Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI YOPHUNZILA 5

“Mutu wa Mwamuna Aliyense Ndi Khristu”

“Mutu wa Mwamuna Aliyense Ndi Khristu”

“Mutu wa mwamuna aliyense ndi Khristu.”—1 AKOR. 11:3.

NYIMBO 12 Mulungu Wamkulu, Yehova

ZIMENE TIKAMBILANE *

1. N’ciani cingapangitse mwamuna kusayendetsa bwino umutu wake?

KODI liwu lakuti “umutu” limatanthauzanji kwa imwe? Amuna ena amacita zinthu na akazi awo komanso ana awo motengela miyambo, cikhalidwe, kapena mmene analeledwela. Onani zimene mlongo Yanita wa ku Europe anakamba. Iye anati: “Kumene nimakhala anthu amakhulupilila kwambili zakuti akazi ni otsika kwa amuna, ndipo ayenela kuonedwa monga anchito cabe.” Ndipo m’bale wina wa ku America dzina lake Luke anati: “Atate ena amaphunzitsa ana awo aamuna kuti zokamba za akazi sizimakhala zothandiza. Conco, m’posayenela kumvela zokamba zawo.” Komabe, maganizo amenewo sagwilizana na mmene Yehova amafunila amuna kuyendetsa umutu wawo. (Yelekezelani na Maliko 7:13) Ndiye kodi mwamuna angacite ciani kuti akhale mutu wa banja wabwino?

2. Kodi mutu wa banja afunika kudziŵa ciani, nanga n’cifukwa ciani?

2 Kuti mwamuna akhale mutu wa banja wabwino, coyamba ayenela kudziŵa zimene Yehova amafuna kuti iye azicita. Ayenelanso kudziŵa cifukwa cake Yehova anakhazikitsa dongosolo la umutu na zimene angacite kuti atengele citsanzo ca Yehova na Yesu. N’cifukwa ciani mwamuna afunika kudziŵa zimenezi? Cifukwa Yehova anapatsa mitu ya mabanja ulamulilo, ndipo amayembekezela kuti iwo aziuseŵenzetsa bwino.—Luka 12:48b.

KODI UMUTU UMATANTHAUZA CIANI?

3. Kodi mawu a pa 1 Akorinto 11:3 atiphunzitsa ciani za umutu?

3 Ŵelengani 1 Akorinto 11:3. Vesiyi ifotokoza mmene Yehova analinganizila banja lake kumwamba na padziko lapansi. Umutu umaphatikizapo mbali ziŵili zikulu-zikulu—ulamulilo komanso mouseŵenzetsela. Yehova ni “mutu” kapena kuti ali na ulamulilo wonse, ndipo ana ake onse, angelo komanso anthu adzayankha mlandu pa mmene amaseŵenzetsela ulamulilo umene anapatsidwa. (Aroma 14:10; Aef. 3:14, 15) Yehova anapatsa Yesu ulamulilo wokhala mutu wa mpingo. Koma Yesu adzayankha kwa Yehova pa mmene amacitila nafe zinthu. (1 Akor. 15:27) Yehova anapatsanso mwamuna ulamulilo pa mkazi wake komanso ana ake. Koma mwamuna adzayankha mlandu kwa Yehova na Yesu pa mmene amacitila zinthu na banja lake.—1 Pet. 3:7.

4. Kodi Yehova na Yesu ali na mphamvu zocita ciani?

4 Monga Mutu wa banja lake lonse m’cilengedwe, Yehova ali na mphamvu zopanga malamulo a mmene ana ake ayenela kukhalila, na kuonetsetsa kuti malamulowo akutsatilidwa. (Yes. 33:22) Yesu nayenso monga mutu wa mpingo wacikhristu ali na ufulu wopanga malamulo na kuonetsetsa kuti akutsatilidwa.—Agal. 6:2; Akol. 1:18-20.

5. Kodi mutu wa banja lacikhristu ali na mphamvu zocita ciani, nanga ali na malile otani?

5 Potengela Yehova na Yesu, mutu wa banja lacikhristu ali na mphamvu zopangila banja lake zosankha. (Aroma 7:2; Aef. 6:4) Komabe, mphamvu zake zili na malile. Mwacitsanzo, malamulo ake ayenela kuzikidwa pa mfundo za m’Mawu a Mulungu. (Miy. 3:5, 6) Ndipo mutu wa banja alibe mphamvu zopangila malamulo anthu ena amene si a m’banja lake. (Aroma 14:4) Cina, ana ake akakula n’kucoka pakhomo amapitiliza kumulemekeza, koma sakhalanso pansi pa umutu wake.—Mat. 19:5.

N’CIFUKWA CIANI YEHOVA ANAKHAZIKITSA DONGOSOLO LA UMUTU?

6. N’cifukwa ciani Yehova anakhazikitsa dongosolo la umutu?

6 Yehova anakhazikitsa dongosolo la umutu cifukwa cokonda banja lake. Imeneyi ni mphatso yocokela kwa iye. Umutu umapangitsa kuti zinthu zizicitika mwamtendele komanso mwadongosolo m’banja la Yehova. (1 Akor. 14:33, 40) Popanda dongosolo la umutu, m’banja la Yehova mukanakhala msokonezo komanso mopanda cimwemwe. Mwacitsanzo, palibe akanadziŵa kuti pothela pake ndani ayenela kupanga zigamulo, komanso amene ayenela kukhala patsogolo polabadila zigamulo zimenezo.

7. Malinga na Aefeso 5:25, 28, kodi ni mmene Yehova anakonzela kuti amuna azipondeleza akazi awo?

7 Koma ngati makonzedwe a Mulungu a umutu ni abwino motelo, nanga n’cifukwa ciani akazi ambili masiku ano amaona kuti amuna awo amawapondeleza? Zili conco cifukwa amuna ambili amanyalanyaza miyezo ya Yehova yokhudza banja, ndipo amasankha kutsatila cikhalidwe kapena miyambo yawo. Nthawi zina amacitila nkhanza akazi awo cifukwa ca dyela longofuna kukhutulitsa zimene mtima wawo ufuna. Mwacitsanzo, mwamuna angapondeleze mkazi wake pofuna kuti azimulemekeza kwambili kapena kuonetsa anthu kuti iye ni “mwamuna weni-weni.” Iye angaganize kuti sangakakamize mkazi wake kuti azimukonda, koma angacite zinthu zomupangitsa kuti azimuwopa. Angaganize kuti mkaziyo akakhala na mantha adzakwanitsa kumulamulila. * N’zoonekelatu kuti kaganizidwe kameneka, komanso kucita zinthu mwanjila imeneyi kumalanda akazi ulemu umene ayenela kupatsidwa. Ndipo izi n’zosiyana kwambili na zimene Yehova amafuna.—Ŵelengani Aefeso 5:25, 28.

KODI MWAMUNA ANGACITE CIANI KUTI AKHALE MUTU WA BANJA WABWINO?

8. Kodi mwamuna angacite ciani kuti akhale mutu wa banja wabwino?

8 Mwamuna angakhale mutu wa banja wabwino mwa kutengela citsanzo ca Yehova na Yesu ca mmene amaseŵenzetsela umutu wawo. Onani makhalidwe aŵili amene Yehova na Yesu amaonetsa, ndipo onaninso mmene mutu wa banja angaonetsele makhalidwe amenewa pocita zinthu na mkazi wake komanso ana ake.

9. Kodi Yehova amaonetsa bwanji kudzicepetsa?

9 Kudzicepetsa. Yehova ni wanzelu kwambili kuposa wina aliyense. Ngakhale n’telo, amamvetsela malingalilo a atumiki ake. (Gen. 18:23, 24, 32) Iye amalola amene ali pansi pa ulamulilo wake kupeleka malingalilo awo. (1 Maf. 22:19-22) Yehova ni wangwilo, koma sayembekezela kuti ife tizicita zinthu mwangwilo. M’malomwake, amathandiza anthu opanda ungwilo amene amam’tumikila kuti zinthu ziziwayendela bwino. (Sal. 113:6, 7) Ndipo Baibo imafotokoza Yehova kuti ni “mthandizi.” (Sal. 27:9; Aheb. 13:6) Mfumu Davide anazindikila kuti angakwanitse kugwila nchito yaikulu imene anapatsidwa, cabe cifukwa ca kudzicepetsa kwa Yehova.—2 Sam. 22:36.

10. Kodi Yesu anaonetsa bwanji kudzicepetsa?

10 Ganizilani citsanzo ca Yesu. Ngakhale kuti anali Mphunzitsi komanso Mbuye wa ophunzila ake, anasambitsa mapazi awo. N’cifukwa ciani Yehova anakonza zakuti nkhani imeneyi ilembedwe m’Baibo? Cifukwa anali kufuna kupeleka citsanzo cimene aliyense angatengele, kuphatikizapo mitu ya mabanja. Yesu iye mwini anati: “Ndakupatsani citsanzo kuti mmene ine ndacitila kwa inu, inunso muzicita cimodzimodzi.” (Yoh. 13:12-17) Ngakhale kuti Yesu anali na ulamulilo waukulu, sanayembekezele kutumikilidwa. M’malomwake, anali kutumikila ena.—Mat. 20:28.

Mutu wa banja angaonetse kudzicepetsa na cikondi mwa kugwilako nchito zapakhomo, komanso kusamalila zosoŵa zauzimu za banja lake (Onani ndime 11, 13)

11. Kodi mwamuna amene ni mutu wa banja angaphunzile ciani pa citsanzo ca kudzicepetsa kwa Yehova na Yesu?

11 Zimene tiphunzilapo. Mutu wa banja angaonetse kudzicepetsa m’njila zambili. Mwacitsanzo, iye sayembekezela kuti mkazi wake na ana ake azicita zinthu mwangwilo. Amamvela malingalilo a ena m’banja, ngakhale kuti malingalilowo ni osiyana na ake. Mlongo Marley wa ku America anati: “Ine na mwamuna wanga nthawi zina timakhala na malingalilo osiyana. Niona kuti mwamuna wanga amaniyamikila komanso kuniganizila cifukwa amanifunsa malingalilo anga na kuwaganizila mosamala asanapange cosankha.” Pamwamba pa izi, mwamuna wodzicepetsa amagwilako nchito zapakhomo, ngakhale kuti anthu angaone kuti zimenezi ni nchito za akazi. Kucita izi kungakhale kovuta. Cifukwa ciani? Mlongo Rachel anati: “Kudela limene n’nakulila, ngati mwamuna athandiza mkazi wake kutsuka mbale kapena kuyeletsa panyumba, anthu komanso acibale ake amakaikila zakuti ni ‘mwamuna weni-weni.’ Amaganiza kuti mwamunayo amalephela kumulamulila mkazi wake.” Ngati maganizo amenewa ni ofala kumene mumakhala, kumbukilani kuti Yesu anasambitsa mapazi a ophunzila ake, ngakhale kuti nchitoyo inali kuonedwa kuti ni ya kapolo. Mutu wa banja wabwino sadela nkhawa zakuti anthu adzamuona bwanji, koma amacita zinthu zokondweletsa mkazi wake na ana ake. Kuwonjezela pa kudzicepetsa, ni khalidwe linanso liti lofunika limene mutu wa banja afunika kukhala nalo?

12. Kodi cikondi cimalimbikitsa Yehova na Yesu kucita ciani?

12 Cikondi: Zocita zonse za Yehova zimasonkhezeledwa na cikondi. (1 Yoh. 4:7, 8) Iye mwacikondi amasamalila zosoŵa zathu zauzimu kupitila m’Mawu ake Baibo, komanso gulu lake. Amatithandiza kumva kuti ndife otetezeka mwa kutitsimikizila kuti amatikonda. Nanga bwanji zosoŵa zathu za kuthupi? Yehova “amatipatsa mowolowa manja zinthu zonse kuti tisangalale.” (1 Tim. 6:17) Tikalakwitsa amatiwongolela, koma saleka kutikonda. Cifukwa cotikonda, Yehova anapeleka dipo kaamba ka ife. Ndipo Yesu amatikonda kwambili cakuti anapeleka moyo wake cifukwa ca ife. (Yoh. 3:16; 15:13) Palibe cimene cingalepheletse Yehova na Yesu kukonda anthu amene amakhala okhulupilika kwa iwo.—Yoh. 13:1; Aroma 8:35, 38, 39.

13. N’cifukwa ciani mutu wa banja afunika kuonetsa cikondi banja lake? (Onaninso bokosi lakuti “ Kodi Mwamuna Amene Wangokwatila Kumene Angacite Ciani Kuti Mkazi Wake Azimulemekeza?”)

13 Zimene tiphunzilapo: Zocita zonse za mutu wa banja ziyenela kusonkhezeledwa na cikondi. N’cifukwa ciani kucita zimenezi n’kofunika kwambili? Mtumwi Yohane anayankha kuti: “Amene sakonda m’bale wake [kapena banja] amene amamuona, sangakonde Mulungu amene sanamuonepo.” (1 Yoh. 4:11, 20) Ndipo mwamuna amene amakonda banja lake na kufuna kutengela citsanzo ca Yehova na Yesu, amayesetsa kusamalila banja lake mwauzimu, kulipangitsa kudzimva lotetezeka, komanso kulisamalila mwakuthupi. (1 Tim. 5:8) Iye amaphunzitsa na kulangiza ana ake. Cina, amapitiliza kuphunzila kupanga zosankha zimene zimalemekeza Yehova komanso zopindulitsa banja lake. Tsopano, tiyeni tikambilane zinthu zitatu zimenezo, na kuona zimene mutu wa banja angacite potengela citsanzo ca Yehova na Yesu.

ZIMENE MUTU WA BANJA AYENELA KUCITA

14. Kodi mutu wa banja angacite ciani kuti azisamalila zosoŵa zauzimu za banja lake?

14 Kusamalila banja lake pa zosoŵa zauzimu. Potengela citsanzo ca Atate wake, Yesu anali kuonetsetsa kuti anthu amene ali pansi pa cisamalilo cake akudya bwino mwauzimu. (Mat. 5:3, 6; Maliko 6:34) Mofananamo, cinthu cofunika kwambili kwa mutu wa banja ni kusamalila banja lake pa zosoŵa zauzimu. (Deut. 6:6-9) Amacita zimenezi mwa kuonetsetsa kuti iye pamodzi na banja lake amaŵelenga na kuphunzila Mawu a Mulungu, kupezeka pamisonkhano, kulalikila uthenga wabwino, komanso kulimbitsa ubale wawo na Yehova.

15. Kodi mutu wa banja angacite ciani kuti athandize banja lake kumva kuti ni lotetezeka?

15 Kuthandiza banja lake kumva kuti ni lotetezeka. Yehova anakamba poyela kuti amam’konda Yesu. (Mat. 3:17) Yesu anaonetsa kuti anali kukonda otsatila ake mwa zocita na zokamba zake. Nawonso otsatila ake anamuuza kuti amam’konda. (Yoh. 15:9, 12, 13; 21:16) Mutu wa banja angaonetse kuti amakonda mkazi wake na ana ake mwa zocita zake monga kuphunzila nawo Baibo. Iye afunika kumawauza ndithu kuti amawakonda na kuwayamikila, ndipo ngati m’poyenela angawayamikile pamaso pa ena.—Miy. 31:28, 29.

Kuti mutu wa banja akondweletse Yehova afunika kusamalila zosoŵa zakuthupi za banja lake (Onani ndime 16)

16. Ni mbali inanso iti imene mutu wa banja afunika kusamalila? Koma kodi pali cenjezo lanji?

16 Kupezela banja lake zosoŵa zakuthupi. Yehova anali kusamalila Aisiraeli pa zosoŵa zawo ngakhale pamene anali kulangidwa cifukwa ca kusamvela. (Deut. 2:7; 29:5) Ifenso amatigaŵila zosoŵa zathu zakuthupi masiku ano. (Mat. 6:31-33; 7:11) Mofananamo, Yesu anadyetsa otsatila ake. (Mat. 14:17-20) Iye anasamalilanso thanzi lawo la kuthupi. (Mat. 4:24) Kuti mutu wa banja akondweletse Yehova ayenela kusamalila banja lake mwakuthupi. Komabe, pali zina zimene ayenela kupewa. Sayenela kutangwanika kwambili na nchito ya kuthupi cakuti n’kulephela kusamalila bwino banja lake mwauzimu, komanso kulithandiza kumva kuti n’lotetezeka.

17. Kodi Yehova na Yesu amapeleka citsanzo cotani ca mmene amatiphunzitsila na kutilangiza?

17 Kuphunzitsa. Yehova amatiphunzitsa na kutilangiza cifukwa amafuna kutithandiza. (Aheb. 12:7-9) Mofanana na Atate wake, Yesu mwacikondi amaphunzitsa anthu amene ali pansi pa ulamulilo wake. (Yoh. 15:14, 15) Amapeleka uphungu mwamphamvu koma mokoma mtima. (Mat. 20:24-28) Iye amadziŵa kuti ndife opanda ungwilo, ndipo nthawi zambili timalakwa.—Mat. 26:41.

18. Kodi mutu wa banja wabwino ayenela kukumbukila ciani?

18 Mutu wa banja amene amatengela citsanzo ca Yehova na Yesu amakumbukila kuti a m’banja lake ni opanda ungwilo. Iye ‘sapsela mtima’ mkazi wake kapena ana ake. (Akol. 3:19) M’malomwake, amaseŵenzetsa mfundo ya pa Agalatiya 6:1 na kuthandiza a m’banja lake “ndi mzimu wofatsa” pokumbukila kuti nayenso ni wopanda ungwilo. Mofanana na Yesu, iye amazindikila kuti njila yabwino yophunzitsila banja lake ni kukhala citsanzo cabwino.—1 Pet. 2:21.

19-20. Kodi mutu wa banja angatengele bwanji citsanzo ca Yehova na Yesu popanga zosankha?

19 Pewani kupanga zosankha modzikonda. Yehova amapanga zosankha zokomela ena. Mwacitsanzo, analenga moyo osati cifukwa cofuna kudzipindulitsa iye yekha, koma kuti nafenso tizikondwela kukhala na moyo. Palibe akanam’kakamiza kupeleka mwana wake kuti aphimbe macimo athu. Anasankha yekha kupeleka nsembe imeneyo kuti itipindulile. Nayenso Yesu anali kupanga zosankha zopindulitsa ena. (Aroma 15:3) Mwacitsanzo, m’malo mopumula anasankha kuphunzitsa khamu la anthu.—Maliko 6:31-34.

20 Mutu wa banja wabwino amadziŵa kuti kupangila banja lake zosankha zanzelu n’cimodzi mwa zinthu zovuta kwambili zimene iye afunika kucita, ndipo satenga udindowo mopepuka. Amapewa kupanga zosankha popanda zifukwa zomveka, kapena cabe cifukwa ca mmene akumvelela. M’malomwake amalola Yehova kuti amuphunzitse. * (Miy. 2:6, 7) Kucita zinthu mwa njila imeneyi kumam’thandiza kuti asamapange zosankha zopindulila iye yekha, koma zopindulilanso ena.—Afil. 2:4.

21. Tidzakambilana ciani m’nkhani yotsatila?

21 Yehova anapatsa mitu ya mabanja nchito yosafuna zibwana. Iwo adzayankha mlandu kwa iye na mmene amagwilila nchitoyo. Koma ngati mwamuna ayesetsa kutengela citsanzo ca Yehova na Yesu, adzakhala mutu wa banja wabwino. Ndipo ngati mkazi wake amacita mbali yake, banja lawo lidzakhala lacimwemwe. Kodi mkazi ayenela kuuona motani umutu wa mwamuna wake? Nanga amakumana na zopinga zotani? Nkhani yotsatila idzayankha mafunso amenewa.

NYIMBO 16 Tamandani Ya Kaamba ka Mwana Wake Wodzozedwayo

^ ndime 5 Mwamuna akakwatila amakhala mutu wa banja latsopano. M’nkhani ino tikambilana zimene umutu umatanthauza, cifukwa cake Yehova anaukhazikitsa, komanso zimene amuna angaphunzile ku citsanzo ca Yehova na Yesu. M’nkhani yotsatila, tidzakambilana zimene mwamuna na mkazi wake angaphunzile kwa Yesu komanso ku zitsanzo zina za m’Baibo. Ndipo nkhani yacitatu idzafotokoza za umutu mu mpingo.

^ ndime 7 Maganizo akuti palibe vuto mwamuna kuvutitsa mkazi wake kapena kum’menya kumene, nthawi zina amaonetsedwa m’mafilimu, m’maseŵelo, komanso m’mabuku a nkhani zoseketsa. Conco, anthu amaona kuti sikulakwa mwamuna kupondeleza mkazi wake.

^ ndime 20 Kuti mudziŵe zambili za mmene mungapangile zosankha zabwino, onani nkhani yakuti “Zosankha Zanu Zizilemekeza Mulungu,” mu Nsanja ya Mlonda ya April 15, 2011, tsa. 13-17.