Cikhulupililo—Khalidwe Limene Limatithandiza Kukhala Olimba Mwauzimu
CIKHULUPILILO n’camphamvu kwambili. Mwacitsanzo, olo kuti Satana amafuna kutiwononga mwauzimu, cikhulupililo cimatithandiza ‘kuzimitsa mivi yonse yoyaka moto ya woipayo.’ (Aef. 6:16) Ngati tili na cikhulupililo, tingapilile mavuto aakulu okhala ngati phili. Yesu anauza ophunzila ake kuti: “Ngati mutakhala ndi cikhulupililo cofanana ndi kanjele ka mpilu kucepa kwake, mudzatha kuuza phili ili kuti, ‘Coka pano upite apo,’ ndipo lidzacokadi.” (Mat. 17:20) Popeza cikhulupililo cingatithandize kukhala wolimba mwauzimu, tingacite bwino kukambilana mafunso aya: Kodi cikhulupililo n’ciani? Kodi kukhala na mtima wokonda coonadi kungatithandize bwanji kukhala na cikhulupililo? Kodi tingalimbitse bwanji cikhulupililo cathu? Nanga tiyenela kukhulupilila ndani?—Aroma 4:3.
KODI CIKHULUPILILO N’CIANI?
Cikhulupililo cimaphatikizapo zambili, osati cabe kukhulupilila zimene Baibo imaphunzitsa, cifukwa ngakhale “ziŵanda nazonso zimakhulupilila [kuti Mulungu aliko] ndipo zimanjenjemela.” (Yak. 2:19) Nanga cikhulupililo n’ciani maka-maka?
Baibo imafotokoza cikhulupililo m’njila ziŵili. Njila yoyamba, imati: “Cikhulupililo ndico ciyembekezo cotsimikizika ca zinthu zoyembekezeledwa.” (Aheb. 11:1a) Ngati muli na cikhulupililo, simudzakayikila olo pang’ono kuti zilizonse zimene Yehova amakamba n’zoona komanso kuti zidzacitika. Mwacitsanzo, Yehova anauza Aisiraeli kuti, “Ngati anthu inu mungathe kuphwanya pangano langa loti kukhale usana ndi pangano langa loti kukhale usiku, kuti usana ndi usiku zisafike pa nthawi yake, ndiye kuti inenso ndingathe kuphwanya pangano langa ndi Davide mtumiki wanga.” (Yer. 33:20, 21) Kodi mumaopa kuti nthawi ina dzuŵa lidzaleka kutuluka komanso kuloŵa, zimene zingapangitse kuti kusakhale usana na usiku? Ngati simukayikila zakuti tsiku lililonse dzuŵa lidzatuluka na kuloŵa, kodi muyenela kukayikila zakuti Mlengi wa zinthu zimenezi adzakwanilitsa zimene analonjeza? Mwacionekele, simungatelo.—Yes. 55:10, 11; Mat. 5:18.
Njila yaciŵili, Baibo imakamba kuti cikhulupililo ni “umboni wooneka wa zinthu zenizeni, ngakhale kuti n’zosaoneka.” Cikhulupililo cikufotokozedwa kuti ni “umboni wooneka” wa zinthu zimene sitingathe kuziona na maso athu, koma ni zeni-zeni. (Aheb. 11:1b) N’citsanzo citi cimene cionetsa kuti tingathe kukhulupilila zinthu olo kuti sitingathe kuziona? Yelekezelani kuti mwana wakufunsani kuti, ‘Mudziŵa bwanji kuti mphepo iliko? Ngakhale kuti mphepo mukalibe kuionapo, mungauze mwanayo zinthu zimene zimaonetsa kuti iliko. Mungamuuze za mpweya umene timapuma, kugwedezeka kwa masamba na mitengo, na zina. Mwana akakhutila na umboni umenewu, amayamba kukhulupilila kuti zinthu zosaoneka ni zeni-zeni. Mofananamo, cikhulupililo cimazikidwa pa umboni wosatsutsika.—Aroma 1:20.
MTIMA WOKONDA COONADI UMATITHANDIZA KUKHALA NA CIKHULUPILILO
Monga takambila, cikhulupililo cimazikidwa pa umboni. Conco, kuti munthu akhale na cikhulupililo, coyamba afunika ‘kudziŵa coonadi molondola.’ (1 Tim. 2:4) Koma kucita izi pakokha sikokwanila. Mtumwi Paulo anati: “Munthu amakhala ndi cikhulupililo mumtima mwake.” (Aroma 10:10) Munthu afunika kukhulupilila coonadi komanso kucikonda. Akatelo, m’pamene angakhale wofunitsitsa kuonetsa cikhulupililo cake, kutanthauza kucita zinthu mogwilizana na coonadi. (Yak. 2:20) Munthu wosayamikila coonadi amakana ngakhale umboni wosatsutsika, cifukwa safuna kusintha zimene amakhulupilila, kapena amafuna kucita zimene mtima wake ufuna. (2 Pet. 3:3, 4; Yuda 18) Ndiye cifukwa cake m’nthawi yakale, anthu ena sanakhale na cikhulupililo, olo kuti anaona zozizwitsa. (Num. 14:11; Yoh. 12:37) Mzimu woyela wa Mulungu umabala khalidwe la cikhulupililo mwa anthu okhawo amene amakonda coonadi.—Agal. 5:22; 2 Ates. 2:10, 11.
ZIMENE ZINATHANDIZA DAVIDE KUKHALA NA CIKHULUPILILO COLIMBA
Mfumu Davide anali mmodzi wa anthu amene anali na cikhulupililo colimba. (Aheb. 11:32, 33) Koma si onse m’banja lawo amene anali na cikhulupililo monga cake. Mwacitsanzo, pa nthawi ina, Davide atakamba mawu oonetsa kuipidwa na citonzo ca Goliyati, Eliyabu, m’bale wake wamkulu kwambili wa Davide, anamudzudzula Davideyo. Izi zinaonetsa kuti Eliyabu analibe cikhulupililo. (1 Sam. 17:26-28) Zionetsanso kuti ife anthu sitibadwa na cikhulupililo, ndipo siticita kucitengela kwa makolo athu monga coloŵa. Conco, Davide anakhala na cikhulupililo cifukwa cakuti anali pa ubale na Yehova.
Zimene Davide anakamba mu Salimo 27, zionetsa zimene zinam’thandiza kukhala na cikhulupililo colimba. (Vesi 1) Davide anali kusinkha-sinkha pa zinthu zimene anakumana nazo mu umoyo wake, komanso za mmene Yehova anagonjetsela adani ake. (Mavesi 2 na 3) Iye anali kuyamikila kwambili makonzedwe amene Yehova anakhazikitsa okhudza kulambila. (Vesi 4) Davide anali kulambila Yehova pa cihema pamodzi na olambila anzake. (Vesi 6) Anali kupemphela kwa Yehova na mtima wonse kuti am’dziŵe bwino. (Mavesi 7 na 8) Cinanso, Davide anali kufuna kulangizidwa na Mulungu kuti aziyenda m’njila zake. (Vesi 11) Khalidwe la cikhulupililo linali lofunika kwambili kwa Davide, cakuti anakamba kuti: “Ngati ndikanakhala wopanda cikhulupililo . . . ndikanataya ciyembekezo.—Vesi 13.
MMENE MUNGALIMBITSILE CIKHULUPILILO CANU
Na imwe mungakhale na cikhulupililo monga ca Davide ngati mutengela kaganizidwe na kacitidwe ka zinthu kamene kafotokozedwa mu Salimo 27. Popeza cidziŵitso colondola ndico maziko a cikhulupililo, muyenela kuŵelenga mwakhama Mawu a Mulungu na zofalitsa zophunzilila Baibo. Mukatelo, zidzakhala zosavuta kukhala na cikhulupililo, cimene ni limodzi mwa makhalidwe amene mzimu wa Mulungu umabala. (Sal. 1:2, 3) Conco, muzipatula nthawi yosinkha-sinkha zimene mwaŵelenga. Kusinkha-sinkha kudzakuthandizani kukhala na mtima woyamikila kwambili Yehova. Izi zidzakuthandizani kukhala wofunitsitsa kuonetsa cikhulupililo canu, mwa kumulambila pa misonkhano ya mpingo na kuuzako ena za ciyembekezo canu. (Aheb. 10:23-25) Komanso, timaonetsa cikhulupililo mwa kupitiliza ‘kupemphela nthawi zonse, osaleka.’ (Luka 18:1-8) Cotelo, “muzipemphela mosalekeza” kwa Yehova, muli na cikhulupililo cakuti “amakudelani nkhawa.” (1 Ates. 5:17; 1 Pet. 5:7) Cikhulupililo cimatisonkhezela kucita zoyenela, ndipo tikamacita zoyenela, cikhulupililo cathu cimalimba kwambili.—Yak. 2:22.
MUZIKHULUPILILA YESU
Usiku wakuti maŵa aphedwa, Yesu anauza ophunzila ake kuti: “Khulupililani Mulungu, khulupililaninso ine.” (Yoh. 14:1) Conco, kuphatikiza pa kukhulupilila Yehova, tiyenelanso kukhulupilila Yesu. Kodi mungaonetse bwanji kuti mumakhulupilila Yesu? Tiyeni tikambilane njila zitatu.
Yoyamba, muziona dipo monga mphatso imene Mulungu anakupatsani inu panokha. Mtumwi Paulo anati: “Ndikukhala mokhulupilila Mwana wa Mulungu, amene anandikonda ndi kudzipeleka yekha cifukwa ca ine.” (Agal. 2:20) Ngati mumakhulupilila Yesu, simukayikila zoti dipo lingakuthandizeni, komanso kuti ni maziko okhululukila macimo anu. Simukayikilanso zakuti limakupatsani ciyembekezo cokapeza moyo wosatha, ndiponso kuti ni umboni waukulu wakuti Mulungu amakukondani. (Aroma 8:32, 38, 39; Aef. 1:7) Kuona dipo mwanjila imeneyi kumakuthandizani kuti musamadzione ngati opanda pake, kapena kudziimba mlandu kwambili cifukwa ca zophophonya zanu.—2 Ates. 2:16, 17.
Yaciŵili, muziyandikila Yehova mwa kupemphela. Zimenezi n’zotheka cifukwa ca nsembe ya Yesu. Cifukwa ca dipo, timapemphela kwa Yehova “ndi ufulu wa kulankhula, kuti aticitile cifundo ndi kutisonyeza kukoma mtima kwakukulu pa nthawi imene tikufunika thandizo.” (Aheb. 4:15, 16; 10:19-22) Pemphelo limatilimbikitsa kuti tisagonje tikayesedwa kuti ticite chimo.—Luka 22:40.
Yacitatu, muzimvela Yesu. Mtumwi Yohane analemba kuti: “Iye wokhulupilila mwa Mwanayo ali nawo moyo wosatha. Wosamvela Mwanayo sadzauona moyowu, koma mkwiyo wa Mulungu ukhalabe pa iye.” (Yoh. 3:36) Onani kuti pa lembali, Yohane anafotokoza kusiyana pakati pa munthu wacikhulupililo na munthu wosamvela. Conco, timaonetsa kuti timakhulupilila Yesu mwa kukhala womvela. Timamvela Yesu mwa kutsatila “cilamulo ca Khristu,” kutanthauza zonse zimene iye anaphunzitsa na kutilamula. (Agal. 6:2) Timamvelanso Yesu mwa kutsatila malangizo amene amapeleka kupitila mwa “kapolo wokhulupilika ndi wanzelu.” (Mat. 24:45) Ngati timvela Yesu, tidzakwanitsa kupilila mavuto aakulu, okhala ngati cimphepo cam’kuntho.—Luka 6:47, 48.
‘DZILIMBITSENI PAMAZIKO A CIKHULUPILILO CANU COYELA KOPAMBANA’
Tsiku lina, mwamuna wina anafuula kwa Yesu kuti: “Cikhulupililo ndili naco! Limbitsani cikhulupililo canga!” (Maliko 9:24) Munthu ameneyu anali naco ndithu cikhulupililo. Koma cifukwa codzicepetsa, anazindikila kuti anafunika cikhulupililo cowonjezeleka. Mofanana na munthu ameneyu, ife tonse pa nthawi ina tidzakumana na zinthu zofuna cikhulupililo colimba. Ndipo tonse tingathe kulimbitsa cikhulupililo cathu pali pano. Monga mmene taonela, timalimbitsa cikhulupililo cathu mwa kuŵelenga Mawu a Mulungu na kuwasinkha-sinkha. Kucita izi kumatithandiza kukhala na mtima woyamikila kwambili Yehova. Kuwonjezela apo, cikhulupililo cathu cimalimba ngati timalambila Yehova pamodzi na Akhristu anzathu, kuuzako ena za ciyembekezo cathu, na kupemphela mosalekeza. Ndipo tikalimbitsa cikhulupililo cathu, timalandila mphoto yapamwamba kuposa zonse. Mawu a Mulungu amatilimbikitsa kuti: “Okondedwa, podzilimbitsa pamaziko a cikhulupililo canu coyela kopambana, . . . pitilizani kucita zinthu zimene zingacititse Mulungu kukukondani.”—Yuda 20, 21.