Kodi Baibo Imakamba Ciani?
Kodi Baibo ingakuthandizeni kutsiliza nkhawa?
Kodi mungayankhe bwanji?
Inde
Iyai
Kapena
Zimene Baibo imakamba
‘Tulilani [Mulungu] nkhawa zanu zonse, pakuti amakudelani nkhawa.’ (1 Petulo 5:7) Baibo imatsimikizila kuti Mulungu angakuthandizeni kutsiliza nkhawa zanu.
Mfundo zina zimene Baibo imakamba
Pemphelo lingakuthandizeni kupeza “mtendele wa Mulungu,” umene ungacepetse nkhawa zanu.—Afilipi 4:6, 7.
Cina, kuŵelenga Mau a Mulungu kungakuthandizeni kulimbana ndi nkhawa. —Mateyu 11:28-30.
Kodi n’zotheka nkhawa kuthelatu?
Ena amakhulupilila kuti . . .nkhawa na kuvutika maganizo ni mbali ya umoyo wa munthu, pamene ena amakhulupilila kuti nkhawa zimakasila m’moyo wina pambuyo pa imfa. Nanga imwe muganiza bwanji?
Zimene Baibo imakamba
Mulungu adzacotsapo zinthu zonse zobweletsa nkhawa. “Imfa sidzakhalaponso. Sipadzakhalanso kulila, kapena kubuula, ngakhale kupweteka.”—Chivumbulutso 21:4.
Mfundo zina zimene Baibo imakamba
Mu Ufumu wa Mulungu, anthu adzakhala pamtendele.—Yesaya 32:18.
Nkhawa zonse na kuvutika maganizo zidzaiŵalika.—Yesaya 65:17.