Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

MBILI YANGA

Nakhala na Umoyo Wosangalatsa Potumikila Yehova

Nakhala na Umoyo Wosangalatsa Potumikila Yehova

MU 1951, n’nafika m’tauni yaing’ono ya Rouyn, mu mzinda wa Quebec m’dziko la Canada. N’tafika n’nagogoda pa khomo imene ananipatsa adilesi yake. M’bale Marcel Filteau, a mmishonale yemwe analoŵa Sukulu ya Giliyadi, anabwela kudzatsegula citseko. Iye anali na zaka 23 ndipo anali wamtali, koma ine n’nali na zaka 16 ndipo n’nali wofupikilapo. N’tamuonetsa kalata yanga ya upainiya, iye anaiŵelenga n’kunena kuti, “Kodi makolo ako adziŵa kuti uli kuno?”

MMENE ZINTHU ZINALILI KUNYUMBA

N’nabadwa m’caka ca 1934. Makolo anga ni a ku Switzerland koma anasamukila m’tauni ya Timmins kumene n’nabadwila. Imeneyi ni tauni ya migodi mu pulovinsi ya Ontario m’dziko la Canada. Mu 1939, amayi anayamba kuŵelenga magazini ya Nsanja ya Mlonda ndipo anayamba kupezeka ku misonkhano ya Mboni za Yehova. Popita kumeneko, anali kutitenga ise ana onse 7. Posakhalitsa, iwo anabatizika na kukhala Mboni ya Yehova.

Atate sanakondwele kuti amayi akhala Mboni, koma amayi anacikondetsetsa coonadi, ndipo anatsimikiza mtima kucigwilitsitsa. Iwo anacigwilitsitsabe coonadi ngakhale kumayambililo kwa zaka za m’ma 1940, pamene nchito ya Mboni za Yehova inali yoletsedwa ku Canada. Nthawi zambili atate anali kunyoza amayi. Ngakhale n’telo, amayi anapitiliza kucita nawo zinthu mwacikondi komanso mwaulemu atate. Citsanzo cawo cabwino, cinathandiza ife ana kusankha kutumikila Yehova. Zinali zosangalatsa kuona atate akusintha na kuyamba kucita nafe zinthu mokoma mtima.

KUYAMBA UTUMIKI WA NTHAWI ZONSE

Mu August 1950, n’napezeka pa msonkhano waukulu wa mutu wakuti “Kuwonjezeka kwa Teokalase,” mu mzinda wa New York ku America. Pa msonkhanowu ninakumana na abale komanso alongo ocokela pa dziko lonse. Tili pa msonkhano. tinamvetsela zocitika zosangalatsa za abale amene analoŵa Sukulu ya Giliyadi. Izi zinanilimbikitsa kucita zambili potumikila Yehova. Cifuno canga coyamba utumiki wa nthawi zonse cinakulilako. Conco, n’tabwelela kunyumba n’nafunsila kuyamba utumiki wa nthawi zonse. Koma ofesi ya nthambi ya ku Canada inayankha pempho langa mwa kuniuza kuti niyenela kubatizika coyamba. Ndipo n’nabatizikadi pa October 1, 1950. Pambuyo pa mwezi umodzi, n’nakhala mpainiya wokhazikika, ndipo ananipempha kukatumikila m’tauni ya Kapuskasing. Tauni imeneyo inali kutali kwambili na kumene banja lathu linali kukhala pa nthawiyo.

Kutumikila ku Quebec

Mu 1951, ofesi ya nthambi inapempha Mboni zimene zinali kukwanitsa kukamba ci French, kuganizila zosamukila ku pulovinsi ya Quebec kumene kunali anthu okamba ci French. Kumeneko kunali kufunikila ofalitsa ambili. N’nali kudziŵa kukamba ci French na Cingelezi, conco n’navomela utumiki umenewo. Ndipo ananitumiza kukatumikila m’tauni ya Rouyn. Sin’nali kudziŵana na munthu aliyense kumeneko. Monga nakambila kuciyambi, n’nalibe ciliconse koma adilesi yokha. Koma zinthu zinaniyendela bwino. M’bale Marcel na ine tinakhala mabwenzi, ndipo tinasangalala kutumikila limodzi ku Quebec kwa zaka 4. Ndipo m’kupita kwa nthawi n’nakhala mpainiya wapadela.

KULOŴA SUKULU YA GILIYADI NA ZOKUMANA NAZO ZINA

Nili ku Quebec, n’nasangalala kwambili kulandila ciitano cokaloŵa nawo kalasi ya nambala 26 ya Giliyadi ku South Lansing, New York. N’namaliza maphunzilo yanga pa February 12, 1956, ndipo n’natumizidwa kudziko la ku West Africa lomwe tsopano limachedwa Ghana. b Koma nikalibe kupita, n’nafunika kubwelela ku Canada kwa milungu yocepa poyembekezela kuti ziphaso zanga zoyendela zikhale m’malo. N’nali kuganiza kuti zimenezi zidzacitika m’milungu iŵili kapena itatu.

Komabe n’nayembekezela ziphaso zimenezo kwa miyezi 7 mu mzinda wa Toronto. Pa nthawi imeneyo n’nali kukhala ku nyumba kwa m’bale Cripps, ndipo n’nadziŵana na mwana wawo wa mkazi Sheila. Ndipo tinagwa m’cikondi. Pamene n’nali kuganiza zom’funsila cikwati, ziphaso zanga zinakhala zokonzeka. Pambuyo poipemphelela nkhaniyi, Sheila na ine tinagwilizana kuti nipite kumene n’natumizidwa. Tinagwilizana kuti tizilembelana makalata kuti tione ngati tingadzakwatilane m’tsogolo. Kucita izi kunali kovuta, koma pambuyo pake tinazindikila kuti kucita zimenezi kunali koyenela.

Ulendo wopita ku mzinda wa Accra ku Ghana unan’tengela mwezi umodzi. Pa ulendowu n’naseŵenzetsa sitima, sitima ya pamadzi, komanso ndeke. N’tafika ku Ghana, n’naikidwa kukhala woyang’anila cigawo. N’nafunika kuzungulila dziko lonse la Ghana komanso maiko ena apafupi monga Ivory Coast (lomwe tsopano limachedwa Côte d’Ivoire) na Togoland (lomwe tsopano limachedwa Togo). Nthawi zambili n’nali kuyenda nekha poseŵenzetsa galimoto limene nthambi linanipatsa. Pa maulendo amenewa opita kukaona abale na alongo, n’nali kukhala wokondwela kwambili!

Ku mapeto kwa mlungu ulionse, n’nali kukhala na mbali pa misonkhano ya dela. Tinalibe mabwalo ocitilako misonkhano. Conco abale anali kupanga mtenje poseŵenzetsa nsungwi komanso nthambi za kanjeza kuti tikhaleko na mthunzi. Popeza tinalibe mafiliji osungilamo zakudya, abale anali kubwela na ziŵeto, ndipo tinali kuzisungila pafupi na malo a msonkhano. Akafuna kupeleka cakudya kwa opezeka pa msonkhano, anali kupha nyama zimenezi.

Nthawi zina pa misonkhano imeneyi panali kucitika zinthu zoseketsa. Mwa citsanzo, pamene m’bale Herb Jennings, c amene anali mmishonale mnzanga anali kukamba nkhani, ng’ombe inathaŵa kumene anali kuisungila. Ndipo inaimilila pakati pa anthu omvetsela na pulatifomu. M’bale Jennings analeka kukamba nkhani. Ng’ombeyo inaoneka yongazima, koma abale anayi anakwanitsa kuigwila na kuibweza kumene inacoka. Ndipo anthu anafuula mosangalala.

Mkati mwa mlungu, n’nali kuonetsa anthu a m’midzi yapafupi filimu yonena za nchito yathu yolalikila ya padziko lonse yamutu wakuti, The New World Society in Action. Kuti nicite zimenezi, n’nali kumanga nsalu pakati pa mitengo iŵili na kuseŵenzetsa pulojekita poonetsa filimu imeneyi. Anthu anaikonda kwambili filimuyo. Ambili a iwo, imeneyi inali filimu yoyamba imene anaonapo. Akaona anthu akubatizika m’vidiyo, iwo anali kuomba m’manja. Filimu imeneyo inathandiza aja amene anaiona kuzindikila kuti ndife gulu logwilizana la padziko lonse.

Tinakwatilana mu 1959 ku Ghana

N’takhala ku Africa pafupifupi zaka ziŵili, n’nasangalala kukapezeka pa msonkhano wa maiko wa mu 1958 womwe unacitikila mu mzinda wa New York. Zinali zokondweletsa kuonananso na Sheila. Iye anabwela kucokela ku Quebec komwe anali kutumikila monga mpainiya wapadela. Tinali kulembelana makalata, koma tsopano cifukwa tinali limodzi, n’namufunsila ukwati ndipo iye anavomela. N’nalembela M’bale Knorr d kalata yom’pempha ngati zinali zotheka Sheila kuloŵa Sukulu ya Giliyadi kuti adzatumikile nane ku Africa. M’bale Knorr anavomela. Patapita nthawi, Sheila anabwela ku Ghana ndipo tinakwatilana pa October 3, 1959 mu mzinda wa Accra. Tinaona kuti Yehova anatidalitsadi cifukwa comuika patsogolo mu umoyo wathu.

KUTUMIKILA NA SHEILA KU CAMEROON

Nikugwila nchito pa beteli ya ku Cameroon

Mu 1961 anatipempha kukatumikila ku Cameroon. Titafika kumeneko, n’nakhala wotangwanika kwambili, cifukwa abale ananipempha kuti nikathandize kukhazikitsa ofesi ya nthambi yatsopano kumeneko. Pokhala mtumiki wa nthambi watsopano, n’nali na zambili zofunika kuphunzila. Kenako mu 1965, Sheila anakhala na pathupi. Koma ninene zoona kuti zinali zovuta kusintha umoyo wathu cifukwa sitinali kuyembekezela kuti tingakhale makolo. Ngakhale n’telo, pomwe tinayamba kusangalala cifukwa ca udindo watsopanowo, komanso tikupanga mapulani obwelela ku Canada, tinalandila nkhani yomvetsa cisoni.

Sheila anapita padela. Dokotala anatiuza kuti mwana amene anamwalilayo anali wam’muna. Zimenezi zinacitika zaka 50 zapitazo koma sitinaziiŵale. Ngakhale kuti tinali a cisoni cifukwa ca zimene zinacitikazo, tinakhalabe mu utumikiwo umene tinali kuukonda ngako.

Tili na Sheila ku Cameroon mu 1965

Nthawi zambili, abale ku Cameroon anali kuzunzidwa cifukwa cosakhalila mbali m’zandale. Ndipo zinthu zinali kuipa kwambili maka-maka pa nthawi yosankha mtsogoleli wa dziko. Pa May 13, 1970, cinthu cimene tinali kupemphelela kuti cisacitike, cinacitika. Pa tsikulo, boma linaletsa nchito ya Mboni za Yehova. Ndipo boma inalanda ofesi yathu ya nthambi yokongola imene tinali titangokhalamo kwa miyezi 5 cabe. Pasanathe mlungu umodzi amishonale onse, kuphatikizapo ine na Sheila, tinacotsedwa m’dzikomo. Zinali zovuta kusiya abale na alongo athu cifukwa tinali kuwakonda kwambili, ndipo tinali kudela nkhawa mmene zinthu zidzakhalile kwa iwo.

Kwa miyezi 6 yotsatila tinali kukhala ku ofesi ya nthambi ya ku France. Nili kumeneko n’napitiliza kucita zonse zimene nikanatha kuti nisamalile zofunikila za abale a ku Cameroon. Mu December caka cimeneco, tinatumizidwa ku ofesi ya nthambi ya ku Nigeria imene inayamba kuyang’anila nchito ya ku Cameroon. Abale na alongo ku Nigeria anatilandila mwansangala, ndipo tinasangalala kutumikila kumeneko kwa zaka zingapo.

CISANKHO COVUTA

Mu 1973, tinafunika kupanga cisankho covuta kwambili. Sheila anali na vuto la thanzi. Pamene tinali pa msonkhano wa cigawo ku New York, mwacisoni Sheila ananiuza kuti, “Siningapitilize utumikiwu! Nalema, ndipo nthawi zambili nimadwaladwala.” Iye anali atatumikila nane ku West Africa kwa zaka zoposa 14. N’nayamikila kwambili kutumikila naye limodzi mokhulupilika, koma tinafunikila kupanga masinthidwe. Titakambilana nkhaniyi na kuipemphelela kwa kanthawi, tinasankha kuti tibwelele ku Canada komwe akanapeza cithandizo ca mankhwala. Kupanga cisankho cosiya utumiki wathu wa umishonale komanso wa nthawi zonse, kunali kovuta kwambili komanso komvetsa cisoni.

Titafika ku Canada, n’nayamba nchito kwa mnzanga wina amene tinadziŵana naye kale kwambili. Mnzangayo anali na kampani yogulitsa mamotoka kumpoto kwa tauni ya Toronto. Tinayamba kukhala m’nyumba ya lendi, ndipo tinagulilamo katundu wofunikila. Katundu umene tinagulawo unali utagwilapo kale nchito. Tinakwanitsa kuyamba umoyo watsopano popanda kukhala na nkhongole. Tinafuna kukhala umoyo wosalila zambili tili na ciyembekezo cakuti tsiku lina tingadzabwelele mu utumiki wa nthawi zonse. Ndipo tinadabwa kuti zimenezi zinacitika mwamsanga kuposa mmene tinali kuyembekezela.

N’nadzipeleka kuti mlungu ulionse pa Ciŵelu, nizipita kukathandiza nchito yomanga Bwalo la Msonkhano latsopano ku Norval, mu mzinda wa Ontario. M’kupita kwa nthawi, ananipempha kuti niyambe kutumikila monga woyang’anila Bwalo la Msonkhano. Thanzi la Sheila linayamba kukhalako bwino. Cotelo tinaona kuti angakwanitse kucita utumiki watsopanowu. Conco mu June 1974, tinasamukila m’nyumba ya pa Bwalo la Msonkhano. Tinali osangalala kwambili kubwelela mu utumiki wa nthawi zonse!

Tinasangalalanso kuona kuti thanzi la Sheila linapitiliza kusinthila kwabwino. Patapita zaka ziŵili, anatipempha kukagwila nchito ya m’dela ndipo tinavomela. Dela imene tinapatsidwa inali mu pulovinsi ya Manitoba, m’dziko la Canada. Dela limeneli linali lozizila kwambili. Ngakhale n’telo, tinasangalala kudziŵana na abale komanso alongo amene anali acikondi kwambili. Tinaphunzila kuti zilibe kanthu kumene tikutumikila, koma cofunika kwambili ni kupitiliza kutumikila Yehova kulikonse kumene tingakhale.

KUPATSIDWA UPHUNGU WOTHANDIZA

Titatumikila m’dela kwa zaka zingapo, mu 1978 anatiitana kuti tikatumikile pa Beteli ya ku Canada. Posakhalitsa, n’napatsidwa uphungu woŵaŵa koma wothandiza. Nthawi ina n’napatsidwa mwayi wokamba nkhani ya ola limodzi na hafu mu ci French, pa msonkhano wapadela umene unacitikila mu mzinda wa Montreal. N’zacisoni kuti nkhani yanga sinawafike pamtima omvetsela, moti ambili anasiya kumvetsela. Conco m’bale wa m’Dipatimenti ya Utumiki ananipatsa uphungu cifukwa ca zimenezi. Kunena zoona, n’nafunika kuzindikila nthawi imeneyo kuti sin’nali mlankhuli waluso kwambili. Koma uphunguwo sin’naulandile bwino. Makambilano athu sanayende bwino. N’nakhumudwa poganiza kuti iye anali kungokhwimitsa zinthu, komanso kuti sananiyamikile pa zimene n’nacita bwino. N’nalakwitsa poganizila kwambili mmene uphunguwo unapelekedwela, komanso mmene n’nali kumuonela m’bale amene anapeleka uphunguwo.

N’napatsidwa uphungu wothandiza pambuyo pokamba nkhani mu ci French

Patapita masiku ocepa, m’bale wa m’Komiti ya Nthambi anabwela kudzakamba nane za nkhaniyo. N’navomela kuti sin’naulandile bwino uphunguwo, ndipo n’napepesa. Kenako n’nakambilana na m’bale amene ananipatsa uphungu uja, iye ananikhululukila mokoma mtima. Cocitikaci, cinaniphunzitsa mfundo yofunika imene sin’dzaiŵala yakuti nifunika kukhala wodzicepetsa. (Miy. 16:18) Nakhala nikupemphela kwa Yehova mobweleza-bweleza pa nkhani imeneyi, ndipo natsimikiza mtima kuti niziona uphungu moyenela.

Tsopano nakhala nikutumikila pa Beteli ya ku Canada kwa zaka zoposa 40. Ndipo kuyambila mu 1985, nakhala nikutumikila m’Komiti ya Nthambi. Mu February 2021, mkazi wanga wokondeka Sheila anagona mu imfa. Kuwonjezela pa kuvutika na cisoni, pali pano nilinso na mavuto a thanzi. Koma nimatangwanika na kutumikila Yehova, ndipo kumanibweletsela cimwemwe, moti ‘nimaona kuti masiku a moyo wanga akudutsa mofulumila kwambili.’ (Mlal. 5:20) Ngakhale kuti nakumana na mavuto ambili pa umoyo wanga, mavuto amenewo sangapose cimwemwe cimene napeza. Kuika Yehova patsogolo pa umoyo wanga komanso kukhala mu utumiki wa nthawi zonse kwa zaka 70, kwanibweletsela madalitso oculuka. Pemphelo langa ni lakuti abale na alongo acinyamata, apitilize kuika Yehova patsogolo. Sinikayikila kuti kucita zimenezi, kudzawathandiza kukhala na umoyo wacimwemwe komanso waphindu umene umatheka kokha cifukwa cotumikila Yehova.

a Onani mbili ya moyo wa m’bale Marcel Filteau, m’nkhani yakuti “Yehova Ndiye Pothaŵirapo Panga ndi Mphamvu Yanga,” mu Nsanja ya Olonda ya February 1, 2000.

b Britain ndiyo inali kulamulila cigawo cimeneci ca Africa mpaka mu 1957, ndipo cinali kuchedwa Gold Coast.

c Onani mbili ya moyo wa m’bale Herbert Jennings, m’nkhani yakuti “Simudziŵa Chimene Chidzagwa Maŵa,” mu Nsanja ya Olonda ya December 1, 2000.

d M’bale Nathan H. Knorr ndiye anali kutsogolela nchito yathu pa nthawiyo.