Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI YOPHUNZILA 33

Muzikondwela na Mwayi Wanu wa Utumiki

Muzikondwela na Mwayi Wanu wa Utumiki

“Kuona ndi maso kuli bwino kuposa kulakalaka ndi mtima.”—MLAL. 6:9.

NYIMBO 111 Zifukwa Zokhalila Acimwemwe

ZIMENE TIKAMBILANE *

1. Kodi anthu ambili akucita zotani kuti awonjezele utumiki wawo?

 TILI na nchito yaikulu yofunika kugwila pamene mapeto a dongosolo lino akuyandikila. (Mat. 24:14; Luka 10:2; 1 Pet. 5:2) Tonsefe timafuna kutumikila Yehova mmene tingathele. Ndipo ambili akuwonjezela utumiki wawo. Ena ali na colinga cofuna kukhala apainiya, kukatumikila pa Beteli, kapena kugwilako nchito zamamangidwe m’gulu la Mulungu. Ndipo abale ambili akukalamila kuti ayenelele kukhala atumiki othandiza kapena akulu. (1 Tim. 3:1, 8) Yehova amakondwela kwambili akaona mzimu wodzipeleka umene anthu ake ali nawo.—Sal. 110:3; Yes. 6:8.

2. Kodi tingamvele bwanji ngati sitinakwanilitse zina mwa zolinga zathu zauzimu?

2 Komabe, tingalefuke tikaona kuti nthawi ikupita koma sitinakwanilitse zina mwa zolinga zathu zauzimu. Kapena tingakhwethemuke tikaona kuti sitingakwanitse kucita mautumiki ena m’gulu la Mulungu cifukwa ca msinkhu wathu, kapena cifukwa ca mmene zinthu zili mu umoyo wathu. (Miy. 13:12) Ni mmene zinalili kwa mlongo Melissa. * Iye anali kufunitsitsa kutumikila pa Beteli, kapena kungena Sukulu ya Alengezi a Ufumu. Anati: “N’nali n’tapitilila zaka zocita mautumiki amenewa. Tsopano, mautumikiwa anangokhala ngati maloto cabe, ndipo nthawi zina zimanilefula.”

3. Kodi ena angafunike kucita ciani kuti ayenelele maudindo owonjezeleka?

3 Ena amene ni acinyamata komanso athanzi labwino, angafunike kukulitsa makhalidwe ena acikhristu asanayenelele maudindo owonjezeleka. N’zoona kuti angakhale anzelu, oganiza bwino, komanso okangalika. Koma angafunikenso kuphunzila kukhala oleza mtima, osamalila bwino nchito imene apatsidwa, komanso aulemu. Ngati muyesetsa kukulitsa makhalidwe amenewa, mwina mukhoza kupatsidwa udindo pa nthawi imene simuyembekezela. Ganizilani cocitika ca m’bale Nick. Pamene anali na zaka 20, iye anakhumudwa kwambili cifukwa sanaikidwe kukhala mtumiki wothandiza. Iye anati: “N’nali kuona kuti pali mbali inayake imene sinicita bwino.” Koma m’bale Nick sanabwelele m’mbuyo. Anapitiliza kucita bwino mu mpingo komanso mu ulaliki. Pano lomba, akutumikila m’Komiti ya Nthambi.

4. Tikambilane ciani m’nkhani ino?

4 Kodi munalefuka cifukwa cakuti simunakwanilitse colinga canu cauzimu? Ngati n’telo, muuzeni Yehova mmene mumvelela. (Sal. 37:5-7) Kuwonjezela apo, pemphani Akhristu ofikapo kuuzimu kuti akuuzenkoni malingalilo a mmene mungapitile patsogolo potumikila Mulungu, ndipo yesetsani kutsatila malangizo awo. Mukatelo, mwina mukhoza kulandila mwayi wautumiki, kapena kukwanilitsa colinga canu. Koma monga zinalili kwa mlongo Melissa, amene tam’chula kuciyambi kwa nkhani ino, mwina n’zosatheka panthawi ino kulandila utumiki umene mumaulakalaka. Ndiye mungacite ciani kuti mukhalebe wacimwemwe? Kuti tiyankhe funsoli, m’nkhani ino tikambilane (1) kumene tingapeze cimwemwe, (2) mmene tingawonjezele cimwemwe cathu, komanso (3) zolinga zimene tingadziikile kuti tiwonjezele cimwemwe cathu.

KUMENE TINGAPEZE CIMWEMWE

5. Kuti tikhale acimwemwe, kodi tiyenela kusumika maganizo athu pa ciani? (Mlaliki 6:9)

5 Malinga na Mlaliki 6:9, tingapeze cimwemwe ngati ticifuna-funa m’njila yoyenela. (Ŵelengani.) Munthu amene amakondwela na ‘zimene maso aona,’ amakhutila na zimene ali nazo, kuphatikizapo zimene angakwanitse kucita pali pano. Koma munthu amene amangolakalaka mu mtima, amafunitsitsa zinthu zimene kwa iye n’zosatheka kukhala nazo. Kodi pali phunzilo lotani pamenepa? Kuti tikhale acimwemwe, tiyenela kusumika maganizo athu pa zimene tili nazo, komanso pa zolinga zimene n’zotheka kuzikwanilitsa.

6. Kodi tikambilane fanizo liti? Nanga tidzaphunzilapo ciani pa fanizo limenelo?

6 Kodi n’zothekadi kukhala okhutila na zimene tili nazo? Inde, n’zotheka ndithu. Koma anthu ambili amaona kuti n’zosatheka, cifukwa mwacibadwa ife anthu timafuna kukhala na zinthu zatsopano. Komabe, n’zothekadi kukhala okondwela na zimene tili nazo. Kodi izi zingatheke bwanji? Kuti tiyankhe funsoli, tiyeni tikambilane fanizo la Yesu la matalente lopezeka pa Mateyu 25:14-30. Fanizoli lidzatiphunzitsa mmene tingakhalile acimwemwe, komanso mmene tingawonjezele cimwemwe cathu pa mautumiki amene tikucita pali pano.

MMENE MUNGAWONJEZELE CIMWEMWE CANU

7. Fotokozani mwacidule fanizo la Yesu la matalente.

7 M’fanizo la matalente, munthu wina anafuna kupita pa ulendo. Asananyamuke, iye anaitana akapolo ake na kuwapatsa matalente kuti acitile malonda. * Podziŵa zimene akapolo akewo angakwanitse kucita, iye anapatsa kapolo woyamba matalente asanu, waciŵili anam’patsa aŵili, ndipo wacitatu anam’patsa imodzi. Akapolo aŵili anagwila nchito molimbika kuti aculukitse ndalama za mbuye wawo. Koma kapolo wacitatu sanacite nayo ciliconse ndalama imene anapatsidwa, ndipo mbuye wake anam’cotsa nchito.

8. N’cifukwa ciani kapolo woyamba wa m’fanizo anakondwela ngako?

8 Kapolo woyamba ayenela kuti anakondwela ngako pamene mbuye wake anam’patsa matalente asanu. Izi zinali ndalama zankhani-nkhani, ndipo zionetsa kuti mbuye wake anali kum’khulupilila kwambili kapoloyo. Koma bwanji za kapolo waciŵili? Iye akanalefuka poona kuti sanapatsidwe matalente ambili poyelekezela na kapolo woyamba. Koma kodi iye anacita ciani?

Kodi tiphunzilapo ciani pa kapolo waciŵili wochulidwa m’fanizo la Yesu?(1) Iye analandila matalente aŵili kwa mbuye wake.(2) Anagwila nchito molimbika kuti aculukitse ndalama za mbuye wake.(3) Anapindula matalente enanso aŵili a mbuye wake (Onani ndime 9-11)

9. Kodi Yesu sanakambe ciani za kapolo waciŵili? (Mateyu 25:22, 23)

9 Ŵelengani Mateyu 25:22, 23. Yesu sanakambe kuti kapolo waciŵili anakwiya, komanso kusunga cakukhosi pamene anam’patsa matalente aŵili. Ndipo Yesu sanachulepo kuti kapoloyo anadandaula mwa kukamba kuti: ‘Kodi n’zimene anganipatse izi? Inenso nimagwila nchito molimbika mofanana na kapolo amene wapatsidwa matalente asanu! Ngati mbuye wanga amaniona kukhala waulesi, mwina ningowafocela pansi matalente aŵiliwa, na kupita kukacita zanga.’

10. Kodi kapolo waciŵili anacita ciani na matalente amene anapatsidwa?

10 Mofanana na kapolo woyamba, kapolo waciŵili anaona nchito imene anapatsidwa kukhala yofunika ngako, ndipo anaigwila molimbika kuti apindulitse mbuye wake. Zotulukapo n’zakuti iye anapindula matalente enanso aŵili a mbuye wake. Kapolo ameneyo anafupidwa cifukwa cogwila nchito molimbika. Mbuye wake anakondwela kwambili cakuti anam’patsa maudindo owonjezeleka.

11. Kodi tingawonjezele bwanji cimwemwe cathu?

11 Mofananamo, tingawonjezele cimwemwe cathu ngati tiikilapo mtima pa nchito iliyonse imene tingapatsidwe m’gulu la Yehova. Muzikhala ‘otanganidwa kwambili’ na nchito yolalikila, komanso kutengako mbali mokwanila pa zocitika za pa mpingo. (Mac. 18:5; Aheb. 10:24, 25) Muzikonzekelanso bwino misonkhano kuti mukapelekepo ndemanga zolimbikitsa. Musamaione mopepuka mbali ya wophunzila imene angakupatseni pa misonkhano ya mkati mwa mlungu. Akakupemphani kugwila nchito inayake mu mpingo, osazengeleza ndipo khalani wodalilika. Musamatenge mopepuka nchito iliyonse imene mungapatsidwe, moti n’kungoicita mwa mwambo cabe. Muziyesetsa kukulitsa maluso anu. (Miy. 22:29) Mukamaikilapo mtima pa zinthu zauzimu komanso pa nchito zina, mudzapita patsogolo mofulumila, ndipo mudzakhala na cimwemwe cowilikiza. (Agal. 6:4) Cina, cidzakhala copepuka kukondwela na ena amene alandila utumiki umene inu munali kuufuna.—Aroma 12:15; Agal. 5:26.

12. Kodi mlongo Melissa komanso m’bale Nick, anacita zotani kuti awonjezele cimwemwe cawo?

12 Kumbukilani Melissa, mlongo amene anali kufunitsitsa kutumikila pa Beteli kapena kungena Sukulu ya Alengezi a Ufumu. Ngakhale kuti zolinga zake sizinakwanilitsike, iye anati: “Nimayesa kucita zambili mu utumiki wanga wa upainiya, komanso kuseŵenzetsa njila zosiyanasiyana za ulaliki. Izi zanibweletsela cimwemwe cacikulu.” Nanga m’bale Nick anacita ciani atakhumudwa cifukwa cosaikidwa kukhala mtumiki wothandiza? Iye anati: “N’nasumika maganizo anga pa zimene ningakwanitse kucita, monga kulalikila na kupeleka ndemanga zolimbikitsa pa misonkhano. Cinanso, n’nafunsila utumiki wa pa Beteli, ndipo ananiyankha caka cotsatila.”

13. Kodi padzakhala zotulukapo zotani ngati mumaikilapo mtima pa utumiki umene mukucita pali pano? (Mlaliki 2:24)

13 Ngati muikilapo mtima pa utumiki umene mukucita pali pano, kodi zitanthauza kuti mudzalandila mautumiki owonjezeleka kutsogolo? Zikhoza kutheka, monga zinacitikila kwa m’bale Nick. Koma ngati sizingatheke, monga zinalili kwa mlongo Melissa, mungawonjezelebe cimwemwe canu, komanso kukhala okhutila na zimene mungakwanitse kucita. (Ŵelengani Mlaliki 2:24.) Koposa zonse, mudzakhala na cimwemwe cowilikiza podziŵa kuti Mbuye wathu, Yesu Khristu, amayamikila kuyesetsa kwanu.

ZOLINGA ZIMENE ZIMAWONJEZELA CIMWEMWE CATHU

14. Pamene tidziikila zolinga zathu zauzimu, kodi tiyenela kukumbukila ciani?

14 Kodi kusumika maganizo athu pa mautumiki amene tikucita pali pano, kutanthauza kuti tileke kufunafuna njila zina zowonjezela utumiki wathu kwa Yehova? Ayi! Tiyenela kudziikila zolinga zauzimu zimene zingatithandize kukhala aluso mu utumiki, komanso othandiza kwa abale na alongo athu. Tidzakwanilitsa zolinga zathu ngati modzicepetsa timasumika maganizo athu pa kutumikila ena m’malo mofuna kutumikilidwa.—Miy. 11:2; Mac. 20:35.

15. Ni zolinga ziti zimene zingakuthandizeni kuwonjezela cimwemwe canu?

15 Kodi mungadziikile zolinga zotani? Pemphani Yehova kuti akuthandizeni kudziŵa zolinga zimene n’zotheka kwa inu kuzikwanilitsa. (Miy. 16:3; Yak. 1:5) Kodi mungadziikile zolinga zimene tachula  m’ndime yoyamba, monga kucita upainiya wothandiza, wanthawi zonse, kukatumikila pa Beteli, kapena kugwilako nchito zamamangidwe m’gulu la Mulungu? Ngati n’kotheka kwa inu, mungaphunzile cinenelo cina n’colinga cakuti muzilalikila anthu a cineneloco m’gawo lanu, kapena kusamukila ku dela la cineneloco. Kuti mudziŵe zambili pa zolinga ngati zimenezi, onani mutu 10 m’buku lakuti, Gulu Lokhazikitsidwa Kucita Cifunilo ca Yehova, kapena kambilanani na akulu a mu mpingo mwanu. * Pamene muyesetsa kukwanilitsa zolinga zimenezo, kupita kwanu patsogolo kudzaonekela kwa onse, ndipo cimwemwe canu cidzawonjezeleka.

16. Mungacite ciani ngati pali pano simungathe kukwanilitsa colinga canu?

16 Bwanji ngati zolinga zimene takambilana m’nkhani ino simungathe kudzikwanilitsa pali pano? Cimene mungacite, ni kudziikila colinga cina cimene muona kuti mungathe kucikwanilitsa. Tiyeni tione zina mwa zolingazo.

N’zolinga zina ziti zimene mungadziikile?(Onani ndime 17) *

17. Malinga na 1 Timoteyo 4:13, 15, kodi m’bale angacite ciani kuti akhale mphunzitsi waluso?

17 Ŵelengani 1 Timoteyo 4:13, 15. Ngati ndinu m’bale wobatizika, mungadziikile colinga cokhala mphunzitsi waluso. Cifukwa ciani? Cifukwa ngati ‘mudzipeleka’ pa kuŵelenga na kuphunzitsa, mudzakhala dalitso kwa omvela anu. Dziikileni colinga coŵelenga na kuseŵenzetsa phunzilo lililonse m’bulosha lakuti, Citani Khama pa Kuŵelenga na Kuphunzitsa. Ŵelengani phunzilo limodzi palokha, kuliyeseza mofikapo pamene muli kunyumba, komanso kuwaseŵenzetsa malangizowo pokamba nkhani. Funsilankoni malingalilo kwa mlangizi wothandiza, kapena kwa akulu ena “amene amacita khama kulankhula ndi kuphunzitsa.” * (1 Tim. 5:17) Musamangofuna kudziŵa cabe malangizo a m’buloshayo, komanso muziyesetsa kuthandiza omvela anu kulimbitsa cikhulupililo cawo, komanso kuwalimbikitsa kugwilitsila nchito zimene aphunzila. Mwa kutelo, mudzawonjezela cimwemwe canu komanso cawo.

N’zolinga zina ziti zimene mungadziikile?(Onani ndime 18) *

18. N’ciani cingatithandize kukwanilitsa zolinga zathu mu ulaliki?

18 Tonsefe tinapatsidwa nchito yolalikila na kupanga ophunzila. (Mat. 28:19, 20; Aroma 10:14) Kodi mungakonde kunola maluso anu pa nchito yofunika ngako imeneyi? Muziŵelenga malangizo a m’bulosha yakuti Kuphunzitsa, ndipo dziikileni zolinga zokuthandizani kuseŵenzetsa zimene mwaphunzila. Mungapezenso malangizo ena othandiza m’Kabuku ka Misonkhano, komanso mavidiyo a ulaliki wacitsanzo amene timatamba pa misonkhano ya mkati mwa mlungu. Yesani njila zosiyanasiyana kuti muone zothandiza kwa inu. Mukaseŵenzetsa malangizo amenewa, mudzakhala mphunzitsi waluso, ndipo izi zidzakubweletselani cimwemwe cowilikiza.—2 Tim. 4:5.

N’zolinga zina ziti zimene mungadziikile?(Onani ndime 19) *

19. Kodi mungakulitse motani makhalidwe acikhristu?

19 Pamene mudziikila zolinga zanu, musanyalanyaze cinthu cofunika kwambili—kukulitsa makhalidwe acikhristu. (Agal. 5:22, 23; Akol. 3:12; 2 Pet. 1:5-8) Mungacite bwanji zimenezi? Mwacitsanzo, ngati mufuna kulimbitsa cikhulupililo canu, mungaŵelenge nkhani za m’zofalitsa zathu zimene zili na malangizo othandiza kulimbitsa cikhulupililo canu. Mungapindulenso mwa kutamba mavidiyo a JW Broadcasting®, ofotokoza mmene abale na alongo aonetsela cikhulupililo cosagwedela polimbana na mayeso osiyana-siyana. Ndiyeno ganizilani njila za mmene mungatengele cikhulupililo cawo.

20. Kodi tingacite ciani kuti tiwonjezele cimwemwe cathu, na kucepetsa zolefula?

20 Mosakayikila, tonsefe timafunitsitsa kucita zambili potumikila Yehova kuposa zimene tikucita pali pano. M’dziko latsopano la Mulungu, tonse tidzam’tumikila mokwanila. Koma pali pano, ngati tiyesetsa kucita zimene tingathe pom’tumikila, tidzawonjezela cimwemwe cathu na kucepetsako maganizo olefula. Ndipo cofunika kwambili, tidzapeleka ulemu na citamando kwa Yehova, “Mulungu [wathu] wacimwemwe.” (1 Tim. 1:11) Conco, tiyeni tizikondwela na mwayi wa utumiki umene tili nawo.

NYIMBO 82 “Onetsani Kuwala Kwanu”

^ ndime 5 Yehova timam’konda kwambili, ndipo timafuna kucita zonse zotheka pom’tumikila. Ndiye cifukwa cake, timafunitsitsa kuwonjezela utumiki wathu, komanso kukalamila maudindo owonjezeleka mu mpingo. Nanga bwanji ngati mwayesetsa kucita zonse zotheka kuti mukwanilitse zolinga zanu, koma zalepheleka? Kodi n’ciani cingatithandize kupitiliza kukhala okangalika, komanso acimwemwe? Tipeza yankho m’fanizo la Yesu la matalente.

^ ndime 2 Maina ena asinthidwa.

^ ndime 7 KUFOTOKOZELA MAWU ENA: Talente inali ndalama yolingana na malipilo amene munthu wamba anali kulandila akagwila nchito kwa zaka pafupi-fupi 20.

^ ndime 15 Abale obatizika akulimbikitsidwa kugwila nchito molimbika mu mpingo kuti ayenelele kukhala atumiki othandiza kapena akulu. Kuti mudziŵe ziyenelezo zimene mufunika kukwanilitsa, onani mutu 5 na 6 m’buku lakuti, Gulu Lokhazikitsidwa Kucita Cifunilo ca Yehova.

^ ndime 17 KUFOTOKOZELA MAWU ENA: Mlangizi wothandiza ni mkulu amene amasankhidwa kuti azipeleka uphungu wamseli, pakakhala pofunikila kwa akulu na atumiki othandiza pa mbali iliyonse imene angasamalile mu mpingo.

^ ndime 64 MAWU OFOTOKOZELA CITHUNZI: M’bale afufuza m’zofalitsa zathu kuti akwanilitse colinga cake cokhala mphunzitsi waluso.

^ ndime 66 MAWU OFOTOKOZELA CITHUNZI: Pambuyo podziikila colinga comacitako ulaliki wamwayi, mlongo agaŵila ka khadi koloŵela pa webusaiti yathu kwa wogwila nchito pa malo odyela cakudya.

^ ndime 68 MAWU OFOTOKOZELA CITHUNZI: Pofuna kuonetsa makhalidwe acikhristu, mlongo apatsa mlongo mnzake mphatso.