Kodi Baibulo Likusinthabe Umoyo Wanu?
“Sandulikani mwa kusintha maganizo anu.” —AROMA 12:2.
1-3. (a) Ndi zinthu ziti zimene zingativute kusintha pambuyo pa ubatizo? (b) Ndi mafunso ati amene tingadzifunse ngati tikulephela kusintha zinthu zina zimene siticita bwino? (Onani cithunzi pamwambapa.)
KWA zaka zambili, Kevin anali kuchova njuga, kukoka fodya, kuledzela, ndi kuseŵenzetsa mankhwala osokoneza ubongo. [1] (Onani mau akumapeto.) Pambuyo pake anaphunzila za Yehova ndipo anafuna kukhala bwenzi lake. Koma kuti acite zimenezo, anafunika kupanga masinthidwe aakulu pa umoyo wake. Iye anasintha mothandizidwa ndi Yehova ndiponso mphamvu ya Mau a Mulungu, Baibulo.—Aheberi 4:12.
2 Ngakhale pambuyo pobatizidwa, Kevin anafunika kupitiliza kusintha umunthu wake kuti akhale Mkristu wabwino. (Aefeso 4:31, 32) Mwacitsanzo, anali kukwiya msanga. Iye anadadwa atadziŵa kuti n’covuta kwambili kulamulila mkwiyo wake. Kevin anakamba kuti kulamulila mkwiyo wake kunali kovuta kwambili kuposa kusintha zizolowezi zoipa zimene anali nazo asabatizidwe.Koma anakwanitsa kusintha cifukwa ca thandizo la Yehova ndiponso cifukwa coŵelenga Baibulo mwakhama.
3 Tisanabatizidwe, ambili a ife tinafunika kusintha umoyo wathu kuti tizicita zimene Baibulo limakamba. Koma ngakhale tsopano timadziŵa kuti pali mbali zina zing’onozing’ono zimene tifunika kusintha kuti titengele Mulungu ndi Kristu. (Aefeso 5:1, 2; 1 Petulo 2:21) Mwacitsanzo, mwina timakonda kudandaula kapena kunena anthu ena. Mwina nthawi zina cifukwa coopa zimene anthu ena angaganize ndi kukamba, mumalephela kucita zoyenela. N’kutheka kuti kwa zaka zambili mwakhala mukuyesetsa kuti musinthe, koma mwalephela. Mungayambe kudzifunsa kuti: ‘N’cifukwa ciani zimandivuta kusintha zinthu zing’onozing’ono zimenezi? Ndingacite ciani kuti ndizicita zimene Baibulo limakamba ndi kupitiliza kusintha umunthu wanga?’
N’ZOTHEKA KUKONDWELETSA YEHOVA
4. N’cifukwa ciani nthawi zina timalephela kukondweletsa Yehova?
4 Timakonda Yehova ndipo timafuna kum’kondweletsa. Koma n’zacisoni kuti nthawi zina timalephela kum’kondweletsa cifukwa ndife opanda ungwilo. Nthawi zambili timamva mofanana ndi mtumwi Paulo amene anakamba kuti: “Ndimafuna kucita zabwino, koma sinditha kuzicita.”—Aroma 7:18; Yakobo 3:2.
5. Ndi zinthu ziti zimene tinasintha tikalibe kubatizika? Nanga ndi zofooka ziti zimene tingakhale tikulimbana nazo mpaka pano?
5 Tisanakhale Mboni, tinafunika kuleka kucita zinthu zimene Yehova amadana nazo. (1 Akorinto 6:9, 10) Komabe, tikali opanda ungwilo. (Akolose 3:9, 10) Conco, nthawi zina timalakwitsabe ngakhale kuti takhala Mboni kwa zaka zambili. Nthawi ndi nthawi, timakhala ndi zilakolako zoipa, kapena timavutika kuthetsa cofooka cinacake cimene tili naco. Mwina takhala tikulimbana ndi cofooka cimeneco kwa zaka zambili.
6, 7. (a) N’ciani cimacititsa kuti tikhale paubwenzi wabwino ndi Yehova ngakhale kuti ndife opanda ungwilo? (b) N’cifukwa ciani sitiyenela kuopa kupempha Yehova kuti atikhululukile?
6 Ngakhale kuti ndife opanda ungwilo, tikhoza kukhala paubwenzi ndi Yehova ndiponso kum’tumikila. Muzikumbukila mmene munakhalila bwenzi la Yehova. Iye ndi amene anaona zabwino mwa inu ndipo anafuna kuti mum’dziŵe. (Yohane 6:44) Iye anali kudziŵa kuti muli ndi zofooka ndipo nthawi zina mudzalakwitsa. Koma Yehova anafunabe kuti mukhale bwenzi lake.
7 Yehova anatikonda kwambili cakuti anatipatsa mphatso yamtengo wapatali. Iye anatumiza Mwana wake, Yesu, padziko kuti apeleke moyo wake kukhala dipo la macimo athu. (Yohane 3:16) Tikalakwa, tiyenela kupempha Yehova kuti atikhululukile. Cifukwa ca dipo limeneli, timakhala otsimikiza kuti iye adzatikhululukila ndipo tidzapitilizabe kukhala mabwenzi ake. (Aroma 7:24, 25; 1 Yohane 2:1, 2) Kumbukilani kuti Yesu anafela anthu olapa. Conco, ngakhale tikuona kuti tinacita colakwa cacikulu, sitiyenela kuleka kupempha Yehova kuti atikhululukile. Ngati sitim’pempha kuti atikhululukile, zingafanane ndi munthu amene akukana kusamba m’manja kuti acotse dothi. Timayamikila kwambili Yehova cifukwa copanga makonzedwe akuti zikhale zotheka kukhala mabwenzi ake ngakhale kuti ndife opanda ungwilo.—Ŵelengani 1 Timoteyo 1:15.
Ngati tifuna kuyandikila Yehova, tiyenela kuyesetsa kupitiliza kutengela iye ndi Mwana wake
8. N’cifukwa ciani sitifunika kunyalanyaza zofooka zathu?
8 Sitiyenela kunyalanyaza zofooka zathu kapena kupeza zifukwa zodzikhululukila nthawi zonse. Yehova watiuza zimene tifunika kucita kuti tikhale mabwenzi ake. (Salimo 15:1-5) Conco, ngati tifuna kuyandikila Mulungu, tiyenela kuyesetsa kutengela iye ndi Mwana wake. Tiyenelanso kuyesetsa kulimbana ndi maganizo olakwika kapena kuwathetselatu. Kaya takhala Mboni kwa utali wotani, tiyenela kupitilizabe kusintha umunthu wathu.—2 Akorinto 13:11.
9. Tidziŵa bwanji kuti kuvala umunthu watsopano ndi cinthu cimene tifunika kucita nthawi zonse?
9 Mtumwi Paulo anauza Akristu kuti: “Muvule umunthu wakale umene umagwilizana ndi khalidwe lanu lakale, umenenso ukuipitsidwa malinga ndi zilakolako zonyenga za umunthuwo. Ndipo munaphunzitsidwa kuti mukhale atsopano mu mphamvu yoyendetsa maganizo anu, ndi kuvala umunthu watsopano umene unalengedwa mogwilizana ndi cifunilo ca Mulungu ndipo umatsatila zofunika pa cilungamo ceniceni ndi pa kukhulupilika.” (Aefeso 4: 22- 24) Izi zitanthauza kuti tiyenela kupitilizabe kusintha ndi “kuvala umunthu watsopano.” Conco, kaya takhala tikutumikila Yehova kwa zaka zingati, pali zinthu zina zambili zimene tingaphunzile zokhudza makhalidwe ake. Baibulo lingatithandize kupitiliza kusintha umunthu wathu kuti titengele Mulungu.
N’CIFUKWA CIANI KUVALA UMUNTHU WATSOPANO KUMAKHALA KOVUTA?
10. Kodi tifunika kucita ciani kuti Baibulo litithandize kusintha umunthu wathu? Nanga tingadzifunse mafunso ati?
10 Tonse timafuna kucita zimene Baibulo limakamba. Koma timafunika kucita khama kuti tipitilizebe kusintha umunthu wathu. N’cifukwa ciani tifunika kucita khama mwa njila imeneyi? N’cifukwa ciani Yehova amalola kuti tizilimbana ndi zofooka?
11-13. N’cifukwa ciani Yehova amafuna kuti tiziyesetsa kulimbana ndi zofooka zathu?
11 Tikaganizila za cilengedwe ndi zonse zili mmenemo, sitikaikila kuti Yehova ali ndi mphamvu zocita ciliconse. Mwacitsanzo, iye anapanga dzuŵa, limene ndi lamphamvu kwambili. Pa sekondi iliyonse, dzuŵa limatulutsa kuwala ndi kutentha kwakukulu. Koma ndi mphamvu yocepa cabe yocoka ku dzuŵa imene imafunika kuti zamoyo zikhalepo pano padziko lapansi. (Salimo 74:16; Yesaya 40:26) Yehova amapelekanso mphamvu kwa atumiki ake a pa dziko pamene akufunikila thandizo. (Yesaya 40:29) N’zoonekelatu kuti Yehova akanafuna, akanacititsa kuti tisamavutike ngakhale pang’ono polimbana ndi zofooka zathu. Akanacititsanso kuti tileke kukhala ndi zilakolako zoipa. Koma n’cifukwa ciani iye sacita zimenezi?
12 Yehova watipatsa ufulu wosankha. Iye watilola kudzisankhila kaya kumumvela kapena ai. Tikasankha kumumvela ndi kucita cifunilo cake, timaonetsa kuti timam’konda ndipo tifuna kum’kondweletsa. Satana amakamba kuti Yehova si woyenela kutilamulila. Koma tikamvela Yehova timaonetsa kuti tikufuna kuti iye azitilamulila. Ndipo tingakhale otsimikiza kuti Atate wathu wacikondi amayamikila kuyesayesa kwathu kuti timumvele. (Yobu 2:3-5; Miyambo 27:11) Tikamayesetsa kuongolela zofooka zathu ngakhale kuti n’zovuta, timaonetsa kuti ndife okhulupilika kwa Yehova ndiponso kuti tifuna kuti iye azitilamulila.
13 Yehova amatiuza kuti tifunika kucita khama kuti titengele makhalidwe ake. (Akolose 3:12; ŵelengani 2 Petulo 1: 5-7.) Iye amafunanso kuti tiziyesetsa kulamulila maganizo athu ndi mmene timamvelela. (Aroma 8:5; 12:9) Tikakwanitsa kusintha cifukwa cocita khama, timakhala osangalala kwambili.
LOLANI KUTI MAU A MULUNGU APITILIZE KUKUSINTHANI
14, 15. Kodi tingacite ciani kuti tikhale ndi makhalidwe amene Mulungu amakondwela nawo? (Onani bokosi lakuti “ Baibulo ndi Pemphelo Zinasintha Umoyo Wao.”)
14 Tingacite ciani kuti tikhale ndi makhalidwe abwino ngati amene Yehova ali nao? M’malo modzisankhila zimene Aroma 12:2 limati: “Musamatengele nzelu za nthawi ino, koma sandulikani mwa kusintha maganizo anu, kuti muzindikile cimene cili cifunilo ca Mulungu, cabwino, covomelezeka ndi cangwilo.” Conco, kuti tidziŵe zimene Yehova amafuna, tiyenela kudalila thandizo limene watipatsa. Tifunika kuŵelenga Baibulo tsiku lililonse, kusinkhasinkha pa zimene taŵelenga, ndi kupempha Yehova kuti atipatse mzimu wake woyela. (Luka 11:13; Agalatiya 5:22, 23) Tikamacita zimenezi, Yehova adzatithandiza kudziŵa zimene zimam’kondweletsa ndipo tidzayamba kuona zinthu mmene iye amazionela. Zotsatila zake n’zakuti zimene timaganiza, kukamba, ndi kucita, zidzakhala zokondweletsa Yehova ndipo tidzaphunzila kulimbana ndi zofooka zathu. Komabe, sitiyenela kuleka kulimbana ndi zofooka zathu.—Miyambo 4:23.
tifuna kusintha, tifunika kulola Mulungu kutitsogolela. Lemba la15 Kuonjezela pa kuŵelenga Baibulo tsiku lililonse, tifunika kuliphunzila pogwilitsila nchito zofalitsa zathu monga Nsanja ya Mlonda ndi Galamukani. Nkhani zambili zopezeka m’magazini amenewa, zimatiphunzitsa mmene tingatengele makhalidwe a Yehova ndi zimene tingacite polimbana ndi zofooka zathu. Nthawi zina tingapeze nkhani zothandiza kapena malemba amene angatilimbikitse kwambili. Tingalembe malemba amenewa penapake ndiponso tingasunge magazini amenewa kuti tiziwaŵelenga nthawi ndi nthawi.
16. N’cifukwa ciani sitiyenela kutaya mtima ngati sitikusintha mwamsanga?
Salimo 37:31; Miyambo 23:12; Agalatiya 5:16, 17.
16 Kutengela makhalidwe a Yehova kumatenga nthawi. Conco, ngati muona kuti pakali zina zimene simucita bwino, musataye mtima. Poyamba mungafunike kudzikakamiza kuti mucite zimene Baibulo limakamba. Mukamayesetsa kuganiza ndi kucita zinthu zimene Yehova amafuna, cidzakhala copepuka kwa inu kuyamba kuona zinthu mmene iye amazionela ndi kucita zinthu zoyenela.—MUZIGANIZILA ZA MADALITSO AMTSOGOLO
17. Kodi tidzapeza madalitso otani ngati tikhalabe okhulupilika kwa Yehova?
17 Tikuyembekezela mwacidwi nthawi pamene tidzakhala angwilo ndi kutumikila Yehova mpaka kalekale. Pa nthawi imeneyo, sitidzalimbana ndi cofooka ciliconse ndipo cidzakhala copepuka kutengela makhalidwe a Yehova. Koma ngakhale masiku ano, timakwanitsa kum’lambila cifukwa ca mphatso ya dipo imene watipatsa. Ngakhale kuti ndife opanda ungwilo, tingam’kondweletse ngati tipitiliza kusintha umunthu wathu ndi kucita zimene amatiphunzitsa kudzela m’Baibulo.
18, 19. Tidziŵa bwanji kuti Baibulo lili ndi mphamvu zotithandiza kusintha umunthu wathu?
18 Kevin anacita zonse zimene akanatha kuti azilamulila mkwiyo wake. Iye anali kusinkhasinkha zimene anaŵelenga m’Baibulo ndipo anacita khama kuti asinthe umunthu wake. Anatsatilanso malangizo amene Akristu anzake anam’patsa. Ngakhale kuti panapita zaka kuti Kevin asinthe, iye anasinthadi ndipo anakhala mtumiki wothandiza. Kevin wakhala akutumikila monga mkulu kwa zaka 20 tsopano. Koma amaonabe kuti ayenela kupitiliza kulimbana ndi cofooka cake.
19 Mofanana ndi Kevin, tifunika kupitilizabe kusintha umunthu wathu. Tikatelo, tidzakhala paubwenzi wolimba kwambili ndi Yehova. (Salimo 25:14) Tikamayesetsa kusintha umunthu wathu kuti tim’kondweletse, iye adzatithandiza kuti tipambane. Komanso tingakhale ndi cidalilo cakuti Baibulo lidzatithandiza kupitilizabe kusintha umunthu wathu.—Salimo 34:8.
^ [1] (ndime 1) Dzina lasinthidwa.