Kodi Baibo Imakamba Ciani?
Kodi tili mu “masiku otsiliza”?
Mungayankhe bwanji?
Inde
Iyai
Kapena
Zimene Baibo imakamba
“Masiku otsiliza adzakhala nthawi yapadela komanso yovuta.” (2 Timoteyo 3:1) Ulosi wa m’Baibo komanso zimene zicitika masiku ano, zionetsa kuti tili mu “masiku otsiliza.”
Mfundo zina zimene Baibo imakamba
Cizindikilo ca masiku otsiliza cidzakhala nkhondo, njala, zivomezi, na kuwanda kwa matenda akupha.—Mateyu 24:3, 7; Luka 21:11.
M’masiku otsiliza, anthu adzavutika cifukwa ca makhalidwe oipa ndi kusakonda zinthu zauzimu.—2 Timoteyo 3:2-5.
Kodi anthu ayembekezela ciani kutsogolo?
Anthu ena amakhulupilila kuti . . . masiku otsiliza adzatha pamene dziko lapansi ndi anthu onse zidzawonongedwa. Koma ena amakhulupilila kuti zinthu zidzakhala bwino. Imwe muganiza bwanji?
Zimene Baibo imakamba
“Olungama adzalandila dziko lapansi, ndipo adzakhala mmenemo kwamuyaya.” —Salimo 37:29.
Mfundo zina zimene Baibo imakamba
Masiku otsiliza adzatha pamene zoipa zonse zidzacotsewapo.—1 Yohane 2:17.
Dziko lapansi lidzasintha kukhala paradaiso.—Yesaya 35:1, 6.