Kodi Dzikoli Lidzatha?
Mwina mudziŵa kuti Baibo imakamba za kutha kwa dziko. (1 Yohane 2:17) Kodi imatanthauza kutha kwa mtundu wa anthu? Kodi Dziko Lapansi lidzakhala malo opanda camoyo ciliconse kapena lidzawonongedwa kothelatu?
YANKHO LA M’BAIBO PA MAFUNSO ONSE AMENEWA NI IYAI
Ni Zinthu Ziti Zimene Sizidzatha?
MTUNDU WA ANTHU
Zimene Baibo imakamba: Mulungu “sanalilenge popanda colinga [dziko lapansi], . . . analiumba kuti anthu akhalemo.” —YESAYA 45:18.
DZIKO LAPANSI
Zimene Baibo imakamba: “M’badwo umapita ndipo m’badwo wina umabwela, koma dziko lapansi lidzakhalapobe mpaka kalekale.”—MLALIKI 1:4.
TANTHAUZO LAKE: Malinga n’zimene Baibo imakamba, dziko lapansi silidzawonongedwa ndipo padzakhalabe anthu nthawi zonse. Nanga kutha kwa dziko kutanthauza ciani?
GANIZILANI IZI: Baibo imayelekezela mapeto a dzikoli amene akubwela na zimene zinacitika m’masiku a Nowa. Pa nthawiyo, dziko lapansi ‘linadzaza ndi ciwawa.’ (Genesis 6:13) Koma Nowa anali munthu wolungama. Conco Mulungu anapulumutsa Nowa na banja lake, koma anawononga anthu oipa na cigumula ca madzi. Pofotokoza zimene zinacitika panthawiyo, Baibo imati: “Dziko la pa nthawiyo linawonongedwa pamene linamizidwa ndi madzi.” (2 Petulo 3:6) Uku ndiye kunali kutha kwa dziko la panthawiyo. Koma kodi n’ciani cinawonongedwa? Silinali dziko lapansi, koma anthu oipa okhala padziko lapansi. Conco Baibo ikamakamba za kutha kwa dziko, sitanthauza kuwonongedwa kwa dziko lapansili. Koma imatanthauza kuwonongedwa kwa anthu oipa padziko lapansi komanso kutha kwa dongosolo la zinthu limene iwo akhazikitsa.
Ni Zinthu Ziti Zimene Zidzatha?
MAVUTO NA KUIPA
Zimene Baibo imakamba: “Patsala kanthawi kocepa, woipa sadzakhalakonso. Udzayang’ana pamene anali kukhala, ndipo sadzapezekapo. Koma anthu ofatsa adzalandila dziko lapansi, ndipo adzasangalala ndi mtendele woculuka.”—SALIMO 37:10, 11.
TANTHAUZO LAKE: Cigumula ca m’nthawi ya Nowa sicinathetseletu kuipa padziko lapansi. Pambuyo pa Cigumula, anthu oipa anayambanso kuvutitsa anthu anzawo. Posacedwa, Mulungu adzathetsa kuipa konse. Wamasalimo anakamba kuti: “Woipa sadzakhalakonso.” Mulungu adzathetsa kuipa konse poseŵenzetsa Ufumu wake, umene ni boma lakumwamba limene lidzalamulila anthu olungama padziko lonse lapansi.
GANIZILANI IZI: Kodi anthu amene akulamulila dziko palipano adzaugonjela ulamulilo wa Ufumu wa Mulungu? Baibo imaonetsa kuti sadzaugonjela. Iwo mopanda nzelu, adzalimbana na Ufumu wa Mulungu. (Salimo 2:2) Kodi zotulukapo zake zidzakhala zotani? Ufumu wa Mulungu udzathetsa maboma onse a anthu, ndipo “udzakhalapo mpaka kalekale.” (Danieli 2:44) Koma n’cifukwa ciani ulamulilo wa anthu uyenela kutha?
CIFUKWA CAKE—Ulamulilo wa Anthu Uyenela Kutha
Zimene Baibo imakamba: “Munthu amene akuyenda alibe ulamulilo wowongolela mapazi ake.” —YEREMIYA 10:23.
TANTHAUZO LAKE: Anthu sanalengedwe kuti azidzilamulila okha. Iwo amalephela kutsogolela bwino anthu na kuthetsa mavuto awo.
GANIZILANI IZI: Buku lina lochedwa Britannica Academic, linakamba kuti cioneka kuti maboma paokha “alephela kuthetsa mavuto a anthu monga umphaŵi, njala, matenda, matsoka a zacilengedwe, nkhondo, kapena zaciwawa zina.” Kenako inapitiliza kuti: “Ena . . . amakhulupilila kuti ni boma la padziko lonse cabe limene lingakwanitse kuthetsa mavuto amenewa.” Komabe, ngakhale maboma onse a anthu atakhala kuti agwilizana, dziko lingamalamulidwebe na anthu opanda ungwilo amene sangakwanitse kuthetsa mavuto amene tachula pamwambapa. Ufumu wa Mulungu ndilo boma lokha limene lili na mphamvu zothetselatu mavuto onse padziko lapansi.
Conco malinga n’zimene Baibo imakamba, kutha kwa dziko kutanthauza kutha kwa dongosolo loipa la zinthu limene lilipoli. Imeneyi si nkhani yocititsa mantha kwa anthu abwino. Koma ni nkhani yopatsa ciyembekezo cifukwa dziko loipali lidzaloŵedwa m’malo na dziko latsopano la Mulungu limene lidzakhala labwino kwambili.
Kodi zonsezi zidzacitika liti? Nkhani yotsatila idzafotokoza yankho la m’Baibo pa funso limeneli.