Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI YOPHUNZILA 33

NYIMBO 130 Khalani Wokhululuka

Mmene Mpingo Umaonetsela Maganizo a Yehova Kwa Munthu Amene Wacita Chimo

Mmene Mpingo Umaonetsela Maganizo a Yehova Kwa Munthu Amene Wacita Chimo

“Wina akacita chimo, tili ndi wotithandiza.”1 YOH. 2:1.

ZOFUNIKA KUMVETSETSA

Zimene tingaphunzilepo tikaona mmene mpingo wa m’zaka za zana loyamba wa ku Korinto unacitila naye munthu amene anacita chimo lalikulu.

1. Kodi Yehova amafuna kuti anthu onse acite ciyani?

 YEHOVA anatilenga na ufulu wodzisankhila zocita. Timaseŵenzetsa ufulu umenewu popanga zisankho. Cisankho cofunika kopambana cimene munthu aliyense angapange ni cisankho codzipatulila kwa Yehova na kukhala m’banja la alambili ake. Yehova amafuna kuti munthu aliyense apange cisankho cimeneci. N’cifukwa ciyani? Amafuna zimenezi cifukwa amakonda anthu, ndipo amafunanso kuti zinthu ziziwayendela bwino. Iye amafuna kuti anthu akhale paubwenzi wabwino na iye, komanso kuti akhale na moyo kwamuyaya.—Deut. 30:​19, 20; Agal. 6:​7, 8.

2. Kodi Yehova amafuna kuti anthu onse osalapa acite ciyani? (1 Yohane 2:1)

2 Komabe, Yehova sakakamiza munthu aliyense kuti am’tumikile. Iye amalola munthu aliyense kupanga cisankho com’tumikila kapena ayi. N’ciyani cimacitika ngati Mkhristu wobatizika waphwanya malamulo a Mulungu na kucita chimo lalikulu? Ngati munthuyo si wolapa, ayenela kucotsedwa mumpingo. (1 Akor. 5:13) Ngakhale n’telo, Yehova amakhala wofunitsitsa kuti munthuyo alape na kubwelela kwa iye. Ni iko komwe, ici ndiye cifukwa cacikulu cimene Yehova anapelekela dipo. Colingaco cinali cakuti zizikhala zotheka munthu wocimwa akalapa kukhululukidwa macimo ake. (Ŵelengani 1 Yohane 2:1.) Mulungu wathu wacikondi amapempha ocimwa kuti alape.—Zek. 1:3; Aroma 2:4; Yak. 4:8.

3. Tikambilana ciyani m’nkhani ino?

3 Yehova amafuna kuti titengele kaganizidwe kake pa nkhani ya mmene amaonela chimo, komanso mmene amaonela anthu amene acita chimo. Nkhani ino itithandiza kuona mmene tingacitile zimenezi. Pamene muŵelenga nkhani ino, onani (1) mmene mpingo wa m’zaka za zana loyamba wa ku Korinto unacitila naye munthu amene anacita chimo lalikulu, (2) malangizo amene Paulo anapeleka okhudza mmene mpingo unayenela kucitila naye wocimwayo amene anali atalapa, komanso (3) mmene nkhani ya m’Baibo imeneyi imatithandizila kumvetsa mmene Yehova amaonela Akhristu amene acita chimo lalikulu.

MMENE MPINGO WA KU KORINTO UNACITILA NAYE M’BALE AMENE ANAGWELA M’CHIMO LALIKULU

4. Ni nkhani yotani imene inacitika m’zaka za zana loyamba mumpingo wa ku Korinto? (1 Akorinto 5:​1, 2)

4 Ŵelengani 1 Akorinto 5:​1, 2. Ali paulendo wake wacitatu waumishonale, Paulo anamva nkhani yocititsa manyazi mumpingo wina watsopano wa mumzinda wa Korinto. M’bale wa mumpingo umenewo anali kucita ciwelewele na amayi ake opeza. Khalidwe limeneli linali locititsa manyazi kwambili moti “ngakhale anthu amitundu ina” sanali kulicita. Mpingo unali kulekelela khalidwe locititsa manyazi limeneli, ndipo n’kutheka unalinso kumunyadila m’baleyo cifukwa ca khalidwe lake. N’kuthekanso ena pocita zimenezo anali kuganiza kuti akutengela cifundo ca Mulungu cimene iye amaonetsa pocita zinthu na anthu opanda ungwilo. Koma Yehova sakondwela nazo zinthu zoipa zomwe zimacitika pakati pa anthu ake. Mwa kucita khalidwe limeneli locititsa manyazi, mwamuna ameneyo anali kuwononga mbili yabwino ya mpingo. Akanacititsanso Akhristu ena amene anali kugwilizana naye kutengelako khalidwe lake loipalo. Conco, kodi Paulo analangiza mpingo kuti ucite ciyani?

5. Kodi Paulo analangiza mpingo wa ku Korinto kucita ciyani? Ndipo anatanthauza ciyani? (1 Akorinto 5:13) (Onaninso cithunzi.)

5 Ŵelengani 1 Akorinto 5:13. Mouzilidwa na Mulungu, Paulo analembela kalata mpingo wa ku Korinto yowauza kuti ayenela kucotsa mumpingo wocimwa wosalapayo. Kodi Akhristu okhulupilika anayenela kucita naye motani zinthu m’baleyo? Paulo anawauza kuti ‘asiye kugwilizana’ naye. Kodi izi zinatanthauza ciyani? Paulo anafotokoza kuti lamulo limenelo linaphatikizapo kuleka “ngakhale kudya naye munthu” ameneyo. (1 Akor. 5:11) Pamene tikudya na munthu, timakhalanso na nthawi yoceza naye. Conco zinali zoonekelatu kuti Paulo anatanthauza kuti mpingo unayenela kuleka kuceza naye munthu ameneyo. Izi zinali kudzateteza kuti khalidwe lakelo lisafalikile mumpingo wonse. (1 Akor. 5:​5-7) Kuwonjezela apo, kupewa kwawo kuceza na munthu ameneyo kukanam’pangitsa kuzindikila kuti anali kucita zinthu zoipa kwambili pamaso pa Yehova. Ndipo izi zikanamupangitsanso kukhala wacisoni na kumusonkhezela kulapa.

Mouzilidwa na Mulungu, Paulo analemba kalata youza mpingo kuti ucotse munthu wocimwa wosalapa mumpingo (Onani ndime 5)


6. Kodi mpingo unacita motani utalandila malangizo ocokela kwa Paulo? Nanga kodi munthu wocimwayo anacita ciyani?

6 Paulo atatumiza kalata yake kwa Akhristu a ku Korinto, iye anayamba kudzifunsa ngati mpingo udzalabadila malangizo a m’kalatayo. Kenako Tito anamubweletsela nkhani imene inamusangalatsa. Iye anafotokoza kuti mpingo unalabadila bwino malangizo a m’kalata ya Paulo. (2 Akor. 7:​6, 7) Mpingo unacotsa munthu wolakwayo mumpingo. Koma pasanapite nthawi yaitali kucokela pamene Paulo anatumiza kalatayo, munthu wocimwayo analapa! Iye anasintha khalidwe lake komanso kaonedwe kake ka zinthu. Ndipo anali atayamba kutsatila mfundo za Yehova za makhalidwe abwino. (2 Akor. 7:​8-11) Kodi tsopano Paulo anauza mpingo kuti ucite naye ciyani munthuyo?

MMENE MPINGO UNACITILA NAYE WOCIMWA WOLAPAYO

7. Kodi kucotsa munthu wocimwa mumpingo kunakhala na zotulukapo zabwino ziti? (2 Akorinto 2:​5-8)

7 Ŵelengani 2 Akorinto 2:​5-8. Paulo anawalembela kuti: “Kudzudzulidwa ndi anthu ambili conci [kunali] kokwanila kwa munthu” ameneyo. M’mawu ena, cilango cimene anapatsidwa cinali citakwanilitsa colinga cake. Colinga cotani? Comuthandiza kuti alape.—Aheb. 12:11.

8. Kodi Paulo anauza mpingo wa ku Korinto kuti ucite ciyani?

8 Cotelo Paulo anauza mpingowo kuti: “Tsopano mukhululukileni ndi mtima wonse ndiponso kumutonthoza” m’bale wocimwayo. Iye anawauzanso kuti: “Mumutsimikizile kuti mumamukonda.” Onani kuti Paulo anauza mpingo kuti unayenela kucita zinthu zina kuwonjezela pa kungomulola munthuyo kubwelela pakati pa anthu a Yehova. Paulo anali kufuna kuti abalewo aonetse kuti anamukhululukila munthuyo, komanso kuti amamukonda m’zocita komanso zokamba zawo. Mwa kucita zimenezi, iwo akanaonetsa kuti anamulandila na manja aŵili mumpingo munthu wolapayo.

9. N’cifukwa ciyani n’kutheka kuti ena anazengeleza kukhululukila wocimwa wolapayo?

9 Kodi ena mu mpingowo anazengeleza kulandila munthu wocimwa wolapayo pakati pawo? Baibo siifotokoza. Koma n’kutheka kuti ni mmene zinalili. Mwina zinali conco cifukwa khalidwe lake linabweletsa mavuto mumpingo, ndipo n’kuthekanso ena anali kucitabe manyazi na khalidwe lakelo. Ena mumpingo anafunika kucita khama kuti atsatile malamulo a Yehova a makhalidwe abwino. Conco ena anaona kuti kunali kupanda cilungamo kulandilanso munthu amene anacita macimo oipa otelowo mumpingo. (Yelekezelani na Luka 15:​28-30) Koma n’cifukwa n’ciyani panali pofunika kuti mpingo umuonetse cikondi ceniceni m’bale wawo wolapayo?

10-11. N’ciyani cikanacitika akulu akanakana kukhululukila munthu wocimwa yemwe analapa?

10 Ganizilani zimene zikanacitika ngati akulu akanakana kubwezeletsa munthu wolapadi ameneyo mumpingo, kapena ngati pambuyo pomubwezeletsa, mpingo ukanalephela kumuonetsa cikondi munthuyo. Iye akanafooka cifukwa ca “cisoni copitilila malile.” Iye akanaona kuti alibenso mwayi wotumikila Yehova. Mwina munthuyo akanafika ngakhale poleka kukonzanso ubale wake na Mulungu.

11 Coipa kwambili kuposa pamenepo n’cakuti, ngati abale na alongo mumpingo sakanakhululukila m’bale wolapayo, akanaika paciswe ubale wawo na Yehova. Cifukwa ciyani? Zikanakhala conco cifukwa kucita zimenezo sikukanaonetsa khalidwe la kukhululuka limene Mulungu amaonetsa kwa anthu ocimwa amene alapa. Koma kukanaonetsa khalidwe la Satana la nkhanza komanso lopanda cifundo. Mwa kucita zimenezi, iwo akanalola Satana kuwaseŵenzetsa kuwononga uzimu wa munthu ameneyo.—2 Akor. 2:​10, 11, Aef. 4:27.

12. Kodi mpingo wa ku Korinto ukanatengela bwanji khalidwe la Yehova la kukhululuka?

12 Kodi mpingo wa ku Korinto ukanatengela bwanji khalidwe la Yehova la kukhululuka osati khalidwe la nkhanza la Satana? Ukanacita zimenezo mwa kukhululukila wolapayo monga mmene Yehova amacitila. Onani zimene olemba Baibo ena anakamba zokhudza kukhululuka kwa Yehova. Pokamba za Yehova, Davide anakamba kuti: “Ndinu wabwino ndipo ndinu wokonzeka kukhululuka.” (Sal. 86:5) Mika analemba kuti: “Kodi pali Mulungu winanso wofanana ndi inu, amene amakhululukila zolakwa ndi macimo?” (Mika 7:18) Ndipo Yesaya anakamba kuti: “Munthu woipa asiye njila yake ndipo munthu wopweteka anzake asiye maganizo ake. Iye abwelele kwa Yehova ndipo adzamucitila cifundo. Abwelele kwa Mulungu wathu, cifukwa adzamukhululukila ndi mtima wonse.”—Yes. 55:7.

13. N’cifukwa ciyani kunali koyenela kubwezeletsa wocimwa wolapayo mumpingo? (Onani danga lakuti “ Ni Liti Pamene Munthu Wocimwa wa ku Korinto Anabwezeletsedwa?”)

13 Kuti atengele khalidwe la Yehova, abale a ku Korinto anafunika kulandila munthu wolapayo na kumutsimikizila kuti amamukonda. Mwa kutsatila malangizo a Paulo akuti alandile munthu wocimwa wolapayo, abale na alongo akanaonetsa kuti analidi “omvela pa zinthu zonse.” (2 Akor. 2:9) N’zoona kuti munthuyo anakhala wocotsedwa kwa miyezi yocepa, koma cilango cimene anapatsidwa cinamuthandiza kuti alape. Conco panalibe cifukwa cimene cikanalepheletsa akulu kuti abwezeletse wocimwa wolapayo mumpingo.

MMENE TINGAONETSELE CILUNGAMO NA CIFUNDO CA YEHOVA

14-15. Taphunzilapo ciyani poona mmene mpingo wa ku Korinto unasamalila nkhani ya munthu wolakwayo? (2 Petulo 3:9) (Onaninso cithunzi.)

14 Nkhani ya mmene mpingo wa ku Korinto unacitila zinthu na munthu amene anacita colakwa inalembedwa m’Baibo ‘kuti itilangize.’ (Aroma 15:4) Nkhani imeneyi imatiphunzitsa kuti Yehova salekelela macimo akuluakulu pakati pa anthu ake. Anthu ena amaganiza kuti, cifukwa Yehova ni wacifundo, amalola anthu ocimwa osalapa kukhalabe mumpingo. Koma umu si mmene zilili. Yehova safuna kuti anthu ocimwa osalapa akhalebe pakati pa alambili ake okhulupilika. N’zoona kuti iye ni wacifundo, koma savomeleza makhalidwe onse. Yehova sasintha miyeso yake pa cabwino na coipa. (Yuda 4) Ngati Yehova angalole anthu ocimwa amene safuna kulapa kupitiliza kukhala mumpingo, zingaonetse kuti alibe cifundo, ndipo zingavulaze mpingo wonse.—Miy. 13:20; 1 Akor. 15:33.

15 Ngakhale n’telo, tidziŵa kuti Yehova safuna kuti munthu aliyense akawonongeke. Iye amafuna kupulumutsa anthu zikakhala zotheka kucita zimenezo. Iye amaonetsa cifundo kwa anthu amene asintha mitima yawo kuti akhalenso paubale wabwino na iye. (Ezek. 33:11; ŵelengani 2 Petulo 3:9.) Conco pamene munthu wa ku Korinto analapa na kusiya njila yake ya ucimo, Yehova anaseŵenzetsa Paulo kulangiza mpingo kuti umukhululukile munthuyo na kumulandilanso mumpingo.

Potengela makhalidwe a Yehova a cikondi na cifundo, mpingo umalandila na manja aŵili amene abwezeletsedwa mumpingo (Onani ndime 14-15)


16. Mumamva bwanji mukaona mmene mpingo wa ku Korinto unasamalila nkhani ya munthu amene anacita chimo?

16 Kukambilana mmene mpingo wa ku Korinto unasamalila nkhani ya munthu amene anacita chimo, kwatithandiza kuona kuti Yehova ni Mulungu wacikondi komanso wacilungamo. (Sal. 33:5) Kudziŵa zimenezi kumatisonkhezela kuti timutamande mokulilapo Mulungu wathu. Ni iko komwe, tonse ndife ocimwa, ndipo nthawi na nthawi timafuna cikhululuko cake. Aliyense wa ife ali na cifukwa cabwino coyamikila Yehova kaamba ka dipo, imene imatheketsa kuti atikhululukile macimo athu. N’zolimbikitsa zedi kudziŵa kuti Yehova amakonda kwambili anthu ake ndiponso kuti amawafunila zabwino!

17. Tidzakambilana ciyani m’nkhani zotsatila?

17 Ngati munthu wacita chimo lalikulu masiku ano, kodi akulu mumpingo angatengele bwanji khalidwe la Yehova la cikondi, na kuthandiza wocimwayo kulapa? Kodi mpingo uyenela kucita ciyani ngati akulu agamula kucotsa munthu mumpingo kapena kumubwezeletsa? Mafunso amenewa adzayankhidwa m’nkhani zotsatila.

NYIMBO 109 Tizikondana ndi Mtima Wonse