Khalani ndi Cikhulupililo Ndipo Muzipanga Zosankha Mwanzelu
“Azipempha ndi cikhulupililo, osakayikila m’pang’ono pomwe.”—YAK. 1:6.
1. N’ciani cinalepheletsa Kaini kupanga cosankha mwanzelu? Nanga zotsatilapo zake zinali zabwanji?
KAINI anafunika kupanga cosankha pa nthawi ina. Iye anafunika kusankha kaya kugonjetsa mkwiyo kapena kuulola kumulamulila. Mulimonse mmene iye akanasankhila, zotulukapo zake zikanakhudza umoyo wake wonse. Monga mmene tidziŵila, Kaini sanapange cosankha cabwino. Cifukwa cakuti sanalamulile mkwiyo wake, iye anapha m’bale wake wokhulupilika Abele. Komanso zinawononga ubale wake ndi Mlengi.—Gen. 4:3-16.
2. N’cifukwa ciani kupanga zosankha mwanzelu n’kofunika kwambili?
2 Nafenso timafunika kupanga zosankha. Sikuti zosankha zonse zimene timapanga zimakhala zazikulu. Komabe, zosankha zambili zimene timapanga zingakhudze kwambili umoyo wathu. Conco, kupanga zosankha mwanzelu kungatithandize kukhala na umoyo wabwino ndi wamtendele, m’malo mokhala na umoyo wosasangalala, wodzala na mavuto.—Miy. 14:8.
3. (a) Kuti tipange zosankha mwanzelu, kodi tifunika kukhulupilila ciani? (b) Ni mafunso ati amene tidzakambilana?
3 N’ciani cingatithandize kupanga zosankha mwanzelu? Yakobo 1:5-8.) Pamene tiyandikila Mulungu ndi kukonda kwambili Mau ake, timayamba kudalila citsogozo cake. Zotulukapo zake, timakhala na cizoloŵezi cofufuza Mau a Mulungu tisanasankhe zocita. Koma kodi tingakulitse bwanji luso lopanga zosankha mwanzelu? Nanga tikapanga cosankha, ndiye kuti sitingacisinthe zivute zitani?
Tifunika kukhulupilila Mulungu, ndipo sitiyenela kukayikila kuti iye angatithandize kupanga zosankha mwanzelu. Tifunikanso kukhulupilila Mau a Yehova, kudalila malangizo ake ouzilidwa, ndi kukhulupilila kuti kacitidwe kake ka zinthu ndiye koyenela. (ŴelenganiKUPANGA ZOSANKHA NI MBALI YA UMOYO
4. Kodi Adamu anafunika kupanga cosankha canji? Nanga zotulukapo zake zinali zotani?
4 Kuyambila paciyambi, anthu akhala akupanga zosankha pa nkhani zazikulu. Adamu anafunika kusankha kumvela Mlengi wake kapena Hava. Iye anapangadi cosankha, koma kodi mumamvela bwanji mukaganizila cosankha cimene anapanga? Mkazi wake atanamizidwa, anamusonkhezela kupanga cosankha coipa ngako, cimene cinapangitsa kuti ataye mwayi wokhala m’Paradaiso, ndipo m’kupita kwa nthawi anafa. Koma zimenezi zinali ciyambi cabe ca zotulukapo zoipa za cosankha cake. Mpaka lomba, tonse tikuvutika kaamba ka cosankha coipa cimene Adamu anapanga.
5. Kodi tiyenela kuuona bwanji udindo wopanga zosankha?
5 Anthu ena amaganiza kuti kukanakhala kuti anthufe tinalibe udindo wopanga zosankha, sembe umoyo ni wokondweletsa kwambili. Kodi inunso mumaona conco? Ngati n’telo, kumbukilani kuti Yehova sanapange anthu monga maloboti, amene saganiza kapena kupanga zosankha. Ndipo Baibo imatiphunzitsa mmene tingapangile zosankha mwanzelu. Yehova amafuna kuti tizipanga tokha zosankha, ndipo zimenezi zili na ubwino wake. Tiyeni tione umboni wotsimikizila mfundo imeneyi.
6, 7. N’cosankha citi cimene Aisiraeli anafunika kupanga? Nanga n’cifukwa ciani iwo analephela kusankha mwanzelu? (Onani pikica kuciyambi.)
6 Aisiraeli atayamba kukhala m’Dziko Lolonjezedwa, anafunika kupanga cosankha cofunika kwambili. Anafunika kusankha kutumikila Yehova kapena kutumikila mulungu wina (kapena milungu ina). (Ŵelengani Yoswa 24:15.) Cosankha cimeneci cingaoneke ngati nkhani yaing’ono. Komabe, zimene akanasankha zikanawacititsa kukhala ndi moyo kapena kufa. M’nthawi ya Oweluza, Aisiraeli mobweleza-bweleza anali kusankha mopanda nzelu. Iwo anali kusiya Yehova ndi kuyamba kutumikila milungu yonama. (Ower. 2:3, 11-23) Ganizilaninso zimene zinacitika panthawi ina, pamene anthu a Mulungu anafunika kupanga cosankha. Panthawiyo, mneneli Eliya anawauza momveka bwino kuti asankhepo pakati pa kutumikila Yehova kapena kutumikila Baala, mulungu wonama. (1 Maf. 18:21) Eliya anadzudzula anthuwo cifukwa colephela kupanga cosankha. Mwina muganiza kuti cosankha cimeneci cinali cosavuta cifukwa nthawi zonse kutumikila Yehova ndiye cinthu canzelu ndi copindulitsa. Ndipo palibe munthu woganiza bwino amene anafunika kukopeka ndi Baala ndi kuyamba kum’tumikila. Ngakhale n’conco, Aisiraeli anali ‘kukayika-kayika.’ Koma Eliya anawalimbikitsa kuti asankhe kulambila Yehova, Mulungu woona.
7 N’cifukwa ciani Aisiraeli analephela kupanga cosankha mwanzelu? Coyamba, iwo analeka kukhulupilila Yehova ndipo anakana kumvetsela Mau ake. Sanacitenso khama kuphunzila coonadi ponena za Mulungu, kapena nzelu zake. Kukhala na Sal. 25:12) Cinanso, iwo analola anthu ena kuwasoceletsa, ngakhale kuwapangila zosankha. Anthu a m’dzikolo amene sanali kulambila Yehova, anasonkhezela Aisiraeli kuyamba kulambila milungu yawo. Komabe, Yehova anali atawacenjezapo kale izi zisanacitike.—Eks. 23:2.
cidziŵitso colongosoka kukanawathandiza kupanga zosankha mwanzelu. (KODI TIYENELA KULOLA ENA KUTIPANGILA ZOSANKHA?
8. Kodi mbili ya Aisiraeli itiphunzitsa mfundo yofunika iti pankhani yopanga zosankha?
8 Taphunzilapo ciani pa zitsanzo zimene tafotokoza m’ndime zapitazi? Taphunzilapo kuti ndi udindo wathu kupanga zosankha. Koma kuti zosankhazo zikhale zanzelu zifunika kuzikidwa pa cidziŵitso colongosoka ca m’Malemba. Pa Agalatiya 6:5 pamati: “Aliyense ayenela kunyamula katundu wake.” Conco, tisapatse munthu wina udindo wotipangila zosankha. M’malomwake, tifunika kuphunzila zimene Mulungu amafuna, ndi kusankha zocita mogwilizana ndi zimene taphunzilazo.
9. N’cifukwa ciani kulola ena kutipangila zosankha kungakhale koopsa?
9 Kodi zingacitike bwanji kuti tilole ena kutipangila zosankha? Kutengela zocita za ena kungaticititse kupanga zosankha zolakwika. (Miy. 1:10, 15) Ngakhale anzathu atitunthe bwanji, ni udindo wathu kupanga cosankha mogwilizana ndi cikumbumtima cathu cophunzitsidwa Baibo. Ngati tilola anthu ena kutipangila zosankha, ndiye kuti tasankha ‘kuwatsatila.’ Cimene tapangaco n’cosankha inde, koma cikhoza kutigwetsela m’mavuto.
10. Kodi Paulo anacenjeza Agalatiya za ciani?
10 Mtumwi Paulo anacenjeza Agalatiya za kuopsa kolola anthu ena kuwapangila zosankha. (Ŵelengani Agalatiya 4:17) Anthu ena mumpingo anafuna kupangila anzawo zosankha pa nkhani zaumwini ndi colinga cowapatutsa kwa atumwi. Cifukwa ciani? Anthu odzikondawo anali kufuna kuchuka. Iwo anacita zinthu mopitilila malile posalemekeza udindo wa Akhristu anzawo wodzipangila zosankha.
11. Kodi tingathandize bwanji anthu ena kupanga zosankha zaumwini?
11 Paulo anali citsanzo cabwino pankhani yolemekeza ufulu wa abale ake 2 Akorinto 1:24) Masiku ano, akulu ayenela kutsatila citsanzo ca Paulo pamene apeleka uphungu kwa ena pa nkhani zaumwini. Iwo amakonda kufotokozela ena mumpingo mfundo za m’Baibo. Komabe, amapewa kupangila zosankha abale ndi alongo pa nkhani zaumwini. Amacita zimenezi kuti asakaŵelengedwe mlandu wa zotulukapo zake. Pamenepa, tiphunzilapo mfundo yofunika kwambili. Tingathandize ena mwa kuwakumbutsa mfundo za m’Baibo kapena kuwapatsa malangizo. Komabe, iwo ali ndi ufulu ndi udindo wodzipangila zosankha. Akapanga zosankha mwanzelu, amapindula. Conco, tiyenela kupewa kudziona monga tili na udindo wopangila abale ndi alongo zosankha.
wodzipangila zosankha. (ŴelenganiOSANGOTSATILA MTIMA WANU POPANGA ZOSANKHA
12, 13. N’cifukwa ciani kupanga zosankha tili okwiya kapena tili na nkhawa n’koopsa?
12 Anthu ambili amaganiza kuti ndi bwino kungotsatila zimene mtima ufuna posankha zocita. Koma kucita zimenezi kumabweletsa mavuto. Ndipo n’kosagwilizana ndi Malemba. Baibo imaticenjeza kuti sitiyenela kungotsatila mtima wathu kapena kucita zinthu mongotengeka popanga zosankha. (Miy. 28:26) Zitsanzo za m’Baibo zimaonetsa kuti ngati munthu amangotsatila mtima wake pocita zinthu, amakumana ndi mavuto. Zili conco cifukwa cakuti ndife opanda ungwilo, ndipo ‘mtima wathu ndi wonyenga kwambili kuposa cina ciliconse ndipo ungathe kucita cina ciliconse coipa.’ (Yer. 3:17; 13:10; 17:9; 1 Maf. 11:9) Ni vuto lanji limene lingakhalepo ngati timangotsatila mtima wathu pocita zinthu?
13 Mtima wa Mkhristu ni mbali yofunika ngako. N’cifukwa cake timauzidwa kuti tizikonda Yehova ndi mtima wathu wonse ndi kukonda anzathu mmene timadzikondela tokha. (Mat. 22:37-39) Koma Malemba amene ali m’palagilafu yapitayi, ationetsa kuopsa kotsatila mtima wathu pocita zinthu. Mwacitsanzo, kodi cingacitike n’ciani ngati tipanga zosankha tili okwiya? Ngati munacitapo zinthu muli wokwiya, ndiye kuti yankho lake mwalidziŵa kale. (Miy. 14:17; 29:22) Komanso bwanji ngati munthu ali na nkhawa, kodi angapange zosankha mwanzelu? (Num. 32:6-12; Miy. 24:10) Mau a Mulungu amaonetsa kuti kukhala “kapolo wa cilamulo ca Mulungu” ndiye cinthu canzelu. (Aroma 7:25) N’zoonekelatu kuti tingasoceletsedwe ngati tilola mtima kutilamulila pamene tipanga zosankha zofunika kwambili.
PAMENE MUNGAFUNIKE KUSINTHA COSANKHA CANU
14. Tidziŵa bwanji kuti nthawi zina kusintha zosankha zathu kuli cabe bwino?
14 Tonse timafunika kupanga zosankha mwanzelu. Komabe zimenezi sizitanthauza kuti tikapanga cosankha, sitiyenela kusintha zivute zitani. Nthawi zina timafunika kuganizilaponso pa cosankha cathu, ndipo mwina tingaone kuti tifunika kucisintha. Mwacitsanzo, ganizilani mmene Yehova anacitila ndi Anineve m’nthawi ya Yona. Baibo imati: “Ndiyeno Mulungu woona anaona nchito zawo. Anaona kuti alapa ndi kusiya njila zawo zoipa. Conco, Mulungu woona anasintha maganizo ake pa tsoka limene ananena kuti awabweletsela, moti sanawabweletsele.” (Yona 3:10) Yehova anasintha maganizo ataona kuti Anineve alapa ndi kusiya njila zawo zoipa. Mwa kucita zimenezo, iye anaonetsa kuti ni wololela, wodzicepetsa, ndi wacifundo. Kuwonjezela apo, Mulungu sacita zinthu cifukwa ca mkwiyo, ngati mmene anthu ambili amacitila.
15. N’ciani cingatipangitse kusintha cosankha cimene tinapanga?
15 Nthawi zina, tingafunike kuganizilaponso pa cosankha cimene tinapanga. Tingacite zimenezi ngati zinthu zina zasintha. 1 Maf. 21:20, 21, 27-29; 2 Maf. 20:1-5) Tingadziŵenso mfundo zina zimene zingatipangitse kuona kuti ndi bwino kusintha zimene tinasankha. Mwacitsanzo, nthawi ina Mfumu Davide inauzidwa zinthu zolakwika zokhudza Mefiboseti, mdzukulu wa Sauli. Koma Davide atadziŵa zeni-zeni zokhudza Mefibosetiyo, anasintha maganizo ake. (2 Sam. 16:3, 4; 19:24-29) Ifenso nthawi zina tingacite bwino kusintha zosankha zathu.
Yehova anasintha maganizo ake pamene zinthu zinasintha. (16. (a) Ni malangizo ati amene angatithandize kupanga zosankha mwanzelu? (b) Kodi zosankha zimene tinapanga kale tifunika kuziona bwanji? Nanga n’cifukwa ciani tifunika kutelo?
16 Mau a Mulungu amatilangiza kuti sitifunika kupupuluma popanga zosankha zofunika kwambili. (Miy. 21:5) Timafunika kupatula nthawi yoganizila mosamala kwambili mfundo zosiyana-siyana zokhudzana ndi cosankha cimene tifuna kupanga. Tikacita conco, ndiye kuti zinthu zidzatiyendela bwino. (1 Thess. 5:21) Mutu wa banja asanasankhe zocita pa nkhani inayake, afunika kupeza nthawi yofufuza m’Malemba ndi m’zofalitsa zosiyana-siyana zacikhristu, ndiponso kufunsa ena m’banja lake kuti afotokozepo maganizo awo. Kumbukilani kuti Mulungu anauza Abulahamu kuti amvele zimene mkazi wake anakamba. (Gen. 21:9-12) Nawonso akulu afunika kupeza nthawi yofufuza asanapange zosankha. Ndipo ngati akulu ndi ololela ndi odzicepetsa, akapeza mfundo yoonetsa kuti afunika kusintha cosankha cawo, amasinthadi. Iwo saopa kuti ena angaleke kuwapatsa ulemu cifukwa cosintha zimene anasankha. Akulu afunika kukhala okonzeka kusintha maganizo awo ndi zosankha zawo ngati m’pofunika. Ndipo tonse tingacite bwino kutsatila citsanzo cawo. Kucita zimenezi kumathandiza kuti mumpingo mukhale bata ndi mtendele.—Mac. 6:1-4.
MUZIKWANILITSA ZIMENE MWASANKHA
17. N’ciani cingatithandize kuti tizipanga zosankha zabwino?
17 Zosankha zina zimakhala zazikulu kuposa zina. Ndipo zosankha zikulu-zikulu zimafunika kuziganizila mosamala ndi kuzipemphelela. Kucita zimenezi kungatenge nthawi yaitali. Akhristu ena amafunika kusankha kaya kukwatila kapena kukhala wosakwatila, ndiponso kusankha munthu amene adzakwatilana naye. Cosankha cina cacikulu, cimenenso cingatibweletsele madalitso, ndi cokhudza kuyamba utumiki wanthawi zonse. Pa zosankha ngati zimenezi, tifunika kudalila Yehova kuti atitsogolele ndi kutipatsa malangizo abwino amene angatithandize. (Miy. 1:5) Conco, tifunika kudalila malangizo anzelu a m’Baibo ndi kupempha Yehova kuti atitsogolele. Ndipo kumbukilani kuti Yehova angatithandize kukhala na makhalidwe amene angatithandize kupanga zosankha mogwilizana ndi cifunilo cake. Ngati mufuna kupanga cosankha cofunika, nthawi zonse muzidzifunsa kuti: ‘Kodi cosankha canga cidzaonetsa kuti nimakonda Yehova? Kodi cidzathandiza banja langa kukhala lacimwemwe ndi lamtendele? Nanga kodi cidzaonetsa kuti ndine woleza mtima ndi wokoma mtima?’
18. N’cifukwa ciani Yehova amafuna kuti tizidzipangila tokha zosankha?
18 Yehova satikakamiza kuti tizim’konda ndi kum’tumikila. Timacita kusankha tokha. Popeza anatilenga ndi ufulu wodzisankhila zocita, iye amalemekeza ufulu ndi udindo wathu ‘wosankha’ tokha kum’tumikila kapena ayi. (Yos. 24:15; Mlal. 5:4) Komabe, amafuna kuti tiziyesetsa kukwanilitsa zosankha zimene tinapanga mogwilizana ndi citsogozo cake. Ngati tidalila citsogozo ca Yehova na kutsatila mfundo zimene watipatsa, tidzatha kupanga zosankha mwanzelu ndipo sitidzakhala wokayika-kayika pa zocita zathu.—Yak. 1:5-8; 4:8.