Tifunikila Dziko Labwino!
“Tikukhala m’dziko lodzala na mavuto,” anatelo António Guterres, kalembela wamkulu wa bungwe la United Nations. Kodi si zoona zimene anakamba?
Nthawi zambili pa nyuzi timamvela nkhani zodetsa nkhawa monga za:
Matenda na milili
Matsoka a zacilengedwe
Umphaŵi na njala
Kuwonongeka kwa cilengedwe na kutentha kwa padziko
Upandu, ciwawa, na katangale
Nkhondo
N’zosacita kufunsa kuti tifunikila dziko labwino. Dziko limene
Tidzakhalamo tili na thanzi labwino
Aliyense adzakhala wotetezeka
Mudzakhala cakudya coculuka
Lidzakhala lokongola
Aliyense adzacitilidwa zinthu mwacilungamo
Mudzakhala mtendele
Koma kodi titanthauza ciani tikanena kuti dziko labwino?
Kodi n’ciani cidzacitikila dziko limene tikukhalamoli?
Nanga tingacite ciani kuti tikakhalemo m’dziko labwino?
Magazini ino ya Nsanja ya Mlonda, ifotokoza mayankho a m’Baibo okhazika mtima pansi pa mafunso amenewa na ena.