Zimene Mungacite Kuti Mukakhalemo m’Dziko Latsopano
Nkhani zapita zaonetsa kuti posacedwapa, Mulungu adzawononga anthu oipa na kuthetsa mavuto onse padzikoli. Sitiyenela kukayikila kuti zimenezi zidzacitika. Cifukwa ciani? Cifukwa Baibo, Mawu a Mulungu, inakambilatu kuti:
“Dziko likupita.”—1 YOHANE 2:17.
Tidziŵa kuti padzakhala opulumuka cifukwa vesi imene ili pamwambayi imakambanso kuti:
“Wocita cifunilo ca Mulungu adzakhala kosatha.”
Conco kuti munthu akapulumuke ayenela kucita cifunilo ca Mulungu. Kuti tidziŵe cifunilo ca Mulungu, coyamba tiyenela kum’dziŵa bwino Mulunguyo.
TIYENELA “KUDZIŴA” MULUNGU KUTI TIKAPULUMUKE MAPETO A DZIKO
Yesu anati: “Pakuti moyo wosatha adzaupeza akamaphunzila ndi kudziwa za inu, Mulungu yekhayo amene ali woona.” (Yohane 17:3) Kuti tikapulumuke mapeto a dzikoli na kudzakhala na moyo kwamuyaya, tiyenela “kudziŵa” Mulungu. Izi sizitanthauza cabe kukhulupilila kuti Mulungu aliko, kapena kudziŵako zinthu zina zocepa zokhudza iye. Koma tiyenela kukhala naye paubwenzi. Kuti ubwenzi wathu na munthu wina ulimbe, timafunika kupatula nthawi yoceza naye. N’zimenenso tiyenela kucita kuti ubwenzi wathu na Mulungu ulimbe. Onani mfundo zina zofunika za coonadi zimene timaphunzila m’Baibo, zimene zingatithandize kukhala pa ubwenzi na Mulungu na kuulimbitsa.
MUZIŴELENGA MAWU A MULULNGU BAIBO TSIKU LILILONSE
Timadya cakudya nthawi zonse kuti tikhalebe na moyo. Koma Yesu anati: “Munthu sangakhale ndi moyo ndi cakudya cokha, koma ndi mawu onse otuluka pakamwa pa Yehova.”—Mateyu 4:4.
Masiku ano, mawu a Yehova timawapeza m’Baibo. Mukamaŵelenga buku lopatulika limeneli, mudzadziŵa zimene Mulungu anacita kalelo, zimene akucita tsopano, na zimene adzacita kutsogolo.
MUZIPEMPHELA KWA MULUNGU KUTI AKUTHANDIZENI
Kodi mungacite ciani ngati mumafuna kumvela Mulungu koma zimakuvutani kuleka kucita zinthu zimene iye amati n’zoipa? Ngati zili conco, kum’dziŵa bwino Mulungu kungakuthandizeni kwambili.
Ganizilani za mayi wina amene tam’patsa dzina lakuti Sakura. Iye anali na khalidwe laciwelewele. Atayamba kuphunzila Baibo, anadziŵa za lamulo la Mulungu lakuti “thawani dama.” (1 Akorinto 6:18) Sakura anapemphela kwa Mulungu kuti amupatse mphamvu, ndipo anakwanitsa kuleka khalidwe loipalo. Koma nthawi zina amalimbanabe na mayeselo. Iye anati: “Maganizo oipa akabwela mumtima mwanga, nimauza Yehova zonse m’pemphelo, cifukwa nidziŵa kuti panekha siningakwanitse kulimbana nazo. Pemphelo lanithandiza kwambili kuti nikhale pafupi na Yehova.” Mofanana na Sakura, anthu mamiliyoni akuphunzila za Mulungu. Iye amawapatsa mphamvu zofunikila kuti asinthe umoyo wawo, na kukhala na umoyo umene umam’kondweletsa.—Afilipi 4:13.
Mukam’dziŵa bwino Mulungu, nayenso ‘adzakudziŵani’ monga bwenzi lake. (Agalatiya 4:9; Salimo 25:14) Mukacita zimenezi, mudzapulumuka na kukaloŵa m’dziko latsopano la Mulungu. Koma kodi dziko latsopano limenelo lidzakhala lotani? Nkhani yotsatila idzafotokoza.
a Baibo imakamba kuti dzina la Mulungu ni Yehova.