NKHANI YOPHUNZILA 2
Tamandani Yehova Pakati pa Mpingo
“Ndidzakutamandani pakati pa mpingo.” —SAL. 22:22.
NYIMBO 59 Tamandani Yehova
ZA M’NKHANI INO *
1. Kodi Davide anali kumuona bwanji Yehova? Nanga zimenezi zinam’sonkhezela kucita ciani?
MFUMU DAVIDE analemba kuti: “Yehova ndi wamkulu ndi woyenela kutamandidwa kwambili.” (Sal. 145:3) Iye anali kum’konda Yehova. Izi zinam’sonkhezela kutamanda Mulungu “pakati pa mpingo.” (Sal. 22:22; 40:5) Mwacionekele, na imwe mumakonda Yehova. Ndipo mumafuna kum’tamanda monga mmene Davide anacitila, pamene anati: “Mudalitsike inu Yehova Mulungu wa Isiraeli atate wathu, kuyambila kalekale mpaka kalekale.”—1 Mbiri 29:10-13.
2. (a) Kodi tingam’tamande bwanji Yehova? (b) Nanga n’ciani cimalepheletsa ena kucita zimenezo? Kodi tidzakambilana ciani m’nkhani ino?
2 Masiku ano, njila imodzi imene timatamandila Yehova ni mwa kupeleka ndemanga pa misonkhano. Komabe, abale na alongo ena zimawavuta kucita zimenezi. Amafuna kutengamo mbali, koma amayopa. Kodi angacite ciani kuti acepetse vutoli? Nanga ni malangizo ati amene angatithandize ife tonse kupeleka ndemanga zolimbikitsa? Tisanayankhe mafunso amenewa, tiyeni coyamba tikambilane zifukwa zinayi zofunika zimene timapelekela ndemanga pamisonkhano.
ZIFUKWA ZIMENE TIMAPELEKELA NDEMANGA PA MISONKHANO
3-5. (a) Mogwilizana ndi Aheberi 13:15, n’cifukwa ciani timapeleka ndemanga pa misonkhano? (b) Kodi tonse tiyenela kupeleka ndemanga zofanana? Fotokozani.
3 Ife tonse, Yehova anatipatsa mwayi wakuti tizim’tamanda. (Sal. 119:108) Ndemanga zathu pamisonkhano ni ‘nsembe imene timapeleka kwa Mulungu,’ ndipo palibe aliyense angatipelekele nsembeyi. (Ŵelengani Aheberi 13:15.) Kodi Yehova amafuna kuti tizipeleka ndemanga zofanana? Iyai.
4 Yehova amadziŵa kuti tili na maluso osiyana-siyana, komanso zocitika mu umoyo wathu zimasiyana-siyana. Ndipo amayamikila kwambili ndemanga zilizonse zimene tingapeleke pa misonkhano. Mwacitsanzo, iye anali kulandila nsembe zosiyana-siyana kucokela Lev. 5:7, 11) Ngakhale kuti ufa unali wotsika mtengo, Yehova anali kulandila nsembeyo, malinga ngati unali “ufa wosalala.”
kwa Aisiraeli. Aisiraeli ena anali kukwanitsa kupeleka nkhosa kapena mbuzi. Koma Aisiraeli osauka anali kupeleka “njiwa ziŵili kapena ana aŵili a nkhunda.” Ngati Mwisiraeli sanakwanitse kupeleka mbalame ziŵili, Yehova anali kulola kuti angopeleka “ufa wosalala wokwana gawo limodzi mwa magawo 10 a muyezo wa efa.” (5 Umu ni mmene Mulungu wathu wokoma mtima, amaonela ndemanga zathu. Iye sayembekezela kuti popeleka ndemanga, tonse tizilankhula mwaluso kwambili monga Apolo, kapena mogwila mtima kwambili monga Paulo. (Mac. 18:24; 26:28) Cimene Yehova amafuna cabe, n’cakuti tizipeleka ndemanga zabwino mmene tingathele, malinga na luso lathu. Kumbukilani mkazi wamasiye amene anapeleka tumakobidi tuŵili twatung’ono. Cifukwa anapeleka zonse zimene akanatha, Yehova anakondwela naye kwambili.—Luka 21:1-4.
6. (a) Mogwilizana ndi Aheberi 10:24, 25, kodi ndemanga zimene ena amapeleka pa misonkhano zingatikhudze bwanji? (b) Mungaonetse bwanji kuti mwayamikila ndemanga zolimbikitsa zimene ena apeleka?
6 Pamene tipeleka ndemanga, timalimbikitsana wina na mnzake. (Ŵelengani Aheberi 10:24, 25.) Tonse timakondwela kumvetsela ndemanga zosiyana-siyana za abale na alongo pa misonkhano. Mwacitsanzo, timayamikila ndemanga zazifupi komanso zocokela pansi pa mtima zimene acicepele amapeleka. Timalimbikitsidwa pomvetsela abale na alongo akufotokoza mwacimwemwe mfundo za coonadi zimene anapeza pokonzekela. Cinanso, timawayamikila abale na alongo amene ‘amalimba mtima’ kupeleka ndemanga pa misonkhano, olo kuti ni amanyazi kapena akuphunzila kumene citundu. (1 Ates. 2:2) Kodi tingaonetse bwanji kuti timawayamikila? Pambuyo pa misonkhano, tingawauze kuti tayamikila ndemanga yawo yolimbikitsa. Tingaonetsenso kuyamikila mwa kupeleka ndemanga pa misonkhano. Tikatelo, timalimbikitsanso ena, m’malo mongoyembekezela kuti iwo atilimbikitse.—Aroma 1:11, 12.
7. Kodi timapindula bwanji ngati timapeleka ndemanga pa misonkhano?
7 Ngati tipeleka ndemanga pa misonkhano, na ife timapindula. (Yes. 48:17) Kodi timapindula bwanji? Coyamba, mtima wofuna kukapelekapo ndemanga pa misonkhano umatilimbikitsa kukonzekela bwino. Tikakonzekela bwino, m’pamene timamvetsetsa Mawu a Mulungu amene timaphunzila. Ndipo tikawamvetsetsa, cimakhala cosavuta kuseŵenzetsa zimene taphunzilazo. Caciŵilli, timakondwela kwambili na misonkhano ngati timatengamo mbali. Cacitatu, popeza kuti pamafunika khama kuti tipeleke ndemanga pa misonkhano, mfundo zimene tayankha sitingaziiŵale mwamsanga.
8, 9. (a) Malinga n’zimene Malaki 3:16 imakamba, kodi muona kuti Yehova amamvela bwanji pamene tapeleka ndemanga? (b) Nanga ni vuto lanji limene ena angakhale nalo?
8 Timakondweletsa Yehova ngati tionetsa cikhulupililo cathu mwa kuyankhapo pa misonkhano. Timadziŵa kuti Yehova amamvetsela ndemanga zathu, ndipo amayamikila kwambili khama limene timaonetsa kuti tipelekepo ndemanga pa misonkhano. (Ŵelengani Malaki 3:16.) Iye amaonetsa kuyamikila kumeneku mwa kutithandiza pamene tiyesetsa kucita zinthu zom’kondweletsa.—Mal. 3:10.
9 Monga taonela, tili na zifukwa zomveka zopelekela ndemanga pa misonkhano. Ngakhale n’conco, ena amayopa kupeleka ndemanga. Ngati umu ni mmene imwe mumamvelela, musagwe mphwayi. Lomba tiyeni tikambilane mfundo zina za m’Baibo, zitsanzo, komanso malangizo amene angatithandize tonse, kuti tizipeleka ndemanga mokwanila pa misonkhano.
MMENE MUNGACEPETSELE MANTHA
10. (a) Ni mantha abwanji amene ambili a ife timakhala nawo? (b) N’cifukwa ciani tikamba kuti kuyopa kupeleka ndemanga kungakhale cizindikilo ca khalidwe labwino?
10 Kodi mumakhuta befu cifukwa ca mantha nthawi iliyonse mukafuna kupeleka ndemanga pa misonkhano? Ngati n’conco, dziŵani kuti sindimwe mwekha. Ambili a ife timakhalako na mantha popeleka ndemanga pa misonkhano. Koma kuti mucepetse mantha amenewa, coyamba muyenela kuzindikila zimene zimakupangitsani kukhala na mantha. Kodi mumayopa cifukwa coganiza kuti mudzaiŵala zokamba popeleka ndemanga? Kapena mumayopa kuti mungapeleke ndemanga yolakwika? Kapenanso mumayopa cifukwa coganiza kuti ndemanga yanu siingakhale yabwino poyelekezela na ndemanga za ena? Mantha amenewa angakhale cizindikilo cakuti muli na khalidwe labwino. Angaonetse kuti ndimwe wodzicepetsa, komanso kuti mumaona ena kukhala okuposani. Ndipo Yehova amakonda anthu odzicepetsa. (Sal. 138:6; Afil. 2:3) Koma Yehova amafunanso kuti muzimutamanda, na kulimbikitsa abale na alongo pa misonkhano. (1 Ates. 5:11) Iye amakukondani, ndipo adzakuthandizani kukhala wolimba mtima kuti mukwanitse kupeleka ndemanga.
11. Ni mfundo za m’Malemba ziti zimene zingatithandize kucepetsa mantha?
11 Ganizilani mfundo za m’Malemba zotsatilazi. Baibo imakamba kuti tonse timalakwitsa pa zokamba zathu. (Yak. 3:2) Cinanso, Yehova, kuphatikizapo Akhristu anzathu sayembekezela kuti tizicita zinthu mwangwilo. (Sal. 103:12-14) Iwo ni abale na alongo athu, ndipo amatikonda. (Maliko 10:29, 30; Yoh. 13:35) Amadziŵa kuti nthawi zina timalephela kupeleka ndemanga zathu ndendende mmene tinakonzekelela.
12-13. Kodi tiphunzilapo ciani pa citsanzo ca Nehemiya ndi ca Yona?
12 Manje, tiyeni tikambilane zitsanzo za m’Baibo, zimene zingatithandize kucepetsa mantha. Citsanzo coyamba n’ca Nehemiya. Iye anali kutumikila m’nyumba ya mfumu yamphamvu. Koma pa nthawi ina, anakhala wacisoni atamva kuti mpanda wa Yerusalemu unagwa, ndipo zipata zake zinatenthedwa na moto. (Neh. 1:1-4) Pamene mfumu inafunsa Nehemiya cifukwa cake nkhope yake inali yacisoni, iye anacita mantha kwambili. Koma mwamsanga, anapemphela kwa Mulungu, ndipo kenako anayankha. Poyankha pempho la Nehemiya, mfumuyo inacita zambili pothandiza anthu a Mulungu. (Neh. 2:1-8) Citsanzo cina n’ca Yona. Pamene Yehova anam’tuma kuti akapeleke uthenga waciweluzo kwa anthu a ku Nineve, Yona anacita mantha kwambili cakuti anathaŵa n’kuloŵela kwina. (Yona 1:1-3) Koma mwa thandizo la Yehova, Yona anakwanitsa kupita ku Nineve kukalalikila. Ndipo cifukwa ca uthenga umene analengeza, anthu a ku Nineve analapa moti sanawonongedwe. (Yona 3:5-10) Citsanzo ca Nehemiya citiphunzitsa kufunika kopemphela tikalibe kupeleka ndemanga. Citsanzo ca Yona citiphunzitsa kuti ngakhale titakhala na mantha aakulu, Yehova angatithandize kucita cifunilo cake. Ndipo kukamba zoona, kupeleka ndemanga pa misonkhano, sikungakhale kocititsa mantha monga mmene nchito yopeleka uthenga waciweluzo kwa Anineve inalili.
13 N’zinthu ziti zimene mungacite kuti muzipeleka ndemanga zolimbikitsa pa misonkhano? Tsopano, tiyeni tikambilane zina zimene zingatithandize.
14. N’cifukwa ciani tifunika kukonzekela bwino misonkhano? Ndipo ni pa nthawi iti pamene tingakonzekele?
14 Muzikonzekela msonkhano uliwonse. Mukakonzekela bwino, mumakhala womasuka kupeleka ndemanga. (Miy. 21:5) Aliyense amakhala na ndandanda yake yokonzekelela misonkhano. Mwacitsanzo, mlongo wamasiye wa zaka za m’ma 80, dzina lake Eloise, amakonzekela Phunzilo la Nsanja kuciyambi kwa wiki. Iye anati: “Nimakondwela kwambili na misonkhano ngati nakonzekela pasadakhale.” Mlongo Joy, amene amagwila nchito yolembedwa, amapatula nthawi pa Ciŵelu kuti akonzekele phunzilo la Nsanja ya Mlonda. Iye anakamba kuti: “Cimakhala cosavuta kukumbukila mfundo zimene n’naŵelenga pokonzekela ngati sipanapite nthawi itali.” M’bale Ike ni mkulu pa mpingo komanso mpainiya, ndipo nthawi zambili amakhala wotangwanika. Iye anati: “Nimaona kuti n’zothandiza kwa ine kukonzekela misonkhano m’zigawo-zigawo masiku angapo pa wiki, m’malo mokonzekela zonse pa nthawi imodzi.”
15. N’zinthu ziti zimene mufunika kucita kuti mukonzekele bwino misonkhano?
15 N’zinthu ziti zimene mufunika kucita kuti mukonzekele bwino misonkhano? Musanayambe kuŵelenga, nthawi zonse muzipempha Yehova kuti akupatseni mzimu woyela. (Luka 11:13; 1 Yoh. 5:14) Ndiyeno, kwa kanthawi kocepa, pendani mwacidule nkhani imene mufuna kuŵelengayo. Ganizilani mutu wa nkhaniyo, tumitu twa mkati, zithunzi, na tumabokosi. Pamene muŵelenga palagalafu iliyonse, ŵelengani malemba ambili osagwila mawu mmene mungathele. Sinkha-sinkhani pa mfundo zimene muŵelenga, maka-maka zimene mufuna kukapelekapo ndemanga. Mukakonzekela bwino, m’pamene mumapindula kwambili na misonkhano, ndiponso cimakhala cosavuta kupelekapo ndemanga.—2 Akor. 9:6.
16. Ni mapulogilamu ati a pa zipangizo zamakono amene mumawaseŵenzetsa? Nanga mumawaseŵenzetsa bwanji?
16 Ngati n’zotheka, seŵenzetsani mapulogilamu a pa zipangizo za makono opezeka m’citundu cimene mudziŵa. Yehova, kupitila m’gulu lake, anatikonzela mapulogilamu a pa zipangizo zamakono kuti azitithandiza pokonzekela misonkhano. Mwacitsanzo, ngati tili na JW Laibulale®, tingacite daunilodi zofalitsa zophunzilila Baibo pa tabuleti kapena pa foni yathu. Ndiyeno, tingathe kuŵelenga zofalitsazo kapena kungozimvetsela pa nthawi iliyonse imene tili na mpata komanso kulikonse. Ena amaseŵenzetsa JW Laibulale® pokonzekela misonkhano pa nthawi yopumula ku nchito kapena ku sukulu, kapenanso pamene ali pa ulendo. Kuseŵenzetsa Watchtower Laibulale komanso LAIBULALE YA PA INTANETI™ ya Watchtower, kumathandiza kwambili ngati tifuna kufufuza zowonjezeleka pa mfundo inayake imene tapeza.
17. (a) N’cifukwa ciani kukonzekela ndemanga zoculukilapo n’kofunika? (b) Kodi munaphunzila mfundo zotani m’vidiyo yakuti Khala Bwenzi la Yehova—Konzekela Yankho Lako?
17 Ngati n’kotheka, muzikonzekela ndemanga zoculukilapo pa phunzilo iliyonse. Cifukwa ciani? Cifukwa cakuti si nthawi zonse pamene mungapatsidwe mwayi wopeleka ndemanga. Mukaimika dzanja, pamakhalanso ena amene amaimika, ndipo wotsogoza phunzilo angasankhe kupatsa munthu wina mwayi woyankhapo. Komanso, pofuna kuti misonkhano ithe pa nthawi yake, nthawi zina wotsogoza phunzilo angapatse anthu ocepa cabe mwayi wopeleka ndemanga pa mfundo inayake. Conco, simuyenela kukhumudwa ngati wotsogoza phunzilo sanakupatseni mwayi woyankhapo m’mapalagilafu oyambilila a phunzilolo. Ngati mwakonzekela ndemanga zoculukilapo, mumakhala na mipata yambili yopeleka ndemanga. Mwina mungakonzekele kukaŵelenga lemba. Koma ngati n’kotheka, mungakonzekelenso kukapeleka ndemanga m’mawu anu-anu. *
18. N’cifukwa ciani tifunika kupeleka ndemanga zacidule?
Miy. 10:19; 15:23) Ngati ndimwe aciyambakale m’coonadi, ndipo mwakhala mukupeleka ndemanga pa misonkhano kwa zaka zambili, muli na udindo waukulu pa nkhaniyi. Muyenela kukhala citsanzo cabwino, mwa kupeleka ndemanga zacidule. Ngati mupeleka ndemanga zazitali komanso zocoloŵana, ena angagwe mphwayi, poganiza kuti sangakwanitse kupeleka ndemanga mmene imwe mumapelekela. Komanso, kupeleka ndemanga zacidule kumathandiza kuti ambili akhale na mwayi woyankhako pa misonkhano. Maka-maka ngati ndimwe woyamba kuyankhapo pa palagilafu, pelekani yankho yacidule komanso yosapita m’mbali. Musafotokoze mfundo zonse m’palagilafu. Ngati mfundo yaikulu yakambiwa kale, mungapeleke ndemanga pa mfundo zina zocilikiza mfundo yaikuluyo.—Onani bokosi yakuti “Kodi Ningapeleke Ndemanga pa Mbali Ziti?”
18 Muzipeleka ndemanga zacidule. Nthawi zambili, ndemanga zacidule n’zimene zimakhala zolimbikitsa kwambili. Conco, muziyesetsa kupeleka ndemanga zacidule, zosapitilila masekondi 30. (19. Mungacite ciani kuti wotsogoza phunzilo akuthandizeni kuti muyankhepo? Nanga nthawi yopeleka ndemanga ikafika, muyenela kucita ciani?
19 Dziŵitsani wotsogoza phunzilo kuti mufuna muyankhepo pa palagilafu inayake. Ngati mwasankha kucita zimenezi, ndiye kuti misonkhano isanayambe, muyenela kumuuzilatu wotsogoza phunzilo za palagilafu imene mufuna muyankhepo. Ndipo nthawi yopeleka ndemanga pa palagilafuyo ikafika, kwezani dzanja kwambili komanso mwamsanga kuti wotsogoza akuoneni.
20. Kodi misonkhano ya mpingo imalingana bwanji na cakudya codyela pamodzi na mabwenzi athu?
20 Muziona misonkhano ya mpingo monga phwando la cakudya codyela pamodzi na mabwenzi abwino. Tiyelekezele kuti mwaitanidwa ku phwando limene ena mu mpingo akonza. Ndipo akuuzani kuti popita kumeneko, mukatengeko zakudya zocepa zimene mungakwanitse. Kodi mungacite ciani? Mwina mungakhaleko na nkhawa kapena mantha ena ake. Koma mwacionekele, mungayesetse kutengako zakudya zilizonse zimene muona kuti ena angakondwele nazo. Nayenso Yehova amatiitana ku phwando la cakudya cauzimu. Iye amatipatsa zakudya zambili zopatsa thanzi pa misonkhano. (Sal. 23:5; Mat. 24:45) Ndipo amakondwela ngati popita ku misonkhano, timatengako kamphatso, kapena kuti kukonzekela ndemanga yoti tikapeleke. Conco, muzikonzekela bwino misonkhano, komanso muzitengamo mbali momasuka mmene mungathele. Mukatelo, ndiye kuti mudzakondwela kudya pa thebulo ya Yehova, komanso mudzakhala na mphatso yokapeleka kwa abale na alongo mu mpingo.
NYIMBO 2 Dzina Lanu Ndimwe Yehova
^ ndime 5 Mofanana na wamasalimo Davide, tonse timakonda Yehova komanso timafunitsitsa kum’tamanda. Pamene tasonkhana na Akhristu anzathu, timakhala na mwayi wapadela woonetsa kuti timakonda Mulungu. Komabe, ena a ife zimativuta kupeleka ndemanga pamisonkhano. Ngati mumayopa kupeleka ndemanga pa misonkhano, nkhani ino idzakuthandizani kudziŵa zimene zimakupangitsani kuyopa. Komanso idzafotokoza zimene mungacite kuti mucepetse vuto limeneli.
^ ndime 17 Tambani vidiyo ya pa jw.org, yakuti Khala Bwenzi la Yehova—Konzekela Yankho Lako. Pitani pa MABUKU > MAVIDIYO > ANA.
^ ndime 63 MAWU OFOTOKOZA ZITHUNZI PEJI 9: Abale na alongo akupeleka ndemanga mwacimwemwe pa Phunzilo la Nsanja ya Mlonda.
^ ndime 65 MAWU OFOTOKOZA ZITHUNZI PEJI 10-11: Ena mwa abale na alongo amene anali kutengako mbali pa Phunzilo la Nsanja ya Mlonda. Olo kuti zocitika mu umoyo wawo n’zosiyana-siyana, onse amapatula nthawi yokonzekela misonkhano.