Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

‘Limba Mtima, Ugwile Nchito Mwamphamvu’

‘Limba Mtima, Ugwile Nchito Mwamphamvu’

“Limba mtima, ugwile nchitoyi mwamphamvu. Usaope kapena kucita mantha cifukwa Yehova . . . ali ndi iwe.”—1 MBIRI 28:20.

NYIMBO: 38, 34

1, 2. (a) Kodi Solomo anapatsidwa nchito iti yofunika kwambili? (b) N’cifukwa ciani Davide anam’dela nkhawa Solomo?

SOLOMO analangizidwa kuti ayang’anile nchito yofunika kwambili yomanga imene inali isanacitikepo n’kale lonse. Nchitoyo inali yomanga kacisi ku Yerusalemu. Kacisiyo anafunika kukhala ‘wokongola, waulemelelo wosaneneka ndiponso wochuka ndi wotamandika kumayiko onse.’ Koposa zonse, kacisiyo anali kudzakhala “nyumba ya Yehova Mulungu woona.” Yehova analamula kuti Solomo ayang’anile nchito yomanga imeneyi.—1 Mbiri 22:1, 5, 9-11.

2 Mfumu Davide anali kukhulupilila kuti Mulungu adzam’thandiza Solomo panchitoyo. Koma panthawiyo, Solomo anali “wamng’ono komanso wosakhwima.” Kodi iye akanalimba mtima kumanga kacisiyo? Kapena akanaopa cifukwa cakuti anali wamng’ono ndi wosakhwima? Kuti akwanitse nchitoyo, Solomo anafunika kukhala wolimba mtima ndi kugwila nchito mwamphamvu.

3. Kodi Solomo ayenela kuti anaphunzila ciani kwa atate wake pankhani ya kulimba mtima?

3 Solomo ayenela kuti anaphunzila zambili kwa atate wake pankhani ya kulimba mtima. Pamene Davide anali wacicepele, anapha zilombo zoopsa zimene zinagwila nkhosa za atate wake. (1 Sam. 17:34, 35) Anaonetsanso kulimba mtima kwambili pamene anamenyana ndi ciphona codziŵa bwino nkhondo. Mothandizidwa na Mulungu, Davide anakwanitsa kugonjetsa Goliyati ndi mwala umodzi cabe wosalala.—1 Sam. 17:45, 49, 50.

4. N’cifukwa ciani Solomo anafunika kukhala wolimba mtima?

4 Conco, m’pomveka kuti Davide analangiza Solomo kukhala wolimba mtima kuti amange kacisi. (Ŵelengani 1 Mbiri 28:20.). Solomo anafunika kukhala wolimba mtima kuti akwanitse kugwila nchito imene anapatsidwa mpaka kuitsiliza. Akanakhala wamantha, sembe analephelelatu nchitoyo.

5. N’cifukwa ciani tifunika kukhala olimba mtima?

5 Mofanana ndi Solomo, timafunika thandizo la Yehova kuti tikhale olimba mtima ndi kugwila nchito imene watipatsa. Kuti tikwanitse kucita zimenezi, tifunika kuganizila zitsanzo za anthu akale amene anacita zinthu molimba mtima. Tifunikanso kuganizila mmene tingaonetsele kulimba mtima kuti tikwanitse kugwila nchito imene tapatsidwa.

ANTHU AMENE ANACITA ZINTHU MOLIMBA MTIMA

6. N’ciani cimakucititsani cidwi na kulimba mtima kwa Yosefe?

6 Ganizilani kulimba mtima kumene Yosefe anaonetsa pamene mkazi wa Potifara anamunyengelela kuti acite naye ciwelewele. Mwacionekele, iye anadziŵa kuti angakumane ndi mavuto aakulu akakana kugona naye. Ngakhale n’conco, iye sanagonje, koma anaonetsa kulimba mtima mwa kum’thawa mkaziyo.—Gen. 39:10, 12.

7. Kodi Rahabi anaonetsa bwanji kulimba mtima? (Onani pikica kuciyambi.)

7 Rahabi nayenso anacita zinthu molimba mtima. Pamene “azondi” aciisiraeli anabwela ku nyumba kwake ku Yeriko, sembe iye anacita mantha ndipo sakanawalandila. Koma cifukwa codalila Yehova, molimba mtima anabisa amuna aŵiliwo ndi kuwathandiza kuti abwelele kwawo bwino-bwino. (Yos. 2:4, 5, 9, 12-16) Rahabi anali kukhulupilila kuti Yehova ndiye Mulungu woona, ndipo anali na cidalilo cakuti adzapeleka dzikolo kwa Aisiraeli. Iye sanalephele kulandila azondiwo cifukwa coopa mfumu ya Yeriko ndi anthu ake. Koma anacita zimene zinapulumutsa iye ndi a m’banja lake.—Yos. 6:22, 23.

8. Kodi kulimba mtima kwa Yesu kunawathandiza bwanji atumwi?

8 Atumwi okhulupilika a Yesu nawonso anapeleka citsanzo cabwino kwambili ca kukhala olimba mtima. Iwo anaona mmene Yesu anaonetsela kulimba mtima. (Mat. 8:28-32; Yoh. 2:13-17; 18:3-5) Citsanzo cake cinawathandiza kukhala olimba mtima. Pamene atumwi anali kutsutsidwa ndi Asaduki, sanaleke kuphunzitsa m’dzina la Yesu.—Mac. 5:17, 18, 27-29.

9. Malinga ni 2 Timoteyo 1:7, ndani maka-maka amene angatithandize kukhala olimba mtima?

9 Kulimba mtima kunathandiza Yosefe, Rahabi, Yesu, ndi atumwi kucita zinthu zoyenela. Anthu amenewa anakwanitsa kucita zinthu molimba mtima, osati cifukwa codzidalila, koma cifukwa codalila Yehova. Ifenso timakumana ndi zinthu zina mu umoyo wathu zimene zimafuna kuti ticite zinthu molimba mtima. Tikakumana ndi zinthu zaconco, sitifunika kudzidalila, koma tifunika kudalila Yehova. (Ŵelengani 2 Timoteyo 1:7.) Tsopano tiyeni tikambilane mmene tingaonetsele kulimba mtima m’banja ndi mumpingo.

ZOCITIKA ZIMENE ZIMAFUNA KUTI TIKHALE OLIMBA MTIMA

10. N’cifukwa ciani Akhristu acicepele afunika kukhala olimba mtima?

10 Akhristu acicepele amakumana ndi zinthu zambili zimene zimafuna kuti akhale olimba mtima kuti akwanitse kutumikila Yehova. Iwo angacite bwino kutsatila citsanzo cabwino ca Solomo. Iye anaonetsa kulimba mtima mwa kupanga zosankha mwanzelu zokhudza nchito yomanga kacisi. Akhristu acicepele afunika kulandila malangizo kucokela kwa makolo awo. Komabe, iwo ali na udindo wopanga zosankha pa nkhani zina zofunika kwambili. (Miy. 27:11) Acicepele amafunika kukhala olimba mtima kuti apewe mabwenzi oipa ndi kukana zosangalatsa zosayenela. Amafunikanso kukhala olimba mtima kuti apewe makhalidwe oipa ndi kuti apange cosankha cobatizika. Kucita zimenezi kumafuna kukhala wolimba mtima cifukwa n’kosemphana ndi cifunilo ca Satana, amene amatonza Mulungu.

11, 12. (a) N’cifukwa ciani Mose ni citsanzo cabwino ca kulimba mtima? (b) Kodi acicepele angatengele bwanji citsanzo ca Mose?

11 Cosankha cimodzi cofunika kwambili cimene acicepele amafunika kupanga ndi cokhudza zolinga zawo. M’maiko ena, acicepele amakakamizidwa kukhala na zolinga monga kucita maphunzilo apamwamba ndi kupeza nchito ya ndalama zambili. Koma m’maiko ena, mavuto a zacuma amacititsa acicepele kuona kuti afunika kuthandizila makolo awo kupeza zofunika pa banja. Imwe acicepele, ngati umu ni mmene zinthu zilili mu umoyo wanu, mungacite bwino kuganizila citsanzo ca Mose. Popeza kuti Mose analeledwa ndi mwana wa Farao, akanafuna akanakhala na colinga cokhala wochuka ndi wolemela. Mwacionekele, makolo ake aciiguputo, aphunzitsi, ndi alangizi anali kumulimbikitsa kukhala na zolinga zimenezi. Koma Mose sanagonje, ndipo molimba mtima anasankha kucilikiza kulambila koona. Pamene Mose anasiya cuma ca Iguputo, anadalila Yehova. (Aheb. 11:24-26) Pa cifukwa cimeneci, Yehova anam’dalitsa, ndipo mosakayikila m’tsogolo adzalandila madalitso ena owonjezeleka.

12 Mofananamo, Yehova adzadalitsa acicepele onse amene amayesetsa molimba mtima kudziikila zolinga zauzimu ndi kuika Ufumu wa Mulungu patsogolo mu umoyo wawo. Komanso akadzaloŵa m’banja, Mulungu adzawathandiza kupeza zosoŵa za mabanja awo. M’zaka 100 zoyambilila, wacicepele Timoteyo anayesetsa kukwanilitsa zolinga zake zauzimu. Inunso mungakwanilitse zolinga zanu zauzimu. *Ŵelengani Afilipi 2:19-22.

Kodi mudzayesetsa kukhala olimba mtima m’mbali zonse za umoyo wanu? (Onani palagilafu 13-17)

13. Kodi kulimba mtima kunamuthandiza bwanji mlongo wina wacicepele kukwanilitsa zolinga zake?

13 Mlongo wina ku Alabama, m’dziko la United States anafunika kulimba mtima kuti adziikile zolinga zauzimu ndi kuzikwanilitsa. Iye analemba kuti: “Pamene n’nali wamng’ono, n’nali wamanyazi kwambili. N’nali kuyopa ngakhale kukamba na abale na alongo pa Nyumba ya Ufumu. Maka-maka kugogoda pa makomo a anthu osawadziŵa mu ulaliki, zinali kunivuta kwambili.” Mothandizidwa na makolo ake ndi ena mumpingo, mlongo wacicepeleyu anakwanilitsa colinga cake cokhala mpainiya wanthawi zonse. Iye anati: “Anthu a m’dziko la Satanali amalimbikitsa acicepele kucita maphunzilo apamwamba, kukhala ochuka, ndi kukhala na cuma coculuka, ndipo amati zimenezi ndiye zolinga zabwino. Nthawi zambili, anthu amene amakhala na zolinga zimenezi sazikwanilitsa, ndipo amakhala na nkhawa kwambili komanso amapwetekedwa mtima. Koma kutumikila Yehova kwanibweletsela cimwemwe cacikulu, ndipo nimakhala okhutila na zimene nacita.”

14. Ni pa zocitika zina ziti pamene makolo acikhristu amafunika kukhala olimba mtima?

14 Nawonso makolo acikhristu afunika kukhala olimba mtima. Mwacitsanzo, abwana anu kunchito angamakupempheni kaŵili-kaŵili kuti mugwile nchito ya ovataimu m’madzulo kapena kumapeto kwa wiki, nthawi imene mumacita kulambila kwa pabanja, kupita mu ulaliki, ndi kupezeka pa misonkhano. Mufunika kukhala wolimba mtima kuti mukwanitse kukana mapempho obweleza-bweleza amenewo, ndi kupeleka citsanzo cabwino kwa ana anu. N’kuthekanso kuti makolo ena mumpingo amalola ana awo kucita zinthu zina zimene imwe simufuna kuti ana anu azicita. Makolo amenewo angakufunseni cifukwa cake simulola anawo kutengako mbali m’zocitika zimenezo. Kodi mudzalimba mtima ndi kuwafotokozela mosamala cifukwa cake mumawaletsa?

15. Kodi malemba awa: Salimo 37:25 ndi Aheberi 13:5, angathandize bwanji makolo?

15 Makolo angaonetsenso kulimba mtima mwa kuthandiza ana awo kudziikila zolinga zauzimu ndi kuzikwanilitsa. Mwacitsanzo, makolo ena amaopa kulimbikitsa ana awo kucita upainiya, kukatumikila kosoŵa, kukatumikila pa Beteli, kapena kugwilako nchito yomanga nyumba zolambilila. Makolowo angacite mantha poganiza kuti akadzakalamba, mwana wawo sadzakwanitsa kuwasamalila. Komabe, makolo anzelu amacita zinthu molimba mtima ndipo amakhulupilila malonjezo a Yehova. (Ŵelengani Salimo 37:25; Aheberi 13:5.) Conco, njila ina imene inu makolo mungaonetsele kuti ndinu olimba mtima komanso kuti mumadalila Yehova ndi mwa kuthandiza ana anu kudziikila zolinga zauzimu na kuzikwanilitsa.—1 Sam. 1:27, 28; 2 Tim. 3:14, 15.

16. Kodi makolo ena athandiza bwanji ana awo kukhala na zolinga zauzimu? Nanga apeza mapindu anji cifukwa cocita zimenezi?

16 Makolo ena ku United States anathandiza ana awo kukhala na zolinga zauzimu. Atate a anawo anakamba kuti: “Ana athu asanayambe kuyenda na kukamba, tinali kuwauza za cimwemwe cimene munthu amakhala naco ngati acita upainiya ndi kutumikila mumpingo. Lomba, iwo ali na colinga cocita upainiya. Kukhala na zolinga zauzimu na kuzikwanilitsa kwathandiza ana athu kuti asagonje ku zokopa za m’dziko la Satanali. Kwawathandizanso kuika maganizo awo pa kutumikila Yehova.” M’bale wina amene ali ndi ana aŵili anati: “Makolo ambili amacita khama ndi kuwononga cuma cawo pothandiza ana awo kuti akhale akatswili a zamaseŵela ndi zosangalatsa zina, ndiponso kuti akhale ophunzila kwambili. Niona kuti ni cinthu canzelu kwambili kucita khama ndi kugwilitsila nchito cuma cathu pothandiza ana kukwanilitsa zolinga zimene zidzawathandiza kukhalabe pa ubwenzi wabwino na Yehova. Timasangalala kwambili kuona ana athu akukwanilitsa zolinga zawo zauzimu, ndipo zimakhala ngati kuti nafenso tikulandila nawo madalitso.” Ndithudi, Mulungu adzadalitsa makolo amene akuthandiza ana awo kukhala na zolinga zauzimu na kuzikwanilitsa.

KUKHALA WOLIMBA MTIMA MUMPINGO

17. Fotokozani njila zina zimene tingaonetsele kulimba mtima mumpingo.

17 Timafunikanso kucita zinthu molimba mtima mumpingo. Mwacitsanzo, akulu amafunika kucita zinthu molimba mtima pamene asamalila nkhani zaciweluzo, kapena pothandiza abale na alongo odwala mwakaya-kaya. Akulu ena amayendela akaidi m’ndende kuti akawaphunzitse Baibo kapena kukacititsa misonkhano. Nanga bwanji alongo amene ni mbeta? Iwo ali na mipata yambili yofutukulila utumiki wawo mwa kucita upainiya, kukatumikila kosoŵa, kugwila nchito ya cimango mogwilizana ndi Dipatimenti Yoona za Mapulani ndi Zomangamanga, komanso kufunsila kukaloŵa Sukulu ya Alengezi a Ufumu. Alongo ena amene ni mbeta afika ngakhale poloŵa Sukulu ya Giliyadi.

18. Kodi alongo acikulile angaonetse bwanji kulimba mtima?

18 Nawonso alongo acikulile ni dalitso mumpingo. Timawakonda kwambili alongo athu amenewa. Ena mwa iwo sangacite zambili potumikila Mulungu poyelekezela na mmene anali kucitila kale. Koma angaonetsebe kulimba mtima ndi kugwila nchito mwamphamvu. (Ŵelengani Tito 2:3-5.) Mwacitsanzo, mlongo wacikulile angafunike kukhala wolimba mtima ngati wapemphedwa kuti akathandize mlongo wacicepele pankhani ya kavalidwe koyenela. Iye sayenela kukalipila mlongoyo cifukwa covala mosayenela, koma angamulimbikitse kuganizila mmene kavalidwe kake kangakhudzile anthu ena. (1 Tim. 2:9, 10) Kukamba naye mwacikondi, kungamuthandize kuwongolela.

19. (a) Kodi abale obatizika angaonetse bwanji kulimba mtima? (b) Kodi malemba awa: Afilipi 2:13 ndi Afilipi 4:13, angathandize bwanji abale kukhala olimba mtima?

19 Abale obatizika nawonso ayenela kukhala olimba mtima ndi kugwila nchito mwamphamvu. Amuna olimba mtima amene amadzipeleka kulandila maudindo ni dalitso mumpingo. (1 Tim. 3:1) Komabe, abale ena amaopa kukalamila maudindo. Mwina angaope cifukwa cakuti analakwitsa zina zake m’mbuyomu, ndipo angaone kuti sangayenelele kutumikila monga mtumiki wothandiza kapena mkulu. Kapena angaope cifukwa coganiza kuti sangakwanitse kusamalila udindo. Ngati nanunso mumaona conco, Yehova angakuthandizeni kukhala wolimba mtima. (Ŵelengani Afilipi 2:13; 4:13.) Kumbukilani Mose. Iye panthawi ina anaona kuti sangakwanitse kugwila nchito imene anapatsidwa. (Eks. 3:11) Koma Yehova anamuthandiza, ndipo m’kupita kwa nthawi, analimba mtima ndi kugwila nchitoyo. Mofananamo, m’bale wobatizika akhoza kukhala wolimba mtima ngati apempha thandizo kwa Mulungu mwa kupemphela mocokela pansi pa mtima ndi kuŵelenga Baibo tsiku na tsiku. Cinanso cimene cingathandize ndi kuganizila zitsanzo za anthu akale olimba mtima. Komanso, angapemphe akulu kuti amuphunzitse nchito ndi kudzipeleka kugwila nchito ina iliyonse mumpingo imene ingafunike. Tikukulimbikitsani abale nonse obatizika kuti mukhale olimba mtima, ndipo mugwile nchito mwamphamvu pothandiza mpingo.

“YEHOVA . . . ALI NDI IWE”

20, 21. (a) Kodi Davide anamutsimikizila za ciani Solomo? (b) Nanga ise tingakhale otsimikiza za ciani?

20 Mfumu Davide anauza Solomo kuti Yehova adzakhala naye mpaka pamene adzatsiliza kugwila nchito yomanga kacisi. (1 Mbiri 28:20) Zimene atate wake anakamba zinam’limbikitsa kwambili Solomo, ndipo anakwanitsa kugwila nchitoyo ngakhale kuti anali wamng’ono ndi wosakhwima. Iye anacita zinthu molimba mtima, anagwila nchito mwamphamvu, ndipo mothandizidwa na Yehova, anatsiliza nchito yomanga kacisi waulemeleloyo m’zaka 7 na hafu.

21 Monga mmene Yehova anathandizila Solomo, nafenso akhoza kutithandiza kukhala olimba mtima ndi kugwila nchito yathu m’banja ndi mumpingo. (Yes. 41:10, 13) Tikamacita zinthu molimba mtima polambila Yehova, tingakhale na cidalilo cakuti tidzapeza madalitso tsopano ndi mtsogolo. Conco, ‘limbani mtima, ndipo mugwile nchito mwamphamvu.’

^ par. 12 Mungapeze malangizo ena othandiza pa nkhani ya kukhala na zolinga zauzimu m’nkhani yakuti “Khalani ndi Zolinga Zauzimu Kuti Mulemekeze Nazo Mlengi Wanu,” yopezeka mu Nsanja ya Olonda ya July 15, 2004.