NSANJA YA MLONDA—YOPHUNZILA September 2019
Magazini ino ili na nkhani zophunzila wiki ya October 28–December 1, 2019.
Yehova Amaona Atumiki Ake Odzicepetsa Kukhala Amtengo Wapatali
Kudzicepetsa ni limodzi mwa makhalidwe ofunika kwambili amene tiyenela kukhala nawo. Kodi kusintha kwa zinthu kungayese bwanji kudzicepetsa kwathu?
Aramagedo ni Nkhani Yokondweletsa!
Ni zocitika zikulu-zikulu ziti zimene zidzatsogolela ku Aramagedo? Nanga tingacitenso ciani kuti tikhalebe okhulupilika pamene Aramagedo ikuyandikila?
Gonjelani Yehova na Mtima Wonse
Akulu, atate, na amayi angaphunzile zambili kwa Bwanamkubwa Nehemiya, Mfumu Davide, na Mariya amayi ake a Yesu pa nkhani ya kugonjela.
“Bwelani kwa Ine . . . Ndipo Ndidzakutsitsimutsani”
Kodi timapita bwanji kwa Yesu? Pali zinthu zitatu zimene tifunika kucita kuti tipitilize kutsitsimulidwa na goli la Yesu.
“Taonani! “Khamu Lalikulu la Anthu”
M’masomphenya a Yohane aulosi, Yehova anatidziŵitsa kuti a “khamu lalikulu” n’ndani, amene adzapulumuka cisautso cacikulu na kukhala na moyo wosatha pano pa dziko lapansi. Anatidziŵitsanso za kuculuka kwawo, komanso zakuti ni wocokela m’mitundu yosiyana-siyana.