Mafunso Ocokela kwa Oŵelenga
Kodi makhalidwe ochulidwa pa Agalatiya 5:22, 23 ndiwo okha “amene mzimu woyela umatulutsa”?
Lemba la Agalatiya 5:22, 23 limachula makhalidwe 9 abwino. Limati: “Makhalidwe amene mzimu woyela umatulutsa ndiwo cikondi, cimwemwe, mtendele, kuleza mtima, kukoma mtima, ubwino, cikhulupililo, kufatsa ndi kudziletsa.” Koma sitiyenela kuganiza kuti awa ni makhalidwe okhawo abwino amene mzimu wa Mulungu umatithandiza kukhala nawo.
Tidziŵa bwanji zimenezi? Onani zimene mtumwi Paulo anakamba akalibe kuchula makhalidwe amene mzimu woyela umabala. Anati: “Nchito za thupi . . . ndizo dama, zinthu zodetsa, khalidwe lotayilila, kupembedza mafano, kucita zamizimu, udani, ndewu, nsanje, kupsa mtima, mikangano, kugawikana, magulu ampatuko, kaduka, kumwa mwaucidakwa, maphwando aphokoso, ndi zina zotelo.” (Agal. 5:19-21) Pa lembali, Paulo anatsiliza na mawu akuti “ndi zina zotelo.” Izi zionetsa kuti iye akanachulanso makhalidwe ena amene ni “nchito zathupi,” monga amene apezeka pa Akolose 3:5. Mofananamo, Paulo atachula makhalidwe 9 abwino pa Agalatiya 5:22, 23, anatsiliza na mawu akuti: “Palibe lamulo loletsa zinthu zotelezi.” Conco, iye sanachule makhalidwe onse abwino amene tingakhale nawo mothandizidwa na mzimu woyela.
Tingamvetsenso bwino mfundo imeneyi tikafananitsa makhalidwe amene mzimu umabala na zipatso za kuwala zimene Paulo anachula polembela mpingo wa ku Efeso. Iye anati: “Zipatso za kuwala ndizo ciliconse cabwino ndi ciliconse colungama ndi coona.” (Aef. 5:8, 9) Pa lembali, makhalidwe a ‘cilungamo ndi coonadi’ akuchulidwa monga zipatso za kuwala pamodzi na “ciliconse cabwino” kapena kuti khalidwe la ubwino, limene ni cipatso ca mzimu. Izi zionetsa kuti ngakhale kuti pa Agalatiya 5:22, 23, Paulo sanachulepo makhalidwe a ‘cilungamo ndi coonadi’ monga mbali ya cipatso ca mzimu, akanafuna sembe anawachula.
Mofananamo, Paulo analimbikitsa Timoteyo kutsatila makhalidwe 6 abwino awa: “Cilungamo, kudzipeleka kwa Mulungu, cikhulupililo, cikondi, cipililo, ndi kufatsa.” (1 Tim. 6:11) Pa makhalidwe amenewa, ni atatu okha (cikhulupililo, cikondi, na kufatsa) amene anachulidwa monga mbali ya “makhalidwe amene mzimu woyela” umabala. Koma n’zoonekelatu kuti Timoteyo anafunikanso thandizo la mzimu woyela kuti akulitse makhalidwe enawo, omwe ni cilungamo, kudzipeleka kwa Mulungu, na kupilila.—Yelekezelani na Akolose 3:12; 2 Petulo 1:5-7.
Conco, lemba la Agalatiya 5:22, 23 silichula makhalidwe onse amene mzimu woyela umabala. N’zoona kuti mzimu wa Mulungu ungatithandize kukulitsa makhalidwe 9 ochulidwa pa lembali. Koma palinso makhalidwe ena amene tiyenela kukhala nawo kuti tikule kuuzimu na “kuvala umunthu watsopano umene unalengedwa mogwilizana ndi cifunilo ca Mulungu.”—Aef. 4:24.