Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI YOPHUNZILA 49

“Pali Nthawi” Yogwila Nchito na Nthawi Yopumula

“Pali Nthawi” Yogwila Nchito na Nthawi Yopumula

“Bwelani kuno, tipite kwatokha kopanda anthu kuti mupumule pang’ono.”—MALIKO 6:31.

NYIMBO 143 Musaleke Kugwila Nchito, Kuyang’anila, na Kuyembekezela

ZIMENE TIKAMBILANE *

1. Kodi anthu ambili amaiona bwanji nchito?

KODI anthu ambili kumene mukhala amaiona bwanji nchito? M’maiko ambili, anthu amagwila nchito kwambili ndiponso kwa maawazi oculuka kuposa kale. Cifukwa cogwila nchito mopitilila malile, kaŵili-kaŵili anthu sapeza nthawi yopumula, yoceza na mabanja awo, kapena yophunzila za Mulungu. (Mlal. 2:23) Palinso anthu ena amene safuna kugwila nchito olo pang’ono, ndipo ali na zifukwa zawo zimene amakanila kugwila nchito.—Miy. 26:13, 14.

2-3. Kodi Yehova na Yesu apeleka citsanzo cotani pa nkhani yogwila nchito?

2 Mosiyana na mmene anthu m’dzikoli amaonela nchito, onani mmene Yehova na Yesu amaionela. N’zosacita kufunsa kuti Yehova ni wolimbikila nchito. Yesu anaonetsa zimenezi pamene anati: “Atate wanga akugwilabe nchito mpaka pano, inenso ndikugwilabe nchito.” (Yoh. 5:17) Ganizilani cabe nchito yaikulu imene Mulungu anacita polenga angelo ambili-mbili na zinthu zakuthambo zosaŵelengeka. Timaonanso zinthu zambili zokongola zimene Mulungu analenga pano pa dziko lapansi. M’pomveka kuti wamasalimo anati: “Nchito zanu ndi zoculuka, inu Yehova! Zonsezo munazipanga mwanzelu zanu. Dziko lapansi ladzaza ndi zinthu zimene munapanga.”—Sal. 104:24.

3 Yesu anatengela Atate wake. Iye anali kuthandiza Mulungu pamene anali “kukonza kumwamba.” Yesu anali pambali pa Yehova “monga mmisili waluso.” (Miy. 8:27-31) Patapita zaka zambili, Yesu anabwela pano pa dziko lapansi ndipo anacita nchito yofunika kwambili. Iye anakamba kuti nchito imene Yehova anam’patsa inali monga cakudya cake. Ndiponso nchito zake zonse zinacitila umboni kuti anatumidwadi na Mulungu.—Yoh. 4:34; 5:36; 14:10.

4. Kodi tiphunzila ciani kwa Yehova na Yesu pa nkhani ya kupumula?

4 Monga taonela, Yehova na Yesu amatipatsa citsanzo cabwino ca kugwila nchito molimbika. Kodi izi zitanthauza kuti kupumula n’kosafunikila kwa ife? Iyai. Yehova salema. Conco, safunikila kupumula akagwila nchito. Baibo imakamba kuti pambuyo polenga kumwamba na dziko lapansi, Yehova “anapuma pa nchito yake.” (Eks. 31:17) Yehova anayamba walekeza nchito yake yolenga zinthu, ndipo anakhutila na zimene anali atalenga. Olo kuti Yesu anali kugwila nchito molimbika pamene anali pa dziko lapansi, anali kupatula nthawi yopumula komanso kusangalala na cakudya pamodzi na mabwenzi ake.—Mat. 14:13; Luka 7:34.

5. Kodi anthu ambili a Mulungu amavutika kucita ciani?

5 Baibo imalimbikitsa anthu a Mulungu kugwila nchito. Iwo afunika kukhala olimbikila nchito osati aulesi. (Miy. 15:19) Mwina mumagwila nchito yakuthupi kuti musamalile banja lanu. Komanso monga ophunzila a Khristu, tonse tili na udindo wogwila nchito yolalikila uthenga wabwino. Koma timafunikanso kupumula mokwanila. Kodi nthawi zina zimakuvutani kulinganiza bwino nthawi yoseŵenza, yolalikila, na yopumula? Kodi tingalinganize bwanji nthawi yogwila nchito na yopumula?

KUKHALA NA MAGANIZO OYENELA PA NKHANI YA NCHITO NA KUPUMULA

6. Kodi Maliko 6:30-34 ionetsa bwanji kuti Yesu anali na maganizo oyenela pa nkhani yogwila nchito na kupumula?

6 Kuona nchito moyenela n’kofunika. Mouzilidwa, Mfumu Solomo analemba kuti: “Ciliconse cocitika padziko lapansi [cili] ndi nthawi yake.” Iye anachula zinthu monga kubzala, kumanga, kulila, kuseka, kuvina, na zina. (Mlal. 3:1-8) N’zoonekelatu kuti kugwila nchito na kupumula ni mbali zofunika ngako mu umoyo wathu. Yesu anali na maganizo oyenela pa nkhani yogwila nchito na kupumula. Mwacitsanzo, pa nthawi ina atumwi atabwelako ku ulendo wokalalikila, anatangwanika kwambili cakuti “analibe nthawi yopuma, ngakhale yoti adye cakudya.” Conco, Yesu anawauza kuti: “Inuyo bwelani kuno, tipite kwatokha kopanda anthu kuti mupumule pang’ono.” (Ŵelengani Maliko 6:30-34.) Olo kuti nthawi zambili Yesu na ophunzila ake anali kukhala otangwanika, iye anali kudziŵa kuti onse anafunika kupumula.

7. Kodi zimene tiphunzile zokhudza lamulo la Sabata zingatithandize bwanji?

7 Nthawi zina, tonse timafunika kupumula kapena kusinthako zocita zathu za tsiku na tsiku. Cimene cionetsa bwino kufunika kocita zimenezi ni makonzedwe amene Mulungu anakonzela anthu ake akale, akuti azisunga Sabata ya wiki iliyonse. Masiku ano, ife sititsatila Cilamulo ca Mose. Ngakhale n’telo, tingapindule mwa kuphunzila zimene Cilamulo cimakamba zokhudza Sabata. Kuphunzila zimenezi kungatithandize kuona ngati tili na maganizo oyenela pa nkhani yogwila nchito na kupumula.

SABATA INALI NTHAWI YOPUMULA KOMANSO YOLAMBILA

8. Malinga na Ekisodo 31:12-15, kodi Sabata linali tsiku locita ciani?

8 Mawu a Mulungu amakamba kuti pambuyo pogwila nchito yolenga zinthu kwa “masiku” 6, Mulungu analeka kulenga zinthu pa dziko lapansi. (Gen. 2:2) Olo n’telo, Yehova amakonda kugwila nchito, ndipo iye “akugwilabe nchito” m’njila zina. (Yoh. 5:17) Monga taonela, Yehova anagwila nchito kwa masiku 6 ndipo pa tsiku la 7 anapumula. Mofananamo, iye anauza Aisiraeli kuti azipumula pa tsiku la 7 wiki iliyonse. Mulungu anakamba kuti Sabata inali cizindikilo pakati pa iye na Aisiraeli. Linali tsiku “lopuma pa nchito zonse . . . , tsiku lopatulika kwa Yehova.” (Ŵelengani Ekisodo 31:12-15.) Pa tsikuli, aliyense sanali kufunika kugwila nchito, kaya ana, akapolo, ngakhale ziŵeto. (Eks. 20:10) Iyi inali nthawi yakuti Aisiraeli asumike maganizo awo pa zinthu zauzimu.

9. Kodi anthu ena m’nthawi ya Yesu anali na maganizo olakwika ati okhudza Sabata?

9 Tsiku la Sabata linali kupindulitsa anthu a Mulungu. Komabe, m’nthawi ya Yesu, atsogoleli ambili acipembedzo anaika malamulo ena okhwima okhudza kusunga Sabata. Mwacitsanzo, iwo anali kukamba kuti ngakhale kubudula ngala za tiligu kapena kucilitsa wodwala pa Sabata kunali kulakwa. (Maliko 2:23-27; 3:2-5) Izi zinali zosiyana kwambili na maganizo a Mulungu ponena za Sabata. Ndipo Yesu anaonetsa bwino kwa omvela ake kuti maganizo amene atsogoleliwo anali nawo anali olakwika.

Banja limene Yesu anakulilamo linali kukonda kucita zinthu zauzimu pa tsiku la Sabata (Onani ndime 10) *

10. Kodi Mateyu 12:9-12 itiphunzitsa ciani za mmene Yesu anali kuonela Sabata?

10 Yesu na otsatila ake aciyuda anali kusunga Sabata cifukwa anali kutsatila Cilamulo ca Mose. * Koma zimene Yesu anakamba na kucita, zinaonetsa bwino kuti kuthandiza ena pa tsiku la Sabata na kuwacitila zinthu mokoma mtima sikunali kulakwa. Iye anakamba mosapita m’mbali kuti: “N’kololeka inde kucita cinthu cabwino pa tsiku la sabata.” (Ŵelengani Mateyu 12:9-12.) Iye sanaone kuti kuthandiza ena na kuwacitila zinthu mokoma mtima pa tsikuli, kunali kuphwanya lamulo la Sabata. Zocita za Yesu zinaonetsa bwino kuti anali kudziŵa colinga cacikulu cimene Mulungu anauzila anthu ake kuti azipumula pa Sabata. Popeza pa tsikuli anthu a Mulungu anali kupumula ku nchito zawo za tsiku na tsiku, anali kukhala na mpata woika kwambili maganizo awo pa kucita zinthu zauzimu. Yesu anakulila m’banja limene linali kucita zinthu zauzimu pa tsiku la Sabata. Cimene cionetsa izi ni mawu amene timaŵelenga okamba za Yesu pamene anali ku tauni ya kwawo ku Nazareti. Baibo imati: “Malinga ndi cizolowezi cake pa tsiku la sabata, analowa m’sunagoge, ndi kuimilila kuti awelenge Malemba.”—Luka 4:15-19.

KODI KUGWILA NCHITO MUMAKUONA BWANJI?

11. N’ndani anapeleka citsanzo cabwino kwa Yesu pa nkhani yogwila nchito?

11 Yosefe anaphunzitsa Yesu nchito ya ukalipentala. Anamuphunzitsanso mmene Mulungu amaonela nchito. (Mat. 13:55, 56) Ndipo mwacionekele, Yesu anali kumuona Yosefe akugwila nchito molimbika tsiku lililonse kuti asamalile banja lake lalikulu. N’zocititsa cidwi kuti pa nthawi ina, Yesu anauza ophunzila ake kuti: “Wanchito ayenela kulandila malipilo ake.” (Luka 10:7) Conco, n’zoonekelatu kuti Yesu anali munthu wolimbikila nchito.

12. Ni malemba ati amene aonetsa kuti tiyenela kukhala olimbikila nchito?

12 Nayenso mtumwi Paulo anali munthu wolimbikila nchito. Nchito yake yaikulu inali kuuza anthu za Yesu na zimene iye anaphunzitsa. Koma anali kugwilanso nchito yakuthupi kuti azipeza zofunikila mu umoyo. Paulo anauza Atesalonika kuti iye anali kugwila nchito ‘mwakhama ndi thukuta lake’ “usiku ndi usana,” n’colinga cakuti aliyense wa iwo ‘asamulipilile kanthu kalikonse pofuna kumuthandiza.’ (2 Ates. 3:8; Mac. 20:34, 35) Pamenepa, n’kutheka kuti Paulo anali kukamba za nchito yake yopanga matenti. Pamene iye anali ku Korinto, anali kukhala ku nyumba kwa Akula na Purisikila, ndipo anali kugwila “nchito pamodzi, pakuti onse anali amisili opanga mahema.” Mfundo yakuti Paulo anali kuseŵenza “usiku ndi usana” sitanthauza kuti anali kuseŵenza nthawi zonse osapumula. Iye anali kupatula nthawi yopumula pa nchito yake yopanga matenti. Mwacitsanzo, anali kupumula pa Sabata. Pa tsikuli, anali kukhala na mwayi wolalikila kwa Ayuda amene nawonso sanali kuseŵenza pa Sabata.—Mac. 13:14-16, 42-44; 16:13; 18:1-4.

13. Kodi tiphunzilapo ciani pa citsanzo ca Paulo?

13 Mtumwi Paulo anatipatsa citsanzo cabwino pa nkhani yolimbikila nchito. Iye anali kugwila nchito yakuthupi, koma nthawi zonse anali kupatula nthawi yogwila ‘nchito yopatulika,’ “yolengeza uthenga wabwino wa Mulungu.” (Aroma 15:16; 2 Akor. 11:23) Paulo anali kulimbikitsanso ena kulalikila nthawi zonse. Conco, Akula na Purisikila anali ‘anchito anzake mwa Khristu Yesu.’ (Aroma 12:11; 16:3) Paulo analimbikitsa Akorinto kukhala ndi “zocita zambili . . . mu nchito ya Ambuye.” (1 Akor. 15:58; 2 Akor. 9:8) Yehova anauzilanso mtumwi Paulo kulemba kuti: “Ngati wina sakufuna kugwila nchito, asadye.”—2 Ates. 3:10.

14. Kodi mawu a Yesu pa Yohane 14:12 atanthauza ciani?

14 Nchito yofunika kwambili imene tiyenela kucita masiku ano otsiliza ni yolalikila na kupanga ophunzila. Ndipo Yesu anakambilatu kuti ophunzila ake adzacita nchito zazikulu kupambana zimene iye anacita. (Ŵelengani Yohane 14:12.) Yesu sanatanthauze kuti tidzayamba kucita zozizwitsa monga zimene iye anacita. M’malomwake, anatanthauza kuti tidzalalikila na kuphunzitsa m’madela ambili, kwa anthu ambili, komanso kwa nthawi yaitali kuposa iye.

15. Ni mafunso ati amene tiyenela kudzifunsa? Nanga n’cifukwa ciani?

15 Ngati mumagwila nchito yolembedwa, dzifunseni kuti: ‘Kodi ku nchito kwathu, nimadziŵika kuti ndine munthu wolimbikila nchito? Kodi nimatsiliza nchito pa nthawi yake, na kucita zonse zimene ningathe pa nchitoyo?’ Ngati mwayankha kuti inde, ndiye kuti wokulembani nchito adzayamba kukudalilani. Ndiponso anthu ku nchito kwanu angakhale na cidwi cofuna kumvetsela uthenga wabwino. Pa nchito yolalikila na kuphunzitsa, dzifunseni kuti: ‘Kodi nimadziŵika kuti ndine mlaliki wakhama? Kodi nimakonzekela bwino ulaliki wa ulendo woyamba? Kodi nimabwelelako mwamsanga kwa anthu amene anaonetsa cidwi? Kodi nimatengako mbali mokwanila pa maulaliki osiyana-siyana amene amacitika?’ Tikamacita zimenezi, tidzapeza cimwemwe mu utumiki wathu.

KODI KUPUMULA MUMAKUONA BWANJI?

16. Kodi Yesu na atumwi ake anali kukuona bwanji kupumula? Nanga izi zisiyana bwanji na mmene anthu ambili amaonela kupumula masiku ano?

16 Yesu anali kudziŵa kuti nthawi zina iye na atumwi ake anali kufunika kupumula. Koma anthu ambili akale ndi a masiku ano, amalingana na munthu wacuma wa m’fanizo la Yesu. Mu mtima mwake, iye anali kudziuza kuti: “Ungoti phee tsopano, ndipo udye, umwe ndi kusangalala.” (Luka 12:19; 2 Tim. 3:4) Iye anali kuona kuti zinthu zofunika kwambili mu umoyo ni kupumula na kusangalala. Koma Yesu na atumwi ake sanali kuona kuti zosangalatsa ndizo zinali zofunika kwambili mu umoyo wawo.

Kukhala na maganizo oyenela pa nkhani ya nchito na kupumula kudzatithandiza kuti tizikonda kucita nchito zabwino zimene zimatitsitsimula (Onani ndime 17) *

17. Kodi nthawi imene tili pa chuti timaiseŵenzetsa bwanji?

17 Masiku ano, timayesetsa kutengela citsanzo ca Yesu. Mwacitsanzo, nthawi ya chuti timaiseŵenzetsa popumula na kucita zinthu zina zokhudza kulambila monga kulalikila na kupezeka pa misonkhano. Ndipo timaona kuti kupezeka pa misonkhano na kugwila nchito yopanga ophunzila n’zofunika kwambili, cakuti nthawi zonse timayesetsa kupatula nthawi yocita zinthu zauzimu zimenezi. (Aheb. 10:24, 25) Komanso ngati tili pa chuti, ndipo tapita kwina kwake, sitileka kupezeka pa misonkhano na kusakila mipata yokambilana ndi anthu mfundo za m’Baibo.—2 Tim. 4:2.

18. Kodi Mfumu yathu, Khristu Yesu, amafuna kuti tizicita ciani?

18 Ndife oyamikila kwambili kuti Mfumu yathu, Khristu Yesu, amafuna kuti tizicita zimene tingathe, ndipo amatithandiza kukhala na maganizo oyenela pa nkhani yogwila nchito na kupumula. (Aheb. 4:15) Iye amafuna kuti tizipumula mokwanila. Amafunanso kuti tiziseŵenza mwakhama kuti tipeze zosoŵa zathu zakuthupi, komanso kuti tizigwila nchito yotsitsimula yopanga ophunzila. M’nkhani yotsatila, tidzakambilana zimene Yesu anacita kuti atimasule ku ukapolo woŵaŵa wa ucimo.

NYIMBO 38 Adzakulimbitsa

^ ndime 5 Malemba amatiphunzitsa mmene tiyenela kuonela nchito na kupumula. M’nkhani ino, tidzakambilana za Sabata imene Aisiraeli anali kusunga wiki iliyonse. Colinga cokambilana zimenezi ni kutithandiza kupendanso bwino mmene timaonela nchito na kupumula.

^ ndime 10 Ophunzila a Yesu anali kulemekeza kwambili lamulo la Sabata, cakuti analekeza kukonza zonunkhilitsa zoti akapake mtembo wa Yesu, mpaka tsiku la Sabata litadutsa.—Luka 23:55, 56.

^ ndime 55 MAWU OFOTOKOZELA ZITHUNZI: Yosefe watenga banja lake kupita nalo ku sunagoge pa Sabata.

^ ndime 57 MAWU OFOTOKOZELA ZITHUNZI: Tate amene amagwila nchito kuti apeze zosoŵa za banja lake, ali pa chuti ndipo wapita kwinakwake pamodzi na banja lake. Iwo akuseŵenzetsa nthawi imeneyi kucita zinthu zauzimu.