NKHANI YOPHUNZILA 7
NYIMBO 15 Tamandani Woyamba Kubadwa wa Yehova
Mmene Kukhululuka kwa Yehova Kumatipindulila
“Inu mumakhululuka ndi mtima wonse.”—SAL. 130:4.
ZOFUNIKA KUMVETSETSA
Tikambilane ena mwa mawu ofanizila amene Baibulo limagwilitsa nchito pofotokoza mmene Yehova amatikhululukila mwapadela. Kukambilana mawu amenewa kudzatithandiza kukulitsa ciyamikilo cathu pa kukhululuka kwa Yehova.
1. N’cifukwa ciyani m’povuta kudziwa zimene munthu akutanthauza akakamba kuti “ndakukhululukilani”?
“NDAKUKHULULUKILANI.” Mawu amenewa amakhazika mtima pansi, makamaka ngati mukudziwa kuti munakamba kapena kucita cinthu cimene cinakhumudwitsa winawake. Kodi mawu akuti “ndakukhululukilani” amatanthauza ciyani kwenikweni? Kodi munthu akakuuzani mawu amenewa, amatanthauza kuti ubwenzi wanu ndi munthuyo wakhalanso bwino? Kapena amangotanthauza kuti sakufunanso kukamba za nkhani imeneyo? Anthu amatanthauza zosiyanasiyana akakamba mawu akuti “ndakukhululukilani.”
2. Kodi Malemba amakufotokoza bwanji kukhululuka kwa Yehova? (Onaninso mawu a m’munsi.)
2 Mmene Yehova amakhululukila anthu opanda ungwilofe n’zosiyana kwambili ndi mmene tingakhululukile ena. Kulibe munthu angakhululuke mmene Yehova amacitila. Ponena za kukhululuka kwa Yehova, wamasalimo anati: “Inu mumakhululuka ndi mtima wonse, kuti anthu azikuopani.” a (Sal. 130:4) Inde, Yehova akakhululuka, ‘amakhululuka ndi mtima wonse.’ Iye ndiye amaika muyeso wa zimene kukhululuka kwenikweni kumatanthauza. M’mavesi ena a Malemba a Ciheberi, ponena za kukhululuka kwa Yehova, olemba Baibulo anagwilitsa nchito mawu amene sanawagwilitsepo nchito ponena za mmene anthu amakhululukila.
3. Kodi kukhululuka kwa Yehova kumasiyana bwanji ndi kwa ife anthu? (Yesaya 55:6, 7)
3 Yehova akakhululukila munthu, chimo la munthuyo limafafanizidwa kothelatu. Ubale umene unawonongeka pakati pa iye ndi Mulungu umakhalanso bwino. Kukhululuka kwa Yehova n’kwacikwanekwane, ndipo amacita zimenezi mowolowa manja.—Welengani Yesaya 55:6, 7.
4. Kodi Yehova amatithandiza bwanji kumvetsa tanthauzo la kukhululuka kwenikweni?
4 Mmene Yehova amakhululukila n’zosiyana ndi mmene ife timacitila. Ndiye zingatheke bwanji anthu opanda ungwilofe kumvetsa tanthauzo la kukhululuka kwenikweni? Yehova amatithandiza kumvetsa kukhululuka kwake mwa kugwilitsa nchito mawu ofanizila. M’nkhani ino tikambilane ena mwa mawu amenewo. Mawuwo adzationetsa mmene Yehova amacotsela ucimo, komanso mmene amabwezeletsela ubale umene wawonongeka cifukwa ca ucimowo. Pamene tikambilana mawu amenewa, tidzakulitsa cikondi cathu pa Atate wathu wacikondi amene amatikhululukila m’njila zambili.
YEHOVA AMACOTSA CHIMO
5. N’ciyani cimacitika Yehova akatikhululukila macimo?
5 M’Baibulo, chimo limayelekezedwa ndi katundu wolemela. Mfumu Davide anafotokoza macimo ake motele: “Zolakwa zanga zakwela kupitilila mutu wanga. Sindingathe kuzisenza cifukwa zikulemela kwambili ngati katundu wolemela.” (Sal. 38:4) Koma Yehova amakhululuka macimo a munthu wolapa. (Sal. 25:18; 32:5) Mawu a Ciheberi amene anamasulidwa kuti “kukhululuka” m’mavesi amenewa amatanthauza “kunyamula.” Yehova akatikhululukila macimo athu timaleka kudziimba mlandu, ndipo zimakhala ngati iye watitula katundu wolemela pamapewa athu.
6. Kodi Yehova amacita nawo ciyani macimo athu akatikhululukila?
6 Mawu ena ofanizila amaonetsa mmene Yehova amaikila kutali macimo athu ndi iye. Salimo 103:12 limatiuza kuti: “Mofanana ndi mmene kotulukila dzuwa kwatalikilana ndi kolowela dzuwa, Mulungu waikanso zolakwa zathu kutali ndi ife.” Kum’mawa kotulukila dzuwa n’kotalikilana kwambili ndi kumadzulo kolowela dzuwa. M’mawu ena, Yehova akatikhululukila, zili ngati amatenga macimo athu ndi kuwaponyela kutali kwambili kosayelekezeka. Mawu amenewa amatitsimikizila kuti Yehova amakhululuka macimo athu ndi mtima wonse.
7. Kodi Baibulo limafotokoza kuti Yehova amacita nawo ciyani macimo athu? (Mika 7:18, 19)
7 Yehova mophiphilitsa amatayila kutali macimo athu, ndipo sapitiliza kuwakumbukila. Ponena za Yehova, Mfumu Hezekiya inalemba kuti: “Macimo anga onse mwawaponyela kumbuyo kwanu.” Monga mmene mawu a m’munsi a pa vesi 17 akuonetsela, mawu amene Hezekiya anakamba anganenedwenso kuti, “mwacotsa macimo anga onse kuti musawaonenso.” (Yes. 38:9, 17; mawu a m’munsi) Mawu ofanizila amenewa amaonetsa kuti Yehova amatenga macimo a munthu wolapa ndi kuwatayila kutali kwambili kuti asawaonenso. Mawu a Hezekiya amenewa tingawanenenso motele: “Mwacititsa macimo anga kukhala ngati sanacitikepo.” Baibulo limagogomeza mfundo imeneyi pogwilitsa nchito mawu ena ofanizila olembedwa pa Mika 7:18, 19. (Welengani.) Palembali, Yehova akufotokozedwa kuti akutayila macimo athu panyanja yakuya. M’nthawi zakale, zinali zosatheka kutenganso cinthu cimene caponyedwa pamalo ozama am’nyanja.
8. Taphunzila ciyani pofika pano?
8 Pogwilitsa nchito mawu ofanizila amene takambilana, taona kuti Yehova akatikhululukila, amacotsa macimo athu kuti tisadzadziimbenso mlandu pa macimowo. Zoonadi, monga Davide anakambila, “osangalala ndi anthu amene akhululukidwa zocita zawo zosamvela malamulo ndipo macimo awo akhululukidwa. Wosangalala ndi munthu amene Yehova sadzawelengela chimo lake.” (Aroma 4:6-8) Uku ndiko kukhululuka kwenikweni!
YEHOVA AMAFAFANIZA MACIMO
9. Ndi mawu ofanizila ati amene Yehova akugwilitsa nchito pofotokoza kukula kwa cikhululuko cake?
9 Yehova amagwilitsa nchito mawu ena ofanizila potithandiza kumvetsa mmene amagwilitsila nchito nsembe ya dipo pofafaniza macimo a anthu olapa. Malemba amaonetsa kuti iye mophiphilitsa amatsuka ndi kuyeletsa macimo amenewo. Zotsatilapo zake n’zakuti munthu wocimwayo amakhala woyela. (Sal. 51:7; Yes. 4:4; Yer. 33:8) Yehova iyemwini akufotokoza zimene zimatsatilapo akayeletsa macimo a munthu. Iye akuti: “Ngakhale kuti macimo anu ndi ofiila kwambili, adzayela kwambili. Ngakhale kuti ndi ofiila ngati magazi, adzayela ngati thonje.” (Yes. 1:18) Inki yofiila ikadonthela pacovala coyela, zimakhala zovuta kuyeletsapo. Komabe, pogwilitsa nchito mawu ofanizila amenewa, Yehova akutitsimikizila kuti macimo athu angayeletsedwe kothelatu moti sangaonekenso.
10. Ndi mawu ena ati ofanizila amene Yehova amagwilitsa nchito pofotokoza kukula kwa cikhululuko cake?
10 Monga tinaphunzilila m’nkhani yapita, macimo amayelekezedwa ndi “nkhongole.” (Mat. 18:32-35) Conco nthawi iliyonse tikacimwila Yehova, zimakhala ngati tikuwonjezela nkhongole imene tili nayo kale kwa iye. Moti nkhongoleyo imakhala yaikulu zedi! Koma Yehova akatikhululukila, zimakhala ngati wafafaniza nkhongoleyo. Iye safuna kuti tibweze nkhogole ya macimo amene anawakhululuka kale. Munthu amamva bwino akauzidwa ndi mnzake kuti asabwezenso nkhongole. Nafenso timamva bwino Yehova akatikhululukila macimo athu.
11. Kodi Baibulo limatanthauza ciyani likakamba kuti macimo athu ‘afafanizidwa’? (Machitidwe 3:19)
11 Yehova samangokhululuka nkhongoleyo kapena kuti macimo athu, koma amawafafanizilatu. (Welengani Machitidwe 3:19.) Tiyeni titsindike mfundoyi motele: Yelekezani kuti munthu amene mufunika kumubwezela nkhongole akulemba cilembo cacikulu ca papepala loonetsa ndalama imene mufunika kumubwezela. Akucita zimenezo poonetsa kuti simufunikilanso kubweza nkhongoleyo. Komabe, manambala oonetsa ndalamayo angakhale kuti akuonekelabe pansi pacilembo ca . Koma kufafaniza cinacake n’kosiyana ndi zimenezi. Kuti timvetse mawu ofanizila amenewa, tiyenela kukumbukila kuti inki imene anali kugwilitsa nchito m’nthawi zakale anali kuifuta mosavuta ndi madzi. Munthu anali kungotenga cinsalu conyowa n’kuifuta. Conco, nkhongole “ikafafanizidwa” sanali kuikumbukilanso. Ndipo zolembedwazo sizinali kuonekelanso. Zinali ngati nkhongoleyo sinakhalepo. Mtima wathu umadzala ndi ciyamikilo podziwa kuti Yehova samangokhululuka macimo athu, koma amawafafaniza kothelatu!—Sal. 51:9.
12. Kodi mawu ofanizila onena za mtambo waukulu atiphunzitsa ciyani?
12 Palinso mawu ena ofanizila amene Yehova amagwilitsa nchito pofotokoza mmene amafafanizila macimo athu. Iye amanena kuti: “Ndidzafafaniza zolakwa zako ndipo zidzakhala ngati ndaziphimba ndi mtambo, ndipo macimo ako adzakhala ngati ndawaphimba ndi mtambo waukulu.” (Yes. 44:22) Yehova akatikhululukila macimo, zimakhala ngati waaphimba ndi mtambo waukulu kuti asaonekele kwa ife komanso kwa iye.
13. Timapindula bwanji Yehova akatikhululukila macimo athu?
13 Kodi mawu ofanizila onsewa amene takambilana atiphunzitsa ciyani? Yehova akatikhululukila macimo, sitiyenela kudziimbanso mlandu pa macimo amenewo kwa moyo wathu wonse. Mwa nsembe ya magazi a Yesu Khristu, Mulungu amatikhululukila macimo ndi mtima wonse. Ndipo iye akatikhululukila macimowo, zimakhala ngati sitinawacitepo. Tikalapa macimo athu, awa ndiwo mapindu omwe timapeza Yehova akatikhululukila.
TIMAKHALANSO PAUBALE WABWINO NDI YEHOVA
14. N’cifukwa ciyani tiyenela kukhulupilila kuti Yehova adzatikhululukila ndi mtima wonse? (Onaninso zithunzi.)
14 Kukhululuka kwenikweni kwa Yehova, kumatipatsa mwayi wokhalanso paubale wabwino ndi iye. Zimenezi zimatithandiza kuti tipewe kudziimba mlandu. Sitikhala ndi nkhawa yoganiza kuti mwina Yehova anatisungila cakukhosi, ndipo akufunafuna njila yotipatsila cilango. Iye sangacite zimenezo. N’ciyani cingatipangitse kumukhulupilila Yehova akakamba kuti watikhululukila? Yehova anauza mneneli Yeremiya kuti: “Ine ndidzawakhululukila zolakwa zawo ndipo macimo awo sindidzawakumbukilanso.” (Yer. 31:34) Paulo anagwilitsa nchito mawu ofananako ponena za Yehova pomwe anati: “Sindidzakumbukilanso macimo awo.” (Aheb. 8:12) Kodi izi zimatanthauza ciyani?
15. Kodi mawu akuti Yehova sadzakumbukilanso macimo athu amatanthauza ciyani?
15 M’Baibulo, mawu akuti “kukumbukila,” si nthawi zonse pamene amatanthauza kuti munthu akuganizila zinthu zimene zinacitika kumbuyo. Nthawi zina angatanthauze kucitapo kanthu. Munthu wocita zoipa amene anapacikidwa pambali pa Yesu, anam’pempha kuti: “Yesu, mukandikumbukile mukakalowa mu Ufumu wanu.” (Luka 23:42, 43) Ndi mawu amenewo, iye sanali kungopempha Yesu kuti akamukumbukile. Koma anali kumupempha kuti akamucitile zinazake akakalowa mu Ufumu wake. Yankho la Yesu lionetsa kuti iye anali kudzacitapo kanthu mwa kudzamuukitsa. Conco, Yehova akakamba kuti sadzakumbukilanso macimo athu, amatanthauza kuti watikhululukila ndipo sadzatipatsa cilango pa macimo amenewo.
16. Kodi Baibulo limayelekezela mkhalidwe wathu ndi wa ndani?
16 Baibulo limagwilitsa nchito mawu ena ofanizila otithandiza kumvetsa ufulu umene timakhala nawo Yehova akatikhululukila ndi mtima wonse. Cifukwa ca kupanda ungwilo kwathu, Baibulo limati tili ngati “akapolo a ucimo.” Koma Yehova akatikhululukila, timakhala ngati akapolo amene ‘amasulidwa ku ucimo.’ (Aroma 6:17, 18; Chiv. 1:5) Yehova akatikhululukila, timamva bwino kwambili kuti tamasulidwa kuukapolo.
17. Kodi pamakhala zotulukapo zabwino ziti tikakhululukidwa? (Yesaya 53:5)
17 Welengani Yesaya 53:5. Mawu othela ofanizila amene tikambilane, amatiyelekezela ndi anthu amene akudwala matenda akupha. Cifukwa ca nsembe ya dipo imene Yehova anapeleka kudzela mwa Mwana wake, timakhala ngati tinacilitsidwa kumatendawo. (1 Pet. 2:24) Dipo limapangitsa kuti zikhale zotheka kukonzanso ubale wathu ndi Yehova umene umawonongeka tikadwala kuuzimu. Munthu akacila matenda ake aakulu, amasangalala kwambili. Mofananamo, nafenso timasangalala tikacilitsidwa kuuzimu ndi kukhalanso paubwenzi ndi Yehova akatikhululukila.
MMENE TIMAPINDULILA NDI KUKHULULUKA KWA YEHOVA
18. Kodi taphunzila ciyani pokambilana mawu ofanizila opezeka m’Baibulo okamba za kukhululuka kwa Yehova? (Onaninso danga lakuti “Mmene Yehova Amatikhululukila.”)
18 Kodi taphunzila ciyani pokambilana mawu ofanizila opezeka m’Baibulo okamba za kukhululuka kwa Yehova? Yehova akakhululuka, amatelo ndi mtima wonse ndipo sakumbukilanso macimo athu. Izi zimatipatsa mwayi wokhalanso paubale wolimba ndi Atate wathu wakumwamba. Taphunzilanso kuti kukhululukidwa macimo ndi mphatso imene Yehova amatipatsa. Amatelo cifukwa amatikonda komanso ndi wowolowa manja, ndipo amacita zimenezi mwa cisomo cake.—Aroma 3:24.
19. (a) Kodi tiyenela kuyamikila ciyani? (Aroma 4:8) (b) Tidzakambilana ciyani m’nkhani yotsatila?
19 Welengani Aroma 4:8. Aliyense wa ife ayenela kuyamikila kwambili podziwa kuti Yehova ndi Mulungu amene ‘amakhululuka ndi mtima wonse’! (Sal. 130:4) Komabe, kuti tikhululukidwe, ifenso tiyenela kucita cinacake cofunikila. Onani zimene Yesu anakamba: “Ngati simukhululukila anthu macimo awo, Atate wanu sadzakukhululukilaninso macimo anu.” (Mat. 6:14, 15) Conco, m’pofunika kuti nafenso tizitengela citsanzo ca Yehova ca kukhululukila ena. Koma kodi tingacite bwanji zimenezi? Nkhani yotsatila idzayankha funso limeneli.
NYIMBO 46 Tikuyamikani Yehova
a Mmene mawu a Ciheberi anawagwilitsila nchito palembali aonetsa kuti uku ndiye kukhululuka kwenikweni. Amaonetsanso kuti ndi Yehova yekhayo amene angakhululuke macimo ndi mtima wonse. Mu Mabaibulo ambili mulibe mfundo yofunika imeneyi palembali, koma mu Baibulo la Dziko Latsopano ilimo. Izi zimapangitsa Baibulo limeneli kukhala lapadela m’njila imene anamasulila lemba la Salimo 130:4.