“Pitani Mukaphunzitse Anthu a Mitundu Yonse Kuti Akhale Ophunzila”
“Pitani mukaphunzitse anthu a mitundu yonse kuti akhale ophunzila anga, muziwabatiza . . . ,ndi kuwaphunzitsa kusunga zinthu zonse zimene ndinakulamulilani.”—MATEYU 28:19, 20.
1, 2. Kodi mau a Yesu a pa Mateyu 24:14 amayambitsa mafunso otani?
YESU anakambilatu kuti m’masiku otsiliza uthenga wabwino wa Ufumu udzalalikidwa kwa anthu onse. (Mateyu 24:14) Ife Mboni za Yehova, timadziŵika padziko lonse cifukwa ca nchito yathu yolalikila. Anthu ena amamvetsela uthenga wathu koma ena samvetsela. Komabe, ngakhale anthu amene samvetsela uthenga wathu amatilemekeza cifukwa ca nchito imeneyi. Ife ndife amene timacita nchito imene Yesu analosela. N’cifukwa ciani takamba zimenezi? Nanga tingatsimikize bwanji kuti nchito yathu yolalikila ikukwanilitsa zimene Yesu anakamba?
2 Anthu a m’zipembedzo zambili amakamba kuti amalalikila uthenga wa Yesu. Komabe, io amangolalikila m’chalichi, pa TV, kapena pa Intaneti, mwinanso amangouza ena mmene anaphunzilila za Yesu. Ena amaganiza kuti akamathandiza anthu osauka kapena kugwila nchito yothandiza anthu monga udokotala, unesi kapena uphunzitsi ndiye kuti akulalikila. Koma kodi kucita zimenezi ndiye kulalikila kumene Yesu anali kukamba?
3. Mogwilizana ndi lemba la Mateyu 28:19, 20, kodi otsatila a Yesu ayenela kucita zinthu zinai ziti?
Mateyu 28:19, 20) Conco, monga otsatila a Yesu, tifunika kucita zinthu zinai izi: Tiyenela kupanga ophunzila, kuwaphunzitsa, ndi kuwabatiza. Koma coyambilila tiyenela kupita kukalalikila kwa anthuwo. Katswili wina wa Baibulo anati: “Mkristu aliyense ali ndi udindo ‘wopita’ kukalalikila, kaya ndi pafupi kapena kutali.”—Mateyu 10:7; Luka 10:3.
3 Kodi Yesu anauza ophunzila ake kuti aziyembekeza anthu kubwela kwa io? Iyai. Yesu ataukitsidwa, anauza khamu la otsatila ake kuti: “Pitani mukaphunzitse anthu a mitundu yonse kuti akhale ophunzila anga, muziwabatiza . . . , ndi kuwaphunzitsa kusunga zinthu zonse zimene ndinakulamulilani.” (4. Kodi kukhala “asodzi a anthu” kumafuna ciani?
4 Kodi Yesu anafuna kuti ophunzila ake azicita ciani? Kodi anafuna kuti aliyense azilalikila payekhapayekha kapena monga gulu logwilizana? Popeza n’zosatheka munthu mmodzi kulalikila ku “mitundu yonse,” ophunzila ake anayenela kukhala gulu locitila zinthu pamodzi. Izi n’zimene Yesu anatanthauza pamene anauza ophunzila ake kuti akhale “asodzi a anthu.” (Ŵelengani Mateyu 4:18-22.) Yesu sanali kukamba za msodzi mmodzi amene amagwilitsila nchito mbedza ndi nyambo kuti akole nsomba. M’malomwake, anali kukamba za kukola nsomba pogwilitsila nchito maneti. Kugwila nsomba ndi neti kumafuna mphamvu, mgwilizano ndiponso anthu ambili.—Luka 5:1-11.
5. Ndi mafunso anai ati amene tifunika kuyankha? Nanga n’cifukwa ciani?
5 Kuti tidziŵe amene akugwila nchito yolalikila masiku ano, tiyenela kuyankha mafunso anai awa:
-
Ndi uthenga wotani umene otsatila a Yesu ayenela kulalikila?
-
Kodi ayenela kukhala ndi colinga cotani?
-
Ndi njila ziti zimene ayenela kuseŵenzetsa?
-
Kodi afunika kugwila nchito imeneyi pa mlingo wotani? Nanga kufikila liti?
Mayankho a mafunso amenewa atithandiza kudziŵa amene akucita nchito yopulumutsa moyo imeneyi, ndiponso atilimbikitsa kuti tipitilize kulalikila.—1 Timoteyo 4:16.
NDI UTHENGA WOTANI UMENE UYENELA KULALIKIDWA?
6. N’cifukwa ciani tingakambe kuti Mboni za Yehova zimalalikila uthenga woyenela?
6 Ŵelengani Luka 4:43. Yesu anali kulalikila “uthenga wabwino wa Ufumu,” ndipo afuna kuti ophunzila ake azicita cimodzimodzi. Kodi ndi gulu liti limene limalalikila uthenga umenewo kwa anthu onse? Ndi Mboni za Yehova zokha. Ngakhale anthu amene amatizonda amavomeleza zimenezi. Mwacitsanzo, mvelani zimene wansembe wina amene anakhalako m’maiko osiyanasiyana anauza Mboni za Yehova. M’dziko lililonse, wansembeyo anafunsa Mboni za Yehova kuti, ‘Kodi mukulalikila uthenga wotani?’ Pambuyo pa kumva mayankho ao, wansembeyo anati, “Onse ndi opusa, anapeleka yankho lofanana lakuti ‘Tikulalikila Uthenga wabwino wa Ufumu.’” Zokamba za wansembeyo zionetsa kuti sindife opusa koma kuti ndife ogwilizana monga Akristu oona. (1 Akorinto 1: 10) Uthenga waukulu umene umapezeka m’magazini yakuti Nsanja ya Mlonda, Imalengeza za Ufumu wa Yehova, ndi wonena za Ufumu wa Mulungu. Magazini imeneyi ikupezeka m’zinenelo 254 ndipo makope pafupifupi 59,000,000 amasindikizidwa mwezi uliwonse. Izi zacititsa kuti ikhale magazini imene ikufalitsidwa kwambili padziko lonse.
Ndi Mboni za Yehova zokha zimene zimalalikila uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu
7. Tidziŵa bwanji kuti atsogoleli a machalichi acikristu salalikila uthenga woyenela?
7 Abusa a machalichi acikristu salalikila za Ufumu wa Mulungu. Ngati akamba za Ufumu, ambili a io amangokamba kuti Ufumu uli mumtima mwa munthu. (Luka 17:21) Iwo saphunzitsa anthu zakuti Ufumu umenewo ndi boma lakumwamba lolamulidwa ndi Yesu. M’malomwake, amakumbuka Yesu panthawi ya Krisimasi ndi Isitala basi. Iwo saphunzitsa zakuti Ufumu wa Mulungu udzathetsa mavuto onse a anthu ndi kuti posacedwapa udzacotsa zoipa zonse padziko lapansi. (Chivumbulutso 19:11- 21) Kukamba zoona, atsogoleli a machalichi acikristu sadziŵa zimene Yesu adzacita monga Mfumu ya Ufumu wa Mulungu. Ndipo cifukwa cakuti sadziŵa uthenga wa Yesu, samvetsetsa cifukwa cake ayenela kulalikila.
KODI TIFUNIKA KUKHALA NDI COLINGA COTANI POGWILA NCHITO IMENEYI?
8. Ndi colinga coipa citi cimene anthu ena amakhala naco pogwila nchito yolalikila?
8 Ophunzila a Yesu sayenela kulalikila n’colinga copeza ndalama kapena kumanga nyumba zapamwamba. Yesu anati: “Munalandila kwaulele, patsani kwaulele.” (Mateyu 10:8) Conco, nchito yolalikila siyenela kukhala bizinesi. (2 Akorinto 2:17) Ophunzila a Yesu sayenela kuuza anthu kuti awalipile cifukwa ca nchito yao yolalikila. (Ŵelengani Machitidwe 20:33-35.) Ngakhale kuti malangizo a Yesu ndi omveka bwino, machalichi ambili amatangwanika ndi kupemphetsa ndalama kuti aziyendetsela chalichi cao ndi kulipila atsogoleli ao ndiponso anthu ena. Izi zacititsa kuti atsogoleli ambili a zipembedzo alemele kwambili.—Chivumbulutso 17:4, 5.
Nchito yolalikila siiyenela kukhala bizinesi
9. Kodi Mboni za Yehova zaonetsa bwanji kuti zimagwila nchito yolalikila ndi colinga cabwino?
9 Kodi Mboni za Yehova zimapemphetsa ndalama ku Nyumba zao za Ufumu kapena pamisonkhano ikuluikulu? Iyai. Nchito yao imacilikizidwa ndi zopeleka zimene anthu amapeleka mwakufuna kwao. (2 Akorinto 9:7) Caka catha, Mboni za Yehova zinalalikila uthenga wabwino kwa maola pafupifupi 2 biliyoni ndipo zinali kucititsa maphunzilo oposa 9 miliyoni mwezi uliwonse. Iwo sapatsidwa ndalama cifukwa colalikila, koma amakhala okondwa ngakhale kuti amaseŵenzetsa ndalama zao pogwila nchito imeneyi. Ponena za nchito ya Mboni za Yehova, wocita kafukufuku wina anati: “Colinga cao cacikulu ndi kulalikila ndi kuphunzitsa anthu.” Iye anakambanso kuti Mboni za Yehova zilibe abusa amene amalipilidwa. Conco, ngati sitilalikila kuti tipeze ndalama, kodi timalalikila cifukwa ca ciani? Timagwila nchitoyi modzipeleka cifukwa timakonda Yehova ndiponso anthu ena. Kukhala ndi maganizo amenewa kumakwanilitsa ulosi umene uli pa Salimo 110:3. (Ŵelengani.)
NDI NJILA ZITI ZIMENE TIYENELA KUSEŴENZETSA POLALIKILA?
10. Kodi Yesu ndi ophunzila ake anali kulalikila bwanji?
10 Kodi Yesu ndi ophunzila ake anali kulalikila bwanji? Iwo anali kupita kulikonse kumene kunali kupezeka anthu. Mwacitsanzo, anali kulalikila m’miseu ndi m’misika. Analinso kufunafuna anthu kunyumba zao. (Mateyu 10:11; Luka 8:1; Machitidwe 5:42; 20:20) Kulalikila kunyumba ndi nyumba inali njila yabwino kwambili yolalikila kwa anthu a mitundu yonse.
11, 12. Kodi Mboni za Yehova zimasiyana bwanji ndi Machalichi Acikhristu pankhani yolalikila uthenga wabwino?
11 Kodi machalichi acikristu amalalikila uthenga wabwino mmene Yesu anacitila? Kaŵilikaŵili, abusa amene amapatsidwa ndalama amalalikila kwa mamembala ao. Atsogoleli amenewa sapanga ophunzila atsopano, koma amayesetsa kunyengelela mamembala ao kuti asawathaŵe. Nthawi zina, amayesa kulimbikitsa mamembala ao kuti azilalikila. Mwacitsanzo, m’caka ca 2001, Papa John Paul waciŵili, analembela kalata mamembala ake ndi kuwauza kuti afunika kulalikila
Uthenga Wabwino mwacangu monga mtumwi Paulo amene anati: “Tsoka kwa ine ngati sindilengeza uthenga wabwino.” Papa anaonjezela kuti nchito yolalikila siyenela kugwilidwa ndi anthu ocepa cabe amene anaphunzitsidwa koma ndi mamembala onse a cipembedzo. Komabe, ndi anthu ocepa amene anatsatila malangizo amenewa.12 Nanga bwanji ponena za Mboni za Yehova? Ndiwo okha amene amalalikila kuti Yesu wakhala akulamulila monga Mfumu kuyambila mu 1914. Iwo amamvela Yesu ndipo amaika nchito yolalikila pamalo oyamba mu umoyo wao. (Maliko 13:10) Buku lina lofotokoza za cipembedzo linakamba kuti cinthu cofunika kwambili kwa Mboni za Yehova ndi nchito yolalikila. Bukulo linakambanso kuti io akapeza anthu anjala, osungulumwa, ndi odwala, amawathandiza, koma saiŵala kuti colinga cao cacikulu ndi kulalikila za kutha kwa dzikoli ndi kuphunzitsa anthu za cipulumutso. (Pillars of Faith—American Congregations and Their Partners) Mboni za Yehova zikulalikilabe uthenga umenewu ndipo zimagwilitsila nchito njila zimene Yesu ndi ophunzila ake anaseŵenzetsa.
KODI NCHITO IMENEYI IYENELA KUGWILIDWA PA MLINGO WOTANI, NANGA KUFIKILA LITI?
13. Kodi nchito yolalikila iyenela kugwilidwa pa mlingo wotani?
13 Yesu anakamba kuti ophunzila ake ayenela kulalikila ndi kuphunzitsa uthenga wabwino “padziko lonse lapansi kumene kuli anthu.” Iwo analamulidwa kupanga ophunzila kucokela ku “mitundu yonse” ya anthu. (Mateyu 24:14; 28:19, 20) Izi zitanthauza kuti uthenga wabwino uyenela kulalikidwa padziko lonse.
14, 15. N’ciani cikuonetsa kuti Mboni za Yehova zikukwanilitsa ulosi wa Yesu malinga ndi mmene zimagwilila nchito yao? (Onani zithunzi kuciyambi kwa nkhani ino.)
14 Ndi Mboni za Yehova zokha zimene zikukwanilitsa ulosi wa Yesu wakuti uthenga wabwino udzalalikidwa padziko lonse. Takamba zimenezi cifukwa ku United States kuli atsogoleli a Machalichi Acikristu okwana 600,000, koma kuli Mboni za Yehova 1,200,000 zimene zimalalikila uthenga wabwino. Padziko lonse pali ansembe a Cikatolika okwana 400,000, koma pali Mboni za Yehova zoposa 8 miliyoni zimene zikulalikila uthenga wabwino m’maiko 240. N’zoonekelatu kuti ndi Mboni za Yehova zokha zimene zikulalikila uthenga wabwino padziko lonse, ndipo uthenga umenewu umapeleka ulemelelo ndi citamando kwa Yehova.—Salimo 34:1; 51:15.
15 Pokhala Mboni za Yehova, colinga cathu ndi kulalikila uthenga wabwino kwa anthu ambili mmene tingathele mapeto asanafike. Kuti tikwanitse kucita nchito imeneyi, tamasulila ndi kufalitsa mabuku, magazini, tumapepala twauthenga, toitainila anthu ku Cikumbutso, ndi ku msonkhano wacigawo m’zinenelo zoposa 700. Timapatsa anthu zinthu zimenezi popanda kulipilitsa. Caka catha, tinafalitsa mabuku ndi zinthu zina zofotokoza Baibulo zokwana 4.5 biliyoni. Tasindikizanso makope a Baibulo la Dziko Latsopano oposa 200 miliyoni m’zinenelo zoposa 130. Komanso webusaiti yathu ikupezeka m’zinenelo zoposa 750. Ndi Mboni za Yehova zokha zimene zikugwila nchito yocititsa cidwi imeneyi.
16. Tidziŵa bwanji kuti Mboni za Yehova zili ndi mzimu woyela wa Mulungu?
Machitidwe 1:8; 1 Petulo 4:14) Anthu ena acipembedzo amakamba kuti “Tili ndi mzimu woyela.” Koma kodi io angathe kugwila nchito imene Mboni za Yehova zikugwila masiku otsiliza ano? Machalichi ena ayesapo kulalikila mmene ife timacitila, koma alephela. Ena amalalikila, koma amacita zimenezi kwa nthawi yocepa. Enanso amakwanitsa kulalikila kunyumba ndi nyumba, koma salalikila uthenga wabwino wa Ufumu. Conco, io sagwila nchito imene Yesu anayambitsa.
16 Kodi nchito yolalikila iyenela kucitika kufikila liti? Yesu anakamba kuti uthenga wabwino udzalalikidwa mpaka mapeto. Ife Mboni za Yehova takhala tikupilila pogwila nchito imeneyi m’masiku otsiliza ano cifukwa tili ndi mzimu woyela wa Yehova. (NDANI KWENIKWENI AMENE AKULALIKILA UTHENGA WABWINO MASIKU ANO?
17, 18. (a) N’cifukwa ciani tingakambe kuti ndi Mboni za Yehova zokha zimene zikulalikila uthenga wabwino wa Ufumu masiku ano? (b) N’ciani cimatithandiza kupitiliza kugwila nchito imeneyi?
17 Ndani amene akulalikila uthenga wabwino wa Ufumu masiku ano? Ndi Mboni za Yehova zokha. Takamba zimenezi cifukwa timalalikila uthenga woyenela, umene ndi uthenga wabwino wa Ufumu. Timafunafuna anthu mu ulaliki wathu, conco timagwilitsila nchito njila zoyenela. Timalalikila ndi colinga cabwino cifukwa cakuti timakonda Yehova ndiponso anthu ena. Timagwila nchito imeneyi pa mlingo waukulu cifukwa timalalikila anthu a mitundu yonse ndi zinenelo zonse. Ndipo tidzapitiliza kulalikila uthenga wabwino wa Ufumu mpaka pamene mapeto adzafika.
18 N’zocititsa cidwi kwambili kuona nchito yaikulu yolalikila uthenga wabwino imene anthu a Yehova akugwila masiku ano otsiliza. Koma kodi timakwanitsa bwanji kugwila nchito imeneyi? Mtumwi Paulo anakamba kuti: “Mulungu amacita zinthu m’njila imene imamusangalatsa. Iye amalimbitsa zolakalaka zanu kuti mucite zinthu zonse zimene iye amakonda. (Afilipi 2:13) Pemphelo lathu n’lakuti Yehova apitilize kutipatsa mphamvu zokwanila kuti tizicita zimene tingathe polalikila uthenga wabwino.—2 Timoteyo 4:5.