NSANJA YA MLONDA Na. 4 2017 | Kodi Baibo Imati Ciani pa Nkhani ya Moyo na Imfa?
MUGANIZA BWANJI?
Kodi n’cifunilo ca Mulungu kuti ife anthu tizifa? Baibo imakamba kuti: “[Mulungu] adzapukuta misozi yonse m’maso mwawo, ndipo imfa sidzakhalaponso.”—Chivumbulutso 21:4.
Nsanja ya Mlonda iyi ifotokoza zimene Baibo imakamba pa nkhani ya moyo na imfa.
NKHANI YA PACIKUTO
Funso Logometsa Mutu
Popeza anthu ambili amakamba zosiyana-siyana zokhudza zimene zimacitika munthu akafa, n’kuti kumene tingapeze yankho la zoona?
NKHANI YA PACIKUTO
Zimene Baibo Imakamba pa Nkhani ya Moyo na Imfa
Kodi pali cinacake m’thupi mwathu cimene cimapitiliza kukhala na moyo tikafa? Kodi tili na mzimu umene sukufa? Kodi akufa ali kuti?
Munthu Amene Mukonda Akadwala Matenda Osacilitsika
Kodi acibululu angatonthoze na kusamalila bwanji wokondedwa wawo wodwala matenda osacilitsika? Kodi odwazika angalimbane bwanji na nkhawa zimene zimakhalapo posamalila wodwala?
Elias Hutter na Mabaibo Ake a Ciheberi Ocititsa Cidwi
Elias Hutter, katswili amene anakhalako zaka za m’ma 1500, anafalitsa Mabaibo aŵili a Ciheberi othandiza kwambili.
Citsimikizo Camphamvu Kucokela ku Kacilembo Kocepetsetsa Kaciheberi
Kodi Yesu anatanthauza ciani pamene anakamba za kacilembo kocepetsetsa mu alifabeti yaciheberi?
Paradaiso Padziko Lapansi—Ni Yeni-yeni Kapena ni Maloto Cabe?
Nkhani yokhudza paradaiso wotaika padziko lapansi yakhala yodziŵika kwambili m’mbili yonse ya anthu. Kodi n’zotheka kubwezeletsa paradaiso ameneyo?
Kodi Baibo Imakamba Ciani?
Munthu aliyense amakhala na nkhawa. Kodi n’zotheka kuthetsa nkhawa?