Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Kodi Mulungu Waticitila Zotani?

Kodi Mulungu Waticitila Zotani?

Ngati mufuna kudziŵa bwino munthu wina wake, zimakhala zothandiza kudziŵa zimene anakwanitsa kucita kumbuyoko na mavuto amene wapilila. Mofananamo, ngati mufuna kum’dziŵa bwino Mulungu, mufunika kudziŵa zimene anakwanitsa kucita kumbuyoko. Pamene mucita zimenezi, mungacite cidwi kudziŵa kuti zambili zimene anacita zimatipindulitsa masiku ano komanso zimakhudza tsogolo lathu.

MULUNGU ANALENGA ZINTHU ZONSE KUTI TIPINDULE NAZO

Yehova Mulungu ni Mlengi Wamkulu ndipo ‘Cilengedwele dziko kupita m’tsogolo, makhalidwe a Mulungu osaoneka ndi maso akuonekela bwino. Makhalidwe a Mulungu amenewa akuonekela m’zinthu zimene anapanga.’ (Aroma 1:20) “Mulungu woona ndi amene anapanga dziko lapansi ndi mphamvu zake, amene mwanzelu zake anakhazikitsa dziko limene anthu amakhalamo. Iye ndi amenenso anayala kumwamba mwa kuzindikila kwake.” (Yeremiya 10:12) Zodabwitsa za m’cilengedwe zimaonetsa kuti Mulungu amatikonda.

Ganizilani mmene Yehova anatilengela mwapadela, iye anatilenga “m’cifanizilo cake” kuti tikhale na umoyo waphindu. (Genesis 1:27) Izi zitanthauza kuti iye anatilenga m’njila yakuti tizionetsako makhalidwe ake abwino kwambili, ndiponso kuti tizikwanitsa kumvetsetsa makhalidwe ake na kudziŵa mmene amaonela zinthu. Pamene tiyesetsa kutengela makhalidwe na kaonedwe kake ka zinthu, timakhala na umoyo waphindu komanso wacimwemwe kwambili. Koma koposa pamenepa, iye anatipatsa mwayi wakuti tingakhale naye pa ubwenzi.

Zimene Mulungu analenga zimacitila umboni wakuti amatikonda. Paulo anakamba kuti Mulungu ‘sanangokhala wopanda umboni wakuti anacita zabwino. Anatipatsa mvula kucokela kumwamba ndi nyengo zimene zokolola zathu zimakhala zambili. Anadzaza mitima yathu ndi cakudya komanso cimwemwe.’ (Machitidwe 14:17) Mulungu anatipatsa zambili kuwonjezela pa zofunikila kuti tikhale na moyo. Anatipatsa zinthu zoculuka komanso za mitundu yosiyana-siyana kuti tizikondwela na umoyo. Zonsezi n’zocepa poyelekezela na zimene anali kufuna kutipatsa.

Yehova analenga dziko lapansi kuti anthu akhalepo kwamuyaya. Baibo imakamba kuti: “Dziko lapansi analipeleka kwa ana a anthu,” ndipo “sanalilenge popanda colinga, amene analiumba kuti anthu akhalemo.” (Salimo 115:16; Yesaya 45:18) Kodi ni anthu otani adzakhalamo ndipo adzakhalamo kwa utali wotani? “Olungama adzalandila dziko lapansi, ndipo adzakhala mmenemo kwamuyaya.”—Salimo 37:29.

Paciyambi Yehova analenga mwamuna na mkazi, Adamu na Hava na kuŵaika m’munda wa paradaiso padziko lapansi kuti “aulime nauyang’anile.” (Genesis 2:8, 15) Mulungu anawapatsa zocita ziŵili. Iye anati: “Mubelekane, muculuke, mudzaze dziko lapansi, ndipo muliyang’anile.” (Genesis 1:28) Conco, Adamu na Hava anali na ciyembekezo cosangalala na moyo wosatha padziko lapansi. N’zacisoni kuti iwo anasankha kusamvela Mulungu ndipo anataya ciyembekezo cokhala pakati pa anthu “olungama” amene “adzalandila dziko lapansi.” Komabe, monga mmene tidzaonela, zocita zawo sizinasokoneze colinga ca Yehova cokhudza dziko lapansi. Koma coyamba tiyeni tione cinthu cina cimene Mulungu wacita.

MULUNGU ANATIPATSA MAWU AKE

Baibo imachedwanso kuti Mawu a Mulungu. N’cifukwa ciani Yehova anatipatsa Baibo? Cifukwa cacikulu n’cakuti afuna tim’dziŵe bwino. (Miyambo 2:1-5) N’zoona kuti Baibo siiyankha mafunso onse amene tingakhale nawo okamba za Mulungu, ndipo palibe ngakhale buku imodzi ingakwanitse kucita zimenezi. (Mlaliki 3:11) Koma zonse zimene zili m’Baibo zimatithandiza kum’dziŵa bwino Mulungu. Timadziŵa makhalidwe ake tikaona mmene amacitila zinthu na anthu. Timadziŵanso anthu amene iye amakonda na amene sakonda. (Salimo 15:1-5) Timadziŵa maganizo ake pa nkhani ya kulambila, makhalidwe, komanso zinthu za kuthupi. Baibo imatipatsa cithunzi cokwanila ca makhalidwe a Yehova tikaona zimene Mwana wake Yesu Khristu anali kukamba komanso kucita.—Yohane 14:9.

Cifukwa cina cimene Yehova anatipatsila Mawu ake Baibo, n’cakuti tidziŵe mmene tingakhale na umoyo wacimwemwe, komanso wacolinga. Kupitila m’Baibo, Yehova amatiuza mmene tingakhalile na banja lacimwemwe, mmene tingakhalile okhutila na zimene tili nazo, komanso zimene zingatithandize kucepetsa nkhawa. Monga mmene idzafotokozela magazini ino, Baibo imapeleka mayankho pa mafunso ofunika kwambili monga akuti: N’cifukwa ciani padziko pali mavuto ambili conco? Kodi kutsogolo kudzakhala zotani? Ifotokozanso zimene Mulungu wacita poonetsetsa kuti colinga cake ca poyamba cikwanilitsike.

Kukamba zoona, Baibo ni buku yapadela kwambili. Ndipo pali maumboni oonetsa kuti Baibo ni buku yapadela imene mlembi wake ni Mulungu. Kulemba Baibo kunatenga zaka zoposa 1,600 na amuna okwana 40, koma nkhani zake zonse n’zogwilizana cifukwa Mlembi wake ni Mulungu. (2 Timoteyo 3:16) Mosiyana na mipukutu ina yakale, Baibo yakhala yotetezeka bwino m’zaka zonsezi, monga mmene masauzande a mipukutu yakale ya Baibo aonetsela. Kuonjezela apo, Baibo nthawi zonse yakhalapo ngakhale kuti anthu ayesetsa kuti isamasulidwe, kufalitsidwa komanso kuŵelengedwa. Baibo ni buku imene yamasulidwa na kufalitsidwa kwambili masiku ano. Kukhalapo kwa Baibo ni umboni wakuti “mawu a Mulungu wathu adzakhala mpaka kalekale.”—Yesaya 40:8.

MULUNGU ANATSIMIKIZA KUTI COLINGA CAKE CIDZAKWANILITSIKA

Cina capadela cimene Mulungu anacita, anatipatsa citsimikizo cakuti adzakwanilitsa colinga cake cokhudza ise anthu. Monga takambila poyamba, colinga ca Mulungu cinali cakuti anthu akhale padziko lapansi kwamuyaya. Koma pamene Adamu anasankha kusamvela Mulungu anacimwa, ndipo iye anataya mwayi wokhala na moyo wosatha komanso wa ana ake odzabadwa kutsogolo. “Ucimo unalowela m’dziko kudzela mwa munthu mmodzi, ndi imfa kudzela mwa ucimo, imfayo n’kufalikila kwa anthu onse cifukwa onse anacimwa.” (Aroma 5:12) Conco, kusamvela kwa munthu kunasokoneza colinga ca Mulungu. Kodi Yehova anacitapo ciani?

Zocita za Yehova pa nkhaniyi zinagwilizana na makhalidwe ake apadela. Iye anapeleka cilango coyenela kwa Adamu na Hava. Koma mwa cikondi cake anapatsa ana awo mwayi wodzakhala na moyo wosatha. Mwa nzelu zake, Yehova anapeza njila yothetsela vuto imeneyi, ndipo mwamsanga anakambilatu mmene adzacitila zimenezi. (Genesis 3:15) Njila yopulumukila ku ucimo na imfa inapelekedwa kupitila mwa Mwana wa Mulungu, Yesu Khristu. Kodi zimenezi zinakwanitsika bwanji?

Pofuna kuwombola anthu ku zotulukapo za kupanduka kwa Adamu, Yehova anatumiza Yesu padziko lapansi kuti aphunzitse anthu njila ya kumoyo na “kudzapeleka moyo wake dipo kuwombola anthu ambili.” a (Mateyu 20:28; Yohane 14:6) Yesu anali woyenelela kupeleka dipo cifukwa anali munthu wangwilo monga Adamu. Koma mosiyana na Adamu, iye anakhalabe womvela mpaka imfa. Popeza Yesu sanali kufunika kufa, Yehova anamuukitsa kukakhala na moyo kumwamba. Iye anakwanitsa kupatsa anthu omvela ciyembekezo ca moyo wosatha. Izi n’zimene Adamu analephela kucita. “Pakuti monga mwa kusamvela kwa munthu mmodziyo, ambili anakhala ocimwa, momwemonso kudzela mwa kumvela kwa munthu mmodziyu, ambili adzakhala olungama.” (Aroma 5:19) Kupitila mu nsembe ya dipo ya Yesu, Mulungu adzakwanilitsa lonjezo lake lakuti anthu akhale padziko lapansi kwamuyaya.

Timadziŵa zambili za Yehova tikaona mmene anacitila zinthu pambuyo pakuti colinga cake casokonezedwa kaamba ka kusamvela kwa Adamu. Timaona kuti palibe ciliconse cingalepheletse Yehova kutsiliza zimene anayamba. Mawu ake “adzakwanilitsidwadi.” (Yesaya 55:11) Timayamikila kwambili kukula kwa cikondi ca Yehova pa ise. “Mulungu anatisonyeza ife cikondi cake pakuti anatumiza m’dziko Mwana wake wobadwa yekha kuti tipeze moyo kudzela mwa iye. Cikondi cimeneci cikutanthauza kuti ife sitinakonde Mulungu, koma iye ndi amene anatikonda ndi kutumiza Mwana wake monga nsembe yophimba macimo athu.”—1 Yohane 4:9, 10.

Mulungu “sanaumile ngakhale Mwana wake koma anamupeleka m’malo mwa ife tonse.” Conco, tili na cidalilo cakuti Mulungu, ‘mokoma mtima adzatipatsa zinthu zina zonse’ zimene anatilonjeza (Aroma 8:32) Kodi Mulungu anatilonjeza kuti adzaticitila ciani? Ŵelengani nkhani yotsatila.

KODI MULUNGU WATICITILA ZOTANI? Yehova analenga anthu kuti akhale padziko lapansi kwamuyaya. Anatipatsa Baibo kuti tim’dziŵe bwino. Kupitila mwa Yesu Khristu, Yehova anapeleka dipo, kutsimikizila kuti colinga cake cikwanilitsike

a Kuti mudziŵe zambili zokhudza dipo, onani phunzilo 27 m’buku la Kondwelani na Moyo Kwamuyaya! yolembewa na Mboni za Yehova. Buku imeneyi ipezekanso pa webusaiti ya www.dan124.com.