NKHANI YOPHUNZILA 9
NYIMBO 75 ’Ine Nilipo, N’tumizeni!’
Kodi Ndinu Wokonzeka Kudzipatulila kwa Yehova?
“Yehova ndidzamubwezela ciyani pa zabwino zonse zimene wandicitila?”—SAL. 116:12.
ZOFUNIKA KUMVETSETSA
Nkhani ino idzakuthandizani kulimbitsa ubale wanu na Yehova, kotelo kuti mukhale na cifuno codzipatulilia kwa iye na kubatizika.
1-2. Kodi munthu ayenela kucita ciyani asanabatizike?
PA ZAKA 5 zapitazo, anthu opitilila 1 miliyoni abatizika na kukhala Mboni za Yehova. Ambili a iwo anaphunzila coonadi kuyambila ali makanda monga zinalili na Timoteyo, wophunzila wa m’zaka za zana loyamba. (2 Tim. 3:14, 15) Ena anaphunzila za Yehova atakula kale, ndipo ena mu ukalamba. Pa nthawi ina, mayi wina anaphunzila Baibo na Mboni za Yehova na kubatizika ali na zaka 97!
2 Ngati mumaphunzila Baibo na Mboni za Yehova, kapena ndinu mwana wa Mboni, kodi mukuganizila zobatizika? Ici n’colinga cabwino! Koma musanabatizike, mufunika kudzipatulila kwa Yehova. Nkhani ino ifotokoza zimene kudzipatulila kumatanthauza kwenikweni. Ikuthandizaninso kuona cifukwa cake simuyenela kudodoma kutenga sitepe imeneyi kuti mukabatizike mukakhala wokonzeka.
KODI KUDZIPATULILA N’CIYANI?
3. Fotokozani zitsanzo za anthu omwe anali odzipatulila kwa Yehova.
3 M’Baibo, kudzipatulila kumatanthauza kudzipeleka mwapadela kuti ucite utumiki wopatulika. Aisiraeli anali mtundu wodzipatulila kwa Yehova. Koma anthu ena mu mtunduwo anali kudzipatulila mwapadela kwa Yehova. Mwacitsanzo, Aroni anali kumvala “cizindikilo copatulika ca kudzipeleka”—comwe cinali kacitsulo konyezimila kagolide patsogolo pa nduwila. Kacitsulo konyezimila kagolide kameneko, kanali cizindikilo cakuti iye anapatulidwa kuti atumikile mwapadela—monga mkulu wa ansembe mu Isiraeli. (Lev. 8:9) Nawonso Anaziri anali odzipatulila kwa Yehova mwapadela. Liwu lakuti “Mnazili,” linacokele ku liwu la Ciheberi lakuti nazirʹ, limene limatanthauza “Wopatulidwa,” kapena “Wodzipeleka Mwapadela.” Anazili sanali kucita zinthu zina zake malinga na Cilamulo ca Mose.—Num. 6:2-8.
4. (a) Kodi amene amadzipatulila kwa Yehova amakhala apadela m’lingalilo lotani? (b) Kodi “kudzikana” kutanthauza ciyani? (Onaninso cithunzi.)
4 Mukadzipatulila kwa Yehova, mumasankha kukhala wophunzila wa Yesu Khristu, ndipo kucita cifunilo ca Yehova kumakhala kofunika kwambili pa umoyo wanu. Kodi kudzipatulila kuti mukhale Mkhristu kumafuna kuti mucite ciyani? Yesu anati: “Ngati munthu akufuna kunditsatila, adzikane yekha.” (Mat. 16:24) Monga mtumiki wodzipatulila wa Yehova, kanani kucita ciliconse cosagwilizana na cifunilo ca Yehova. (2 Akor. 5:14, 15) Izi ziphatikizapo kukana “nchito za thupi,” monga ciwelewele. (Agal. 5:19-21; 1 Akor. 6:18) Kodi kutsatila malamulo ngati amenewa kungapangitse umoyo wanu kukhala wosasangalatsa? Sizingakhale telo ngati mumakonda Yehova, komanso ngati mumavomeleza kuti colinga ca malamulo akewo n’cakuti akupindulileni. (Sal. 119:97; Yes. 48:17, 18) M’bale wina dzina lake Nicholas anafotokoza motele: “Mungaone malamulo a Yehova ngati mipilingidzo ya ndende yokuphelani ufulu wocita zomwe mungafune, kapena ngati mipilingidzo yokutetezani ya chinga la mikango yolusa.”
5. (a) Kodi mungadzipatulile motani kwa Yehova? (b) Kodi pali kusiyana kotani pakati pa kudzipatulila na ubatizo? (Onaninso cithunzi.)
5 Kodi mungadzipatulile motani kwa Yehova? Mwa kum’lonjeza kupitila m’pemphelo kuti mudzalambila iye yekha na kutsogoza cifunilo cake mu umoyo wanu. Kwenikweni mumalonjeza Yehova kuti mudzapitiliza kumukonda ‘ndi mtima wanu wonse, moyo wanu wonse, maganizo anu wonse, ndi mphamvu zanu zonse.’ (Maliko 12:30) Kudzipatulila kumacitika mseli pakati pa inu na Yehova. Mosiyana na zimenezi, ubatizo umacitika poyela pamaso pa anthu; kuwaonetsa kuti munadzipatulila. Kudzipatulila ni lumbilo lopatulika limene mumafuna kulikwanilitsa, ndipo n’zimene Yehova amayembekezela.—Mlal. 5:4, 5.
N’CIFUKWA CIYANI MUYENELA KUDZIPATULILA KWA YEHOVA?
6. N’ciyani cimakolezela munthu kuti adzipatulile kwa Yehova?
6 Cifukwa cacikulu cimene muyenela kudzipatulila kwa Yehova, n’cakuti mumam’konda. Cikondi canu sicidalila mmene mukumvela basi, koma cimatsamila pa kudziŵa zinthu molondola, komanso ‘kumvetsetsa zinthu zauzimu’—zinthu zomwe munaphunzila zokhudza Yehova zomwe zinacititsa kuti cikondi canu pa iye cikule. (Akol. 1:9) Kuphunzila kwanu Malemba kwakukhutilitsani kuti (1) Yehova ni weniweni, (2) Baibo ni Mawu ake ouzilidwa, ndiponso (3) iye amagwilitsa nchito gulu lake pokwanilitsa cifunilo cake.
7. Kodi tiyenela kucita ciyani tisanadzipatulile kwa Mulungu?
7 Amene amadzipatulila kwa Yehova ayenela kudziŵa ziphunzitso zoyambilila za m’Baibo, ndipo ayenela kutsatila miyeso ya Yehova pa umoyo wawo. Amauzako ena za cikhulupililo cawo malinga na mmene zinthu zilili pa umoyo wawo. (Mat. 28:19, 20) Cikondi cawo pa Yehova cakula ndipo ali na mtima wofunitsitsa kudzipeleka kwa iye kwathunthu. Kodi si mmenenso zilili kwa inu? Mukakhala na cikondi cotelo, simudzadzipatulila kungofuna kukondweletsa wokuphunzitsani Baibo kapena makolo anu; kapenanso kungotengela mabwenzi anu.
8. Kodi kuyamikila kungakuthandizeni bwanji popanga cisankho codzipatulila kwa Yehova? (Salimo 116:12-14)
8 Cisankho codzipatulila kwa Yehova sicikhala covuta kupanga mukaganizila pa zonse zimene wakucitilani. (Ŵelengani Salimo 116:12-14.) Moyenela Baibo imacha Yehova Mpatsi wa “mphatso iliyonse yabwino ndi yangwilo.” (Yak. 1:17) Mphatso yaikulu pa zonse ni nsembe ya Mwana wake, Yesu. Tangoganizani, dipo limapangitsa kuti cikhale cotheka kukhala pa ubale wabwino na Yehova. Ndipo wakupatsani ciyembekezo codzakhala na moyo kwamuyaya. (1 Yoh. 4:9, 10, 19) Kudzipatulila kwanu kwa Yehova ni njila yabwino zedi yoonetsela kuyamikila kwanu cikondi copambana cimene iye anakuonetsani, kuphatikizaponso madalitso ena amene iye wakukonzelani. (Deut. 16:17; 2 Akor. 5:15) Mfundo imeneyi inafotokozedwa bwino mu phunzilo 46 pa mfundo 4, m’buku la Kondwelani Na Moyo Kwamuyaya! Ndipo iphatikizapo vidiyo ya mphindi zitatu ya mutu wakuti Kupeleka Mphatso Kwa Mulungu.
KODI NDINU WOKONZEKA KUDZIPATULILA KUTI MUKABATIZIKE?
9. N’cifukwa ciyani munthu sayenela kumva kukakamizika popanga cisankho ca kudzipatulila?
9 Mwina mumaona kuti sindinu wokonzeka kudzipatulila na kubatizika. Mwina mufunikilabe kupanga masinthidwe mu umoyo wanu kuti ukhale wogwilizana na miyeso ya Yehova, kapena mufunikilabe nthawi kuti mulimbitse cikhulupililo canu. (Akol. 2:6, 7) Ophunzila sapita patsogolo mofanana, ndipo acicepele sakhala okonzeka kudzipatulila na kubatizidwa pa msinkhu wofanana. Yesani kudziunika kuti muone mmene mukupitila patsogolo mwauzimu malinga na zomwe mungakwanitse kucita, osati modziyelekezela na munthu wina.—Agal. 6:4, 5.
10. Muyenela kucita ciyani ngati pali pano mwaona kuti sindinu wokonzeka kudzipatulila na kubatizidwa? (Onaninso danga lakuti “ Kwa Amene Akuleledwa m’Banja la Mboni.”)
10 Ngakhale kuti pali pano muona kuti sindinu wokonzeka kudzipatulila kwa Yehova, pitilizani kupanga sitepe imeneyi kukhala colinga canu. Pemphani Yehova kuti adalitse khama lanu pomwe mukupanga masinthidwe ofunikila. (Afil. 2:13; 3:16) Khalani wotsimikiza kuti iye adzamva pemphelo lanu na kuliyankha.—1 Yoh. 5:14.
CIFUKWA CAKE ENA AMADODOMA
11. Kodi Yehova adzatithandize motani kuti tikhalebe okhulupilika kwa iye?
11 Ngakhale kuti ena amakhala okonzeka kudzipatulila na kubatizidwa, amazengeleza. Angakhale na nkhawa yakuti, ‘Bwanji ngati pambuyo pobatizika nacita chimo lalikulu na kucotsedwa mu mpingo?’ Ngati mumamva conco, musakaikile zakuti Yehova adzakupatsani zonse zofunikila kuti “muziyenda mogwilizana ndi zimene [iye] amafuna.” (Akol. 1:10) Adzakupatsaninso mphamvu yokuthandizani kucita zoyenela. Angakwanitse kucita zimenezi cifukwa anathandizapo kale ena m’mbuyomu kucita zoyenela. (1 Akor. 10:13) Ici n’cimodzi mwa zifukwa zimene zimapangitsa kuti pakhale anthu ocepa amene amacotsedwa mu mpingo wa Cikhristu. Yehova amapeleka zonse zofunikila kwa anthu ake zowathandiza kukhalabe okhulupilika.
12. N’ciyani cingatithandize kupewa kucita macimo akulu-akulu?
12 Munthu aliyense wopanda ungwilo amakhalako pa mayeselo ofuna kucita zoipa. (Yak. 1:14) Koma ufulu umakhala wanu, kusankha kucita coipaco kapena kukana. Zoona zake n’zakuti, inuyo ndinu muli na mphamvu zosankha mmene umoyo wanu udzakhalila. Ngakhale kuti anthu ena amanena kuti n’zosatheka kulamulila mmene mukumvela kapena kulamulila moyo wanu, koma n’zotheka ndithu. Mukayesedwa kuti mucite zosayenela, mungasankhe kusagonja kumayeselo amenewo. Kuti mucite zimenezi, muzipemphela tsiku lililonse, ndipo muzikhala na ndandanda yabwino yocita phunzilo la munthu mwini. Kuwonjezela apo, muzipezeka pa misonkhano ya Cikhristu nthawi zonse, ndipo muziuzako ena za cikhulupililo canu. Kucita izi nthawi zonse kudzakupatsani mphamvu zokuthandizani kusunga lumbilo la kudzipatulila kwanu. Ndipo musaiŵale kuti Yehova adzakuthandizani kucita zimenezi.—Agal. 5:16.
13. Kodi Yosefe anapeleka citsanzo cotani kwa ife?
13 Cingakhale cosavuta kusunga lumbilo lanu la kudzipatulila ngati mwasankhilatu zocita musanayang’anizane na ciyeso. Baibo imachula anthu angapo omwe anacita zimenezi ngakhale kuti anali opanda ungwilo monga ife. Mwacitsanzo, mkazi wa Potifara mobweleza-bweleza ananyengelela Yosefe kuti agone naye. Koma Yosefe anali wotsimikiza kutsatila zomwe anasankha kucita. Baibo imatiuza kuti “Yosefe anali kukana,” ndipo anati: “Ndingacitilenji coipa cacikulu conci n’kucimwila Mulungu?” (Gen. 39:8-10) N’zoonekelatu kuti Yosefe anali odziŵa kale zimene adzacita ngakhale asanayesedwe. Mwa ici, cinakhala cosavuta kwa iye kugonjetsa mayeselo atakumana nawo.
14. Tingatani kuti tikane kucita zoipa?
14 Kodi mungatengele bwanji citsanzo ca Yosefe? Mwa kusankhilatu pali pano zimene mudzacita mukakumana na mayeselo. Phunzilani kukaniza mwamsanga zinthu zimene Yehova amadana nazo ngakhale kupewa kuziganizila. (Sal. 97:10; 119:165) Mwa kutelo, simudzagonja mukayesedwa. Mudzakhala mutadziŵilatu zocita mayeselo akakupezani.
15. Kodi munthu angaonetse bwanji kuti amafuna-funa Yehova na mtima wonse? (Aheberi 11:6)
15 Pa inu nokha, mungakhale wotsimikiza kuti munapeza coonadi, ndipo mukufunitsitsa kutumikila Yehova na mtima wanu wonse. Ngakhale n’telo, mungakhalebe na cina cake comwe cingakulepheletseni kudzipatulila na kubatizika. Ngati n’conco, mungatengele citsanzo ca Mfumu Davide. Mungamucondelele Yehova kuti “Ndifufuzeni, inu Mulungu, ndi kudziwa mtima wanga. Ndisanthuleni ndi kudziŵa malingalilo anga amene akundisowetsa mtendele, ndipo muone ngati mwa ine muli ciliconse cimene cikundicititsa kuyenda m’njila yoipa, ndipo munditsogolele m’njila yamuyaya.” (Sal. 139:23, 24) Yehova amadalitsa “anthu omufunafuna ndi mtima wonse.” Kulimbikila kwanu kuti mukwanilitse colinga ca kudzipatulila na kubatizika cimaonetsa kuti mumamufuna-funa na mtima wonse.—Ŵelengani Aheberi 11:6.
PITILIZANI KUMUYANDIKILA YEHOVA
16-17. Kodi amene akuleledwa m’banja la Mboni ayenela kucita ciyani kuti Yehova awakoke? (Yohane 6:44)
16 Yesu anakamba kuti Yehova ndiye amakoka anthu kukhala ophunzila ake. (Ŵelengani Yohane 6:44.) Ganizilani mawu olimbikitsa amenewa na kuganizila zimene amatanthauza kwa inu. Yehova amaona zabwino mwa munthu aliyense amene amakokedwela kwa iye. Iye amaona munthuyo kukhala “cuma cake capadela.” (Deut. 7:6) Umu ni mmenenso amakuonelani.
17 Mwina ndinu wacicepele, ndipo makolo anu ni Mboni za Yehova. Mwina mungaganize kuti mumatumikila Yehova cabe cifukwa makolo anu amacita zimenezo, osati cifukwa cakuti Yehova anakukokelani kwa iye. Mulimonsemo, Baibo imatiuza kuti: “Yandikilani Mulungu, ndipo iyenso adzakuyandikilani.” (Yak. 4:8; 1 Mbiri 28:9) Ngati mwayamba ndinu kumuyandikila Yehova, iyenso adzacitapo kanthu mwa kukuyandikilani. Yehova samangokuonelani m’gulu la anthu ake. Amakoka munthu aliyense payekha-payekha—kuphatikizapo amene akuleledwa m’banja la Mboni. Ngati munthuyo wacitapo kanthu kuti ayandikile Yehova, nayenso amamuyandikila monga taonela pa Yakobo 4:8.—Yelekezelani na 2 Atesalonika 2:13.
18. Tidzakambilane ciyani m’nkhani yotsatila? (Salimo 40:8)
18 Mukadzipatulila kwa Yehova na kubatizika, mumatengela citsanzo ca Yesu. Iye anadzipeleka kucita zonse zimene Atate wake anamuuza kucita. (Ŵelengani Salimo 40:8; Aheb. 10:7) M’nkhani yotsatila tidzakambilana zomwe zingakuthandizeni kuti musaleke kutumikila Yehova mokhulupilika pambuyo pa ubatizo wanu.
KODI MUNGAYANKHE BWANJI?
-
Kodi kudzipatulila kwa Yehova kutanthauza ciyani?
-
Kodi kukhala woyamikila kungakuthandizeni bwanji kudzipatulila?
-
N’ciyani cingakuthandizeni kupewa macimo aakulu?
NYIMBO 38 Adzakulimbitsa