NSANJA YA MLONDA—YOPHUNZILA July 2018

Magazini ino ili na nkhani zophunzila wiki ya September 3-30, 2018.

ANADZIPELEKA NA MTIMA WONSE

Anadzipeleka na Mtima Wonse—ku Myanmar

N’ciani cinapangitsa Mboni za Yehova zambili kukukila ku Myanmar kukathandiza pa nchito yokolola mwauzimu?

Kodi Mumafuna Kukhala Wodziŵika kwa Ndani?

Tiphunzilapo ciani tikaganizila mmene Mulungu amaonetsela kuti amawadziŵa atumiki ake okhulupilika?

Kodi Maso Anu Amayang’ana kwa Ndani?

Pali phunzilo lofunika kwambili pa zimene Mose analakwitsa.

“Ndani Ali Kumbali ya Yehova?”

Nkhani ya m’Baibo ya Kaini, Solomo, komanso ya Mose na Aroni, zionetsa cifukwa cake kukhala ku mbali ya Yehova n’cinthu canzelu.

Ndise Anthu a Yehova

Tingamuyamikile bwanji Yehova potipatsa mwayi wokhala naye pa ubwenzi?

Muzicitila Cifundo Anthu “Kaya Akhale a Mtundu Wotani”

Tengelani cifundo ca Yehova mwa kuzindikila mavuto a ena na kuwathandiza mmene mungathele

Mafunso Ocokela kwa Oŵelenga

Ngati mwamuna na mkazi osakwatilana anakhala m’nyumba imodzi usiku wonse popanda zifukwa zomveka, kodi angaimbidwe mlandu wocita chimo lalikulu?