NKHANI YOPHUNZILA 21
Kodi Mumayamikila Mphatso Zimene Mulungu Anakupatsani?
“Inu Yehova Mulungu wanga, mwaticitila zinthu zambili zodabwitsa, ndipo mumatiganizila.”—SAL. 40:5.
NYIMBO 5 Nchito Zodabwitsa za Mulungu
ZIMENE TIKAMBILANE *
1-2. Malinga na Salimo 40:5, kodi Yehova watipatsa mphatso zotani? Nanga n’cifukwa ciani tikambilana mphatso zimenezi?
YEHOVA ni Mulungu woolowa manja. Ganizilani zina mwa mphatso zimene anatipatsa. Anatipatsa dziko lapansi, malo athu okhala abwino ndiponso okongola; ubongo wathu wopangidwa modabwitsa; komanso Mawu ake amtengo wapatali, Baibo. Cifukwa ca mphatso zocokela kwa Yehova zimenezi, tili na malo okhala, timakwanitsa kuganiza na kukambilana na ena, komanso tadziŵa mayankho pa mafunso ofunika kwambili amene timakhala nawo.—Ŵelengani Salimo 40:5.
2 M’nkhani ino, tikambilanako mwacidule mphatso zitatu zimenezi. Kusinkha-sinkha pa mphatsozi, kudzatithandiza kukhala na mtima woyamikila kwambili, ndipo tidzakhala ofunitsitsa kukondweletsa Mlengi wathu wacikondi, Yehova. (Chiv. 4:11) Kudzatithandizanso kuti tizitha kukambilana mogwila mtima ndi anthu amene asoceletsedwa na ciphunzitso cabodza ca cisanduliko.
DZIKO LAPANSI LINAPANGIDWA MWAPADELA
3. Kodi dziko lapansi limasiyana bwanji na mapulaneti ena?
3 Nzelu za Yehova zimaonekela bwino tikaona mmene anapangila dziko lapansi, malo athu okhala. (Aroma 1:20; Aheb. 3:4) Dziko ni limodzi mwa mapulaneti amene amazungulila dzuŵa. Koma linapangidwa mwapadela cifukwa lili na zonse zofunikila kuti anthufe tipitilize kukhala na moyo.
4. Kodi nzelu za Mulungu zimaonekela bwanji tikaona mmene anapangila dziko lapansi? Fotokozani citsanzo.
4 Mwanjila ina, dziko lapansi tingaliyelekezele na nyumba yokhoma imene ili kutali kwambili, ndipo mkati mwake muli anthu ambili. Koma pali mbali zina zosiyana kwambili pakati pa nyumba yotelo na dziko lapansi. Mwacitsanzo, tiyelekezele kuti anthu amene ali
m’nyumbayo auzidwa kuti azidzipangila okha mpweya wa oxygen, cakudya, madzi, komanso kuti asamataye kunja zonyansa na zinyalala. Kodi muganiza kuti angakhale na moyo kwa nthawi yaitali? Ayi. Anthuwo angafe posapita nthawi. Mosiyana na izi, dziko lapansi limakwanitsa kucilikiza zamoyo mabiliyoni ambili. Lili na zinthu zonse zimene timafunikila monga mpweya wa oxygen, zakudya, komanso madzi. Ndipo zinthu zofunika zimenezi sizikutha. Ngakhale kuti zonyansa zonse na zinyalala zimatayidwa pamene pano padziko lapansi, dzikoli limakhalabe lokongola komanso labwino kukhalamo. Kodi zimatheka bwanji zimenezi? Yehova anapanga dziko lapansi mwadongosolo kuti lizitha kusintha zonyansa n’kukhala zinthu zabwino zimene tingathe kuziseŵenzetsanso. Tiyeni tsopano tikambilane mwacidule dongosolo locititsa cidwi la zungulile-zungulile wa mpweya wa oxygen komanso madzi.5. N’cifukwa ciani mpweya wa oxygen sukutha? Nanga zimenezi zimatsimikizila mfundo iti?
5 Oxygen ni mpweya umene ife anthu na zinyama timapuma kuti tikhalebe na moyo. Akatswili ena amakamba kuti pa caka, anthu na nyama amapuma mpweya wabwino wa oxygen wambili-mbili. Ngakhale n’telo, mpweya wabwino umenewu sukutha. Kuwonjezela apo, anthu na nyama amatulutsa mpweya “woipa” wochedwa carbon dioxide. Komabe, mpweya umenewu sufika poculuka kwambili mu mlengalenga. N’cifukwa ciani zili conco? Cifukwa Yehova analenga zomela zosiyana-siyana, zazikulu na zazing’ono, zimene zimatenga na kugwilitsila nchito mpweya wa carbon dioxide na kutulutsa mpweya wa oxygen. Kuzungulila kumeneku kwa mpweya kumathandiza kuti tizikhala na mpweya wa oxygen umene timapuma. Izi zionetsa kuti mfundo ya pa Machitidwe 17:24, 25 ni ya zoona. Lembali limakamba kuti, ‘Mulungu amapatsa anthu onse moyo na mpweya.’
6. N’cifukwa ciani madzi sakutha padziko lapansi? Nanga izi zionetsa ciani? (Onaninso bokosi yakuti “Zungulile-zungulile wa madzi ni Mphatso Yocokela kwa Yehova.”)
6 Padziko lapansi pali madzi cifukwa cakuti dziko lili pa mtunda woyenelela kucokela ku dzuŵa. Dziko likanakhalako pafupi na dzuŵa, sembe madzi onse anauma, ndipo padziko pakanakhala potentha kwambili ndiponso popanda camoyo ciliconse. Komanso, dziko likanakhala kutali pang’ono na dzuŵa, madzi onse akanaundana, ndipo padziko pakanakhala ayisi yekha-yekha na sinoo. Popeza kuti Yehova anaika dziko lapansi pamalo oyenelela, zungulile-zungulile wa madzi padzikoli umathandiza kuti pakhalebe zamoyo. Dzuŵa likawomba pa nyanja ndiponso pa mtunda, madzi amacita nthunzi n’kukwela kumwamba kukapanga mitambo. Pa caka, madzi amene amakwela kumwamba monga nthunzi cifukwa ca dzuŵa, amakhala ambili kuposa a m’nyanja zonse padziko lapansi, kupatulapo cabe a m’nyanja zamcele (maosheni). Madzi akakwela kumwamba monga nthunzi, amakhala kumeneko kwa masiku pafupi-fupi 10, kenako amagwa monga mvula kapena sinoo. Zikatelo, madziwo amabwelelanso ku nyanja na ku mitsinje, ndipo zomwe takamba zija zimayambanso kucitika. Yehova anapanga dongosolo limeneli n’colinga cakuti padziko pazikhala madzi nthawi zonse. Izi zionetsa kuti iye ni wanzelu komanso wamphamvu.—Yobu 36:27, 28; Mlal. 1:7.
7. Ni njila zina ziti zimene tingaonetsele kuti timayamikila mphatso yochulidwa pa Salimo 115:16?
7 N’ciani cingatithandize kukhala oyamikila kwambili kaamba ka dziko lapansi, malo athu okhala opangidwa modabwitsa, na zonse zili mmenemo? (Ŵelengani Salimo 115:16.) Cimodzi cimene cingatithandize ni kusinkha-sinkha pa zimene Yehova analenga. Kucita izi kudzatisonkhezela kuti tiziyamikila Yehova tsiku lililonse cifukwa ca zinthu zabwino zimene amatipatsa. Tingaonetsenso kuti timayamikila mphatso ya dziko lapansi mwa kuyesetsa kusamalila bwino malo amene timakhala.
UBONGO WATHU UNAPANGIDWA MODABWITSA
8. N’ciani cionetsa kuti ubongo wathu unapangidwa modabwitsa kwambili?
8 Ubongo wa munthu unapangidwa modabwitsa kwambili. Pamene mwana ali m’mimba mwa mayi
ake, ubongo wake umapangidwa mwadongosolo kwambili. Ndipo pa mphindi iliyonse, maselo atsopano masauzande ambili a ubongo amapangika. Akatswili amakamba kuti ubongo wa munthu wamkulu umakhala na maselo pafupi-fupi 100 biliyoni. Ndipo umalemela pafupi-fupi kilogilamu imodzi na hafu. Tsopano tiyeni tione zina mwa zinthu zimene timakwanitsa kucita cifukwa ca ubongo wathu wopangidwa modabwitsa.9. N’ciani cimakupangitsani kukhulupilila kuti kulankhula ni mphatso yocokela kwa Mulungu?
9 Timakwanitsa kulankhula. Kulankhula ni mphatso yocititsa cidwi. Ganizilani zimene zimacitika tikamakamba. Kuti munthu akambe liwu limodzi cabe, ubongo wake umafunika kugwilizanitsa kayendedwe ka minofu pafupi-fupi 100 ya lilime, m’melo, milomo, nsagwada, komanso ya m’cifuwa. Ndipo kuti akwanitse kukamba mawu omveka bwino, minofu imeneyi imafunika kuyenda mwadongosolo. Ponena za kulankhula, zotsatila za kafuku-fuku wina zimene zinafalitsidwa mu 2019, zionetsa kuti makanda ongobadwa kumene amakwanitsa kumva mawu na kukhudzika na zimene amvela. Kafuku-fuku ameneyu agwilizana na mfundo imene akatswili ambili amakhulupilila, yakuti anthufe timabadwa na luso lokwanitsa kumva na kuphunzila vitundu. Kukamba zoona, kulankhula ni mphatso yocokela kwa Mulungu.—Eks. 4:11.
10. Tingaonetse bwanji kuti timayamikila mphatso ya kulankhula yocokela kwa Mulungu?
10 Njila imodzi imene tingaonetsele kuti timayamikila mphatso ya kulankhula, ni mwa kuuzako anthu okhulupilila cisanduliko cifukwa cake ife timakhulupilila kuti Mulungu ndiye analenga zinthu zonse. (Sal. 9:1; 1 Pet. 3:15) Anthu amene amakhulupilila ciphunzitso cimeneci amafuna kuti nafenso tizikhulupilila kuti dziko na zamoyo zonse zili mmenemo zinangokhalako zokha. Ngati tiseŵenzetsa Baibo komanso mfundo zina zimene takambilana m’nkhani ino, tidzakwanitsa kuikila kumbuyo Atate wathu wakumwamba. Ndiponso tidzakwanitsa kufotokozela anthu a maganizo oyenela, cifukwa cake timakhulupilila kuti Yehova ndiye analenga kumwamba na dziko lapansi.—Sal. 102:25; Yes. 40:25, 26.
11. N’ciani cina cimene cionetsa kuti ubongo wathu unapangidwa modabwitsa?
11 Timatha kukumbukila zinthu zambili-mbili. Zimenezi n’zocititsa cidwi kwambili. Kumbuyoku, katswili wina anakamba kuti cifukwa ca mphamvu imene ubongo wathu uli nayo, tingathe kukumbukila zinthu zolembedwa m’mabuku ofika 20 miliyoni. Koma tsopano akatswili amakamba kuti munthu angakwanitse kukumbukila zinthu zambili kuposa pamenepa. Pa cifukwa ici, anthu amakwanitsa kucita zinthu zimene zolengedwa zina padzikoli sizikwanitsa kucita.
12. Kodi kukwanitsa kuphunzila makhalidwe kumatisiyanitsa bwanji na vinyama?
12 Pa zolengedwa zonse padzikoli, ni anthu cabe amene amakwanitsa kuphunzila makhalidwe mwa kukumbukila zimene zinawacitikila na kuganizilapo. Mwa kucita izi, timakwanitsa kuphunzila mfundo za makhalidwe abwino na kusintha kaganizidwe kathu komanso umoyo wathu. (1 Akor. 6:9-11; Akol. 3:9, 10) Timakwanitsa ngakhale kuphunzitsa cikumbumtima cathu kusiyanitsa coyenela na cosayenela. (Aheb. 5:14) Timaphunzilanso kukhala acikondi ndi acifundo. Timakwanitsanso kutengela khalidwe la Yehova la cilungamo.
13. Mogwilizana na Salimo 77:11, 12, kodi mphatso yathu yotha kukumbukila zinthu tiyenela kuiseŵenzetsa bwanji?
Salimo 77:11, 12; 78:4, 7) Njila ina, ni mwa kukumbukila zinthu zabwino zimene ena amaticitila na kuwayamikila. Akatswili anapeza kuti anthu oyamikila, nthawi zambili amakhala acimwemwe. Tingacitenso bwino kutengela citsanzo ca Yehova mwa kusankha kuiŵala zinthu zina. Yehova angakwanitse kukumbukila zinthu zonse. Koma tikacita chimo n’kulapa, iye amasankha kutikhululukila na kuiŵala zolakwa zimene tinacita. (Sal. 25:7; 130:3, 4) Yehova amafuna kuti nafenso tizikhululukila anthu na kuiŵalako zimene anatilakwila ngati alapa.—Mat. 6:14; Luka 17:3, 4.
13 Njila imodzi imene tingaonetsele kuti timayamikila mphatso yotha kukumbukila zinthu, ni mwa kuyesetsa kukumbukila zonse zimene Yehova anaticitila potithandiza na kutitonthoza m’mbuyomo. Kucita zimenezi kudzatithandiza kukhala na cidalilo cakuti adzatithandizanso kutsogolo. (Ŵelengani14. Tingaonetse bwanji kuti timayamikila mphatso yapadela ya ubongo?
14 Tingaonetse kuyamikila mphatso yapadela ya ubongo mwa kuuseŵenzetsa polemekeza Yehova amene anatipatsa mphatsoyi. Anthu ena amaseŵenzetsa ubongo wawo pokwanilitsa zolinga zadyela. Amadziikila miyezo yawo ya cabwino na coipa. Koma popeza kuti Yehova ndiye anatilenga, n’zosacita kufunsa kuti miyezo yake ya cabwino na coipa ndiyo yabwino kwambili kuposa imene tingadziikile tokha. (Aroma 12:1, 2) Tikamatsatila miyezo yake, timakhala na mtendele mu umoyo wathu. (Yes. 48:17, 18) Cinanso, timazindikila colinga cimene Yehova anatilengela, comwe ni kum’lemekeza na kucita zinthu zom’kondweletsa monga Mlengi komanso Tate wathu.—Miy. 27:11.
BAIBO NI MPHATSO YAPADELA
15. Kodi mphatso ya Baibo imene Yehova anatipatsa imaonetsa bwanji kuti amatikonda?
15 Baibo ni mphatso yocokela kwa Mulungu yoonetsa kuti iye amatikonda. Atate wathu wakumwamba anauzila amuna ena kuti alembe Baibo cifukwa iye amatikonda kwambili. Kupitila m’Baibo, Yehova amatithandiza kupeza mayankho pa mafunso ofunika kwambili amene timakhala nawo, monga akuti: Kodi tinacokela kuti? Kodi colinga ca moyo n’ciani? Kodi zinthu zidzakhala bwanji kutsogolo? Yehova afuna kuti ana ake onse adziŵe
mayankho pa mafunso amenewa. N’cifukwa cake kwa zaka zambili, iye wakhala akusonkhezela anthu kumasulila Baibo m’vitundu vambili. Masiku ano, Baibo yathunthu kapena mbali yake cabe ipezeka m’vitundu voposa 3,000! Baibo ni buku limene lamasulidwa m’vitundu vambili na kufalitsidwa m’madela ambili kuposa buku lina lililonse. Anthu ambili ali na mwayi woŵelenga uthenga wa m’Baibo m’citundu cawo, mosasamala kanthu za kumene akhala kapena citundu cimene amakamba.—Onani bokosi yakuti Kumasulila Baibo m’Vitundu va mu Africa.”16. Malinga na Mateyu 28:19, 20, tingaonetse bwanji kuti timayamikila mphatso ya Baibo?
16 Tingaonetse kuti timayamikila mphatso ya Baibo mwa kuiŵelenga tsiku lililonse, kusinkha-sikha pa zimene taŵelengazo, na kuyesetsa kuseŵenzetsa zimene timaphunzila. Kuwonjezela apo, tingaonetse kuti timamuyamikila Mulungu cifukwa ca mphatso imeneyi, mwa kuyesetsa kuuzako anthu ambili coonadi ca m’Baibo mmene tingathele.—Sal. 1:1-3; Mat. 24:14; ŵelengani Mateyu 28:19, 20.
17. Kodi m’nkhani ino takambilana za mphatso ziti? Nanga tidzakambilana ciani m’nkhani yotsatila?
17 M’nkhani ino, takambilana za mphatso zimene Mulungu anatipatsa monga dziko, limene ni malo athu okhala; ubongo wathu wopangidwa modabwitsa; komanso Mawu ouzilidwa a Mulungu, Baibo. Koma palinso mphatso zina zimene Yehova anatipatsa zimene sitiziona na maso. M’nkhani yotsatila, tidzakambilana za mphatso zosaoneka zimenezo.
NYIMBO 12 Mulungu Wamkulu, Yehova
^ ndime 5 Nkhani ino itithandiza kuyamikila kwambili Yehova komanso mphatso zitatu mwa mphatso zimene iye anatipatsa. Itithandizanso kudziŵa mmene tingakambile ndi anthu amene amakayikila zakuti kuli Mulungu.
^ ndime 64 MAWU OFOTOKOZELA CITHUNZI: Mlongo akuphunzila citundu ca ku dziko lina n’colinga cakuti azitha kuphunzitsa anthu ocokela ku maiko ena coonadi ca m’Baibo.