Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Yehova Amatsogolela Anthu Ake m’Njila ya ku Moyo

Yehova Amatsogolela Anthu Ake m’Njila ya ku Moyo

“Njila ndi iyi. Yendani mmenemu.”​—YESAYA 30:21.

NYIMBO: 65, 48

1, 2. (a) Ndi cenjezo lotani limene lateteza anthu ambili? (Onani cithunzi pamwamba.) (b) Kodi anthu a Mulungu amalandila malangizo otani amene angawapulumutse?

“IMANI, ONANI, MVELANI.” Awa ndi mau amene ali pa zikwangwani zikuluzikulu ku North America, ndipo akhalapo kwa zaka zoposa 100. Zikwangwani zimenezo zinaikidwa pa malo amene mseu unadutsa pa njanji. Analembapo mau amenewa n’colinga cakuti magalimoto amene amapita pamalowo asagundidwe ndi sitima zoyenda mothamanga. Kutsatila malangizo a pa zikwangwani zimenezo kwapulumutsa miyoyo ya anthu ambili.

2 Yehova amacita zinthu zabwino kuposa kupeleka zikwangwani za malangizo ocenjeza. Iye amatsogolela anthu ake n’colinga cakuti adzapeze moyo wosatha ndiponso kuti apewe mavuto. Yehova ali ngati m’busa wacikondi amene amatsogolela ndi kucenjeza nkhosa zake kuti zisayende m’njila zoipa.—Ŵelengani Yesaya 30:20, 21.

YEHOVA WAKHALA AKUTSOGOLELA ANTHU AKE

3. N’ciani cinacititsa kuti anthu akhale pa njila yopita ku imfa?

3 Kucokela pamene Yehova analenga anthu, iye wakhala akuwapatsa malangizo omveka bwino. Mwacitsanzo, m’munda wa Edeni, Yehova anapeleka malangizo omveka bwino otsogolela anthu ku moyo wosatha ndi wacimwemwe. (Genesis 2:15-17) Koma Adamu ndi Hava anakana malangizo amene Atate wao wacikondi anawapatsa. Hava anamvela malangizo amene Satana anapeleka kudzela mwa njoka, ndipo Adamu anamvela mkazi wake. Kodi zotsatilapo zake zinali zotani? Onse aŵili anayamba kuvutika, kenako anafa alibe ciyembekezo ciliconse. Komanso cifukwa ca kusamvela kwao, anthu onse anali pa njila yopita ku imfa.

4. (a) N’cifukwa ciani Mulungu anapeleka malangizo ena pambuyo pa Cigumula? (b) Pamene zinthu zinasintha, kodi Mulungu anaonetsa bwanji maganizo ake?

4 Mulungu anapatsa Nowa malangizo amene anapulumutsa anthu. Cigumula citatha, Yehova analamula anthu kuti asamadye kapena kumwa magazi. N’cifukwa ciani anapeleka lamulo limeneli? Cifukwa cakuti anafuna kupatsa anthu ufulu wakuti azidya nyama. Cifukwa ca kusintha kumeneku, anthu anapatsidwa malangizo atsopano akuti: “Musadye nyama pamodzi ndi magazi ake, amene ndiwo moyo wake.” (Genesis 9:1-4) Lamulo limeneli limatithandiza kudziŵa mmene Mulungu amaonela moyo. Iye ndiye mwiniwake wa moyo. Mulungu ndi Mlengi amene anatipatsa moyo, ndipo ali ndi ufulu wotipatsa malamulo a mmene tiyenela kuonela moyo. Mwacitsanzo, iye analamula kuti munthu safunika kupha mnzake. Mulungu amaona kuti moyo ndi magazi n’zopatulika, ndipo adzalanga aliyense amene amazigwilitsila nchito molakwika.—Genesis 9:5, 6.

5. Kodi tikambilana ciani tsopano? Nanga n’cifukwa ciani?

5 Nowa atafa, Mulungu anapitilizabe kutsogolela anthu ake. M’nkhani ino, tikambilana zitsanzo zocepa zoonetsa mmene Mulungu wakhala akutsogolela anthu ake. Kukambilana zimenezi kutilimbikitsa kutsatila malangizo a Yehova otsogolela ku moyo wosatha.

MTUNDU WATSOPANO UNALANDILA MALANGIZO ATSOPANO

6. N’cifukwa ciani anthu a Mulungu anafunika kumvela malamulo amene Mulungu anawapatsa kudzela mwa Mose? Nanga anafunika kuwaona bwanji malamulowo?

6 M’nthawi ya Mose, Yehova anapatsa anthu ake malangizo omveka bwino pankhani ya makhalidwe ndi kulambila. Anacita zimenezi cifukwa cakuti zinthu zinasinthanso panthawiyo. Kwa zaka zoposa 200, Aisiraeli anali akapolo ku Iguputo. Anthu amene anali kukhala nao kumeneko anali kulambila akufa, kupembedza mafano, ndi kucita zinthu zina zambili zimene Mulungu amadana nazo. Atatulutsidwa mu ukapolo ku Iguputo, anthu a Mulungu anafunika kulandila malangizo atsopano. Yehova anali kufuna kuti io azimvela Cilamulo cake. Mabuku ena amanena kuti liu laciheberi lomasulidwa kuti “cilamulo” ndi logwilizana ndi liu limene limatanthauza “kutsogolela” ndi “kulangiza.” Cilamulo cinateteza Aisiraeli kuti asatengele mitundu yoyandikana nao imene inali kukonda ciwelewele ndi kulambila mafano. Aisiraeli akamvela Mulungu, iye anali kuwadalitsa. Koma akapanda kumumvela, anali kukumana ndi mavuto aakulu.—Ŵelengani Deuteronomo 28:1, 2, 15.

7. (a) N’cifukwa ciani Yehova anapatsa malangizo anthu ake? (b) Kodi Cilamulo cinakhala bwanji mtsogoleli kwa Aisiraeli?

7 Panalinso cifukwa cina cimene Mulungu anapelekela malangizo atsopano. Cilamulo cinathandiza Aisiraeli kukonzekela cocitika cofunika kwambili pokwanilitsa cifunilo ca Yehova. Cocitika cimeneco ndi kubwela kwa Yesu Kristu, yemwe ndi Mesiya. Cilamulo cinali kukumbutsa Aisiraeli kuti ndi opanda ungwilo. Cinawathandizanso kudziŵa kuti anafunika dipo, kapena kuti nsembe yangwilo imene ikanacotselatu ucimo wao wonse. (Agalatiya 3:19; Aheberi 10:1-10) Kuonjezela pamenepo, Cilamulo cinateteza mzele wa makolo a Mesiya ndi kuthandiza Aisiraeli kumuzindikila atabwela. Cotelo, Cilamulo cinali ngati “mtsogoleli” wowafikitsa kwa Kristu.—Agalatiya 3:23, 24.

8. N’cifukwa ciani tiyenela kutsatila mfundo za m’Cilamulo ca Mose?

8 Nafenso Akristu tingapindule ndi Cilamulo cimene Yehova anapeleka. Kodi tingacite ciani kuti tipindule? Tiyenela kuphunzila ndi kumvetsetsa mfundo zimene panazikidwa Cilamulo. Ngakhale kuti sitili pansi pa Cilamulo ca Mose, malangizo ambili opezeka m’Cilamuloci angatithandize pa umoyo wathu wa tsiku ndi tsiku ndi polambila Yehova. Mulungu anaonetsetsa kuti malamulowo alembedwa m’Baibulo n’colinga cakuti tiziphunzilapo cinacake. Anafunanso kuti mfundo zake zizititsogolela komanso kuti tizindikile kuti Yesu anatiphunzitsa mfundo zapamwamba kuposa za m’Cilamulo. Mwacitsanzo, Yesu ananena kuti: “Inu munamva kuti anati, ‘Usacite cigololo.’ Koma ine ndikukuuzani kuti aliyense woyang’anitsitsa mkazi mpaka kumulakalaka, wacita naye kale cigololo mumtima mwake.” Cotelo, sitiyenela kupewa cabe kucita ciwelewele koma tiyenelanso kupewa maganizo ndi zilakolako zoipa zimene zingaticititse ciwelewele.—Mateyu 5:27, 28.

9. Ndi kusintha kotani kumene kunacititsa kuti Mulungu apelekenso malangizo atsopano?

9 Yesu atabwela monga Mesiya, Yehova anapelekanso malangizo atsopano, ndipo anavumbula mfundo zina zambili zokhudza colinga cake. N’cifukwa ciani zimenezi zinali zofunika? Cifukwa cakuti m’caka ca 33 C.E.,Yehova anakana mtundu wa Aisiraeli ndi kusankha mpingo wa Akristu kukhala anthu ake. Cotelo, zinthu zinasinthanso pakati pa anthu a Mulungu.

MALANGIZO OPELEKEDWA KWA ISIRAELI WAUZIMU

10. N’cifukwa ciani mpingo wacikristu unapatsidwa malamulo atsopano? Nanga malamulo amenewo anasiyana bwanji ndi amene Aisiraeli analandila?

10 Yehova anapeleka Cilamulo ca Mose kwa Aisiraeli kuti awaphunzitse mmene anayenela kukhalila ndi mmene anayenela kum’lambilila. Kuyambila m’nthawi ya atumwi, anthu a Mulungu akhala akucokela m’mitundu ndi m’zikhalidwe zosiyanasiyana, ndipo amachedwa Isiraeli wauzimu. Iwo anapanga mpingo wacikristu ndipo anali m’pangano latsopano. Yehova anawapatsa malangizo atsopano, ndipo anaonjezela mfundo zina pa nkhani ya cikhalidwe ndi kulambila. Ndithudi, “Mulungu alibe tsankho. Iye amalandila munthu wocokela mu mtundu uliwonse, amene amamuopa ndi kucita cilungamo.” (Machitidwe 10:34, 35) Akristu oyambilila anali kutsatila “cilamulo ca Kristu,” cimene cinali cozikidwa makamaka pa mfundo zimene zinalembedwa m’mitima yao, osati pa mwala. Kucokela panthawiyo, Akristu onse akhala akutsatila Cilamulo cimeneci, ndipo akupindula.—Agalatiya 6:2.

11. Kodi “cilamulo ca Kristu” cinali kukhudza mbali ziŵili ziti za umoyo wa Mkristu?

11 Isiraeli wauzimu anapindula kwambili ndi malangizo amene Yehova anapeleka kudzela mwa Yesu. Atatsala pang’ono kukhazikitsa pangano latsopano, Yesu anapeleka malamulo aŵili ofunika kwambili. Lamulo loyamba linali lokhudza nchito yolalikila. Laciŵili linali lokhudza mmene Akristu ayenela kukhalila ndi mmene ayenela kucitila zinthu ndi Akristu anzao. Malamulo amenewa anapelekedwa kwa Akristu onse. Cotelo tonsefe tiyenela kuwatsatila, kaya tili ndi ciyembekezo codzakhala ndi moyo wosatha kumwamba kapena padziko lapansi.

12. N’ciani cinasintha pa nchito yolalikila?

12 Kale, anthu anali kupita ku Isiraeli kukatumikila Yehova. (1 Mafumu 8:41-43) Koma m’kupita kwa nthawi, Yesu anapeleka lamulo limene lili pa Mateyu 28:19, 20. (Ŵelengani.) Yesu anauza ophunzila ake kuti ‘apite’ kwa anthu onse. Pa Pentekosite mu 33 C.E., Yehova anaonetsa kuti amafuna kuti uthenga wabwino ulalikidwe padziko lonse lapansi. Tsiku limenelo, anthu 120 a mumpingo watsopano wacikristu anadzazidwa ndi mzimu woyela ndipo anayamba kulankhula zinenelo zosiyanasiyana kwa Ayuda ndi anthu otembenukila ku Ciyuda. (Machitidwe 2:4-11) Kenako, gawo lao linakula ndipo anayamba kulalikila ngakhale kwa Asamariya. Ndiyeno, m’caka ca 36.C.E., gawo lao linakula kwambili cifukwa anayamba kulalikila ngakhale kwa anthu osadulidwa. Zimenezi zinatanthauza kuti Akristu anayenela kulalikila munthu aliyense padziko lapansi.

13, 14. Kodi “lamulo latsopano” limene Yesu anapeleka limaphatikizapo ciani? (b) Tikuphunzila ciani pa citsanzo cimene Yesu anapeleka?

13 Yesu anapeleka “lamulo latsopano” la mmene Akristu ayenela kucitila zinthu ndi abale ndi alongo ao. (Ŵelengani Yohane 13:34, 35.) Tifunika kukonda abale athu nthawi zonse, koma tifunikanso kukhala okonzeka kuwafela. Lamulo limeneli munalibe m’Cilamulo ca Mose.—Mateyu 22:39; 1 Yohane 3:16.

14 Yesu ndi citsanzo cabwino kwambili ca munthu amene anaonetsa cikondi codzimana cotelo. Iye anali kukonda kwambili ophunzila ake moti anapeleka moyo wake cifukwa ca io. Ndipo amafuna kuti otsatila ake onse azicita cimodzimodzi. Conco, tiyenela kukhala okonzeka kuvutikila abale ndi alongo athu ngakhale kuwafela kumene.—1 Atesalonika 2:8.

MALANGIZO A MASIKU ANO NDIPONSO AMTSOGOLO

15, 16. Kodi zinthu zasintha bwanji masiku ano? Nanga Mulungu amatitsogolela bwanji?

15 Yesu anaika “kapolo wokhulupilika ndi wanzelu” kuti azipeleka “cakudya [cakuuzimu] pa nthawi yoyenela” kwa otsatila ake. (Mateyu 24:45-47) Cakudya cimeneci cikuphatikizapo malangizo ofunika kwambili amene anthu a Mulungu amalandila zinthu zikasintha. Kodi zinthu zasintha bwanji masiku ano?

16 Tikukhala ‘m’masiku otsiliza,’ ndipo posacedwapa tikumana ndi cisautso cacikulu cimene sicinacitikepo n’kale lonse. (2 Timoteyo 3:1; Maliko 13:19) Komanso Satana ndi ziŵanda zake anacotsedwa kumwamba ndi kuponyedwa kudziko lapansi. Zimenezi zinacititsa kuti anthufe tiyambe kuvutika kwambili. (Chivumbulutso 12:9, 12) Kuonjezela pamenepa, tikutsatila lamulo la Yesu mwa kulalikila anthu ambili padziko lonse lapansi m’zinenelo zambili kuposa kale lonse!

17, 18. Kodi tiyenela kucita ciani ndi malangizo amene timalandila?

17 Gulu la Mulungu limatipatsa zida zambili zotithandiza pa nchito yolalikila. Kodi inuyo mumazigwilitsila nchito? Pa misonkhano yathu, timalandila malangizo a mmene tingagwilitsile nchito mwaluso zida zimenezi. Kodi mumaona kuti malangizo amenewa ndi ocokeladi kwa Mulungu?

18 Kuti tilandile madalitso a Mulungu, tifunika kutsatila malangizo amene iye amatipatsa kudzela mumpingo wacikristu. Tikakhala omvela masiku ano, cidzakhala cosavuta kutsatila malangizo pa “cisautso cacikulu,” pamene dongosolo lonse loipa la Satana lidzaonongedwa. (Mateyu 24:21) Pambuyo pa cisautso cacikulu, tidzalandila malangizo atsopano amene tidzayenela kutsatila m’dziko latsopano limene simudzakhala Satana.

M’dziko latsopano, tidzalandila mipukutu ya malangizo atsopano amene tidzayenela kutsatila (Onani ndime 19 ndi 20)

19, 20. Ndi mipukutu yotani imene idzafunyululidwa mtsogolo?

19 M’nthawi ya Mose, mtundu wa Isiraeli unafunikila malangizo atsopano. Cotelo, Mulungu anawapatsa Cilamulo ca Mose. Pambuyo pake, mpingo wacikristu unayamba kutsatila “cilamulo ca Kristu.” Mofananamo, Baibulo limatiuza kuti m’dziko latsopano tidzalandila mipukutu ya malangizo atsopano. (Ŵelengani Chivumbulutso 20:12.) Mwacionekele, mipukutuyo idzafotokoza malangizo amene Yehova adzafuna kuti anthu azitsatila panthawiyo. Mwa kuphunzila mipukutu imeneyi, anthu onse, kuphatikizapo oukitsidwa, adzatha kudziŵa zimene Mulungu afuna kuti io acite. Mipukutuyo idzatithandiza kumvetsa maganizo a Yehova. Ndiponso tidzalimvetsetsa Baibulo, moti m’Paradaiso tidzayamba kucita zinthu mwacikondi kwambili, ndi mwaulemu kwa anzathu. (Yesaya 26:9) N’zoonekelatu kuti padzakhala zinthu zoculuka zimene tidzaphunzila ndi kuphunzitsa ena motsogoleledwa ndi Mfumu yathu, Yesu Kristu.

20 Tikadzamvela malangizo ‘olembedwa m’mipukutuyo’ ndi kukhalabe okhulupilika kwa Yehova pa ciyeso comaliza, iye adzalemba maina athu mu “mpukutu wa moyo.” Tilidi ndi mwai wolandila moyo wosatha. Motelo, tifunika kupatula nthawi yoŵelenga Baibulo, kusinkhasinkha kuti tilimvetsetse, ndi kutsatila malangizo ake. Tikamacita zimenezi, tidzapulumuka cisautso cacikulu ndi kusangalala cifukwa cophunzila za Yehova Mulungu wathu wanzelu ndi wacikondi kwamuyaya.—Mlaliki 3:11; Aroma 11:33.