Kufunafuna Cuma Ceni-ceni
“Dzipezeleni mabwenzi ndi cuma cosalungama.”—LUKA 16:9.
1, 2. N’cifukwa ciani nthawi zonse m’dziko la Satanali mudzakhala anthu osauka?
DZIKOLI n’lopondeleza ndi lopanda cilungamo pa zacuma. Acicepele ambili amayesetsa kusakila nchito, koma sazipeza. Anthu ambili amaika moyo wawo paciswe pofuna kusamukila ku maiko olemela. Koma umphawi uli ponse-ponse, ngakhale m’maiko olemela ulimo. Ndipo masiku ano, pali kusiyana kwakukulu pakati pa anthu olemela na osauka. Mwacitsanzo, lipoti ina yaposacedwa inakamba kuti anthu olemela kwambili, amene ciŵelengelo cawo cikwana cabe 1 pelesenti ya anthu onse padziko, ali na cuma colingana ndi ca anthu onse padziko lapansi tikaciphatikiza pamodzi. N’zoona kuti anthu ena angakayikile zimenezi. Koma palibe amene angatsutse kuti anthu mabiliyoni ali pa umphawi wosaneneka, ngakhale kuti ampondamatiki ena ali na cuma coculuka kwambili cimene iwo, ana awo, ndi azidzukulu awo angacigwilitsile nchito koma osacitsiliza. Pozindikila mfundo imeneyi, Yesu anakamba kuti: “Osaukawo muli nawo nthawi zonse.” (Maliko 14:7) N’cifukwa ciani pali kusiyana kwakukulu conco pakati pa anthu?
2 Yesu anadziŵa kuti mavuto a zacuma sadzathelatu m’dzikoli mpaka pamene Ufumu wa Mulungu udzabwela. Magulu adyela a zamalonda, amene anayelekezeledwa ndi “amalonda oyendayenda” pa Chivumbulutso 18:3, pamodzi ndi andale ndi acipembedzo, ndiwo dziko la Satana. Ise anthu a Mulungu timapewelatu kutengako mbali m’zandale kapena m’zinthu zokhudzana ndi cipembedzo conama. Koma ambili sitingapeweletu kutengako mbali m’zamalonda m’dziko la Satanali.
3. Kodi tidzakambilana mafunso ati?
3 Pokhala Akhristu, tifunika kudzipenda kuti tidziŵe mmene timaonela cuma ca m’dzikoli. Tingacite zimenezi mwa kudzifunsa mafunso monga awa: ‘Ningaseŵenzetse bwanji cuma canga kuti nionetse kuti ndine wokhulupilika kwa Mulungu? Ningapeŵe bwanji kuloŵelela kwambili m’zamalonda m’dzikoli? Nanga ni zitsanzo ziti zimene zionetsa kuti Akhristu oona amadalila Mulungu na mtima wonse m’nthawi yovuta ino?’
FANIZO LA MTUMIKI WOSALUNGAMA
4, 5. (a) Ndi vuto lanji limene mtumiki wa m’fanizo la Yesu anakumana nalo? (b) Ni malangizo ati amene Yesu anapeleka kwa otsatila ake?
4 Ŵelengani Luka 16:1-9. Fanizo la Yesu la mtumiki wosalungama n’locititsa cidwi. Mtumiki ameneyo atamuneneza kuti anali kusakaza cuma ca bwana wake, “anacita mwanzelu” mwa ‘kudzipezela mabwenzi’ kuti adzam’thandize akadzacotsedwa nchito. * Apa, Yesu sanali kulimbikitsa ophunzila ake kuti azicita zacinyengo n’colinga cakuti apeze zofunikila pa umoyo wawo. Iye anakamba kuti zimene mtumikiyu anacita ni khalidwe la “ana a m’dziko lino.” Koma anagwilitsila nchito fanizoli pofuna kuphunzitsa otsatila ake mfundo inayake yofunika.
5 Yesu anadziŵa kuti mofanana ndi mtumiki amene anapezeka m’vuto ameneyu, ambili mwa otsatila ake anafunika kudzipezela zofunikila pa umoyo m’dzikoli, lomwe n’lopanda cilungamo pa zamalonda. Conco, anawalimbikitsa kuti: “Dzipezeleni mabwenzi ndi cuma cosalungama, kuti cumaco cikatha, [Yehova na Yesu] akakulandileni m’malo okhala amuyaya.” Tingaphunzilepo ciani pa malangizo a Yesu amenewa?
6. Tidziŵa bwanji kuti kucita malonda siinali mbali ya colinga ca Mulungu?
6 Ngakhale kuti Yesu sanafotokoze cifukwa cake anakamba kuti cuma ni “cosalungama,” Baibo imaonetselatu kuti kucita malonda si mbali ya colinga ca Mulungu. Yehova anali kupatsa Adamu na Hava zonse zofunikila pamene anali m’munda wa Edeni. (Gen. 2:15, 16) Ndipo m’zaka 100 zoyambilila, pamene mzimu woyela unayamba kugwila nchito pampingo wa odzozedwa, “panalibe ngakhale mmodzi wonena kuti zinthu zimene anali nazo zinali zayekha. Zonse zimene anali nazo zinali za onse.” (Mac. 4:32) Komanso, mneneli Yesaya anakambilatu za nthawi pamene anthu onse adzakhala na ufulu woseŵenzetsa cuma ca padziko lapansi. (Yes. 25:6-9; 65:21, 22) Koma pali pano, otsatila a Yesu afunika kucita zinthu “mwanzelu” pogwilitsila nchito “cuma cosalungama kuti apeze zofunikila pa umoyo.” Panthawi imodzi-modzi, afunika kuyesetsa kucita zinthu zokondweletsa Mulungu.
KUSEŴENZETSA MWANZELU CUMA COSALUNGAMA
7. Kodi pa Luka 16:10-13 pali malangizo anji?
7 Ŵelengani Luka 16:10-13. Mtumiki wa m’fanizo la Yesu anadzipezela mabwenzi na zolinga zadyela. Koma Yesu analimbikitsa otsatila ake kuti afunika kudzipezela mabwenzi kumwamba ndi zolinga zabwino. Mavesi otsatila palembali aonetsa kuti pali kugwilizana pakati pa mmene timagwilitsila nchito “cuma cosalungama,” ndi kukhala okhulupilika kwa Mulungu. Mfundo ya Yesu pamenepa inali yakuti mmene timagwilitsila nchito cuma cathu, zingaonetse kuti ndise ‘okhulupilika’ kwa Mulungu kapena ayi. Kodi zimenezi zingacitike bwanji?
8, 9. Fotokozani zitsanzo za mmene ena aonetsela kukhulupilika poseŵenzetsa cuma cawo.
8 Njila imodzi imene tingaonetsele kukhulupilika na cuma cathu ni mwa kupeleka ndalama zothandizila pa nchito yolalikila padziko lonse, imene Mat. 24:14) Mwacitsanzo, mtsikana wina wang’ono ku India anasunga kabokosi, ndipo anayamba kuikamo tundalama twasiliva. Anafika ngakhale pogulitsa tukadoli twake ndi kuika ndalama m’kabokosiko. Pamene kabokosiko kanadzala, anapeleka ndalamazo kuti zithandizile pa nchito yolalikila. M’bale wina wa ku India, amene ali na famu ya makokonati, anapeleka makokonati ambili ku ofesi yomasulila mabuku ya Cimalayalam, monga copeleka caufulu. Anaona kuti ni bwino kupeleka makokonati kusiyana ndi kupeleka ndalama, cifukwa pa ofesiyo abale amafunika kugula makokonati. Kumeneku ndiye kucita zinthu mwanzelu. Nawonso abale a ku Greece amapeleka mafuta a maolivi, chizi, ndi zakudya zina ku banja la Beteli.
Yesu anakamba kuti idzacitika. (9 M’bale wina wa ku Sri Lanka, amene lomba akhala ku dziko lina, anapeleka malo ndi nyumba yake m’dziko lawo kuti abale azicitilapo misonkhano yampingo ndi yadela, komanso kuti pazikhala atumiki anthawi zonse. Pamenepa, m’baleyu anaonetsa mzimu wodzimana, ndipo izi zathandiza kwambili abale na alongo osoŵa a m’delalo. M’dziko lina limene nchito yathu ni yoletsedwa, abale amapeleka nyumba zawo kuti zizigwilitsidwa nchito monga Nyumba za Ufumu. Izi zathandiza kuti apainiya ndi abale ena amene ali na ndalama zocepa akhale na malo olambilila aulele m’malo mocita lendi.
10. Ni mapindu ena ati amene timapeza tikakhala owoloŵa manja?
10 Zitsanzo zimene tafotokoza zionetsa mmene anthu a Mulungu akhalila ‘okhulupilika pa cinthu cacing’ono,’ kapena kuti cuma cakuthupi, cimene cili na phindu locepa tikaciyelekezela na cuma cauzimu. (Luka 16:10) Kodi mabwenzi a Yehova amenewa amamvela bwanji akaganizila zopeleka zimene amacita? Amadziŵa kuti kukhala owoloŵa manja ndiyo njila yopezela cuma “ceniceni.” (Luka 16:11) Mlongo wina amene kaŵili-kaŵili amacita zopeleka zocilikizila nchito ya Ufumu, anafotokoza madalitso amene wapeza. Anati: “Cifukwa cokhala wowoloŵa manja, umoyo wanga wasintha ngako m’zaka zapitazi. Naona kuti kukhala wowoloŵa manja, kwanithandiza kukhala wokoma mtima kwambili kwa anthu ena. Nakhala munthu wokonzeka kukhululukila ena, woleza mtima, wopilila, ndi wokonzeka kulandila uphungu.” Anthu ambili aona kuti kukhala wowoloŵa manja kumawathandiza kukhala olimba mwauzimu.—Sal. 112:5; Miy. 22:9.
11. (a) Kodi kukhala opatsa kumaonetsa bwanji kuti ndise ‘anzelu’? (b) Kodi anthu a Mulungu amathandizana bwanji kuti pakhale kufanana pakati pawo? (Onani pikica kuciyambi.)
11 Kuseŵenzetsa cuma pocilikiza zinthu za Ufumu kumaonetsa kuti ndise ‘anzelu’ m’njila inanso. Kumatipatsa mwayi wothandiza ena ndi zinthu zimene tili nazo. Anthu amene ali na cuma koma sangakwanitse kucita utumiki wa nthawi zonse kapena kusamukila m’dziko lina, amakondwela podziŵa kuti zopeleka zawo zimathandiza ena amene akucita utumiki. (Miy. 19:17) Zopeleka zaufulu zimathandiza pa nchito yofalitsa mabuku, ndiponso zimathandiza pa nchito yolalikila m’maiko osauka, kumene nchito yathu ikupita patsogolo kwambili. Kwa zaka zambili, m’maiko monga Congo, Madagascar, ndi Rwanda, Mabaibo anali odula ngako cakuti mtengo wake unali kulingana ndi malipilo amene munthu woseŵenza anali kulandila pa wiki kapena a pa mwezi. Conco, nthawi zambili abale anali kukhala na njala n’colinga cakuti agule Mabaibo. Koma kaamba ka zopeleka za ena zimene zikugwilitsidwa nchito m’njila yakuti “pakhale kufanana,” gulu la Yehova laseŵenzetsa ndalama zambili pocilikiza nchito yomasulila ndi kufalitsa Mabaibo. Lomba, aliyense pabanja ali na Baibo, kuphatikizapo maphunzilo a Baibo anjala ya coonadi. (Ŵelengani 2 Akorinto 8:13-15.) Mwanjila imeneyi, opatsa ndi olandila, onse ali na mwayi wokhala mabwenzi a Yehova.
MUSALOŴELELE KWAMBILI ‘M’ZAMALONDA ZIMENE ANTHU WAMBA AMACITA’
12. Kodi Abulahamu anaonetsa bwanji kuti anali kudalila Mulungu?
12 Cina cimene cingatithandize kukhala pa ubwenzi wolimba na Yehova ndi kupewa kuloŵelela kwambili m’zamalonda m’dzikoli. M’malomwake, tifunika kufuna-funa cuma “ceni-ceni’. Abulahamu, munthu wakale wacikhulupililo colimba, anamvela Mulungu ndi kucoka mumzinda wolemela wa Uri, n’kukakhala m’mahema n’colinga cakuti akhale pa ubwenzi wolimba na Yehova. (Aheb. 11:8-10) Nthawi zonse, iye anali kudalila Mulungu monga Gwelo la cuma ceni-ceni, ndipo sanali kufuna-funa cuma cakuthupi cifukwa kucita zimenezo kukanaonetsa kuti analibe cikhulupililo. (Gen. 14:22, 23) Yesu anagogomeza kufunika kwa cikhulupililo cotelo, pamene anauza mnyamata wina wacuma kuti: “Ngati ukufuna kukhala wangwilo, pita kagulitse katundu wako ndipo ndalama zake upatse osauka. Ukatelo udzakhala ndi cuma kumwamba, ndiyeno ubwele udzakhale wotsatila wanga.” (Mat. 19:21) Mnyamatayo analibe cikhulupililo ngati ca Abulahamu. Koma pali anthu ena amene aonetsa kuti ali na cikhulupililo colimba mwa Mulungu.
13. (a) Ni malangizo anji amene Paulo anapeleka kwa Timoteyo? (b) Nanga tingaonetse bwanji kuti timamvela malangizo a Paulo?
13 Timoteyo anali na cikhulupililo colimba. Paulo anachula Timoteyo kuti ndi “msilikali wabwino wa Khristu Yesu.” Pambuyo pake anamuuza kuti: “Msilikali amene ali pa nkhondo sacita nawo zamalonda zimene anthu wamba amacita, pofuna kukondweletsa amene anamulemba usilikali.” (2 Tim. 2:3, 4) Lelolino, otsatila a Yesu, kuphatikizapo khamu la atumiki a nthawi zonse oposa 1,000,000, amvela malangizo a Paulo amenewa kulingana ndi mmene zinthu zilili pa umoyo wawo. Iwo satengeka na zokamba za otsatsa malonda kapena zinthu zina zokopa za m’dzikoli. Ndipo amakumbukila mfundo yakuti: “Wobweleka amakhala kapolo wa wobweleketsayo.” (Miy. 22:7) Satana amafuna kuti tiziwononga nthawi yathu ndi mphamvu zathu zonse pocilikiza dongosolo la zamalonda la m’dzikoli. Zosankha zina zimene tingapange zingatipangitse kukhala akapolo a nkhongole kwa zaka zambili. Mwacitsanzo, ena amatenga loni ya ndalama zambili kuti agulile nyumba, kulipilila ana a sukulu, kugulila galimoto yodula, kapena kuti acitile cikwati capamwamba. Tingaonetse kuti ndise anzelu mwa kukhala na umoyo wosalila zambili, kupewa nkhongole zazikulu, kapena kugula zinthu zodula. Tikatelo, tidzatha kutumikila Mulungu momasuka, m’malo mokhala akapolo a anthu amalonda a m’dzikoli.—1 Tim. 6:10.
14. Kodi tifunika kukhala na mtima wotani? Pelekani zitsanzo.
14 Tifunika kuika patsogolo zinthu zofunika kwambili kuti tikwanitse kukhala na umoyo wosalila zambili. Mwacitsanzo, m’bale wina na mkazi wake anali na bizinesi yaikulu imene inali kuyenda bwino. Komabe, cifukwa cofunitsitsa kuyambanso utumiki wanthawi zonse, iwo anagulitsa bizinesiyo, boti, ndi katundu wina. Pambuyo pake, anadzipeleka kukagwila nawo nchito yomanga likulu latsopano ku Warwick, mumzinda wa New York. Kwa mawiki angapo, iwo anali na mwayi wotumikila pamodzi ndi makolo a m’baleyo, amene anali kugwilanso nchito yomanga ku Warwick. Komanso amaona kuti ni dalitso lalikulu kutumikila pa Beteli pamodzi na mwana wawo wamkazi ndi mwamuna wake. Citsanzo cina ni ca mlongo wa ku Colorado, m’dziko la United States, amene ni mpainiya. Iye anapeza nchito yoseŵenza maola ocepa ku banki. Akulu-akulu a bankiyo anakondwela na mmene anali kuseŵenzela cakuti anam’pempha kuti ayambe
kuseŵenza tsiku lonse. Anamuuza kuti adzawonjezela katatu malipilo amene anali kulandila. Komabe, iye anakana cifukwa anadziŵa kuti nchitoyo idzamulepheletsa kucita upainiya. Izi ni zina mwa zinthu zambili-mbili zimene atumiki a Yehova amadzimana pom’tumikila. Kukhala na mtima wodzimana waconco pofuna kuika zinthu za Ufumu patsogolo, ni umboni wakuti timaona ubwenzi wathu na Mulungu komanso cuma cauzimu, kukhala zofunika kwambili kuposa cuma cimene tingapeze m’dzikoli.‘CUMA CIKATHA’
15. Ni cuma citi cimene cimatipatsa cimwemwe ceni-ceni?
15 Kulemela si umboni wakuti Mulungu watidalitsa. Yehova amadalitsa anthu amene ni “olemela pa nchito zabwino.” (Ŵelengani 1 Timoteyo 6:17-19.) Mwacitsanzo, pamene Lucia * anamva kuti ku Albania kuli alaliki ocepa, anacoka ku Italy ndi kusamukila kumeneko mu 1993. Panthawiyo, analibe nchito imene ikanamuthandiza kupeza zofunikila pa umoyo, koma anadalila Yehova na mtima wonse. Kumeneko, iye anaphunzila citundu ca Cialubaniya, ndipo wathandiza anthu oposa 60 kuphunzila coonadi mpaka kubatizika. Anthu ambili a Mulungu satumikila m’magaŵo aconde ngati limene mlongoyu anali kulalikilamo. Ngakhale n’conco, ciliconse cimene timacita pothandiza ena kupeza njila ya ku moyo na kupitiliza kuyendamo, cidzathandiza ise pamodzi ndi anthuwo kudzapeza cuma cosatha.—Mat. 6:20.
16. (a) N’ciani cidzacitikila dongosolo la zamalonda la m’dzikoli? (b) Kodi kuganizila zimene zidzacitika mtsogolo kuyenela kukhudza bwanji mmene timaonela cuma cakuthupi?
16 Yesu anati: “Cumaco cikatha,” osati ‘ngati cumaco catha,’ kusonyeza kuti cuma cakuthupi n’cosadalilika, cidzatha. (Luka 16:9) Kusokonezeka kwa zacuma kumene kukucitika m’masiku otsiliza ano, ndi vuto locepa poyelekezela ndi mavuto aakulu azacuma amene adzacitika padziko lonse posacedwapa. Dongosolo lonse la Satana, kutanthauza magulu a ndale, acipembedzo, ndi amalonda, onse adzatha nchito. Mneneli Ezekieli ndi Zefaniya anakambilatu kuti golide na siliva, zinthu zimene amalonda amaziona kukhala zofunika ngako, zidzakhala zopanda phindu. (Ezek. 7:19; Zef. 1:18) Kodi inu mungamvele bwanji ngati muli pafupi kufa, ndipo mwazindikila kuti munataya cuma ceni-ceni pofuna kudziunjikila “cuma cosalungama”? Mungamvele monga mmene munthu angamvelele ngati waseŵenza kwa moyo wake wonse n’kudziunjikila vindalama, koma pambuyo pake n’kuzindikila kuti ndalamazo n’zabodza. (Miy. 18:11) Ndithudi, cuma cakuthupi cidzatha. Conco, musataye mwayi wociseŵenzetsa mwanzelu kuti ‘mudzipezele mabwenzi’ kumwamba. Inde, ciliconse cimene timacita popititsa patsogolo zinthu za Ufumu wa Yehova zimaticititsa kukhala wolemela mwauzimu.
17, 18. Kodi mabwenzi a Mulungu adzalandila madalitso otani?
17 Ufumu wa Mulungu ukadzabwela, sikudzakhala kulipila malendi kapena kutenga nkhongole. Cakudya cidzakhala camahala ndi ca mwanaalilenji. Sikudzakhalanso madokota kapena mankhwala. Anthu a Yehova padziko lapansi adzasangalala na zinthu zambili zabwino. Golide, siliva, ndi miyala ina yamtengo wapatali zidzakhala zinthu zokongoletsela, osati zogulitsa kapena zosunga monga cuma. Kudzakhala zipangizo zabwino zamiyala, zamitengo, ndi zacitsulo zimene tidzayamba kuseŵenzetsa pomanga nyumba zokongola. Zipangizo zimenezo zidzakhala zamahala. Anzathu adzayamba kutithandiza mwa kufuna kwawo, osati cifukwa cofuna ndalama. M’dziko latsopano, aliyense azikagaŵana zinthu na anzake.
18 Izi ni zocepa cabe mwa zinthu zokondweletsa zimene anthu amene adzipezela mabwenzi kumwamba adzasangalala nazo. Olambila Yehova padzikoli adzakondwela kosaneneka pamene adzamva mau a Yesu akuti: “Bwelani, inu amene mwadalitsidwa ndi Atate wanga. Loŵani mu ufumu umene anakonzela inu kucokela pa kukhazikitsidwa kwa dziko.”—Mat. 25:34.
^ par. 4 Yesu sanaonetse kuti zimene anthu ananenela mtumikiyu zinali zoona kapena zabodza. Liu la Cigiriki limene linamasulidwa kuti “anamuneneza,” pa Luka 16:1, lingatanthauze kuti mtumikiyu anamunamizila. Koma Yesu anasumika maganizo ake pa zimene mtumikiyu anacita, osati pa mlandu umene anafuna kum’cotsela nchito.
^ par. 15 Mbili ya mlongo Lucia Moussanett inalembedwa mu Galamukani! ya July 8, 2003, mapeji 28-32.