Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI YOPHUNZILA 20

Pitilizani Kukhala na Maganizo Oyenela pa Ulaliki Wanu

Pitilizani Kukhala na Maganizo Oyenela pa Ulaliki Wanu

Bzala mbewu zako . . . ndipo dzanja lako lisapume.”—MLAL. 11:6.

NYIMBO 70 Funa-funani Oyenelela

ZIMENE TIKAMBILANE *

Yesu atapita kumwamba, ophunzila ake analalikila mokangalika mu Yerusalemu na kumadela ena (Onani ndime 1)

1. Kodi Yesu anawapatsa citsanzo cotani otsatila ake? Nanga iwo anacita ciani? (Onani cithunzi pacikuto.)

YESU anakhalabe na maganizo oyenela pa utumiki wake wonse padziko lapansi. Ndipo amafuna kuti otsatila ake nawonso azikhala na maganizo oyenela pankhani ya ulaliki. (Yoh. 4:35, 36) Pamene Yesu anali na ophunzila ake, ophunzilawo anali kugwila nchito yolalikila mokangalika. (Luka 10:1, 5-11, 17) Koma pamene Yesu anamangidwa na kuphedwa, kwa kanthawi, cangu ca ophunzilawo panchito yolalikila cinacepa. (Yoh. 16:32) Ataukitsidwa, Yesu anawalimbikitsa kusumika maganizo awo pa ulaliki. Ndipo iye atabwelela kumwamba, ophunzilawo analalikila mwacangu cakuti adani awo anadandaula kuti: “Taonani tsopano! Mwadzaza Yerusalemu yense ndi ciphunzitso canuci.”—Mac. 5:28.

2. Kodi Yehova waidalitsa bwanji nchito yolalikila?

2 Yesu anatsogolela panchito yolalikila imene Akhristu a m’nthawi ya atumwi anali kugwila. Ndipo Yehova anawadalitsa moti ciŵelengelo ca ophunzila cinawonjezeka. Mwacitsanzo, pa Pentekosite wa mu 33 C.E., anthu pafupi-fupi 3,000 anabatizidwa. (Mac. 2:41) Ndipo ciŵelengelo ca ophunzila cinapitiliza kukula modabwitsa. (Mac. 6:7) Yesu anali atakambilatu kuti nchito yolalikila idzacitika pamlingo waukulu m’masiku otsiliza.—Yoh. 14:12; Mac. 1:8.

3-4. N’cifukwa ciani nchito yolalikila ingakhale yovuta m’madela ena? Nanga tikambilane ciani m’nkhani ino?

3 Tonsefe timapitiliza kuona ulaliki wathu moyenela. M’maiko ena, n’zosavuta kuona ulaliki moyenela. Cifukwa ciani? Cifukwa ambili ali na cidwi cofuna kuphunzila Baibo, cakuti ena amacita kuyembekezela kuti wa Mboni za Yehova akawalalikile! Koma m’maiko ena, nchito yolalikila imakhala yovuta kwa ofalitsa. Anthu sapezeka kaŵili-kaŵili panyumba, ndipo amene amapezeka amakhala alibe cidwi kweni-kweni pa Baibo.

4 Ngati mumakhala m’dela limene nchito yolalikila ni yovuta, malingalilo a m’nkhani ino adzakuthandizani. Tikambilane zimene ena acita kuti azikambilana na anthu ambili mu ulaliki. Ndipo tionenso cifukwa cake tifunika kukhalabe na maganizo oyenela, kaya anthu alandile uthenga wathu kapena ayi.

KHALANIBE NA MAGANIZO OYENELA NGATI N’ZOVUTA KUPEZA ANTHU

5. Kodi Mboni zambili zimakumana na zopinga zotani?

5 Kwa Mboni za Yehova zambili, vuto la kusapeza anthu panyumba likukulila-kulila. Ofalitsa ena amakhala m’madela amene nyumba zambili zili m’mipanda kapena zili na citetezo cokhwima. Pakhomo pa mipandayo pangakhale mlonda amene amaletsa aliyense kulowa popanda cilolezo cocokela kwa amene akhala mkati. Ofalitsa ena angapite kukalalikila ku nyumba na nyumba popanda zovuta, koma amapeza anthu ocepa m’makomo. Ndipo ofalitsa ena amalalikila m’madela akutali kumene kumakhala anthu ocepa. Ofalitsa ena angafunike kuyenda misenga yaitali, kuti akalalikile cabe munthu mmodzi amenenso mwina sangapezeke panyumba. Tikakumana na zopinga zotele, sitiyenela kufooka. Kodi tingacite ciani kuti tigonjetse zopinga zimenezi na kupangitsa ulaliki wathu kukhala wopindulitsa?

6. Kodi alaliki afanana bwanji na asodzi?

6 Yesu anayelekezela nchito yolalikila na nchito ya msodzi. (Maliko 1:17) Asodzi ena, angaseŵenze kwa masiku koma osaphako nsomba iliyonse. Koma samaleka, amayesa kusintha zinthu zina. Iwo amayesa kusintha nthawi, malo, kapena njila zophela nsomba. Nafenso tingapange masinthidwe ofananawo mu ulaliki. Tsopano tiyeni tikambilane malingalilo otsatilawa amene tingaseŵenzetse.

Mukamalalikila m’dela limene n’zovuta kupeza anthu panyumba, yesani kuwafikila pa nthawi zosiyana-siyana, ku malo osiyana-siyana, kapena kuseŵenzetsa njila zosiyana-siyana (Onani ndime 7-10) *

7. Kodi kulalikila pa nthawi zosiyana-siyana kungakhale na zotulukapo zotani?

7 Yesani kufikila anthu panthawi zosiyana-siyana. Tidzapeza anthu ambili ngati tilalikila pa nthawi imene iwo angapezeke panyumba. Paja munthu aliyense ali na nthawi imene amapezeka panyumba! Abale na alongo ambili, amaona kuti cimakhala cothandiza kulalikila masana kapena madzulo cifukwa m’pamene amapeza anthu ambili. Kuwonjezela apo, anthu angakhale kuti akupumula, ndipo amakhala okonzeka kukambilana nawo pa nthawi ngati zimenezo. Mwina mungayese kuseŵenzetsa malingalilo a m’bale wina dzina lake David amene ni mkulu. M’baleyo anakamba kuti akalalikila-lalikila m’gawo, iye na mnzake amabwelelanso kunyumba zimene sanapezeko anthu pa ulendo woyamba. Iye anakamba kuti, “Nimadabwa kuona kuculuka kwa anthu amene amapezeka panyumba tikabwelelako kaciŵili.” *

Mukamalalikila m’dela limene n’zovuta kupeza anthu panyumba, yesani kuwafikila pa nthawi zosiyana-siyana (Onani ndime 7-8)

8. Kodi tingaseŵenzetse bwanji Mlaliki 11:6 pa ulaliki wathu?

8 Sitiyenela kufooka. Lemba la mutu wa nkhani ino, litithandiza kukhala na maganizo oyenela. (Ŵelengani Mlaliki 11:6.) M’bale David amene tam’chula kumayambililo sanafooke. Pamapeto pake, iye anapeza mwininyumba panyumba ina imene kwa maulendo ambili sanali kupezapo anthu. Munthuyo anali na cidwi cofuna kuphunzila Baibo, ndipo anakamba kuti, “Nakhala pano kwa zaka pafupi-fupi 8, ndipo palibe wa Mboni za Yehova aliyense amene anabwelapo pakhomo pano.” M’bale David ananena kuti, “Tikawapeza anthu pakhomo, nthawi zambili amakhala okonzeka kumvela uthenga umene timalalikila.”

Mukamalalikila m’dela limene n’zovuta kupeza anthu panyumba, yesani kuwafikila ku malo osiyana-siyana (Onani ndime 9)

9. Kodi ofalitsa ena amacita ciani kuti akambilane na anthu amene n’zovuta kuwapeza panyumba?

9 Yesani kusintha malo. Pofuna kukambilana na anthu amene n’zovuta kuwapeza panyumba, ofalitsa ena anasintha malo olalikilako. Mwacitsanzo, ulaliki wa mu msewu komanso kuseŵenzetsa tumasitandi twa ulaliki kwakhala njila yothandiza kwambili pofikila anthu okhala m’nyumba zikulu-zikulu zansanjika, kumene ulaliki wa nyumba na nyumba ni wosaloledwa. Izi zimathandiza Mboni za Yehova kukambilana na anthu pamaso-m’pamaso, amene zikanakhala zovuta kuwafikila. Kuwonjezela apo, ofalitsa ambili apeza kuti anthu ambili amakhala okonzeka kukambilana nawo, kapena kulandila zofalitsa m’mapaki, m’misika, ndiponso mkati mwa tauni. M’bale Floiran woyang’anila dela ku Bolivia ananena kuti: “Timapita kumsika na ku masitolo pakati pa 13:00 awazi na 15:00 awazi, pamene ogulitsa sakhala otangwanika kwambili. Timakhala na makambilano abwino ngakhalenso kuyambitsa maphunzilo a Baibo.”

Mukamalalikila m’dela limene n’zovuta kupeza anthu panyumba, yesani kuwafikila mwa kuseŵenzetsa njila zosiyana-siyana (Onani ndime 10)

10. Kodi mungaseŵenzetse njila ziti kuti mulalikile anthu?

10 Yesani njila ina. Tiyelekeze kuti mwayesa kukambilana na munthu wina mwacindunji. Mwayesa kum’fikila pa nthawi zosiyana-siyana, koma sakupezeka ndithu panyumba. Kodi pali njila zina zimene mungaseŵenzetse kuti mum’peze munthuyo? Mlongo Katarína anati, “Nimalemba makalata kwa anthu amene sin’nawapeze panyumba, na kuwafotokozela zimene n’kanawauza n’kanawapeza.” Mfundo yake ni iti? Yesani kukambilana na munthu aliyense m’gawo lanu mwa kuseŵenzetsa njila zosiyana-siyana pocita ulaliki wanu.

KHALANIBE NA MAGANIZO OYENELA NGATI ANTHU ALIBE CIDWI

11. N’cifukwa ciani anthu ena alibe cidwi na uthenga wathu?

11 Anthu ena alibe cidwi na uthenga wathu. Iwo amaona kuti safunikila Mulungu kapena Baibo. Sakhulupilila Mulungu cifukwa amaona kuti padzikoli pali mavuto ambili. Iwo alibe cidwi na Baibo cifukwa amaona cinyengo ca atsogoleli acipembedzo amene amakamba kuti amayendela mfundo za m’Baibo. Ena amaganizila kwambili za nchito yawo, mabanja awo, kapena mavuto awo. Ndipo amalephela kuona mmene Baibo ingawathandizile. Tingacite ciani kuti tikhalebe acimwemwe pamene tilalikila kwa anthu amene alibe cidwi kweni-kweni na uthenga wathu?

12. Kodi kuseŵenzetsa mawu a pa Afilipi 2:4 kungatithandize bwanji mu ulaliki?

12 Aonetseni cidwi anthu. Anthu ambili amene poyamba analibe cidwi, analandila uthenga wabwino ataona kuti wofalitsa wawaonetsa cidwi ceni-ceni. (Ŵelengani Afilipi 2:4.) Mwacitsanzo, m’bale David amene tam’gwila mawu kumayambililo ananena kuti, “Ngati munthu wakana kukambilana naye za m’Baibo, timaika Baibo yathu kapena zofalitsa zathu m’cola na kumufunsa kuti: ‘Kodi mungatiuzeko cifukwa cake?’” Anthu amatha kuona ngati tili nawo cidwi. Iwo angaiŵale zina zimene tinakamba, koma adzakumbukila mmene anamvelela titawaonetsa cidwi. Ngakhale kuti eninyumba sangatilole kukamba nawo, kacitidwe kathu ka zinthu komanso kaonekedwe ka nkhope yathu, zingaonetse kuti timasamala za iwo.

13. Kodi tingasinthe bwanji uthenga wathu kuti ugwilizane na zofunikila za mwininyumba aliyense?

13 Timaonetsa cidwi mwa kusintha uthenga wathu kuti ugwilizane na zofunikila za mwininyumba na zimene angacite nazo cidwi. Mwacitsanzo, kodi pali zimene zionetsa kuti panyumbapo pali ana? Makolo angacite cidwi na malangizo a m’Baibo okhudza mmene angalelele ana, kapena malangizo ake othandiza a mmene angakhalile na umoyo wabanja wacimwemwe. Kodi pa zitseko zawo pali maloko ambili? Mwina tingasankhe kukambilana nawo za upandu, komanso mantha amene anthu ali nawo m’dzikoli. Pambuyo pake, mwininyumba angayamikile kudziŵa mmene upandu udzathetsedwela. Mulimonsemo, yesani kuthandiza anthu amene amamvetsela, kuona mmene malangizo a m’Baibo angawathandizile. Mlongo Katarína amene tam’chula kuciyambi ananena kuti, “Nimayesa kukumbukila mmene coonadi cinasinthila umoyo wanga kukhala wabwino.” Cotulukapo cake n’cakuti mlongo Katarína amakamba mwacidalilo, ndipo anthu amene amakamba nawo, mosakayikila amaona zimenezo.

14. Mogwilizana na Miyambo 27:17, kodi ofalitsa angathandizane bwanji mu ulaliki?

14 Pindulani na thandizo la ena. M’zaka za zana loyamba, Paulo anaphunzitsa Timoteyo njila zoyenela kuseŵenzetsa polalikila na kuphunzitsa. Ndipo anam’limbikitsa kuthandizakonso ena kuseŵenzetsa njila zimenezo. (1 Akor. 4:17) Mofanana na Timoteyo, nafenso tingaphunzile zambili kwa aja amene ni aciyambakale mumpingo. (Ŵelengani Miyambo 27:17.) Ganizilani citsanzo ca m’bale wina dzina lake Shawn. Kwa kanthawi, iye anacita upainiya ku dela la kumidzi kumene anthu ambili anali okhutila na cipembedzo cawo. N’ciani cinam’thandiza kukhalabe wacimwemwe? Iye ananena kuti. “Nthawi zonse zikakhala zotheka, n’nali kuyenda na anzanga mu ulaliki. Tinali kuseŵenzetsa nthawi yocoka panyumba ina kupita pa ina kuthandizana mmene tingawongolele luso lathu la kuphunzitsa. Mwacitsanzo, tinali kukambilana mmene tacitila panyumba imene tacoka. Kenako, tinali kukambilana mmene tingacitile mosiyanako tikakumananso na cocitika cofananaco.”

15. N’cifukwa ciani pemphelo n’lofunika pa ulaliki wathu?

15 Pemphani Yehova kuti akuthandizeni. Pemphani Yehova kuti akutsogoleleni nthawi zonse mukapita mu ulaliki. Popanda mphamvu yake ya mzimu woyela, palibe aliyense wa ife angathe kucita ciliconse. (Sal. 127:1; Luka 11:13) Popempha Yehova kuti akuthandizeni, chulani zinthu mwacindunji. Mwacitsanzo, mungam’pemphe kuti akutsogoleleni kwa aliyense amene ali na maganizo oyenelela, komanso amene ni wokonzeka kumvetsela. Ndiyeno citani zinthu mogwilizana na pemphelo lanu mwa kulalikila onse amene mungakumane nawo.

16. N’cifukwa ciani phunzilo laumwini n’lofunika pa nchito yathu yolalikila?

16 Pangani nthawi yocita phunzilo laumwini. Mawu a Mulungu amanena kuti: ‘Zindikilani cimene cili cifunilo ca Mulungu, cabwino, covomelezeka ndi cangwilo.’ (Aroma 12:2) Tikakhala otsimikiza kuti timadziŵadi coonadi cokhudza Mulungu, m’pamene timalankhula mwacidalilo pokambilana na ena mu ulaliki. Mlongo Katarína amene tamuchula kumayambililo anati: “Kumbuyoku, n’nazindikila kuti n’nafunika kulimbitsa cikhulupililo canga pa ziphunzitso zina zikulu-zikulu za m’Baibo. Conco, n’nayamba kuphunzila mozama za umboni wotsimikizila kuti kuli Mlengi, kuti Baibo ni Mawudi a Mulungu, ndiponso kuti Mulungu ali na gulu limene limamuimilako masiku ano.” Mlongo Katarína ananena kuti phunzilo laumwini linam’thandiza kulimbitsa cikhulupililo cake, na kuwonjezela cimwemwe cake mu ulaliki.

CIFUKWA CAKE TIMAKHALABE NA MAGANIZO OYENELA MU ULALIKI

17. N’cifukwa ciani Yesu anakhalabe na maganizo oyenela pa utumiki wake?

17 Yesu anakhalabe na maganizo oyenela na kupitiliza kulalikila, ngakhale kuti ena anali kukana uthenga wake. Cifukwa ciani? Iye anali kudziŵa kuti anthu anafunikila kudziŵa coonadi, ndipo anafuna kupeleka mpata kwa anthu ambili kuti alandile uthenga wa Ufumu. Anadziŵanso kuti anthu amene poyamba anakana uthengawo, m’kupita kwa nthawi adzaulandila. Ganizilani zimene zinacitika m’banja lake leni-leni. Panthawi yonse imene Yesu anacita utumiki wake kwa zaka zitatu na hafu, palibe aliyense wa m’banja lake amene anakhala wophunzila wake. (Yoh. 7:5) Ngakhale n’telo, pambuyo pa kuukitsidwa kwake, iwo anakhala Akhristu.—Mac. 1:14.

18. N’cifukwa ciani timapitiliza kulalikila?

18 Sitidziŵa kuti ndani amene m’kupita kwa nthawi adzaphunzila coonadi ca m’Baibo cimene timaphunzitsa. Anthu ena, amatenga nthawi kusiyana na ena kuti alandile uthenga wathu. Ngakhale aja amene amasankha kusatimvetsela, amaona khalidwe lathu labwino, ndipo m’kupita kwa nthawi angayambe ‘kutamanda Mulungu.’—1 Pet. 2:12.

19. Malinga na 1 Akorinto 3:6, 7, tifunika kukumbukila ciani?

19 Pamene tibyala na kuthilila, tiyenela kukumbukila kuti Mulungu ndiye amakulitsa. (Ŵelengani 1 Akorinto 3:6, 7.) M’bale Getahun amene akutumikila ku Ethiopia ananena kuti: “Kwa zaka zoposa 20, ine nekha ndine n’nali Mboni m’gawo losafoledwa kaŵili-kaŵili. Koma tsopano kuli ofalitsa 14. Ofalitsa 13 anabatizika kuphatikizapo mkazi wanga, na ana anga atatu. Pa avaleji, timapezeka anthu 32 pa misonkhano.” M’bale Getahun ni wokondwela kwambili kuti anapitiliza kulalikila, akuyembekezela moleza mtima pa Yehova kukokela anthu oona mtima ku gulu lake.—Yoh. 6:44.

20. Kodi tili monga opulumutsa anthu m’lingalilo lotani?

20 Yehova amaona kuti moyo wa anthu onse ni wamtengo wapatali. Iye watipatsa mwayi woseŵenzela pamodzi na Mwana wake, posonkhanitsa anthu a mitundu yonse mapeto a dongosolo lino asanafike. (Hag. 2:7) Nchito yathu yolalikila tingaiyelekezele na nchito yopulumutsa anthu. Ndipo zili monga kuti ife tili m’gulu limene latumidwa kukapulumutsa anthu amene atsekeledwa pamgodi. Ngakhale kuti ni anthu ocepa cabe ogwila nchito za pamgodi amene angapezeke amoyo, nchito yopulumutsa anthu imene onsewo agwila ni yofunika kwambili. N’cimodzimodzinso na nchito yathu yolalikila. Sitidziŵa kuti ni anthu angati amene adzapulumutsidwa ku dongosolo la Satana. Koma Yehova angaseŵenzetse aliyense wa ife powathandiza. M’bale Andreas wa ku Bolivia ananena kuti, “Nikaona kuti munthu waphunzila coonadi ca m’Baibo ndipo wabatizika, nimadziŵa kuti siinali nchito ya munthu mmodzi.” Tiyeni tipitilize kukhala na maganizo amenewa pa utumiki wathu. Tikacita zimenezi, Yehova adzatidalitsa, ndipo utumiki wathu udzakhala gwelo la cimwemwe ceni-ceni.

NYIMBO 66 Lengezani Uthenga Wabwino

^ ndime 5 Kodi zingatheke bwanji kukhalabe na maganizo oyenela mu ulaliki, ngakhale pamene ambili sapezeka panyumba kapena amaoneka kuti safuna kumvetsela uthenga wathu? Nkhani ino, idzapeleka malangizo amene angatithandize kukhalabe na maganizo oyenela.

^ ndime 7 Ofalitsa ayenela kuseŵenzetsa njila zosiyana-siyana za ulaliki zimene takambilana m’nkhani ino mogwilizana na malamulo oteteza cinsinsi ca anthu ena.

^ ndime 60 MAWU OFOTOKOZELA ZITHUNZI: (kucoka pamwamba kupita pansi): Mwamuna na mkazi wake akulalikila m’dela limene n’zovuta kupeza anthu panyumba. Mwininyumba woyamba ali ku nchito, waciŵili ali ku cipatala, ndipo wacitatu akugula zinthu m’sitolo. Ofalitsawo afikila mwininyumba woyamba pa nthawi ina pa tsikulo. Akambilana na mwininyumba waciŵili pamene akucita ulaliki wapoyela pafupi na cipatala. Iwo akambilana na mwininyumba wacitatu mwa kum’tumila foni.