Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Lolani Malamulo a Mulungu na Mfundo Zake Kuphunzitsa Cikumbumtima Canu

Lolani Malamulo a Mulungu na Mfundo Zake Kuphunzitsa Cikumbumtima Canu

“Ndimasinkhasinkha zikumbutso zanu.”—SAL. 119:99.

NYIMBO: 127, 88

1. Chulani cinthu cimodzi cimene cimapangitsa anthu kukhala apamwamba kuposa nyama.

CINTHU cimodzi cimene cimasiyanitsa anthu na nyama n’cakuti anthu analengedwa na cikumbumtima. Umu ni mmene zinthu zakhalila kungoyambila pamene anthu analengedwa pa dziko lapansi. Mwacitsanzo, pamene Adamu na Hava anaphwanya lamulo la Yehova, anathaŵa n’kukabisala. Izi zionetsa kuti cikumbumtima cawo cinali kuwavutitsa.

2. Kodi cikumbumtima cathu cimafanana bwanji na kampasi? (Onani pikica pamwambapa.)

2 Anthu amene ali na cikumbumtima cosaphunzitsidwa bwino ali monga sitima ya pamadzi imene ili na kampasi yosaseŵenza bwino. * Kuyenda pa sitima yaconco kungapangitse kuti ticite ngozi. Zili conco, cifukwa mphepo na mafunde a m’nyanja zingacititse kuti sitimayo iyambe kuyenda njila yolakwika. Koma kampasi yoseŵenza bwino ingathandize woyendetsa kudziŵa kumene afunika kuloŵela. Cikumbumtima cathu tingaciyelekezele na kampasi. Cikumbumtima ni mphamvu yacibadwa imene imatithandiza kuzindikila cabwino na coipa na kutitsogolela m’njila yoyenela. Koma kuti cikumbumtima cizititsogolela bwino, tifunika kuciphunzitsa.

3. N’ciani cingacitike ngati cikumbumtima cathu n’cosaphunzitsidwa bwino?

3 Ngati cikumbumtima ca munthu si cophunzitsidwa bwino, sicingamuletse kucita zoipa. (1 Tim. 4:1, 2) Cikumbumtima caconco cingaticititse kuona ngati “coipa n’cabwino.” (Yes. 5:20) Yesu anacenjeza ophunzila ake kuti: “Nthawi ikubwela pamene aliyense wakupha inu adzaganiza kuti wacita utumiki wopatulika kwa Mulungu.” (Yoh. 16:2) Umu ni mmene anthu amene anapha wophunzila wa Yesu, Sitefano, anali kuganizila. Ndipo pali enanso amene anacita zofanana ndi zimenezi. (Mac. 6:8, 12; 7:54-60) Anthu ambili acipembedzo akhala akucita zinthu zoipa, monga kupha anthu, n’kumakamba kuti akucita cifunilo ca Mulungu, pamene m’ceni-ceni akuphwanya malamulo ake. (Eks. 20:13) Ndithudi! Iwo asoceletsedwa kothelatu na cikumbumtima cawo.

4. Tingacite ciani kuti cikumbumtima cathu cizititsogolela bwino?

4 Tingacite ciani kuti cikumbumtima cathu cizititsogolela bwino? Malamulo na mfundo za m’Mau a Mulungu ‘n’zopindulitsa pa kuphunzitsa, kudzudzula, kuwongola zinthu ndi kulangiza m’cilungamo.’ (2 Tim. 3:16) Conco, tifunika kumaŵelenga Baibo mwakhama, kusinkha-sinkha zimene imakamba, na kuziseŵenzetsa mu umoyo wathu. Tikatelo, tidzaphunzitsa cikumbumtima cathu kuti cizititsogolela mogwilizana na maganizo a Mulungu. Cikumbumtima caconco cikhoza kutithandiza kupanga zosankha mwanzelu. Lomba tiyeni tikambilane mmene malamulo a Yehova na mfundo zake zingatithandizile kuphunzitsa cikumbumtima cathu.

LOLANI KUTI MALAMULO A MULUNGU AKUPHUNZITSENI

5, 6. Kodi timapindula bwanji ngati timvela malamulo a Mulungu?

5 Kuti tipindule na malamulo a Mulungu, tifunika kucita zambili osati cabe kuyaŵelenga kapena kuyadziŵa. Tifunika kumayakonda na kuyalemekeza. Mau a Mulungu amati: “Danani ndi coipa ndipo muzikonda cabwino.” (Amosi 5:15) Koma kodi tingacite bwanji zimenezi? Cofunika kwambili ni kuphunzila kuona zinthu mmene Yehova amazionela. Mwacitsanzo, tiyelekezele kuti imwe muli na vuto losoŵa tulo. Mutapita kucipatala, dokota wakupatsani malangizo okhudza kadyedwe, kucita maseŵela olimbitsa thupi, na kusintha zinthu zina mu umoyo wanu. Pambuyo potsatila malangizowo, mukuona kuti mwayamba kugona bwino tsopano. Mwacionekele, mungamuyamikile dokotayo cifukwa cokuthandizani kuthetsa vuto lanu.

6 Mofanana ndi zimenezi, Mlengi wathu watipatsa malamulo amene angatiteteze ku zotulukapo zoipa za ucimo na kutithandiza kukhala na umoyo wabwino. Ganizilani cabe mmene timapindulila cifukwa comvela malamulo a m’Baibo oletsa kunama, kucita cinyengo, kuba, ciwelewele, ciwawa, na zamizimu. (Ŵelengani Miyambo 6:16-19; Chiv. 21:8) Tikaona mapindu amene timapeza cifukwa comvela malamulo a Yehova, timayamba kukonda na kuyamikila kwambili Yehova na malamulo ake.

7. Kodi kuŵelenga na kusinkha-sinkha nkhani za anthu ochulidwa m’Baibo kungatithandize kucita ciani?

7 Sitifunika kucita kuphwanya malamulo a Mulungu kuti tidziŵe kuopsa kocita zimenezo. Tingaphunzilepo kanthu pa zolakwa za ena, amene nkhani zawo zinalembedwa m’Mau a Mulungu. Lemba la Miyambo 1:5, limati: “Munthu wanzelu amamvetsela ndi kuphunzila malangizo owonjezeleka.” Kukamba zoona, timalandila malangizo abwino kwambili kucokela kwa Mulungu. Imodzi mwa njila zimene timalandilila malangizowo ni mwa kuŵelenga na kusinkha-sinkha nkhani za anthu ochulidwa m’Baibo. Mwacitsanzo, ganizilani mavuto amene Mfumu Davide anakumana nawo cifukwa cophwanya lamulo la Yehova mwa kucita cigololo na Bati-seba. (2 Sam. 12:7-14) Pamene tiŵelenga nkhaniyi, tingacite bwino kudzifunsa kuti: ‘Kodi Davide akanapewa bwanji mavuto amene anakumana nawo cifukwa cocita cigololo na Bati-seba? Ngati nitakumana na ciyeso cofanana na cimeneci, ningacite ciani? Kodi ningathawe monga mmene Yosefe anacitila, kapena ningagonje ngati Davide?’ (Gen. 39:11-15) Ngati tiganizila zotulukapo zoipa za chimo, tidzayamba kudana kwambili na coipa.

8, 9. (a) Kodi cikumbumtima cathu cimatithandiza bwanji? (b) Kodi mfundo za Yehova na cikumbumtima cathu zimagwilizana bwanji?

8 Mwina timayesetsa kupewa zinthu zimene Mulungu amazonda. Koma pali nkhani zina zimene palibe malamulo acindunji a m’Malemba. Pa nkhani zaconco, kodi tingadziŵe bwanji zimene zili zovomelezeka na zokondweletsa kwa Mulungu? Apa m’pamene cikumbumtima cathu cophunzitsidwa Baibo cimathandiza.

9 Mwacikondi cake, Yehova anatipatsa mfundo zimene tingazigwilitsile nchito mogwilizana na cikumbumtima cathu cophunzitsidwa Baibo. Iye anati: “Ine Yehova ndine Mulungu wanu, amene ndimakuphunzitsani kuti zinthu zikuyendeleni bwino, amene ndimakucititsani kuti muyende m’njila imene muyenela kuyendamo.” (Yes. 48:17, 18) Ngati tiganizila mozama mfundo za m’Baibo na kuzilola kutifika pa mtima, tingawongolele cikumbumtima cathu. Ndipo cikumbumtima cotelo cidzatithandiza kupanga zosankha mwanzelu.

MUZILOLA MFUNDO ZA MULUNGU KUKUTSOGOLELANI

10. Kodi mfundo za m’Baibo n’ciani? Nanga Yesu anaziseŵenzetsa bwanji pophunzitsa?

10 Mfundo za m’Baibo ni ‘mfundo za coonadi zofunika kwambili kapena ziphunzitso zimene zimatitsogolela popanga zosankha kapena kucita zinthu.’ Kumvetsetsa mfundozo kumaphatikizapo kudziŵa bwino maganizo a Mulungu, amene ndiye Wopeleka malamulo, komanso kumvetsetsa zifukwa zimene anapelekela malamulowo. Mu utumiki wake wonse, Yesu anaphunzitsa mfundo za coonadi pofuna kuthandiza ophunzila ake kuzindikila zotulukapo za khalidwe loipa kapena maganizo oipa. Mwacitsanzo, anawaphunzitsa kuti kusunga mkwiyo kungasonkhezele munthu kucita ciwawa, ndipo cilakolako coipa cingapangitse munthu kucita ciwelewele. (Mat. 5:21, 22, 27, 28) Kuti tiphunzitse bwino cikumbumtima cathu, tiyenela kulola mfundo za Mulungu kutitsogolela. Tikacita izi, Mulungu adzalandila ulemelelo.—1 Akor. 10:31.

Mkhristu wokhwima mwauzimu amaganizila cikumbumtima ca ena (Onani palagilafu 11, 12)

11. Kodi zikumbumtima zingasiyane bwanji?

11 Pa nkhani zina, Akhristu angapange zosankha zosiyana olo kuti onse ali na zikumbumtima zophunzitsidwa bwino Baibo. Mwacitsanzo, ganizilani nkhani ya kumwa moŵa. Baibo siiletsa kumwa moŵa pang’ono. Koma imaticenjeza kuti tifunika kupewa kumwa kwambili ndi ucakolwa. (Miy. 20:1; 1 Tim. 3:8) Komabe, izi sizitanthauza kuti ngati Mkhristu amamwa pa mlingo woyenela, ndiye kuti basi zonse zili bwino. Pali mbali zina zimene afunika kuziganizila. Mwacitsanzo, olo kuti cikumbumtima cake sicingamuvutitse, iye afunikanso kuganizila cikumbumtima ca ena.

12. Kodi mau a pa Aroma 14:21 angatilimbikitse bwanji kulemekeza cikumbumtima ca ena?

12 Pofotokoza mfundo yakuti Mkhristu afunika kuganizila cikumbumtima ca ena, Paulo anati: “Ndi bwino kusadya nyama kapena kusamwa vinyo kapena kusacita kalikonse kamene kamakhumudwitsa m’bale wako.” (Aroma 14:21) Kodi mungapewe kucita zinthu zina n’colinga cakuti musakhumudwitse cikumbumtima ca ena, olo kuti muli na ufulu wocita zinthuzo? Mosakayikila, mungatelo. Kumbukilani kuti ena mwa abale athu asanaphunzile coonadi, anali na vuto la kumwa kwambili moŵa. Koma lomba ni otsimikiza mtima kupewelatu khalidwe limeneli. Mwacionekele, palibe aliyense wa ise amene angafune kucita zinthu zimene zingasonkhezele m’bale wathu kuyambilanso khalidwe limene lingamuwononge mwauzimu. (1 Akor. 6:9, 10) Conco, si cikondi kukakamiza m’bale kumwa moŵa ngati iye wakana.

13. N’citsanzo cabwino citi cimene Timoteyo anaonetsa popititsa patsogolo zinthu za Ufumu?

13 Pamene Timoteyo anali na zaka pafupi-fupi 20 kapena kupitililako pang’ono, analolela kudulidwa pofuna kuti asakakhumudwitse Ayuda amene anali kukawalalikila. Iye anali na maganizo monga a mtumwi Paulo. (Mac. 16:3; 1 Akor. 9:19-23) Mofanana ndi Timoteyo, kodi ndimwe wokonzeka kudzimana zinthu zina pofuna kuthandiza ena?

“YESETSANI MWAKHAMA KUTI MUKHALE OKHWIMA MWAUZIMU”

14, 15. (a) Kodi kukhala wokhwima mwauzimu kumaphatikizapo ciani? (b) Kodi kukonda ena kumaonetsa bwanji kuti ndise okhwima mwauzimu?

14 Akhristu onse ayenela kukhala na colinga cophunzila zambili osati kungodziŵa cabe ciphunzitso “coyambilila ca Khristu.” Ayenelanso ‘kuyesetsa mwakhama kuti akhale okhwima mwauzimu.’ (Aheb. 6:1) Izi sizicitika zokha. Tifunika ‘kuyesetsa mwakhama,’ kapena kuti kugwililapo nchito. Kukhala okhwima mwauzimu kumaphatikizapo kuwonjezela cidziŵitso na luso lathu la kuzindikila. Ndiye cifukwa cake nthawi zambili timalimbikitsidwa kuti tiziŵelenga Baibo tsiku lililonse. (Sal. 1:1-3) Kodi imwe munadziikila colinga coŵelenga Baibo tsiku lililonse? Kucita zimenezi kungakuthandizeni kudziŵa bwino malamulo a Yehova na mfundo zake. Kungakuthandizeninso kukhala na cidziŵitso cozama ca Mau a Mulungu.

15 Lamulo lalikulu kwambili kwa ise Akhristu ni lakuti tiyenela kukondana. Yesu anauza ophunzila ake kuti: “Mwakutelo, onse adzadziŵa kuti ndinu ophunzila anga, ngati mukukondana.” (Yoh. 13:35) Yakobo, m’bale wake wa Yesu, anakamba kuti cikondi ni “lamulo lacifumu.” (Yak. 2:8) Nayenso Paulo anati: “Cilamulo cimakwanilitsidwa m’cikondi.” (Aroma 13:10) N’zosadabwitsa kuti Baibo imagogomeza kufunika kwa cikondi cifukwa “Mulungu ndiye cikondi.” (1 Yoh. 4:8) Mulungu amaonetsa cikondi cake mwa zocita. Yohane analemba kuti: “Mulungu anatisonyeza ife cikondi cake pakuti anatumiza m’dziko Mwana wake wobadwa yekha kuti tipeze moyo kudzela mwa iye.” (1 Yoh. 4:9) Inde, cikondi n’cimene cinasonkhezela Mulungu kucita zimenezi. Conco, tikamakonda kwambili Yehova, Mwana wake, Akhristu anzathu, ndi anthu ena, timaonetsa kuti ndise okhwima mwauzimu.—Mat. 22:37-39.

Tikamaganizila mfundo za m’Baibo, cikumbumtima cathu cimatitsogolela bwino (Onani palagilafu 16)

16. N’cifukwa ciani Mkhristu akayamba kukhwima mwauzimu amayambanso kuona mfundo za m’Baibo kukhala zofunika kwambili?

16 Lamulo limakhudza cabe mbali imodzi, koma mfundo imakhudza mbali zambili mu umoyo. Pa cifukwa cimeneci, Mkhristu akayamba kukhwima mwauzimu, amayambanso kuona kuti kukonkha mfundo za m’Baibo n’kofunika kwambili. Mwacitsanzo, mwana wamng’ono sangamvetsetse kuopsa kogwilizana na anthu oipa. Conco, kholo lozindikila lingamuikile malamulo n’colinga comuteteza. (1 Akor. 15:33) Koma pamene mwanayo akukula, luso lake la kuganiza limakulanso, ndipo amatha kuganizila mfundo za m’Baibo posankha zocita. Akafika pamenepa, iye angakwanitse kudzisankhila yekha mabwenzi mwanzelu. (Ŵelengani 1 Akorinto 13:11; 14:20.) Tikamaganizila mfundo za m’Baibo posankha zocita, cikumbumtima cathu cimatitsogolela bwino, cifukwa cimakhala cogwilizana kwambili na maganizo a Mulungu.

17. N’cifukwa ciani tingakambe kuti tili na zonse zofunikila kuti tithe kupanga zosankha mwanzelu?

17 Kodi tili na zonse zofunikila zimene zingatithandize kupanga zosankha zokondweletsa Yehova? Inde. Ngati tiseŵenzetsa bwino malamulo na mfundo za m’Mau a Mulungu, tikhoza kukhala “woyenelela bwino ndi wokonzeka mokwanila kucita nchito iliyonse yabwino.” (2 Tim. 3:16, 17) Conco, muzifufuza mfundo za m’Malemba n’colinga cakuti muthe “kuzindikila cifunilo ca Yehova.” (Aef. 5:17) Muziseŵenzetsa mokwanila zida zofufuzila zimene gulu la Mulungu lapeleka, monga Watch Tower Publications Index, Buku Lofufuzila Nkhani la Mboni za Yehova, Watchtower Library, LAIBULALE YA PA INTANETI ya Watchtower, na JW Laibulale. Zida zimenezi zinakonzedwa kuti zizitithandiza kupindula kwambili na phunzilo lathu laumwini ndi labanja.

KUKHALA NA CIKUMBUMTIMA COPHUNZITSIDWA BAIBO KUMABWELETSA MADALITSO

18. Ni madalitso anji amene timapeza ngati ticita zinthu mogwilizana na malamulo a Yehova na mfundo zake?

18 Kumvela malamulo a Yehova na kutsatila mfundo zake kumabweletsa madalitso. Izi n’zimene Salimo 119:97-100 imakamba. Imati: “Ndimakonda kwambili cilamulo canu! Ndimasinkhasinkha cilamuloco tsiku lonse. Malamulo anu amandicititsa kukhala wanzelu kuposa adani anga, cifukwa ndi anga mpaka kalekale. Ndakhala wozindikila kwambili kuposa aphunzitsi anga, cifukwa ndimasinkhasinkha zikumbutso zanu. Ndimacita zinthu mozindikila kuposa anthu acikulile, cifukwa ndimasunga malamulo anu.” Tikamapatula nthawi ‘yosinkha-sinkha’ malamulo a Mulungu na mfundo zake, timayamba kucita zinthu mwanzelu komanso mozindikila kwambili. Ndipo ngati tiyesetsa kulola malamulo a Mulungu na mfundo zake kuphunzitsa cikumbumtima cathu, tikhoza kufika “pa msinkhu waucikulile umene Khristu anafikapo.”—Aef. 4:13.

[Mau apansi]

^ par. 2 Kampasi ni kacipangizo kolingana na wochi yamivi, koma kamakhala na muvi umodzi wa magineti umene nthawi zonse umalata kumpoto. Ngati kacipangizo kameneka kamagwila bwino nchito kangathandize munthu kuti asasocele.