Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI YOPHUNZILA 33

Tengelani Citsanzo ca Danieli

Tengelani Citsanzo ca Danieli

“Iwe ndiwe munthu wokondedwa kwambili.”—DAN. 9:23.

NYIMBO 73 Tilimbitseni Mtima

ZIMENE TIKAMBILANE a

1. N’cifukwa ciyani Ababulo anacita naye cidwi mneneli Danieli?

 MNENELI Danieli anali wacinyamata pamene Ababulo anam’tengela kutali na kwawo monga mkaidi. Koma Ababulowo anacita naye cidwi Danieli. Iwo anaona kuti iye ‘analibe cilema ciliconse, anali wooneka bwino,’ komanso kuti anacokela m’banja lolemekezeka. (1 Sam. 16:7) Pa zifukwa zimenezi, Ababulowo anam’phunzitsa kuti akatumikile m’nyumba yacifumu.—Dan. 1:3, 4, 6.

2. Kodi Yehova anali kumuona motani Danieli? (Ezekieli 14:14)

2 Yehova anali kum’konda Danieli, osati cifukwa ca maonekedwe ake kapena udindo umene anali nawo m’nyumba yacifumu ayi, koma cifukwa ca khalidwe lake labwino. Ndipo Danieli ayenela kuti anali na zaka za m’ma 20 pamene Yehova anam’chula kuti wolungama pamodzi na Nowa komanso Yobu—amuna amene anapanga mbili yabwino na Mulungu kwa zaka zambili. (Gen. 5:32; 6:9, 10; Yobu 42:16, 17; ŵelengani Ezekieli 14:14.) Yehova sanaleke kum’konda Danieli pa umoyo wake wonse.—Dan. 10:11, 19.

3. Kodi tikambilane ciyani m’nkhani ino?

3 M’nkhani ino, tikambilana makhalidwe aŵili a Danieli amene anam’pangitsa kukhala wamtengo wapatali kwa Yehova. Coyamba, tikambilane khalidwe lililonse palokha, na zocitika pamene anaonetsa khalidwelo. Kenaka, tione cimene cinathandiza Danieli kukhala na makhalidwe amenewo. Ndipo cothela, tikambilana mmene tingatengele citsanzo cake. Ngakhale kuti nkhani ino anailembela acinyamata, tonsefe tingapindule na citsanzo ca Danieli.

TENGELANI KULIMBA MTIMA KWA DANIELI

4. Kodi Danieli anaonetsa bwanji kulimba mtima? Fotokozani citsanzo.

4 Anthu olimba mtima angacite mantha, koma samalola kuti manthawo awalepheletse kucita zoyenela. Danieli anali mnyamata wolimba mtima kwambili. Onani zocitika ziŵili izi pamene anaonetsa kulimba mtima kwake. N’kutheka kuti coyamba cinacitika patapita zaka ziŵili Ababulo atawononga Yerusalemu. Mfumu Nebukadinezara ya Babulo inalota maloto othetsa nzelu okhudza cifanizilo cacikulu. Inaopseza kuti idzapha amuna onse anzelu, kuphatikizapo Danieli, akalephela kuiuza zimene yalota komanso kumasulila kwake. (Dan. 2:3-5) Danieli anacitapo kanthu mwamsanga, cifukwa anthu ambili akanaphedwa. Iye “anapita kwa mfumu kukapempha kuti imupatse nthawi kuti adzamasulile maloto ake.” (Dan. 2:16) Izi zinafuna kulimba mtima na cikhulupililo. Baibo siionetsa kuti Danieli anamasulilapo maloto m’mbuyomo. Iye anapempha anzake atatu, amene maina awo acibabulo anali Sadirake, Mesake, na Abedinego, kuti “apemphe Mulungu wakumwamba kuti awacitile cifundo ndi kuwaululila cinsinsi cimeneci.” (Dan. 2:18) Yehova anayankha mapemphelo awo, moti anathandiza Danieli kumasulila maloto a Nebukadinezara. Conco, Danieli na anzakewo sanaphedwe.

5. Ni pa nthawi ina iti pamene Danieli anaonetsa kulimba mtima?

5 Patapita nthawi Danieli atamasulila maloto a Nebukadinezara okhudza cifanizilo cacikulu cija, kulimba mtima kwake kunaikidwanso pa mayeso. Nebukadinezara analotanso maloto ena ovutitsa maganizo. Analota mtengo waukulu komanso wautali. Molimba mtima Danieli anafotokozela Mfumu tanthauzo la malotowo, kuphatikizapo ciweluzo cakuti Mfumuyo idzacita misala na kuleka kulamulila kwa kanthawi. (Dan. 4:25) Cinali capafupi mfumuyo kuona Danieli kuti anali woukila, ndipo ikanamupha. Koma Danieli anaonetsa kulimba mtima moti anapelekabe uthengawo.

6. N’ciyani cinathandiza Danieli kukhala wolimba mtima?

6 N’ciyani cinathandiza Danieli kukhala wolimba mtima kwa moyo wake wonse? Ali mwana, mosakaikila Danieli anaphunzila zambili kwa makolo ake. Mosapeneka, iwo anatsatila malangizo amene Yehova anapatsa makolo aciisraeli, ndipo anaphunzitsa ana awo Cilamulo ca Mulungu. (Deut. 6:6-9) Danieli sanangophunzila cabe Malamulo Khumi a m’Cilamulo, koma anaphunzilanso mfundo zambili za m’Cilamuloco. Mwacitsanzo, anali kudziŵa nyama imene Mwisiraeli angadye komanso imene sangadye. b (Lev. 11:4-8; Dan. 1:8, 11-13) Iye anaphunzilanso mbili yakale ya anthu a Mulungu, ndipo anali kudziŵa zimene zinacitika kwa iwo atalephela kutsatila malamulo a Yehova. (Dan. 9:10, 11) Zocitika pa umoyo wa Danieli zinam’tsimikila kuti Yehova na angelo ake amphamvu anali kum’thandiza.—Dan. 2:19-24; 10:12, 18, 19.

Danieli anakulitsa khalidwe la kulimba mtima cifukwa coŵelenga Mawu a Mulungu, kupemphela, na kudalila Yehova (Onani ndime 7)

7. N’ciyani cina cinathandiza Danieli kukhala wolimba mtima?(Onaninso cithunzi)

7 Danieli anali kuŵelenga zolemba za aneneli a Mulungu, kuphatikizapo maulosi a Yeremiya. Mwa kutelo, iye anazindikila kuti Ayuda amene anali mu ukapolo kwa zaka zambili ku Babulo anali pafupi kumasulidwa. (Dan. 9:2) Cidalilo ca Danieli mwa Yehova cinalimba ngako ataona kukwanilitsika kwa maulosi a m’Baibo. Ndipo anthu amene amadalila Yehova na mtima wonse amakhala olimba mtima kwambili. (Yelekezelani na Aroma 8:31, 32, 37-39.) Coposa zonse, Danieli anali kupemphela nthawi zonse kwa Atate wake wakumwamba. (Dan. 6:10) Anavomeleza macimo ake kwa Yehova, na kumuuza mmene anali kumvela, ndipo anali kupempha thandizo lake. (Dan. 9:4, 5, 19) Iye anali munthu ngati ife tomwe. Conco, kulimba mtima sanacite kubadwa nako. M’malo mwake, anakulitsa khalidweli mwa kuŵelenga Mawu a Mulungu, kupemphela, na kudalila Yehova.

8. Kodi tingacite ciyani kuti tikhale olimba mtima?

8 Kuti tikhale olimba mtima, kodi tiyenela kucitanji? Makolo athu angatilimbikitse kukhala olimba mtima, koma kulimba mtima kumeneko si coloŵa cimene iwo angangosiyila ana awo. Kukhala olimba mtima kuli ngati kuphunzila luso latsopano. Njila imodzi imene tingakhalile na luso, ni kuyang’anitsitsa zimene wokuphunzitsani amacita, na kutengela citsanzo cake. Mofananamo, timaphunzila kukhala olimba mtima tikamayang’anitsitsa mmene ena amaonetsela khalidweli, na kutengela citsanzo cawo. Kodi taphunzila ciyani kwa Danieli? Monga iye, tiyenela kuwadziŵa bwino Mawu a Mulungu. Tiyenela kupanga ubwenzi wathithithi na Yehova mwa kupemphela kwa iye nthawi zonse, na kumuuza mmene tikumvela. Ndipo tizim’dalila, na kukhala otsimikiza kuti adzatithandiza. Ndiyeno cikhulupililo cathu cikayesedwa, tidzakhala olimba mtima.

9. Kodi timapindula bwanji tikakhala olimba mtima?

9 Kulimba mtima kumatipindulila m’njila zambili. Onani citsanzo ici ca m’bale wina dzina lake Ben. Pa sukulu imene anali kuphunzila ku Germany, aliyense anali kukhulupilila za cisanduliko, ndipo anali kuona kuti nkhani ya m’Baibo yakuti zamoyo zinacita kulengedwa ni nthano cabe. Tsiku lina, m’bale Ben anapatsidwa mwayi kuti apite kutsogolo na kufotokoza cifukwa cake amakhulupilila kuti zamoyo zinacita kulengedwa. Molimba mtima iye anafotokoza cikhulupililo cake. Kodi panakhala zotulukapo zotani? Mwiniwakeyo anati: “Aphunzitsi anga anamvetsela mwachelu. Ndipo anapanga makope a cofalitsa cimene n’nagwilitsa nchito, na kugaŵila aliyense m’kalasimo.” Kodi anzake a m’kalasi anakhudzika motani? M’bale Ben anati, “Ambili a iwo anamvetsela zimene n’nafotokoza, ndipo anati anacita nane cidwi.” Monga mmene citsanzo ca m’ble Ben cionetsela, anthu olimba mtima amalemekezedwa na anthu ena. Cina, amakopa anthu oona mtima kuti abwele kwa Yehova. Kukamba zoona, tili na zifukwa zabwino zokhalila olimba mtima.

TENGELANI KUKHULUPILIKA KWA DANIELI

10. Kodi kukhulupilika n’kutani?

10 M’Baibo, liwu laciheberi lomasulidwa kuti “kukhulupilika” kapena kuti “cikondi cosasintha,” limapeleka lingalilo la mmene Mulungu amadzipelekela mwacikondi kwa atumiki ake. Liwulo, limagwilitsidwanso nchito pofotokoza cikondi cimene atumiki a Mulungu amaonetsana. (2 Sam. 9:6, 7)Kukhulupilika kwathu kumalimbilako m’kupita kwa nthawi. Izi ndizo zinacitika kwa Danieli.

Yehova anadalitsa Danieli cifukwa cokhala wokhulupilika mwa kum’tumizila mngelo, na kutseka mikango pakamwa (Onani ndime 11)

11. Kodi kukhulupilika kwa Danieli kunayesedwa bwanji atakalamba? (Onaninso cithunzi pa cikuto.)

11 Pa umoyo wake wonse, Danieli anakumana na zocitika zimene zinayesa kukhulupilika kwake kwa Yehova. Koma mayeso aakulu kwambili anakumana nawo ali na zaka za m’ma 90. Pa nthawiyo, Ababulo anali atagonjetsedwa na Amedi na Aperisiya, ndipo anayamba kulamulidwa na Mfumu Dariyo. Nduna za mfumu zinali kudana naye Danieli, ndipo sizinali kulemekeza Mulungu wake. Conco, anakonza ciwembu kuti Danieli aphedwe. Ndunazo zinanyengelela mfumu Dariyo kukhazikitsa lamulo limene linayesa kukhulupilika kwa Danieli, cifukwa anafunika kusankha kaya kukhala wokhulupilika kwa Mulungu wake kapena kwa mfumu. Kuti Danieli aonetse kuti anali wokhulupilika kwa mfumu, komanso kuti apewe cilango, anangofunikila kuleka kupemphela kwa Yehova kwa masiku 30 cabe. Koma Danieli sanagonje pa mayesowo. Pa cifukwa cimeneci, iye anaponyedwa m’dzenje la mikango. Komabe, Yehova anafupa kukhulupilika kwa Danieli mwa kum’pulumutsa ku mikangoyo. (Dan. 6:12-15, 20-22) Kodi tingacite ciyani kuti tikhalebe okhulupilika kwa Yehova monga Danieli?

12. N’ciyani cinathandiza Danieli kukhalabe wokhulupilika kwa Yehova?

12 Monga takambila kale, cikondi n’cimene cimatisonkhezela kukhala okhulupilika. Danieli anakhalabe wokhulupilika kwa Yehova cifukwa anali kum’konda kwambili Atate wake wakumwamba. Mosakaikila, iye anakulitsa cikondico mwa kuganizila makhalidwe a Yehova, komanso kusinkhasinkha mmene anali kuwaonetsela. (Dan. 9:4) Cina, Danieli anasinkhasinkha na kuyamikila zinthu zabwino zimene Yehova anali kum’citila, komanso kucitila anthu a mtundu wake.—Dan. 2:20-23; 9:15, 16.

Mukam’konda kwambili Yehova mofanana na Danieli, mungakhalebe wokhulupilika kwa iye (Onani ndime 13)

13. (a) Ni zinthu ziti zimene zimayesa kukhulupilika kwa acicepele athu? Fotokozani citsanzo. (Onaninso cithunzi) (b) Malinga na vidiyo ija, kodi mungayankhe motani anthu akakufunsani mmene Mboni za Yehova zimaonela anthu ocita zamathanyula?

13 Mofanana na Danieli, acicepele athu amapezeka kuti ali pakati pa anthu osalemekeza Yehova, na malamulo ake. Anthu otelo amadana na aliyense amene amati amakonda Mulungu. Ena amavutitsa acicepele athu pofuna kuwapangitsa kuti asakhale okhulupilika kwa Yehova. Mwacitsanzo, onani zinacitika kwa mnyamata wina dzina lake Graeme wa ku Australia. Ali ku sekondale, iye anakumana na mayeso. Mphunzitsi anafunsa onse m’kalasi zimene angacite ngati mnzawo waauza kuti amacita mathanyula. Mphunzitsiyo anati onse amene akugwilizana na mcitidwe umenewu aime kulamanja, koma amene sakugwilizana nawo aime kumanzele. M’bale Graeme anati, “Onse m’kalasi anaima kulamanja, kuonetsa kuti akuuvomeleza mcitidwe umenewo, kupatulapo ine na mnzanga wina amene nayenso anali Mboni.” Zimene zinatsatilapo zinayesa kwambili kukhulupilika kwa m’bale Graeme. Iye anati, “Anzathu a m’kalasiwo, ngakhale mphunzitsiyo anayamba kutitonza. N’nayesetsa kukhalila kumbuyo cikhulupililo canga, na kuwafotokozela modekha. Koma ayi ndithu, sizinaphule kanthu.” Kodi m’bale Graeme anamva bwanji atakumana na mayeso amenewa? Mwiniwakeyo anati, “Sin’namve bwino pamene anzanga anali kunitonza. Koma n’nali wacimwemwe podziŵa kuti nakhalila kumbuyo cikhulupililo canga, ndiponso kuti sin’nagonje.” c

14. N’ciyani cingatithandize kukhalabe okhulupilika kwa Yehova?

14 Tingakhalebe okhulupilika kwa Yehova ngati tizamitsa cikondi cathu pa iye monga anacitila Danieli. Timazamitsa cikondi cimeneco tikamaphunzila makhalidwe a Yehova. Mwacitsanzo, tingaphunzile makhalidwe ake ku zinthu zimene anapanga. (Aroma. 1:20) Mungaŵelenge nkhani zazifupi zakuti “Kodi Zinangocitika Zokha?” kapena kupenyelela mavidiyo ake. Zidzakuthandizani kum’konda kwambili Yehova na kum’lemekeza. Mungaŵelengenso bulosha yakuti Kodi Zamoyo Zinacita Kulengedwa? kapena yakuti, Mmene Moyo Unayambila—Mafunso 5 Ofunika Kwambili. Onani zimene mlongo wina wacitsikana wa ku Denmark dzina lake Esther ananena pa mabulosha amenewa. Anati: “Mfundo zake ni zogwila mtima. Mabulosha amenewo sasankhila munthu zimene ayenela kukhulupilila. Koma amangofotokoza mfundo mosavuta, ndipo umasankha wekha zoyenela kukhulupilila.” Nayenso m’bale Ben amene tam’chula uja anati: “Mabulosha amenewo analimbitsa kwambili cikhulupililo canga. Ananitsimikizila kuti Mulungu ndiye analengadi moyo.” Mukaŵelenga nkhani zonsezo, mosakaikila mudzavomeleza zimene Baibo imanena kuti: “Ndinu woyenela, inu Yehova Mulungu wathu wamphamvu, kulandila ulemelelo ndi ulemu, cifukwa munalenga zinthu zonse.”—Chiv. 4:11. d

15. N’ciyaninso cimene tingacite kuti tikhalebe pa ubale wathithithi na Yehova?

15 Cina cingatithandize kukulitsa cikondi cathu pa Yehova, ni kuphunzila za Mwana wake Yesu. Izi n’zimene mlongo wina wacitsikana dzina lake Samira wa ku Germany anacita. Iye anati: “N’nafika pom’dziŵa bwino Yehova kupitila mwa Yesu.” Mlongo Samira ali mwana, cinali kumuvuta kumvetsa kuti Yehova amakhudzika mtima. Koma sanavutike kumvetsa kuti Yesu amakhudzika mtima. Iye anawonjezela kuti, “N’nali kum’konda Yesu cifukwa anali waubwenzi komanso wokonda ana.” Ataphunzila zambili za Yesu, anafika pom’dziŵa bwino Yehova na kuyamba kum’konda kwambili. N’cifukwa ciyani? Mwiniwakeyo anati: “Pang’onom’pang’ono n’nayamba kumvetsa kuti Yesu amatengela ndendende Atate wake. Iwo amafanana m’zambili. N’nazindikila kuti ici n’cimodzi mwa zifukwa zimene Yehova anatumila Yesu padziko lapansi kuti anthu am’dziŵe bwino Yehova.” (Yoh. 14:9) Ngati mufuna kulimbikitsa ubale wanu na Yehova, bwanji osapatula nthawi kuti muphunzile za Yesu mmene mungathele? Mukatelo, cikondi canu pa Yehova cidzakula, komanso mudzakhalabe wokhulupilika kwa iye.

16. Kodi timapindula bwanji tikakhala okhulupilika? (Salimo 18:25; Mika 6:8)

16 Anthu okhulupilika, nthawi zambili amakhala na mabwenzi abwino komanso okhulupilika. (Rute 1:14-17) Kuwonjezela apo, anthu okhulupilika kwa Yehova ali na zifukwa zabwino zokhalila na mtendele wa mumtima. Cifukwa ciyani? Cifukwa Yehova analonjeza kuti adzakhala wokhulupilika kwa anthu okhulupilika kwa iye. (Ŵelengani Salimo 18:25; Mika 6:8.) Tangoganizani—Mlengi wamphamvuzonse ni wofunitsitsa kupalana nafe ubwenzi wathithithi! Ndipo akatelo, palibiletu cidzatilekanitsa na iye, kaya ni mayeso, anthu otsutsa, ngakhalenso imfa imene. (Dan. 12:13; Luka 20:37, 38; Aroma. 8:38, 39) Conco, n’kofunika ngako kutengela citsanzo ca Danieli, cokhalabe wokhulupilika kwa Yehova!

PITILIZANI KUPHUNZILA KWA DANIELI

17-18. N’ciyani cina cimene tingaphunzile kwa Danieli?

17 M’nkhani ino, takambilana makhalidwe aŵili cabe a Danieli. Koma pali zambili zimene tingaphunzile kwa iye. Mwacitsanzo, Yehova anaonetsa Danieli masomphenya angapo komanso kum’lotetsa maloto, ndipo anam’patsa mphamvu zotha kumasulila maulosi. Ambili mwa maulosi amenewo anakwanilitsika kale. Koma ena akufotokoza zocitika zam’tsogolo zimene zidzakhudza munthu aliyense padziko lapansi.

18 M’nkhani yotsatila, tidzakambilana maulosi aŵili amene Danieli analemba. Kumvetsa maulosi amenewo kudzathandiza ife tonse, acicepele komanso acikulile, kupanga zisankho zanzelu. Maulosiwo adzatithandizanso kukhalabe olimba mtima komanso okhulupilika, kuti tikhale okonzeka kudzayang’anizana na mayeso amene akubwela m’tsogolomu.

NYIMBO 119 Tikhale na Cikhulupililo

a Atumiki a Yehova acinyamata amakumana na zocitika zimene zimayesa kulimba mtima kwawo, na kukhulupilika kwawo kwa Yehova. Anzawo a m’kalasi angamawanyodole pokhulupilila kuti zinthu zinacita kulengedwa. Kapena acinyamata anzawo angamawaseke cifukwa cotumikila Mulungu, na kutsatila malamulo ake. Koma monga tionele m’nkhani ino, aja amene amatengela citsanzo ca mneneli Danieli, komanso amene amatumikila Yehova molimba mtima ndiponso mokhulupilika, amakhaladi anzelu.

b Pali zifukwa zitatu zimene ziyenela kuti zinapangitsa Danieli kukana kudya cakudya ca Ababulo: (1) Nyama zimene Ababulo anali kudya zinali zoletsedwa m’Cilamulo. (Deut. 14:7, 8) (2) N’kutheka kuti nyama zimenezo zinali zosakhetsa. (Lev. 17:10-12) (3) Kudya nyamazo kukanakhala ngati kulambila milungu yonyenga.—Yelekezelani na Levitiko 7:15 komanso 1 Akorinto 10:18, 21, 22.

c Onelelani vidiyo yakuti Nchito ya Cilungamo Ceniceni Idzakhala Mtendele,” pa jw.org.

d Cina cingakuthandizeni kukulitsa cikondi canu pa Yehova, ni buku lakuti Yandikirani kwa Yehova. Bukuli limafotokoza mozama makhalidwe a Yehova.