Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI YOPHUNZILA 26

“Bwelelani kwa Ine”

“Bwelelani kwa Ine”

“Bwelelani kwa ine ndipo ine ndibwelela kwa inu.”—MAL. 3:7.

NYIMBO 102 “Thandizani Ofooka”

ZIMENE TIKAMBILANE *

1. Kodi Yehova amamvela bwanji ngati imodzi mwa nkhosa zake zosocela yabwelela kwa iye?

MONGA tinaphunzilila m’nkhani yapita, Yehova amadziyelekezela na m’busa wabwino amene amasamalila mwacikondi nkhosa yake iliyonse. Iye amasakila nkhosa iliyonse imene inasocela. Yehova anauza Aisiraeli amene anamusiya, kuti: “Bwelelani kwa ine ndipo ine ndibwelela kwa inu.” Tidziŵa kuti ni mmenenso Yehova amamvelela masiku ano, cifukwa iye anati: “Ine ndine Yehova, sindinasinthe.” (Mal. 3:6, 7) Yesu anakamba kuti Yehova na angelo amakondwela kwambili ngati mmodzi cabe mwa atumiki ake osocela wabwelela kwa Iye.—Luka 15:10, 32.

2. Kodi tikambilana ciani m’nkhani ino?

2 Tiyeni lomba tikambilane mafanizo atatu a Yesu amene amatiphunzitsa mfundo zofunika za mmene tingathandizile Akhristu ozilala. Tikambilananso makhalidwe ena amene timafunika kukhala nawo kuti tikwanitse kuthandiza nkhosa zosocela kubwelela kwa Yehova. Kuwonjezela apo, tiona mapindu amene timapeza tikamacita khama kuthandiza ozilala.

KUSAKILA KOINI YOTAIKA

3-4. N’cifukwa ciani mzimayi wochulidwa pa Luka 15:8-10, anasakila mwakhama ndalama yake ya dalakima imene inataika?

3 Pamafunika khama kuti tipeze anthu ozilala amene afuna kubwelela kwa Yehova. M’fanizo lina lolembedwa m’buku la Uthenga Wabwino la Luka, Yesu anakamba za mzimayi wina amene anasakila koini yofunika kwambili ya dalakima imene inam’taika. Fanizoli limagogomeza kwambili za khama limene mzimayiyo anaonetsa posakila koiniyo.—Ŵelengani Luka 15:8-10.

4 Yesu anafotokoza mmene mzimayiyo anasangalalila atapeza ndalama yake yamtengo wapatali ya dalakima imene inam’taika. M’masiku a Yesu, cioneka kuti amayi ena Aciyuda anali kupatsa ana awo aakazi makoini 10 a dalakima pa tsiku la cikwati cawo. N’kutheka kuti koini ya mzimayi wa m’fanizoli inali imodzi mwa makoini 10 amenewo. Mzimayiyo anali na cikhulupililo cakuti koiniyo yagwela pansi m’nyumba. Conco, anayatsa nyale na kuyamba kuisakila, koma sanaione. N’kutheka kuti nyaleyo siinali kuwala mokwanila, ndipo mwina ndiye cifukwa cake iye sanali kukaona ka ndalama kasilivako. Pamapeto pake, iye anapyanga mosamala m’nyumba monsemo. Ndiyeno anangoona koini yake yamtengo wapataliyo ikunyezimila potelo, pa dothi limene anapyanga. Tangoganizilani cimwemwe cimene anakhala naco! Zitatelo, mzimayiyo anaitana mabwenzi ake na maneba kuti awauzeko nkhani yokondweletsa imeneyo.

5. N’cifukwa ciani nthawi zina zingakhale zovuta kupeza Akhristu ozilala?

5 Monga taonela m’fanizo la Yesu, pamafunika khama kuti tipeze cinthu cimene cataika. M’cimodzi-modzi na nchito yosakila anthu ozilala. Tifunika kucita khama kuti tiwapeze. Ena akhala ozilala kwa zaka zambili. Ndipo ena angakhale kuti anakukila ku dela lina kumene abale na alongo sawadziŵa. N’zodziŵikilatu kuti pali pano, ena mwa abale na alongo ozilala amenewa amafunitsitsa kubwelela kwa Yehova. Iwo amafuna kuyambanso kutumikila Yehova pamodzi na banja la olambila oona, koma amafunika thandizo lathu.

6. N’ciani cimene aliyense angacite mumpingo pothandiza kusakila ozilala?

6 Kodi ndani angathandize pa nchito yosakila ozilala? Tonsefe, kaya ndife akulu, apainiya, acibululu a munthu wozilala, kapena ofalitsa mumpingo, tingathandize posakila ozilala. Kodi muli na mnzanu kapena wacibululu amene analeka kusonkhana na kulalikila? Kodi munakumanapo na munthu wozilala pamene munali mu ulaliki wa kunyumba na nyumba kapena pamene munali kucita ulaliki wa poyela? Ngati munthuyo angalole kucezeledwa, mupempheni kuti akupatseni namba yake ya foni kapena adresi, na kumuuza kuti mungakonde kukaipeleka kwa akulu a mumpingo.

7. Mwaphunzilapo ciani pa zimene m’bale Thomas anakamba?

7 Akulu ndiwo ali na udindo waukulu posakila anthu ozilala amene afuna kubwelela kwa Yehova. Kodi angacite bwanji zimenezi? Onani zimene mkulu wina wa ku Spain dzina lake Thomas * anakamba. Iye wathandiza abale na alongo ozilala oposa 40 kuyambanso kutumikila Yehova. M’bale Thomas anati: “Coyamba, nimafunsa abale na alongo ngati adziŵako kumene ozilala a mumpingo mwathu amakhala. Nthawi zina nimapempha ofalitsa kuti anifotokozele ngati akumbukilako aliyense amene analeka kusonkhana. Ofalitsa ambili mumpingo amakondwela kuthandiza cifukwa amaona kuti umenewo ni mwayi wawo wocilikiza pa nchito yosakila anthu ozilala. Nikapita kukacezela abale na alongo ozilalawo, nimawafunsa za umoyo wa ana awo komanso wa acibululu awo. Anthu ena ozilala amakhala kuti anali kusonkhana pamodzi ndi ana awo, ndipo panthawiyo anawo anapita patsogolo mpaka kufika pokhala ofalitsa. Nawonso anawo tingawathandize kubwelela kwa Yehova.”

ABWEZENI ANA A YEHOVA OSOCELA

8. M’fanizo la mwana woloŵelela la pa Luka 15:17-24, kodi tate anamulandila bwanji mwana wake wolapa?

8 Kodi ni makhalidwe ati amene tiyenela kukhala nawo kuti tikwanitse kuthandiza anthu amene afuna kubwelela kwa Yehova? Onani mfundo zimene tingaphunzilepo pa fanizo la Yesu la mwana woloŵelela. (Ŵelengani Luka 15:17-24.) Yesu anakamba kuti m’kupita kwa nthawi, mwanayo anazindikila kuti anacita zinthu mopanda nzelu, ndipo anaganiza zobwelela kunyumba. Atate wake atamuona, anamuthamangila na kumukumbatila pofuna kum’tsimikizila kuti amam’konda. Mwanayo anali kuvutitsidwa na cikumbumtima, komanso anali kudziona wosayenelela kuchedwa mwana wawo. Atate wake anamumvela cifundo mwanayo pamene anali kuwafotokozela mocokela pansi pa mtima mmene anali kumvelela. Ndiyeno, atate wake anacita zinthu zina zimene zinathandiza mwanayo kuona kuti amulandila na manja aŵili, osati monga wanchito, koma monga mwana wawo wokondedwa. Pofuna kuonetsa kuti amamukondadi mwana wolapayo, anamukonzela phwando na kum’patsa zovala zabwino.

9. Ni makhalidwe otani amene tiyenela kukhala nawo kuti tithandize ozilala kubwelela kwa Yehova? (Onani bokosi yakuti, “ Mmene Tingathandizile Ozilala Amene Afuna Kubwelela kwa Yehova.”)

9 Yehova ali ngati tate wa m’fanizo limeneli. Amawakonda abale na alongo athu ozilala ndipo amafuna kuti abwelele kwa iye. Mwa kutengela citsanzo ca Yehova, tingawathandize ozilala kubwelela kwa iye. Kuti tikwanitse kucita zimenezi, tifunika kukhala oleza mtima, acifundo, komanso acikondi. N’cifukwa ciani tifunika kuonetsa makhalidwe amenewa? Nanga tingacite bwanji zimenezi?

10. N’cifukwa ciani kuleza mtima n’kofunika pothandiza munthu kubwelela kwa Yehova?

10 Tiyenela kukhala oleza mtima cifukwa zimatenga nthawi kuti munthu abwelele kwa Yehova. Ambili amene kale anali ozilala amakamba kuti anayambanso kugwilizana na mpingo pambuyo pocezeledwa mobweleza-bweleza na akulu komanso ofalitsa ena. Mlongo wina wa ku Southeast Asia, dzina lake Nancy, analemba kuti: “Mnzanga wina wapamtima mumpingo ananithandiza kwambili. Anali kunikonda kwambili monga mng’ono wake. Anali kunikumbutsa zinthu zokondweletsa zimene tinali kucita kale. Anali kunimvetsela moleza mtima pamene n’nali kufotokoza mmene n’nali kumvelela, ndipo sanali kuyopa kunipatsa malangizo. Anaonetsa kuti analidi bwenzi langa leni-leni, lokonzeka kunithandiza nthawi iliyonse.”

11. N’cifukwa ciani tifunika kukhala acifundo pothandiza munthu amene anakhumudwa?

11 Munthu akakhumudwa, amamvela kupweteka mumtima monga kuti ali na cilonda. Cifundo cili ngati mankhwala amphamvu amene angathandize munthu wotelo kumvelako bwino. Ena anazilala cifukwa cakuti winawake mumpingo anawakhumudwitsa zaka zambili zapitazo, ndipo akali okhumudwa. Pa cifukwa cimeneci, safuna kubwelela kwa Yehova. Mwina iwo amaona kuti anacitilidwa zinthu mopanda cilungamo. Amafuna munthu amene angawamvetsele, komanso amene angamvetsetse mmene akumvelela mumtima. (Yak. 1:19) Mlongo María, amene anali wozilala pa nthawi inayake, anati: “N’nali kufuna munthu amene akananimvetsela, kunitonthoza, kunithandiza, na kunipatsa malangizo abwino.”

12. Fotokozani fanizo loonetsa mmene cikondi ca Yehova cimakokela anthu ozilala kuti abwelele ku gulu lake.

12 Baibo imayelekezela cikondi ca Yehova pa anthu ake na cingwe, kapena kuti nthambo. Kodi cikondi ca Mulungu cili ngati cingwe m’njila yotani? Cabwino, tiyeni tiyelekezele motele: Tikambe kuti mwagwela mu cimgodi conoka, ndipo mukulephela kutulukamo. Kuti mutulukemo, pafunika munthu wina amene angakuponyeleni nthambo na kukudonselani kunja. Tsopano mvelani zimene Yehova anakamba ponena za Aisiraeli amene anasocela. Anati: “Ndinali kuwakoka ndi . . . zingwe zacikondi.” (Hos. 11:4, ftn.) Mulungu amamvelanso cimodzi-modzi akaganizila za anthu amene analeka kum’tumikila, ndipo akusautsika na mavuto komanso nkhawa za pa umoyo. Zili monga kuti iwo ali m’cimgodi conoka. Yehova amafuna kuti iwo adziŵe kuti iye amawakonda. Amafunanso kuwakoka kuti abwelele kwa iye. Ndipo iye angaseŵenzetse imwe poonetsa cikondi cake pa iwo.

13. Fotokozani citsanzo coonetsa kuti cikondi ca paubale n’camphamvu kwambili.

13 Tifunika kutsimikizila ozilala kuti Yehova amawakonda ndiponso kuti nafenso timawakonda. M’bale Pablo amene tinamuchula m’nkhani yapita, anali wozilala kwa zaka zoposa 30. Iye anati: “Tsiku lina m’maŵa pamene n’nali kucoka panyumba, n’nakumana na mlongo wacikulile wokoma mtima. Iye anayamba kukamba nane mwacikondi. Ndipo ine n’nakhudzika mtima kwambili moti n’nayamba kulila ngati mwana. N’nauza mlongoyo kuti, ‘Cioneka monga kuti ni Yehova wakutumani kuti mubwele kudzakamba nane.’ Kucokela pa nthawiyo, n’naganiza zobwelela kwa Yehova.”

MWACIKONDI, THANDIZANI OFOOKA

14. Mu fanizo la pa Luka 15:4, 5, kodi m’busa anacita ciani atapeza nkhosa yosocela?

14 Tifunika kupitiliza kuthandiza anthu ozilala tikawapeza. Mofanana na mwana woloŵelela wa m’fanizo la Yesu, ozilala angakhale opwetekedwa mtima. Ndipo nthawi zambili amakhala ofooka mwauzimu cifukwa ca zimene anakumana nazo m’dziko la Satana. Tifunika kuwathandiza kulimbitsa cikhulupililo cawo mwa Yehova. M’fanizo la nkhosa yosocela, Yesu anafotokoza kuti m’busa ananyamula paphewa nkhosa yosocela na kubwelela nayo ku gulu la nkhosa. Anacita izi olo kuti anali atawononga kale nthawi yoculuka na mphamvu zake posakila nkhosayo. N’cifukwa ciani anacita zimenezo? Cifukwa anadziŵa kuti nkhosayo ilibe mphamvu zoyenda yokha kubwelela ku gulu la nkhosa zinzake.—Ŵelengani Luka 15:4, 5.

15. Kodi tingawathandize bwanji ozilala amene afuna kubwelela kwa Yehova? (Onani bokosi yakuti, “ Cida Cothandiza Kwambili.”)

15 Tingafunike kuthela nthawi yoculuka na mphamvu zathu pothandiza ozilala kuthetsa zopinga zimene zikuwalepheletsa kutumikila Yehova. Koma mwa thandizo la mzimu wa Yehova, komanso pogwilitsila nchito Mawu ake, na zofalitsa zimene timalandila, tingakwanitse kuwathandiza kukhalanso olimba mwauzimu. (Aroma 15:1) Tingacite bwanji zimenezi? Mkulu wina amene watumikila kwa nthawi yaitali anati: “Akhristu ambili ozilala amene afunadi kubwelela kwa Yehova, amafunika kuphunzila nawo Baibo.” * Conco, ngati akulu akupemphani kuti muzitsogoza phunzilo kwa munthu amene anali wozilala, bwanji osaulandila na manja aŵili mwayi umenewo? Mkuluyo anakambanso kuti: “Wofalitsa amene amatsogoza phunzilolo, afunika kukhala bwenzi labwino kwa wozilalayo, amene angamudalile na kumasuka naye.”

CIMWEMWE KUMWAMBA NA PADZIKO LAPANSI

16. Tidziŵa bwanji kuti angelo amaseŵenzela nafe pamodzi pothandiza ozilala kubwelela kwa Yehova?

16 Pali zambili zimene zakhala zikucitika zoonetsa kuti angelo amaseŵenzela nafe pamodzi pothandiza ozilala amene ni ofunitsitsa kubwelela kwa Yehova. (Chiv. 14:6) Mwacitsanzo, Silvio wa ku Ecuador, anapemphela kwa Yehova na mtima wonse kuti amuthandize kubwelela mu mpingo. Pamene anali kupemphela, akulu aŵili anafika kunyumba kwake kudzam’cezela. Panthawiyo, akuluwo anakondwela kuyamba kupeleka thandizo lofunikila kwa iye kuti abwelele kwa Yehova.

17. Kodi timapindula bwanji tikamathandiza ozilala?

17 Tidzapeza cimwemwe coculuka ngati tithandiza ozilala kubwelela kwa Yehova. Mpainiya wina dzina lake Salvador, amene amayesetsa kuthandiza ozilala, anati: “Nikaganizila za ozilala amene abwelela kwa Yehova, nthawi zina, nimagwetsa misozi ya cisangalalo. Nimakondwela ngako kuona kuti Yehova wapulumutsa imodzi mwa nkhosa zake zokondedwa kucoka m’dziko la Satana, ndiponso kuti n’nali na mwayi wogwila naye nchito yopulumutsayo.”—Mac. 20:35.

18. Kodi simuyenela kukayikila za ciani ngati ndimwe ozilala?

18 Ngati ndimwe ozilala, musakayikile kuti Yehova akali kukukondani, ndipo amafuna kuti mubwelele kwa iye. N’zoona kuti pamafunika khama kuti mukwanitse kubwelela kwa Yehova. Koma dziŵani kuti mofanana na tate wa m’fanizo la Yesu, Yehova akukuyembekezelani mwacidwi kuti mubwelele, ndipo adzakulandilani na manja aŵili.

NYIMBO 103 Abusa ni Mphatso za Amuna

^ ndime 5 Yehova amafuna kuti Akhristu amene analeka kusonkhana na kulalikila abwelela kwa iye. Pali zambili zimene tingacite kuti tithandize ozilala amene amafuna kulabadila ciitano ca Yehova cakuti: “Bwelelani kwa ine.” M’nkhani ino, tikambilana mmene tingawathandizile kubwelela kwa Yehova.

^ ndime 7 Maina ena asinthidwa.

^ ndime 68 MAWU OFOTOKOZELA ZITHUNZI: Abale atatu osiyana-siyana akuthandiza m’bale wozilala amene afuna kubwelela kwa Yehova. Akumuthandiza mwa kum’tumilako foni, kum’citila zinthu zoonetsa kuti amam’konda, komanso kumumvetsela mokoma mtima.