Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI YOPHUNZILA 9

Tengelani Citsanzo ca Yesu Cotumikila Ena

Tengelani Citsanzo ca Yesu Cotumikila Ena

“Kupatsa kumabweletsa cimwemwe coculuka kuposa kulandila.”—MAC. 20:35.

NYIMBO 17 ‘Nifuna’

ZIMENE TIKAMBILANE *

1. Ni mzimu wabwino uti umene timaona pakati pa anthu a Yehova?

 KALE kwambili, Baibo inakambilatu kuti anthu a Mulungu “adzadzipeleka mofunitsitsa” kuti atumikile Yehova motsogoleledwa na Mwana wake. (Sal. 110:3) Ulosi umenewo ukukwanilitsika masiku ano. Caka ciliconse, atumiki a Yehova okangalika amataila maola mamiliyoni ambili-mbili pa nchito yolalikila. Amacita zimenezi mwa kufuna kwawo, ndipo salipilidwa kalikonse. Iwo amapatulanso nthawi yothandiza Akhristu anzawo kuthupi, kuuzimu, komanso kuwalimbikitsa. Abale a paudindo amathela maola osaŵelengeka pokonzekela nkhani zokakamba ku mpingo, komanso pocita maulendo aubusa kwa abale na alongo. N’ciani cimawalimbikitsa kugwila nchito zonsezi? Cikondi. Inde, cikondi pa Yehova komanso pa anthu anzawo.—Mat. 22:37-39.

2. Malinga na Aroma 15:1-3, kodi Yesu anapeleka citsanzo cotani?

2 Yesu anapeleka citsanzo cabwino koposa pa nkhani yoika zofunikila za ena patsogolo pa zofunikila zake. Timayesetsa mmene tingathele kutsatila mapazi ake. (Ŵelengani Aroma 15:1-3.) Amene amatengela citsanzo cake adzapindula kwambili. Yesu anati: “Kupatsa kumabweletsa cimwemwe coculuka kuposa kulandila.”—Mac. 20:35.

3. Tikambilane ciani m’nkhani ino?

3 M’nkhani ino, tikambilane kudzimana kumene Yesu anacita kuti atumikile ena, komanso mmene tingatengele citsanzo cake. Tikambilanenso mmene tingakulitsile mzimu wotumikila ena.

TENGELANI CITSANZO CA YESU

Olo kuti Yesu anali atalema, kodi anacita ciani khamu la anthu litabwela kwa iye? (Onani ndime 4)

4. Kodi Yesu anaika bwanji zofunikila za ena patsogolo pa zofunikila zake?

4 Yesu anadzipeleka kutumikila ena olo kuti anali atalema. Ganizilani zimene anacita pamene khamu la anthu linabwela kwa iye m’mbali mwa phili, mwina pafupi na Kaperenao. Yesu anali atapemphela usiku wonse, ndipo ayenela kuti anali atalema kwambili. Koma ataona khamu la anthu, iye anamvelela cifundo anthu osauka komanso odwala pakati pawo. Iye sanangocilitsa cabe odwala, koma anapelekanso nkhani ya anthu onse yolimbikitsa kwambili, yochedwa ulaliki wa pa phili.—Luka 6:12-20.

Kodi tingatengele mzimu wodzimana wa Yesu m’njila ziti? (Onani ndime 5)

5. Kodi mutu wa banja angatengele bwanji mzimu wa Yesu wa kudzimana pamene ali wolema?

5 Mmene mitu ya mabanja imatengela citsanzo ca Yesu. Ganizilani cocitika ici: Pambuyo pogwila nchito tsiku lonse, mutu wa banja akufika panyumba ali wolema kwambili. Cifukwa colema, iye angafune kuti asacititse kulambila kwa pabanja tsikulo, koma akupempha mphamvu kwa Yehova kuti acititse kulambilako. Yehova akuyankha pemphelo lake, ndipo kulambilako kukucitika mwa nthawi zonse. Ana akuphunzilapo cinthu cofunika kwambili pamenepa. Akuona kuti makolo awo amaika zinthu zauzimu patsogolo pa cina ciliconse.

6. Fotokozani citsanzo coonetsa mmene Yesu anadzimanila nthawi yake kuti athandize ena.

6 Yesu anadzimana nthawi yake kuti athandize ena. Tangoganizilani mmene Yesu anamvelela atamva kuti bwenzi lake Yohane M’batizi waphedwa. Iye anali na cisoni cacikulu. Baibo imati: “Yesu atamva [za imfa ya Yohane], anacoka kumeneko pa ngalawa n’kupita kumalo kopanda anthu kuti akakhale payekha.” (Mat. 14:10-13) Tingamvetse cifukwa cake iye anali kufuna kukhala payekha. Ambili a ife timafuna kukhala patokha tikakhala na cisoni. Koma izi sizinatheke kwa Yesu. Khamu la anthu linatsogola kufika kumalo opanda anthu amenewo iye asanafike. Kodi iye anacita ciani? Anaganizila zosoŵa za anthuwo, “ndipo anawamvela cifundo.” Anaona kuti anthuwo anali kufunika kutsitsimulidwa mwauzimu, ndipo mwamsanga anacita zimenezo. Iye “anayamba kuwaphunzitsa [osati zinthu zocepa, koma] zinthu zambili.”—Maliko 6:31-34; Luka 9:10, 11.

7-8. Fotokozani citsanzo coonetsa mmene akulu acikondi amatengela citsanzo ca Yesu, wina mu mpingo akafunikila thandizo.

7 Mmene akulu acikondi amatengela citsanzo ca Yesu. Timayamikila kwambili nchito zimene akulu odzimana amagwila kaamba ka ife. Ndipo zambili mwa nchitozo sizimaonekela ku mpingo. Mwacitsanzo, ngati m’bale kapena mlongo wadwala mwadzidzidzi, a m’Komiti Yokamba na a Cipatala amathangila kucipatala kuti akathandize abale awo. Kambili zimenezi zimacitika pakati pa usiku. Koma cifukwa cocitila cifundo m’bale kapena mlongo amene wakumana na vutolo, akulu okondedwa amenewo pamodzi na mabanja awo, amaika zofuna za Akhristu anzawo patsogolo pa zofuna zawo.

8 Akulu amagwilanso nchito zomanga Nyumba za Ufumu na zimango zina, komanso yopeleka thandizo pakacitika matsoka. Kuwonjezela apo, amatailanso maola osaŵelengeka pophunzitsa mu mpingo mwathu, potilimbikitsa, komanso potithandiza. Tiziwayamikila mocokela pansi pamtima abale onsewa, pamodzi na mabanja awo. Yehova awadalitse ndithu cifukwa coonetsa mzimu umenewu. Komabe, mofanana na aliyense, akulu ayenela kulinganiza bwino zinthu. Sayenela kutangwanika kwambili na zocitika zauzimu ngati zimenezi, moti n’kusoŵa nthawi yosamalila zosoŵa zauzimu za banja lawo.

MMENE TINGAKULITSILE MZIMU WODZIMANA

9. Malinga n’kunena kwa Afilipi 2:4, 5, kodi Akhristu onse ayenela kukhala na maganizo otani?

9 Ŵelengani Afilipi 2:4, 5. Inde, akulu komanso tonsefe, tiyenela kutengela mzimu wodzimana wa Yesu. Baibo imati iye ‘anakhala ngati kapolo.’ (Afil. 2:7) Ganizilani zimene tiphunzilapo pa vesiyi. Kapolo wabwino, kapena mtumiki wabwino, amafuna-funa mipata yokondweletsela mbuye wake. Popeza ndife akapolo a Yehova komanso atumiki kwa abale athu, mosakayikila timafuna kutumikila Yehova ndiponso abale athu mokwanila. Kuti mucite zimenezi, yesani kupenda malingalilo otsatilawa.

10. Kodi tiyenela kudzifunsa mafunso ati?

10 Dzisanthuleni nokha. Dzifunseni mafunso monga akuti: ‘Kodi ndine wokonzeka kudzimana zinthu zina kuti nithandize ena? Mwacitsanzo, kodi ningacite ciani akanipempha kukathandiza m’bale ku nyumba yosungilako okalamba? Kapena kukatenga mlongo wokalamba na kupita naye ku misonkhano? Kodi nimadzipeleka mwamsanga pakafunika anchito oyeletsa malo ocitilapo msonkhano kapena Nyumba ya Ufumu?’ Yehova amakondwela kwambili tikaseŵenzetsa mowolowa manja nthawi yathu, komanso zinthu zathu zimene anatipatsa kuti tithandize ena. Tikaona mbali yofunika kuwongolela, kodi tiyenela kucita ciani?

11. Kodi pemphelo lingatithandize bwanji kukulitsa mzimu wodzimana?

11 Pemphelani kwa Yehova mocokela pansi pa mtima. Tiyelekeze kuti mwazindikila mbali yofunika kuwongolela, koma cikukuvutani kupanga masinthidwe ofunikila. Zikakhala conco, pemphelani kwa Yehova mocokela pansi pa mtima. Ndipo mufotokozeleni moona mtima. Muuzeni Yehova mmene mumvelela, na kumupempha kuti ‘alimbitse zolakalaka zanu’ kuti mucite zinthu zonse zimene iye amakonda.—Afil. 2:13.

12. Kodi m’bale wacinyamata wobatizika angathandize bwanji mu mpingo wawo?

12 Ngati ndimwe m’bale wacinyamata wobatizika, pemphani Yehova kuti akuthandizeni kukulitsa cikhumbu canu cofuna kucita zambili mu mpingo. Ku maiko ena, mipingo ili na akulu ambili kuposa atumiki othandiza. Ndipo ambili mwa atumiki othandiza amenewo, ni akulu-akulu kapenanso okalamba. Pamene gulu la Mulungu likupita likulila-kulila, pakufunikila abale acinyamata ambili kuti athandize kusamalila anthu a Yehova. Ngati ndinu ofunitsitsa kutumikila kulikonse kumene mungafunikile, mudzakhala acimwemwe. Cifukwa ciani? Cifukwa mudzakondweletsa Yehova, mudzakhala na mbili yabwino, komanso mudzakhala na cimwemwe cimene cimabwela cifukwa cothandiza ena.

Akhristu a ku Yudeya anaoloka mtsinje wa Yorodano n’kuthaŵila ku Pela. Aja amene anatsogola kufika akugaŵila zakudya Akhristu anzawo amene angofika kumene (Onani ndime 13)

13-14. Kodi tingacite ciani kuti tithandize abale na alongo athu? (Onani cithunzi pacikuto.)

13 Khalani chelu kuti muone zosoŵa za ena. Mtumwi Paulo analangiza Akhristu a ku Yudeya kuti: “Musaiŵale kucita zabwino ndi kugaŵana zinthu ndi ena, pakuti nsembe zotelo Mulungu amakondwela nazo.” (Aheb. 13:16) Awa anali malangizo othandiza ngako! Pasanapite nthawi yaitali kucokela pamene analandila kalatayi, Akhristu ku Yudeya anafunika kusiya nyumba zawo, mabizinesi awo, na acibale awo osakhulupilila na kuyamba ‘kuthaŵila kumapili.’ (Mat. 24:16) Pa nthawiyo, kunali kofunikila kwambili kuti iwo azithandizana. Ngati iwo anali kutsatila malangizo a Paulo asanayambe kuthaŵila ku mapili, cinali cosavuta kwa iwo kukhala na umoyo wosalila zambili.

14 Si nthawi zonse pamene abale na alongo athu angatiuze za zosoŵa zawo zakuthupi. Mwacitsanzo, mlongo angamwalile n’kusiya mwamuna wake ali wacisoni kwambili. Kodi m’bale wofedwayo angafunikile thandizo la zakudya, mayendedwe, kapena kumugwililako nchito zapakhomo? Mwina iye sangapemphe thandizo lathu, poopa kukhala mtolo kwa ife. Komabe, angayamikile kwambili ngati tadzipeleka kumuthandiza asanatipemphe. Tipewe kukhala na maganizo akuti wina wake adzamuthandiza, kapena kuyembekezela kuti acite kutipempha kuti timuthandize. Dzifunseni kuti, ‘Vutoli likanagwela ine, kodi nikanakonda kuti ena anicitile ciani?’

15. Kodi tiyenela kucita ciani ngati tifuna kuthandiza ena?

15 Khalani wofikilika. Mosakayikila, mudziŵako abale na alongo mu mpingo mwanu amene nthawi zonse ni okonzeka kuthandiza ena. Iwo satipangitsa kuona kuti ndife mtolo kwa iwo. Timadziŵa kuti iwo ni ofunitsitsa kutithandiza pa nthawi ya mavuto, ndipo timafuna kutengela citsanzo cawo. M’bale Alan, wa zaka 45 amene ni mkulu, ali na colinga cofuna kukhala wofikilika. Posinkhasinkha citsanzo ca Yesu, iye anati: “Yesu anali kukhala wotangwanika, koma anthu a misinkhu yonse anali kumasuka kupita kwa iye na kumupempha thandizo. Anthuwo anaona kuti iye amasamala kwambili za iwo. Nifunitsitsa kwambili kutengela citsanzo ca Yesu pa nkhani yokhala wofikilika, waubwenzi, komanso woganizila ena.”

16. Kodi Salimo 119:59, 60, ingatithandize bwanji kutsatila citsanzo ca Yesu mosamala kwambili?

16 Tisalefuke tikalephela kutengela citsanzo ca Yesu ndendende. (Yak. 3:2) Kumbukilani kuti wophunzila saposa mphunzitsi wake. Ngakhale n’telo, pamene wophunzilayo akuphunzila zinthu kwa mphunzitsi wake, n’kutheka kuti azilakwitsa zinthu zina. Koma ngati iye aphunzilapo kanthu pa zimene akulakwitsa na kuyesetsa kutengela citsanzo ca mphunzitsi wake, adzakhala akupitabe patsogolo. Mofananamo, tikamaseŵenzetsa zimene timaphunzila m’Baibo, na kuyesetsa kuwongolela mbali zimene timalakwitsa, tidzakwanitsa kutengela citsanzo ca Yesu.—Ŵelengani Salimo 119:59, 60.

MAPINDU A KUKHALA WODZIMANA

Akulu akatengela mzimu wodzimana wa Yesu, amapeleka citsanzo cabwino cimene acicepele angatengele (Onani ndime 17) *

17-18. Kodi tidzapindula bwanji tikamatengela mzimu wodzimana wa Yesu?

17 Khalidwe lathu la kudzimana lingayambukile ena. Mkulu wina dzina lake Tim anati: “Tili na abale acinyamata amene apita patsogolo n’kukhala atumiki othandiza. Ndipo kutengela mzimu wodzimana wa anthu ŵena, ni mbali ina imene inawathandiza kuti aikidwe pa udindo. Abale acinyamata amenewa, amathandiza kwambili mu mpingo na kucilikiza akulu.”

18 Tikukhala m’dziko lodzala na ŵanthu odzikonda. Koma anthu a Yehova ni osiyana kwambili na iwo. Talimbikitsidwa kuona mzimu wodzimana wa Yesu, ndipo ndife ofunitsitsa kutengela citsanzo cake. N’zoona kuti sitingatsatile mapazi ake ndendende, koma tingatsatile mapazi ake mosamala kwambili.’ (1 Pet. 2:21) Tikamayesetsa kutengela mzimu wodzimana wa Yesu, tidzakhala acimwemwe podziŵa kuti tikukondweletsa Yehova.

NYIMBO 13 Khristu ni Citsanzo Cathu

^ ndime 5 Nthawi zonse, Yesu anali kuika zabwino za ena patsogolo pa zofuna zake. M’nkhani ino, tikambilane mmene tingatengele citsanzo cake. Tikambilanenso mapindu amene tidzapeza tikatengela mzimu wodzimana wa Yesu.

^ ndime 57 MAWU OFOTOKOZELA CITHUNZI: Dan m’bale wacinyamata, akuyang’ana pamene akulu aŵili abwela kudzaona atate ake ku cipatala. Citsanzo ca akulu amenewa cikumulimbikitsa kuti nayenso afunefune mipata yothandizila ena mu mpingo. M’bale wina wacinyamata Ben, akuona zimene Dan akucita. Citsanzo ca Dan cikulimbikitsa Ben kuthandiza kuyeletsa nawo Nyumba ya Ufumu.