“Munthu Wopatsa Mowolowa Manja Adzalandila Mphoto”
KUYAMBILA kale, anthu a Mulungu akhala akupeleka nsembe monga mbali ya kulambila koona. Mwacitsanzo, Aisiraeli anali kupeleka nsembe za nyama, ndipo Akhristu nthawi zonse akhala akupeleka nsembe zotamanda Mulungu. Komabe, pali nsembe zinanso zimene Mulungu amakondwela nazo. (Aheb. 13:15, 16) Nsembe zimenezi zimabweletsa cimwemwe na madalitso, monga mmene tidzaonela m’zitsanzo zotsatila.
Hana, mtumiki wokhulupilika wakale wa Mulungu, anali kufunitsitsa kukhala na mwana. Koma sanali kubeleka. Nthawi ina, iye popemphela anacita lumbilo pamaso pa Yehova kuti ngati adzakhala na mwana wamwamuna, ‘adzam’peleka kwa Yehova masiku onse a moyo wake.’ (1 Sam. 1:10, 11) M’kupita kwa nthawi, Hana anakhala na pakati, ndipo anabala mwana wamwamuna dzina lake Samueli. Samueli ataleka kuyamwa, Hana anapita kukam’peleka ku cihema, mogwilizana na lumbilo lake. Yehova anam’dalitsa Hana cifukwa ca kudzimana kwake. Iye anabalanso ana ena asanu, ndipo Samueli anakhala mneneli ndi wolemba Baibo.—1 Sam. 2:21.
Molingana na Hana na Samueli, ise Akhristu masiku ano tili na mwayi woseŵenzetsa moyo wathu potumikila Mlengi wathu. Yesu anakamba kuti ngati tidzimana zinthu zina cifukwa colambila Yehova, tidzadalitsidwa maningi.—Maliko 10:28-30.
M’nthawi ya atumwi, mkazi wina wacikhristu dzina lake Dorika anali kudziŵika ngako cifukwa ‘cocita nchito zabwino, na kupeleka mphatso zacifundo.’ Inde, anali wodzipeleka pothandiza ena. Koma n’zomvetsa cisoni kuti iye “anadwala n’kumwalila.” Zimenezi zinacititsa kuti mpingo wonse ukhale na cisoni. Ophunzila a Yesu atamvela kuti Petulo ali pafupi, anapita kukamupempha kuti abwele mwamsanga. Ganizilani cabe cisangalalo cimene ophunzilawo anakhala naco pamene Petulo anabwela na kuukitsa Dorika. Iye ni munthu woyamba wochulidwa m’Baibo amene anaukitsidwa na atumwi. (Mac. 9:36-41) Mulungu sanaiŵale zinthu zabwino zimene Dorika anacita. (Aheb. 6:10) Mbili ya kuwoloŵa manja kwake inalembewa m’Mau a Mulungu monga citsanzo cabwino cimene ise tonse tiyenela kutengela.
Nayenso mtumwi Paulo anapeleka citsanzo cabwino kwambili mwa kudzipeleka na kugwilitsila nchito nthawi yake pothandiza ena. Polembela Akhristu a ku Korinto, iye anati: “Koma ineyo ndidzagwilitsa nchito zinthu zanga zonse ndipo ndidzadzipeleka ndi moyo wanga wonse cifukwa ca miyoyo yanu.” (2 Akor. 12:15) Pa utumiki wake, Paulo anaphunzila kuti kudzipeleka pothandiza anthu ena kumabweletsa cimwemwe. Komanso kuposa pamenepo, kumapangitsa kuti Yehova atiyanje na kutidalitsa.—Mac. 20:24, 35.
N’zoonekelatu kuti Yehova amakondwela ngati tiseŵenzetsa nthawi na mphamvu zathu popititsa patsogolo zinthu za Ufumu na pothandiza okhulupilila anzathu. Nanga n’ciani cina cimene tingacite pocilikiza nchito yolalikila Ufumu? Kuwonjezela pa nchito zathu za cikondi, tingalemekeze Mulungu mwa kucita zopeleka zaufulu. Zopeleka zimenezi amaziseŵenzetsa popititsa patsogolo nchito yolalikila padziko lonse. Izi ziphatikizapo kucilikiza amishonale na atumiki a nthawi zonse apadela. Komanso, zopeleka zathu zaufulu zimathandiza pa nchito yokonza na kumasulila mabuku na mavidiyo, nchito yothandiza okhudzidwa na masoka, ndi yomanga Nyumba za Ufumu zatsopano. Sitiyenela kukayikila kuti “munthu wopatsa mowoloŵa manja adzalandila mphoto.” Kuwonjezela apo, Yehova amalemekezeka ngati tim’patsa zinthu zathu zamtengo wapatali.—Miy. 3:9; 11:25.