Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

“Mau a Mulungu . . . Ndi Amphamvu”

“Mau a Mulungu . . . Ndi Amphamvu”

“Mau a Mulungu ndi amoyo ndi amphamvu.”—AHEB. 4:12.

NYIMBO: 96, 94

1. Tidziŵa bwanji kuti Mau a Mulungu alidi na mphamvu? (Onani pikica pamwamba.)

POKHALA anthu a Yehova, timakhulupilila kuti mau a Mulungu, amene ndi uthenga wake kwa anthu, “ndi amoyo ndi amphamvu.” (Aheb. 4:12) Ambili a ise tadzionela tekha kuti Baibo ilidi na mphamvu cifukwa yatithandiza kusintha umoyo wathu. Asanaphunzile coonadi, ena mwa abale na alongo athu anali kuseŵenzetsa mankhwala osokoneza ubongo, kuba, ndi kucita ciwelewele. Ndipo ena zinthu zinali kuwayendela bwino m’dzikoli, koma anali kuonabe kuti cinacake cikusowa mu umoyo wawo. (Mlal. 2:3-11) Anthu ambili amene kale anali kuoneka monga otayika, apeza njila ya ku moyo cifukwa ca mphamvu ya Baibo yosintha anthu. Mwacionekele, munaŵelenga ndi kusangalala kwambili na nkhani za anthu aconco zopezeka mu Nsanja ya Mlonda, za mutu wakuti “Baibo Imasintha Anthu.” Komanso, mwaona kuti ngakhale pambuyo pophunzila coonadi, Akhristu amapitiliza kupita patsogolo mwauzimu cifukwa ca mphamvu ya Mau a Mulungu.

2. Kodi Mau a Mulungu anaonetsa bwanji mphamvu yake m’zaka 100 zoyambilila?

2 N’zosadabwitsa kuti anthu ambili masiku ano asintha kwambili umoyo wawo cifukwa cophunzila Mau a Mulungu. Zimenezi zimatikumbutsa za abale na alongo athu a m’zaka 100 zoyambilila, amene anali na ciyembekezo copita kumwamba. (Ŵelengani 1 Akorinto 6:9-11.) Mtumwi Paulo atafotokoza za anthu a makhalidwe oipa osiyana-siyana amene sadzaloŵa mu Ufumu wa Mulungu, ananenanso kuti: “Ena mwa inu munali otelo.” Iwo anali atasintha mothandizidwa na Mau a Mulungu ndi mzimu wake woyela. Komabe, ngakhale pambuyo pophunzila coonadi, ena mwa iwo anali akali kucita macimo aakulu. Mwacitsanzo, Baibo imakamba kuti mmodzi wa Akhristu odzozedwa a m’zaka 100 zoyambilila anacotsedwa mumpingo. Koma pambuyo pake anabwezeletsedwa. (1 Akor. 5:1-5; 2 Akor. 2:5-8) Kodi si zolimbikitsa kudziŵa kuti abale na alongo athu akwanitsa kupilila mavuto osiyana-siyana mu umoyo wawo mothandizidwa na Mau a Mulungu?

3. Kodi m’nkhani ino tidzakambilana ciani?

3 Popeza kuti tili na Mau a Mulungu, omwe ni amphamvu kwambili, timafuna kuwaseŵenzetsa bwino. (2 Tim. 2:15) Conco, m’nkhani ino tidzakambilana zimene tingacite kuti tilole mphamvu ya Mau a Mulungu kugwila nchito (1) mu umoyo wathu, (2) mu ulaliki, ndi (3) pophunzitsa papulatifomu. Kukambilana zimenezi kudzatithandiza kudziŵa mmene tingaonetsele kuti timakonda ndi kuyamikila Atate wathu wacikondi wakumwamba, amene amatiphunzitsa kuti tipindule.—Yes. 48:17.

MU UMOYO WATHU

4. (a) Tifunika kucita ciani kuti Mau a Mulungu atithandize pa umoyo wathu? (b) Kodi mumapeza bwanji nthawi yoŵelenga Baibo?

4 Kuti Mau a Mulungu atithandize pa umoyo wathu, tifunika kuyesetsa kumawaŵelenga tsiku lililonse. (Yos. 1:8) N’zoona kuti ambili a ise timakhala otangwanika kwambili. Komabe, sitifunika kulola ciliconse, kaya nchito kapena maudindo athu, kusokoneza pulogilamu yathu yoŵelenga Baibo. (Ŵelengani Aefeso 5:15, 16.) Anthu a Yehova ambili amayesetsa kupatula nthawi yoŵelenga Baibo tsiku lililonse, kaya ni m’maŵa, m’madzulo, kapena m’masana. Iwo amamvela monga mmene wamasalimo anamvelela, amene analemba kuti: “Ndimakonda kwambili cilamulo canu! Ndimasinkhasinkha cilamuloco tsiku lonse.”—Sal. 119:97.

5, 6. (a) N’cifukwa ciani kusinkha-sinkha n’kofunika? (b) Tingacite ciani kuti kusinkha-sinkha kwathu kuzikhala kwaphindu? (c) Fotokozani mmene inu panokha mwapindulila cifukwa coŵelenga Mau a Mulungu ndi kuwasinkha-sinkha.

5 Kuwonjezela pa kuŵelenga Baibo, tifunikanso kusinkha-sinkha zimene taŵelengazo. (Sal. 1:1-3) Tikacita conco, m’pamene tidzatha kuseŵenzetsa mokwanila malangizo a m’Baibo pa umoyo wathu. Kaya tiŵelenga Mau a Mulungu m’Baibo mweni-mweni, pa foni, kapena pa tabuleti, colinga cathu ciyenela kukhala cakuti tiwamvetsetse ndi kuwalola kusintha umoyo wathu.

6 Tingacite ciani kuti kusinkha-sinkha kwathu kuzikhala kwaphindu? Ena amaona kuti zimathandiza kuima pambuyo poŵelenga mavesi ena, n’kudzifunsa mafunso monga awa: ‘Kodi zimenezi ziniphunzitsa ciani ponena za Yehova? Kodi mfundo imeneyi n’nayamba kale kuiseŵenzetsa pa mbali ziti m’moyo wanga? Nanga ni mbali ziti zimene nifunika kuwongolela?’ Ngati tisinkha-sinkha Mau a Mulungu na kupemphela, tidzalimbikitsidwa kutsatila malangizo a m’Baibo. Komanso, tidzalola mphamvu ya Mau a Mulungu kugwila nchito mokwanila mu umoyo wathu.—2 Akor. 10:4, 5.

MU ULALIKI

7. Kodi Mau a Mulungu tingawaseŵenzetse bwanji moyenela mu ulaliki?

7 Kodi Mau a Mulungu tingawagwilitsile nchito bwanji moyenela mu ulaliki? Cimodzi cimene tifunika kucita ni kuseŵenzetsa kwambili Baibo polalikila ndi pophunzitsa. M’bale wina pofotokoza mfundo imeneyi, anafunsa kuti: “Mukanakhala kuti mukulalikila ku nyumba ndi nyumba pamodzi na Yehova, kodi sembe mukamba mwekha cabe, kapena sembe mumulola iye kukamba?” Cimene anali kutanthauza n’cakuti, ngati tiŵelengela mwininyumba Mau a Mulungu mu ulaliki, ndiye kuti tikulola Yehova kukamba naye. Kuŵelengela munthu lemba losankhidwa bwino kumakhala kothandiza ngako kuposa ciliconse cimene tingakambe. (1 Ates. 2:13) Dzifunseni kuti, ‘Nikamalalikila uthenga wabwino, kodi nimayesetsa kupeza mipata yoŵelengela anthu Mau a Mulungu?’

8. N’cifukwa ciani kuŵelengela anthu malemba mu ulaliki pakokha si kokwanila?

8 Komabe, kuŵelengela anthu Baibo tikakhala muulaliki, pakokha si kokwanila. Cifukwa ciani? Cifukwa cakuti ambili saidziŵa bwino Baibo, ndipo ena saidziŵa n’komwe. Umu ni mmenenso zinalili m’zaka 100 zoyambilila. (Aroma 10:2) Conco, sitiyenela kuganiza kuti ngati munthu tamuŵelengela lemba, ndiye kuti basi adzamvetsetsa tanthauzo lake. Tifunika kuunika mfundo yofunika pa lembalo, mwina mwa kuŵelenganso mau amene agwilizana kwambili na mfundoyo, kenako n’kufotokoza tanthauzo lake. Kucita zimenezi, kudzathandiza kwambili kuti Mau a Mulungu awafike pamtima anthu amene tikamba nawo.—Ŵelengani Luka 24:32.

9. Kodi tingathandize bwanji anthu kulemekeza Mau a Mulungu pamene tifuna kuwaŵelengela Baibo? Chulani citsanzo.

9 Cinanso, pamene tifuna kuŵelengela munthu lemba, tifunika kukamba mau amene angamuthandize kulemekeza Baibo. Mwacitsanzo, tingakambe kuti, “Taonani zimene Mlengi anakamba pankhaniyi.” Pokamba na munthu amene si wacipembedzo cacikhristu, tinganene kuti, “Onani zimene Mau Opatulika amakamba.” Kapena ngati tilalikila munthu wosapembedza, tingamufunse kuti, “Kodi munaumvelapo mwambi wakale uwu?” Inde, tifunika kukumbukila kuti anthu amasiyana-siyana, ndipo tiyenela kusintha-sintha ulaliki wathu kuti ugwilizane na munthu amene tikamba naye.—1 Akor. 9:22, 23.

10. (a) Fotokozani zimene zinacitika pamene m’bale wina anali kulalikila. (b) Fotokozani zocitika za mu ulaliki zimene zinakucititsani kutsimikiza kuti Mau a Mulungu ni amphamvu.

10 Ofalitsa ambili aona kuti kuseŵenzetsa Mau a Mulungu mu ulaliki kumawakhudza ngako anthu amene timawalalikila. Mwacitsanzo, m’bale wina anapita kukacita ulendo wobwelelako kwa munthu wina wacikulile amene wakhala akuŵelenga magazini athu kwa zaka zambili. M’baleyo sanangopatsa munthuyo magazini atsopano a Nsanja ya Mlonda n’kucoka, koma anamuŵelengela lemba limodzi la m’magaziniyo. Anaŵelenga 2 Akorinto 1:3, 4, imene imati: “Tate wacifundo cacikulu ndi Mulungu amene amatitonthoza m’njila iliyonse, . . . amatitonthoza m’masautso athu onse.” Munthuyo anakhudzidwa ngako na lembali cakuti anapempha m’baleyo kuti aŵelengenso lembalo. Mwininyumbayo anafotokoza kuti iye na mkazi wake afunikila kwambili citonthozo, ndipo anayamba kucita cidwi na uthenga wa m’Baibo. Kodi simukuvomeleza kuti Mau a Mulungu ni amphamvu mu ulaliki?—Mac. 19:20.

POPHUNZITSA PAPULATIFOMU

11. Kodi abale amene amaphunzitsa papulatifomu ali na udindo wanji?

11 Tonsefe timasangalala kupezeka pa misonkhano yampingo, yadela, ndi yacigawo. Colinga cacikulu cimene timapezekela pa misonkhanoyi ni kulambila Yehova. Timapindulanso kwambili na malangizo auzimu amene timalandila. Abale amene amakamba nkhani pa misonkhano imeneyi amakhala na mwayi waukulu ngako. Koma afunikanso kukumbukila kuti ali na udindo waukulu kwambili. (Yak. 3:1) Nthawi zonse, iwo afunika kuonetsetsa kuti zimene amaphunzitsa n’zozikidwadi m’Mau a Mulungu. Ngati mwapatsidwa mwayi wokamba nkhani, kodi mungaseŵenzetse bwanji mphamvu ya Mau a Mulungu pokamba nkhaniyo?

12. Kodi wokamba nkhani angacite ciani kuti Malemba akhale maziko a nkhani yake?

12 Pangani Malemba kukhala maziko a nkhani yanu. (Yoh. 7:16) Mungacite bwanji zimenezi? Coyamba, musalole ciliconse, kaya zitsanzo, mafanizo, kapena kakambidwe kanu, kuphimba mfundo ya Malemba amene mwaŵelenga. Cinanso, kumbukilani kuti kuphunzitsa kozikidwa pa malemba sikutanthauza kungoŵelenga malemba ambili. Ndipo kuŵelenga malemba ambili-mbili kungacititse kuti omvela asagwilepo mfundo iliyonse pa malembawo. Conco, mufunika kusankha mosamala malemba a mfundo zazikulu, kuŵaŵelenga, kuwafotokoza, kupelekapo fanizo, ndi kumveketsa bwino mmene tingaseŵenzetsele mfundo zake. (Neh. 8:8) Ngati nkhani yanu ili na autilaini yokonzewa ndi gulu la Mulungu, muyenela kuiŵelenga mosamala pamodzi na malemba ake. Yesetsani kumvetsa mmene mfundo za mu autilainiyo zikugwilizanilana ndi malembawo. Ndiyeno, pokamba nkhaniyo, seŵenzetsani malemba oyenelela amene munasankha. (Mungapeze mfundo zina zothandiza m’buku la Pindulani ndi Sukulu ya Utumiki wa Mulungu, phunzilo 21 mpaka 23.) Koposa zonse, pemphani Yehova kuti akakuthandizeni kumveketsa bwino mfundo zofunika kwambili za m’Mau ake.—Ŵelengani Ezara 7:10; Miyambo 3:13, 14.

13. (a) Kodi mlongo wina anakhudzidwa bwanji na malemba amene anagwilitsidwa nchito pa msonkhano? (b) Kodi imwe mwapindula bwanji na mfundo za m’Malemba zimene timaphunzila pa misonkhano yathu?

13 Mlongo wina ku Australia anakhudzidwa kwambili na mmene wokamba nkhani wina anafotokozela malemba pamsonkhano wampingo. Iye anakula movutika, koma analabadila uthenga wa m’Baibo ndi kudzipeleka kwa Yehova. Ngakhale n’conco, anali kukayikila kuti Yehova amam’konda. Koma m’kupita kwa nthawi, anakhutila kuti Mulungu amam’kondadi. N’ciani cinamuthandiza kusintha maganizo? Anasinkha-sinkha lemba limene linafotokozedwa pa umodzi mwa misonkhano yathu, ndipo anagwilizanitsa mfundo ya pa lembalo na malemba ena. * Kodi inunso munakhudzidwapo na Malemba amene anagwilitsidwa nchito pa misonkhano yathu, kaya yampingo, yadela, kapena yacigawo?—Neh. 8:12.

14. Tingaonetse bwanji kuti timayamikila Mau a Yehova?

14 Ndithudi, timamuyamikila kwambili Yehova cifukwa cotipatsa Mau ake, Baibo! Iye watipatsa Baibo cifukwa amatikonda. Kuwonjezela apo, wakwanilitsa lonjezo lake lakuti Mau ake adzakhalapo mpaka kale-kale. (1 Pet. 1:24, 25) Conco, tifunika kumaŵelenga Mau a Mulungu nthawi zonse, kuwaseŵenzetsa mu umoyo wathu ndi pophunzitsa ena. Tikacita conco, tidzaonetsa kuti timakonda ndi kuyamikila cuma camtengo wapatali cimeneci. Koposa zonse, tidzaonetsa kuti timayamikila Mlembi wa Baibo, Yehova Mulungu.

^ par. 13 Onani bokosi yakuti “ Mmene Anasinthila.”