Coonadi ‘Sicibweletsa Mtendele Koma Lupanga’
“Musaganize kuti ndinabweletsa mtendele padziko lapansi, sindinabweletse mtendele koma lupanga.”—MAT. 10:34.
1, 2. (a) Ni mtendele wanji umene tingakhale nawo palipano? (b) N’ciani cimatilepheletsa kupeza mtendele weni-weni masiku ano? (Onani pikica pamwambapa.)
TONSE timafuna kukhala na umoyo wamtendele ndi wopanda nkhawa. Conco, timamuyamikila ngako Yehova cifukwa cotipatsa “mtendele wa Mulungu.” Umenewu ni mtendele wa m’maganizo umene umatiteteza ku nkhawa za paumoyo. (Afil. 4:6, 7) Komanso cifukwa ca kudzipeleka kwathu kwa Yehova, tili “pa mtendele ndi Mulungu,” kapena kuti pa ubale wabwino na iye.—Aroma 5:1.
2 Ngakhale n’conco, nthawi yakuti Mulungu abweletse mtendele weni-weni sinakwane. Masiku otsiliza ano, mikangano ili ponse-ponse, ndipo anthu ambili safuna kugwilizana ndi anzawo. (2 Tim. 3:1-4) Kuwonjezela apo, ise Akhristu tili pa nkhondo yauzimu yolimbana ndi Satana na ziphunzitso zonama zimene amafalitsa. (2 Akor. 10:4, 5) Koma vuto lalikulu limene lingasokoneze mtendele wathu, lingacokele kwa acibululu osakhulupilila. Ena angayambe kunyoza zikhulupililo zathu, kutiimba mlandu wakuti tagaŵanitsa banja, kapena kutiopseza kuti adzatikana ngati tipitiliza kucita zimene timakhulupilila. Zikakhala conco, kodi tizikhala na kaonedwe kotani pokumana ndi citsutso ca m’banja? Nanga mavuto ake tingathane nawo bwanji?
PAMENE ACIBULULU ATITSUTSA
3, 4. (a) Kodi ziphunzitso za Yesu zimawakhudza bwanji anthu? (b) Ni liti pamene kutsatila Yesu kungakhale kovuta kwambili?
3 Yesu anadziŵa kuti ziphunzitso zake zidzagaŵanitsa anthu. Anadziŵanso kuti otsatila ake adzafunika kukhala olimba mtima kuti akhalebe okhulupilika pamene akutsutsidwa. Citsutso cimeneci cingasokoneze mgwilizano pakati pa otsatila ake na abululu awo. Yesu anati: “Musaganize kuti ndinabweletsa mtendele padziko lapansi, sindinabweletse mtendele koma lupanga. Pakuti ndinabwela kudzagawanitsa anthu. Ndinabwela kudzacititsa munthu kutsutsana ndi bambo ake, mwana wamkazi kutsutsana ndi mayi ake, ndiponso mtsikana wokwatiwa kutsutsana ndi apongozi ake aakazi. Kunena zoona, adani a munthu adzakhala a m’banja lake lenileni.”—Mat. 10:34-36.
4 Pamene Yesu anakamba kuti, “Musaganize kuti ndinabweletsa mtendele,” anatanthauza kuti omvela ake anafunika kuganizila mavuto amene angakumane nawo cifukwa comutsatila. Uthenga wake unali kudzagaŵanitsa anthu. Koma sikuti colinga ca Yesu cinali cofuna kuwononga cibululu ca anthu. Colinga cake cinali kulengeza uthenga wa Mulungu wonena za coonadi. (Yoh. 18:37) Komabe, kukhala wokhulupilika ku ziphunzitso za Khristu kungakhale kovuta ngati mnzathu wapamtima kapena m’bululu wathu amakana coonadi.
5. Kodi ophunzila a Yesu akhala akukumana na mavuto anji?
5 Limodzi mwa mavuto amene Yesu anakamba kuti otsatila ake afunika kuwapilila ni citsutso ca m’banja. (Mat. 10:38) Kuti akhale oyenela Khristu, ophunzila ake akhala akupilila mavuto monga kunyozewa, kapena kusankhiwa na anthu a m’banja lawo. Ngakhale n’conco, apeza madalitso ambili poyelekezela na zimene ataya.—Ŵelengani Maliko 10:29, 30.
6. Kodi tiyenela kukumbukila ciani ngati acibululu akutitsutsa cifukwa colambila Yehova?
6 Ngati abululu athu amatitsutsa cifukwa colambila Yehova, tifunika kupitiliza kuwakonda. Koma tifunika kuika patsogolo cikondi cathu pa Mulungu na Khristu. (Mat. 10:37) Tikumbukilenso kuti Satana angaloŵele ku cikondi ca pacibululu kuti awononge cikhulupililo cathu. Tiyeni tikambilane za mavuto obwela cifukwa ca citsutso ca m’banja, na zimene tingacite kuti tithane nawo.
MNZANU WA M’CIKWATI WOSAKHULUPILILA
7. Kodi amene ali m’cikwati na mnzawo wosakhulupilila afunika kukhala na kaonedwe kotani?
7 Baibo imacenjeza kuti amene aloŵa m’banja “adzakhala ndi nsautso m’thupi mwawo.” (1 Akor. 7:28) Ngati mwamuna kapena mkazi wanu ni wosakhulupilila, nkhawa na mavuto zimakhala zoculukilapo m’banja. Ngakhale n’conco, muyenela kuona zinthu mmene Yehova amazionela. Ngati palipano mnzanu wa m’cikwati safuna kukhala wotsatila Khristu, sindiye kuti muli na cifukwa comveka copatukilana kapena kusudzulana naye. (1 Akor. 7:12-16) Ngakhale kuti mwamuna wosakhulupilila sangatsogolele banja lake pa zinthu zauzimu, iye afunikabe kulemekezedwa cifukwa ni mutu wa banja. N’cimodzi-modzinso na mkazi wosakhulupilila. Iye afunika kuonetsedwa cikondi ceni-ceni na mwamuna wake wacikhristu.—Aef. 5:22, 23, 28, 29.
8. Ni mafunso ati amene mungadzifunse ngati mwamuna kapena mkazi wanu akukuikilani malile pa nkhani ya kulambila?
8 Nanga bwanji ngati mwamuna kapena mkazi wanu wosakhulupilila akukuikilani malile pa kulambila kwanu? Mwacitsanzo, mlongo wina, mwamuna wake anamuuza kuti azipita mu ulaliki pa masiku amene mwamunayo anamulamula. Ngati inunso mukumana na vuto laconco, dzifunseni kuti: ‘Kodi mwamuna kapena mkazi wanga akuniletsa kulambila Mulungu? Ngati siconco, kodi sicingakhale bwino kuvomeleza zimene waniuza?’ Kukhala wololela kungakuthandizeni kupewa kukangana pa zilizonse m’banja.—Afil. 4:5.
9. Kodi Akhristu angaphunzitse bwanji ana awo kuti azilemekeza kholo losakhulupilila?
Aef. 6:1-3) Koma bwanji ngati mnzanu wa m’cikwati satsatila mfundo za m’Baibo za makhalidwe abwino? Khalani citsanzo cabwino mwa kumulemekeza. Muziyang’ana kwambili pa makhalidwe ake abwino, ndipo muzimuyamikila. Pewani kukamba zinthu zoipitsa mnzanu wa m’cikwati mukakhala pamodzi ndi ana. M’malomwake, afotokozeleni kuti munthu aliyense ali na ufulu wosankha kutumikila Yehova kapena ayi. Ngati ana ali na makhalidwe abwino, kholo losakhulupilila lingakopeke n’kuyamba kulambila Mulungu.
9 Kuphunzitsa ana kungakhale kovuta kwambili ngati mnzanu wa m’cikwati ni wosakhulupilila. Mwacitsanzo, mumafunika kuphunzitsa ana anu kumvela lamulo la m’Baibo lakuti: “Uzilemekeza bambo ako ndi mayi ako.” (10. Kodi makolo acikhristu angaphunzitse bwanji ana awo ngati mnzawo wa m’cikwati si Mboni?
10 Nthawi zina, mnzanu wa m’cikwati amene si Mboni angafune kuti ana azicitako zikondwelelo zacikunja, mwinanso kuti aziphunzila zikhulupililo za cipembedzo conama. Amuna ena amaletsa akazi awo acikhristu kuphunzitsa ana Baibo. Ngakhale n’conco, mkazi wacikhristu amacita zimene angathe kuti aphunzitse ana coonadi. (Mac. 16:1; 2 Tim. 3:14, 15) Mwacitsanzo, mwamuna wosakhulupilila, angaletse mkazi wacikhristu kucititsa phunzilo la Baibo lokhazikika kwa ana awo aang’ono, kapena kupita nawo ku misonkhano yacikhristu. Mkazi angafunike kulemekeza zosankha za mwamuna wake wosakhulupilila. Komabe, akapeza mpata, mkaziyo afunika kuwaphunzitsa coonadi anawo. Mwanjila imeneyi, amawathandiza kuti akule na makhalidwe abwino ndiponso kuti adziŵe Yehova. (Mac. 4:) Ngakhale n’conco, m’kupita kwa nthawi anawo adzafunika kupanga okha cosankha pankhani ya kulambila.— 19, 20Deut. 30:19, 20. *
ACIBULULU AMENE SAGWILIZANA NDI KULAMBILA KOONA
11. N’ciani cingacititse kusamvana pakati pa ise na acibululu amene si Mboni?
11 Pamene tinayamba kuphunzila Baibo, mwina abululu athu sitinawauze kuti tayamba kugwilizana ndi Mboni za Yehova. Koma pamene cikhulupililo cathu cinayamba kukula, tinaona kuti tifunika kuwauza za colinga cathu cotumikila Yehova. (Maliko 8:38) Ngati cosankha cathu cacititsa kuti pakhale kusamvana pakati pa ise na abululu athu amene si Mboni, tingacite ciani kuti ticepetse mikangano na kukhalabe okhulupilika? Tiyeni tikambilane zimene tingacite.
12. N’ciani cingapangitse abululu athu osakhulupilila kutitsutsa? Nanga tingaonetse bwanji kuti timawaganizila?
12 Tiziwaganizila acibululu osakhulupilila. Tingakondwele ngako na coonadi ca m’Baibo cimene taphunzila, koma abululu athu angaganize kuti tapusitsidwa kapena taloŵa m’kagulu kampatuko. Iwo angaganize kuti taleka kuwakonda poona kuti siticita nawo zikondwelelo za pa maholide. Angayambenso kudela nkhawa za tsogolo lathu. Zikakhala conco, tifunika kuonetsa kuti timawaganizila mwa kuyesetsa kuona zinthu mmene iwo akuzionela, ndi kuwamvetsela mwachelu kuti tidziŵe cimene cikuwadetsa nkhawa kweni-kweni. (Miy. 20:5) Mtumwi Paulo anayesetsa kucita zinthu ndi “anthu osiyanasiyana” mowaganizila n’colinga cakuti awalalikile uthenga wabwino. Kucita zinthu mwanjila imeneyi nafenso kungatithandize.—1 Akor. 9:19-23.
13. Kodi acibululu osakhulupilila tizikamba nawo bwanji?
13 Muzikamba nawo mofatsa. Baibo imakamba kuti: “Nthawi zonse mau anu azikhala acisomo.” (Akol. 4:6) Tiyenela kupempha Yehova kuti atipatse mzimu wake woyela kuti utithandize kukhala ofatsa ndi okoma mtima pokamba na abululu athu. Tisamangotsutsa ziphunzitso zilizonse zabodza zimene amakhulupilila. Ngati zokamba kapena zocita zawo zatikhumudwitsa, tifunika kutengela citsanzo ca atumwi. Paulo analemba kuti: “Pamene akutinenela zacipongwe, timadalitsa. Pozunzidwa, timapilila. Ponyozedwa, timayankha mofatsa.”—1 Akor. 4:12, 13.
14. Ni mapindu anji amene tingapeze ngati tipitiliza kukhala na khalidwe labwino?
14 Muzikhala na khalidwe labwino. Kukamba mofatsa pamene ticita zinthu ndi acibululu amene akutitsutsa kumathandiza. Koma khalidwe lathu labwino, n’limene lingathandize ngako. (Ŵelengani 1 Petulo. 3:1, 2, 16) Zocita zanu zidzathandiza abululu anu kuona kuti a Mboni za Yehova amakhala na vikwati vabwino, amasamalila bwino ana awo, amakhala aukhondo ndi akhalidwe labwino, ndiponso amakhala na umoyo wacimwemwe. Ngakhale abululu athu atapanda kuphunzila coonadi, tingakhale na cimwemwe podziŵa kuti Yehova amakondwela pamene timutumikila mokhulupilika.
15. Kodi tingakonzekele bwanji zocitika zimene zingayambitse mikangano?
15 Muzikhala okonzeka. Ganizilani zocitika zimene zingayambitse mikangano, ndipo pezani njila ya mmene mungazithetsele. (Miy. 12:16, 23) Mlongo wina wa ku Australia anati: “Apongozi anga aamuna anali kutsutsa kwambili coonadi. Conco, ine na mwamuna wanga tikafuna kupita kukawaona, tinali kupemphela kwa Yehova kuti akatithandize kuyankha modekha ngati atikambitsa mwaukali. Tinali kukonzekelatu nkhani zokakamba nawo poceza kuti maceza athu akayende bwino. Komanso, tinali kupangana pasadakhale za nthawi imene tikacokeko. Tinali kucita izi pofuna kupewa maceza amtatakuya, amene akanacititsa kuti tiyambe kukangana pa nkhani za cipembedzo.”
16. Mungacite ciani ngati mumadela nkhawa kuti zocita zanu zidzakhumudwitsa abululu anu?
Yes. 48:17, 18.
16 N’zosatheka kupewelatu vuto la kusemphana maganizo na acibululu anu osakhulupilila. Vuto limeneli lingakucititseni kudziimba mlandu, cifukwa cakuti mumawakonda kwambili abululu anuwo, ndipo mwakhala mukuyesa-yesa kuwacitila zinthu zabwino. Ngati mumamvela conco, yesetsani kucita zinthu zoonetsa kuti mumaona kukhulupilika kwanu kwa Yehova kukhala kofunika kwambili kuposa cikondi ca pacibululu. Kucita zinthu mwanjila imeneyi kudzathandiza abululu anu kuona kuti kutumikila Yehova n’kofunika ngako. Mulimonse mmene zingakhalile, sitiyenela kuwakakamiza kuphunzila coonadi. M’malomwake, aloleni kuti adzionele okha mmene kutsatila mfundo za Yehova kwakuthandizilani. Kumbukilani kuti nawonso, Mulungu wathu wacikondi anawapatsa ufulu wodzisankhila njila imene afuna kuyendamo.—NGATI WA M’BANJA WASIYA YEHOVA
17, 18. N’ciani cingakuthandizeni kupilila ngati wa m’banja wasiya Yehova?
17 Wa m’banja akacotsedwa mumpingo kapena akadzilekanitsa, zimapweteka kwambili mumtima cakuti munthu angamvele monga walasiwa na lupanga. N’ciani cingakuthandizeni kupilila vuto limeneli?
18 Musaleke kucita zinthu zauzimu. Pitilizani kulimbitsa cikhulupililo canu mwa kuŵelenga Baibo, kukonzekela misonkhano na kupezekapo, kulalikila, ndi kupemphela kwa Mulungu kuti akupatseni mphamvu zokuthandizani kupilila. (Yuda 20, 21) Nanga bwanji ngati muona kuti zimene mumacita sizicokela pansi pa mtima, koma mumangozicita mwamwambo cabe? Musagwe mphwayi! Kukhala na cizoloŵezi cocita zinthu zauzimu kungakuthandizeni kuti mukhalenso na maganizo oyenela, ndiponso kuti musamakhale na nkhawa kwambili. Ganizilani zimene zinacitikila wolemba Salimo 73. Iye anayamba kuona zinthu mosayenela, ndipo anavutika maganizo kwambili. Koma anasintha maganizo olakwikawo pamene analoŵa m’malo a Mulungu olambilila. (Sal. 73:16, 17) Inunso ngati mulambila Yehova mokhulupilika, mungakhale na maganizo oyenela.
19. Tingaonetse bwanji kuti timalemekeza makonzedwe a Yehova opelekela cilango kwa anthu osalapa?
19 Onetsani kuti mukugwilizana ndi cilango ca Yehova. Kucotsa munthu wosalapa mumpingo kumabweletsa madalitso okhalitsa kwa onse, kuphatikizapo kwa wolakwayo, ngakhale kuti poyamba cilangoco cimakhala coŵaŵa. (Ŵelengani Aheberi 12:11.) Mwacitsanzo, Yehova amatilangiza kuti tifunika ‘kuleka kuyanjana’ ndi anthu ocita zoipa amene safuna kulapa. (1 Akor. 5:11-13) Ngakhale kuti cimaŵaŵa mumtima, tifunika kupewa kukambitsana kosafunikila ndi wa m’banja wocotsedwa, kaya m’pa foni, pa meseji, m’kalata, kapena pa intaneti.
20. Kodi tifunika kukhalabe na ciyembekezo cotani?
20 Khalanibe na ciyembekezo. Cikondi “cimayembekezela zinthu zonse,” kuphatikizapo zakuti anthu amene anasiya Yehova adzabwelela kwa iye. (1 Akor. 13:7) Ngati mwaona zizindikilo zakuti wa m’banja lanu wocotsedwa wayamba kusintha, mungamupemphelele kuti apeze mphamvu kucokela m’Malemba, ndi kuti alabadile ciitano ca Yehova cakuti: “Bwelela kwa ine.”—Yes. 44:22.
21. Kodi muyenela kucita ciani ngati mwayamba kusiyana maganizo ndi a m’banja lanu cifukwa cotsatila Yesu?
21 Yesu anakamba kuti ngati tikonda anthu ena koposa iye, ndiye kuti sindife oyenela iye. Komabe, anali na cidalilo cakuti ophunzila ake adzalimba mtima ndi kukhalabe okhulupilika olo atakumana ndi citsutso ca m’banja. Ngati kutsatila Yesu kwabweletsa “lupanga” m’banja lanu, dalilani Yehova kuti akuthandizeni kupilila. (Yes. 41:10, 13) Khalani osangalala podziŵa kuti Yehova na Yesu amakondwela namwe, ndipo adzakudalitsani cifukwa ca kukhulupilika kwanu.
^ par. 10 Kuti mudziŵe zambili pa nkhani yophunzitsa ana ngati mnzanu wa m’cikwati si Mboni, onani “Mafunso Ocokela kwa Oŵelenga” mu Nsanja ya Olonda, ya August 15, 2002.