NKHANI YA PACIKUTO | ANGELO KODI ALIKO ZOONA? CIFUKWA CAKE TIFUNA KUDZIŴA
Kodi Angelo Amakhudza Umoyo Wanu?
Tsiku lina pa Sondo kumasana, Kenneth na Filomena, amene akhala ku Curaçao, anapita kunyumba kwa banja lina limene amaphunzitsa Baibo.
Kenneth anati: “Titafika, citseko cinali cokhoma ndipo motoka panalibe. Koma cinacake cinanipangitsa kutumila foni mayi wa panyumbapo.”
Mayiyo anayankha foni na kufotokoza kuti mwamuna wake ali kunchito. Komabe, atazindikila kuti Kenneth na Filomena ali panja, anatsegula citseko na kuwauza kuti angene.
Atangomuona cabe, anazindikila kuti anali kulila. Pamene Kenneth anali kupeleka pemphelo kuti ayambe kuphunzila, mayiyo anayambanso kulila. Conco, mokoma mtima iwo anam’funsa cifukwa cake iye akulila.
Mayiyo anakamba kuti anali kufuna kudzipha masana omwewo, ndipo pamene Kenneth anatuma foni, apo n’kuti akulembela mwamuna wake kakalata komudziŵitsa kuti wadzipha. Anaŵauza kuti iye anali wovutika maganizo kwambili. Conco, iwo anam’limbikitsa mwa kukambilana naye malemba otonthoza a m’Baibo. Cilimbikitso cimeneco cinapangitsa kuti asadziphe.
Kenneth anati: “Tiyamikila Yehova potiseŵenzetsa kuthandiza mayi wovutika maganizo ameneyo, maka-maka potipangitsa kutumila foni mayiyo, mwina kupitila mwa mngelo kapena mwa mzimu woyela.” *
Kodi tingati Kenneth na Filomena analakwitsa kukhulupilila kuti Mulungu anawathandiza kupitila mwa mngelo, mzimu Wake woyela, kapena mphamvu yake yogwila nchito? Kodi zinangocitika mwangozi kuti Kenneth atume foni panthawi yoyenela?
Sitingakambe motsimikiza. Koma cimene tidziŵa n’cakuti Mulungu amaseŵenzetsa angelo kuthandiza anthu mwauzimu. Mwacitsanzo, Baibo imakamba kuti Mulungu anatuma mngelo kukatsogolela Filipo mlaliki wacikhristu kuti akathandize nduna ya ku Itiyopiya, imene inali kufuna-funa citsogozo cauzimu.—Machitidwe. 8:26-31.
Zipembedzo zambili zimakhulupilila kuti kuli zolengedwa zauzimu zamphamvu, zimene amati n’zacifundo, ndipo zimacita cifunilo ca Mulungu na kuteteza anthu. Anthu ambili amakhulupilila kuti angelo aliko, ndi kuti amawathandiza. Koma pali enanso ambili amene sakhulupilila angelo olo pang’ono.
Kodi angelo aliko zoona? Ngati aliko, anacokela kuti? Nanga iwo n’ndani? Kodi amakhudza umoyo wanu? Tiyeni tikambilane mayankho ake.
^ par. 8 Yehova ni dzina la Mulungu lopezeka m’Baibo.—Salimo 83:18.