Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Wacicepele, Limbitsa Cikhulupililo Cako

Wacicepele, Limbitsa Cikhulupililo Cako

“Cikhulupililo ndico . . . umboni wooneka wa zinthu zenizeni, ngakhale kuti n’zosaoneka.”—AHEB. 11:1.

NYIMBO: 41, 69

1, 2. Kodi nthawi zina acicepele angakhumbile ciani? Nanga ni masitepu ati amene angathandize?

MLONGO wacicepele ku Britain anauzidwa na mnzake kusukulu kuti: “Zoona munthu wanzelu monga iwe umakhulupilila Mulungu!” M’bale wacicepele ku Germany analemba kuti: “Matica kusukulu kwathu amaona kuti nkhani za m’Baibulo ni nthano cabe. Ndipo amangoona ngati ana a sukulu onse amakhulupilila za cisanduliko.” Mlongo wacicepele ku France anati: “Matica kusukulu kwathu amadabwa ngako akamvela kuti pakali ana a sukulu amene amakhulupilila Baibulo.”

2 Monga mtumiki wacicepele wa Yehova, kapena wophunzila za iye, tidziŵa kuti iwe umakhulupilila mwa Mlengi. Koma kodi nthawi zina, umakhumbila zimene anzako ambili amakhulupilila, monga ciphunzitso ca cisanduliko? Ngati inde, pali masitepu amene angakuthandize kulimbilitsa cikhulupililo cako. Sitepu yoyamba ni kuseŵenzetsa luso la kulingalila limene Mulungu anakupatsa. Luso limenelo ‘lidzakuyang’anila’ na kukucinjiliza ku ziphunzitso zimene zingawononge cikhulupililo cako.—Ŵelengani Miyambo 2:10-12.

3. Kodi tidzakambilana ciani m’nkhani ino?

3 Cikhulupililo ceni-ceni cimacokela pa kum’dziŵa bwino Mulungu. (1 Tim. 2:4) Conco, pamene uphunzila Mau a Mulungu na zofalitsa zathu, osangoŵelenga mwacisawawa yayi. Uziseŵenzetsa luso lako la kulingalila kuti ‘uzindikile tanthauzo’ la zimene uŵelenga. (Mat. 13:23) M’nkhani ino, tidzaona mmene kucita zimenezi kungakuthandizile kulimbitsa cikhululupililo cako mwa Mulungu Mlengi, na m’Mau ake Baibulo. Ndipo pali maumboni ambili otsimikizilika okhudza nkhani zimenezi.—Aheb. 11:1.

MMENE UNGALIMBITSILE CIKHULUPILILO CAKO

4. N’cifukwa ciani kuvomeleza za Mulungu kaya za cisanduliko, konse kumaloŵetsapo cikhulupililo? Nanga muyenela kucitanji kuti mudziŵe zeni-zeni?

4 Kodi unamvelako anthu amene amakamba kuti amakhulupilila cisanduliko cifukwa ni sayansi, osati za Mulungu cifukwa amati ni za cikhulupililo cabe? Ambili amaganiza conco. Koma dziŵa izi: Kaya munthu amavomeleza za Mulungu kapena za cisanduliko, nkhani ya cikhulupililo imakhalapo ndithu. Tifunse conco. Kodi alipo munthu anaonapo Mulungu, kapena kuonako pamene anali kulenga cinthu ciliconse? (Yoh. 1:18) Kodi kuli munthu aliyense—wasayansi kapena wina—amene anaonapo camoyo cina cikusandulika n’kukhala ca mtundu wina? Monga njoka kapena buluzi kusanduka mkango kapena njovu? (Yobu 38:1, 4) Conco, tonse tifunika kuona umboni na kuseŵenzetsa luso lathu la kulingalila kuti tidziŵe zeni-zeni. Pokamba za cilengedwe, mtumwi Paulo analemba kuti: “Makhalidwe a Mulungu osaoneka ndi maso akuonekela bwino. Makhalidwe a Mulungu amenewa, ngakhalenso mphamvu zake zosatha, ndiponso Umulungu wake, zikuonekela [zizindikilika] m’zinthu zimene anapanga moti anthuwo alibenso cifukwa comveka cosakhulupilila kuti kuli Mulungu.”—Aroma 1:20.

Pokambilana ndi ena, uziseŵenzetsa zida zimene zilipo m’cinenelo canu (Onani ndime 5)

5. Kodi tapatsidwa zida ziti zotithandiza kuseŵenzetsa luso la kulingalila?

5 Kuzindikila kumatanthauza kudziŵa cinthu cobisika kapena cosaonekela msanga. (Aheb. 11:3) Ndiye cifukwa cake anthu ozindikila amaseŵenzetsa kwambili maganizo awo, osati maso na matu cabe yayi. Gulu la Yehova lapeleka zida zambili zofufuzila nkhani. Zida zimenezo zimatithandiza ‘kuona’ Mlengi wathu ndi maso athu a cikhulupililo. (Aheb. 11:27) Zina mwa zida zimenezo ni vidiyo yakuti The Wonders of Creation Reveal God’s Glory, kabuku kakuti Was Life Created? na kakuti The Origin of Life—Five Questions Worth Asking, na buku yakuti Is There a Creator Who Cares About You? M’magazini athu mumakhalanso nkhani zabwino zofuna kuseŵenzetsa luso la kulingalila. Mu Galamukani! mumakhalako nkhani zofunsa asayansi ndi akatswili ena kuti afotokoze cimene cinapangitsa kuti ayambe kukhulupilila Mulungu. Nkhani zakuti “Kodi Zinangocitika Zokha?” zimaonetsa zinthu zacilengedwe zopangidwa mwa luso lapamwamba kwambili. Ngakhale asayansi akopelako zacilengedwe zimenezo.

6. Kodi mwapindula bwanji poseŵenzetsa zida zimene tili nazo?

6 Kunena za tumabuku tumene tachula pamwambapa, m’bale wa ku America wa wazaka 19 anakamba kuti: “Tumabuku utu twan’thandiza kwambili. Natuŵelenga nthawi zambili.” Mlongo wina ku France anati: “Nkhani zakuti ‘Kodi Zinangocitika Zokha?’ nimazikonda ngako! Zimaonetsa kuti, ngakhale kuti akatswili opanga zinthu ali na luso lapatali, safikako olo pang’ono kwa amene anapanga zacilengedwe.” Makolo a wacicepele wa zaka 15 ku South Africa anati: “Mwana wathu akangolandila Galamukani! amathamangila pa mbali ‘yofunsa munthu mafunso.’” Nanga iwe? Kodi umapatula nthawi yoŵelenga nkhani zimenezi? Zingakuthandize kuti cikhulupililo cako cikhale monga mtengo wa mizu yofika patali. Mwa ici, udzakhala na cikhulupililo cokuthandiza kulimbana ndi zimphepo za ciphunzitso conama.—Yer. 17:5-8.

KUKHULUPILILA BAIBULO

7. N’cifukwa ciani Mulungu amafuna kuti acicepele aziseŵenzetsa luso la kuganiza?

7 Kodi n’kulakwa kufunsa moona mtima mafunso okhudza Baibulo? Iyai. Yehova amafuna kuti uziseŵenzetsa ‘luso la kuganiza’ kuti udziŵe coonadi. Safuna kuti uzingotengela cikhulupililo ca ena. Conco, uziseŵenzetsanso mutu kuti upeze cidziŵitso colongosoka. Cidziŵitso cimeneco cidzakhala maziko olimba a cikhulupililo ceni-ceni. (Ŵelengani Aroma 12:1, 2; 1 Timoteyo 2:4.) Njila ina imene ungakhalile na cidziŵitso n’kukhalako na mapulojekiti osankha nkhani kapena buku imene ufuna kuiphunzila mwapadela.

8, 9. (a) Ni mapulojekiti aphindu ati amene mungakonde kucitako? (b) Nanga ena apindula bwanji posinkhasinkha pa zimene aŵelenga?

8 Anzako ena asankha mapulojekiti ophunzila maulosi a m’Baibulo, kapena zimene Baibulo yakambapo pa nkhani zokhudza mbili yakale, zofukula m’matongwe, ndi za sayansi. Ulosi wocititsa cidwi kwambili ni wa pa Genesis 3:15. Lembali limatidziŵitsa za nkhani ikulu m’Baibulo yonse. Nkhaniyo ni kukweza ucifumu wa Mulungu na kuyeletsa dzina lake kupitila mu Ufumu wake. Lemba limodzi limeneli, mwa mau ophiphilitsa, limaonetsa mmene Yehova adzacotsela mavuto onse amene anthu akumana nawo kuyambila mu Edeni. Kodi ungaliphunzile bwanji lemba la Genesis 3:15? Ungalembe chati na kuikapo malemba oonetsa mmene Mulungu anaunikila pang’ono-pang’ono zokhudza anthu na makonzedwe ochulidwa pa lemba limeneli, na mmene ulosi umenewu udzakwanilitsidwila. Pamene uona kugwilizana bwino kwa malemba, iwenso udzavomeleza kuti n’zoona aneneli a m’Baibulo ndi alembi ake ‘anatsogoleledwa na mzimu woyela.’—2 Pet. 1:21.

9 M’bale wina ku Germany anacita cidwi kuti buku iliyonse m’Baibulo ili na mfundo zokhudza Ufumu wa Mulungu. Iye anati: “Zili conco ngakhale kuti Baibulo inalembedwa ndi anthu 40. Ambili a iwo anakhalako pa nthawi zosiyana-siyana ndipo sanali kudziŵana.” Mlongo wina ku Australia anakhudzika mtima ataŵelenga nkhani yofotokoza tanthauzo la Pasika mu Nsanja ya Mlonda ya December 15, 2013. Pali kugwilizana kwakukulu pakati pa Lemba la Genesis 3:15, mwambo wa Pasika, ndi kubwela kwa Mesiya. Mlongoyo anapitiliza kuti: “Nkhani imeneyo inan’thandiza kuona ubwino waukulu wa Yehova. Mmene iye anacitila makonzedwe a Pasika kwa Aisiraeli, na mmene anakwanilitsidwila pa Yesu, zinanifika pamtima kwambili! N’naganizilapo kwambili za cakudya ca Pasika cokambidwa m’maulosi.” Kodi mlongoyu anamvela conco cifukwa ciani? Cifukwa anaganizila mozama pa zimene anaŵelenga na “kuzindikila tanthauzo lake.”—Mat. 13:23.

10. N’ciani cimatithandiza kukhulupilila zimene olemba Baibulo analemba?

10 Cina cimene cingalimbikitse cikhulupililo cako ni kuona mmene olemba Baibulo analili oona mtima ndi opanda mantha. Olemba nkhani ambili akale anali kukometsela nkhani kuti akondweletse mafumu awo na kukweza mtundu wawo. Koma aneneli a Yehova anali kungolemba zoona basi, ngakhale zolakwa za anthu a mtundu wawo, ngakhalenso za mafumu awo. (2 Mbiri 16:9, 10; 24:18-22) Komanso sanali kubisa olo zolakwa za iwo eni, ndi za atumiki ena a Yehova. (2 Sam. 12:1-14; Maliko 14:50) M’bale wacicepele ku Britain anati: “Kuona mtima kwa conco n’kosoŵa kwambili. Ni umboni wakuti Baibulo inacokeladi kwa Yehova.”

11. Kodi acicepele angazindikile bwanji phindu la mfundo za m’Baibulo?

11 Poona mfundo za m’Baibulo zothandiza, anthu afika povomeleza kuti n’zoona inauzilidwadi na Mulungu. (Ŵelengani Salimo 19:7-11.) Wacicepele wina ku Japan analemba kuti: “Pamene tinayamba kutsatila mfundo za m’Baibulo m’banja mwathu, timakhala acimwemwe kwambili. Timakhala amtendele, ogwilizana, ndi okondana.” Mfundo za m’Baibulo zimaticinjiliza ku cipembedzo conyenga ndi zamalaulo zimene zimamanga anthu mu ukapolo. (Sal. 115:3-8) Kodi maganizo akuti kulibe Mulungu amasoceletsa anthu zoona? Ziphunzitso monga cisanduliko zimatenga cilengedwe kukhala mulungu, ndi kucipatsa mphamvu zimene kweni-kweni n’za Yehova yekha. Amene amati kulibe Mulungu amakamba kuti tsogolo lathu lonse lili m’manja mwathu.—Sal. 146:3, 4.

POKAMBILANA NDI ENA

12, 13. Uyenela kucita bwanji kuti ukambilane bwino za cilengedwe kapena za Baibulo na anzako a kusukulu, matica, ndi ena?

12 Monga wacicepele, kodi ungathandize bwanji anthu mogwila mtima pokambilana nawo za cilengedwe na za Baibulo? Coyamba, osafulumila kuganiza kuti udziŵa zimene ena amakhulupilila. Anthu ena amati amakhulupilila cisanduliko, koma amaganizanso kuti Mulungu aliko. Amaganiza kuti Mulungu anaseŵenzetsa cisanduliko kupanga zinthu zosiyana-siyana. Ena amaona kuti sembe cisanduliko si coona, sembe saciphunzitsa ku sukulu. Palinso amene amaleka kukhulupilila Mulungu cifukwa cokhumudwa na zocitika za cipembedzo. Conco, pokambilana ndi munthu mmene moyo unayambila, ni bwino kum’funsako mafunso coyamba. Yamba wadziŵa zimene amakhulupilila. Ngati uonetsa kumuganizila na kumvetsela zokamba zake, nayenso adzamvetsela zimene ukamba.—Tito 3:2.

13 Ngati munthu wina atsutsa cikhulupililo cako pa cilengedwe, mosamala ungam’bwezele nkhaniyo. Ungam’pemphe kuti afotokoze mmene moyo unayambila popanda Mlengi. Kuti moyo woyamba upitilize, unafunikila kubala wina—winanso kubala unzake, ndi kupitiliza conco. Pulofesa wina wa chemistry anati: “Kuti moyo upitilize pamafunikila (1) cibelekelo, (2) mphamvu ya moyo, (3) malangizo a m’majini, ndi (4) mphamvu yokopela malangizo a m’majiniwo. Ngakhale kamoyo kakang’ono-ng’ono, moyo wake ni wocolowana modabwitsa kwambili.”

14. Mungacite bwanji ngati muona kuti simungafotokoze bwino-bwino za cisanduliko kapena cilengedwe?

14 Ngati uona kuti sungakwanitse kufotokoza bwino-bwino za cisanduliko kapena za cilengedwe, ungayese njila yosavuta imene Paulo anaseŵenzetsa. Iye anati: “Nyumba iliyonse inamangidwa ndi winawake, koma amene anapanga zinthu zonse ndi Mulungu.” (Aheb. 3:4) Kufotokoza mwa njila imeneyi n’kwabwino ndipo n’kofika pamtima. Zoona, kuseli kwa cinthu ciliconse copangidwa mwaluso kuli munthu wanzelu. Ungagwilitsilenso nchito cofalitsa coyenelela. Mlongo wina anaseŵenzetsa tumabuku tuŵili tumene tatomola m’ndime 5 pokambilana na mnyamata wina amene anayamba kukhulupilila za cisanduliko cifukwa coganiza kuti Mulungu kulibe. Patapita monga wiki imodzi, mnyamata uja anasintha maganizo. Anati: “Nakhulupilila lomba kuti Mulungu aliko.” Phunzilo la Baibulo linakhazikitsidwa, ndipo pano tikamba mnyamatayo ni m’bale.

15, 16. Kodi mungakambilane bwanji za Baibulo ndi anthu? Ndipo colinga canu ciyenela kukhala ciani?

15 Ungaseŵenzetse njila yofananayo pokambilana ndi munthu wokaikila za Baibulo. Coyamba, dziŵa zimene iye amakhulupilila na nkhani zimene angakonde kuti mukambilane. (Miy. 18:13) Ngati amakonda nkhani za sayansi, angafune kukambapo ukachula mmene Baibulo imakambila zoona za sayansi. Anthu ena angakhudzike mtima akamvela mmene Baibulo imakambila zoona pa maulosi ndi mbili yakale. Ungachulenso mfundo zothandiza za m’Baibulo, monga zopezeka mu Ulaliki wa pa Phili.

16 Kumbukila, colinga cako ni kuwafika pamtima anthu, osati kuwagometsa iyai. Conco, uzikhala mnvetseli wabwino. Uzifunsa mafunso moona mtima, ndi kukamba modzicepetsa ndi mwaulemu, maka-maka pokambilana ndi acikulile. Ukamatelo, ena nawonso azikumvetsela mwaulemu. Azionanso kuti zimene umakhulupilila unaziganizilapo mozama. N’zimene acicepele ambili sacita. Komanso, kumbukila kuti suyenela kuyankha munthu aliyense amene angofuna kutsutsana nawe, kapena wongofuna kuseka zimene umakhulupilila.—Miy. 26:4.

TENGA COONADI KUKHALA CAKO-CAKO

17, 18. (a) N’ciani cingakuthandizeni kutenga coonadi kukhala canu-canu? (b) Tidzakambilana funso lakuti ciani m’nkhani yotsatila?

17 Ngati ungodziŵa cabe ziphunzitso zoyambilila za m’Baibulo, sungakhale na cikhulupililo colimba kweni-kweni. Conco, uyenela kukumba mozama, ngati kuti ufuna-funa miyala ya mtengo wapatali. (Miy. 2:3-6) Uziseŵenzetsa zida zofufuzila zimene zilipo m’cinenelo canu, monga DVD ya Watchtower Library, LAIBULALE YA PA INTANETI, komanso Watch Tower Publications Index, kapena Buku Lofufuzila Nkhani la Mboni za Yehova. Ndiponso, dziikile colinga coŵelenga Baibulo yonse. Ungayese kuitsiliza m’miyezi 12 cabe. Palibe cinthu cingalimbitse cikhulupililo cako kupambana kuŵelenga Mau a Mulungu. Pokumbukila pamene anali wacicepele, wadela wina anati: “Kuŵelenga Baibulo yonse n’kumene kunan’thandiza kutsimikiza kuti Baibulo ni Maudi a Mulungu. M’pamene n’namvetsetsa nkhani za m’Baibulo zimene n’naphunzila pamene n’nali mwana kwambili. Apa m’pamene n’natengela coonadi kukhala canga-canga.”

18 Inu makolo, mumacita mbali yaikulu yothandiza ana anu kukula kuuzimu. Nanga mungawathandizenso bwanji kukhala na cikhulupililo colimba? Ndiyo nkhani imene tidzakambilana mlungu wamawa.