtendele? Coyamba, muyenela kupemphela kwa Yehova mocokela pansi pa mtima. M’pempheni kuti adalitse zoyesa-yesa zanu n’colinga cakuti zokambilana zanu na m’bale wanuyo zikayende bwino. Kumbukilani kuti nayenso ni bwenzi la Yehova. (Sal. 25:14) Mulungu amam’konda. Yehova amacita zinthu mokoma mtima na mabwenzi ake, ndipo amafuna kuti na imwe muzicita cimodzi-modzi. (Miy. 15:23; Mat. 7:12; Akol. 4:6) Caciŵili, ganizilani zimene mukakambe mukapita kukakambilana naye. Musaumilile maganizo akuti iye anacitila dala kukukhumudwitsani. Komanso, pokamba naye, onetsani kuti mukuzindikila kuti pangakhale zinthu zina zimene simunacite bwino zimene zinayambitsa vutolo. Mungayambe kukamba naye mwa kunena kuti: “Mwina ine n’nangofulumila kukwiya, koma pamene munakamba na ine dzulo, n’namva monga . . . ” Ngati zokambilana zanu sizinayende bwino kweni-kweni, yesani kusakila mpata wina wabwino wokakamba naye kuti mukhazikitse mtendele. Koma poyembekezela kuti mpata ukapezeke, muzim’pemphelela m’bale wanuyo. Muzipempha Yehova kuti amudalitse. M’pempheni kuti akuthandizeni kuyang’ana kwambili pa makhalidwe ake abwino. Mulimonse mmene zingakhalile, dziŵani kuti Yehova adzakondwela poona khama lanu lofuna kuyanjananso na m’bale wanu, amenenso ni bwenzi lake.
NGATI TIMADZIIMBA MLANDU CIFUKWA CA CHIMO LAKALE
17. Kodi Yehova anaika makonzedwe anji otithandiza kukonzanso ubwenzi wathu na iye ngati tacita chimo? Nanga n’cifukwa ciani tifunika kugwilitsila nchito makonzedwe amenewa tikacita chimo?
17 Akhristu ena amadziona kuti ni osayenelela kutumikila Yehova cifukwa anacita chimo lalikulu. Kudziimba mlandu cifukwa ca chimo limene tinacita kungakhale ngati cimtolo colemetsa. Pa nthawi ina, Mfumu Davide atacita chimo, anazunzika na cikumbumtima cake. Iye anati: “Pamene ndinakhala cete osaulula macimo anga, mafupa anga anafooka, cifukwa tsiku lonse ndinali kuvutika mumtima mwanga. Pakuti dzanja lanu linali kundilemela usana ndi usiku.” Koma cokondweletsa n’cakuti Davide anacita zinthu monga mwamuna wauzimu kuti athetse vuto lake. Iye analemba kuti: “Pamapeto pake ndinaulula chimo langa kwa inu. Ndipo inu munandikhululukila zolakwa zanga ndi macimo anga.” (Sal. 32:3-5) Conco, ngati munacita chimo lalikulu, dziŵani kuti Yehova ni wokonzeka kukuthandizani kukonzanso ubwenzi wanu na iye. Koma mufunika kulandila thandizo limene amapeleka kupitilia mu mpingo wake. (Miy. 24:16; Yak. 5:13-15) Musacedwe kucita zimenezi, cifukwa tsogolo lanu lili paciwopsezo. Koma kodi mungacite ciani ngati munalapa ndipo Mulungu anakukhululukilani chimo lanu, koma cikumbumtima canu cikali kukuvutitsani?
18. Kodi mau a Paulo angawalimbikitse bwanji anthu amene amadziona ngati osafunika?
18 Nthawi zina, nayenso mtumwi Paulo anali kuvutika na cikumbumtima cifukwa ca zolakwa zake zakale. Iye anati: “Ndine wamng’ono kwambili mwa atumwi onse, ndipo si ine woyenela kuchedwa mtumwi, cifukwa ndinazunza mpingo wa Mulungu.” Komabe, iye anakambanso kuti: “Koma mwa kukoma mtima kwakukulu kwa Mulungu, ndili monga ndililimu.” (1 Akor. 15:9, 10) Inde, Yehova anam’landila Paulo ngakhale kuti m’mbuyomo analakwitsa zinthu zina. Ndipo Mulungu anali kufuna kuti iye asamakayikile mfundo imeneyi. Ngati ndinu wolapa moona mtima, ndipo munaulula macimo anu, musakayikile kuti Yehova anakukhululukilani. Conco, khulupililani zimene mau ake amakamba pa nkhaniyi, ndipo landilani cikhululuko cake.—Yes. 55:6, 7.
19. Kodi lemba la caka ca 2018 n’liti? Nanga n’cifukwa ciani n’loyenelela?
19 Pamene mapeto a dziko loipali akuyandikila, n’zodziŵikilatu kuti mavuto aziculukila-culukila. Komabe, khalani na cikhulupililo cakuti Mulungu adzakuthandizani kupilila mavuto aliwonse amene mungakumane nawo. Baibo imakamba kuti iye “amapeleka mphamvu kwa munthu wotopa, ndipo wofooka amam’patsa nyonga zoculuka.” (Yes. 40:29; Sal. 55:22; 68:19) M’caka ca 2018, nthawi zonse tikapita ku Nyumba ya Ufumu kukasonkhana, tizikumbutsidwa mfundo yofunika kwambili imeneyi tikaona lemba la caka ku pulatifomu. Lemba la caka ca 2018 n’lakuti: “Anthu odalila Yehova adzapezanso mphamvu.”—Yes. 40:31.