Khalani Okoma Mtima Komanso Oganizila Ena Monga Yehova
“Wodala ndi munthu amene amacita zinthu moganizila munthu wonyozeka.”—SAL. 41:1.
1. Kodi cikondi cimaonekela bwanji pakati pa anthu a Mulungu?
ANTHU a Mulungu ni banja lauzimu, ndipo amadziŵika na khalidwe la cikondi. (1 Yoh. 4:16, 21) Nthawi zina, cikondi cawo cimaonekela pa zinthu zazikulu zimene amacita pothandiza abale awo. Koma cimaonekela kwambili pa zinthu zing’ono-zing’ono zimene amacitilana kaŵili-kaŵili, monga kukamba mau olimbikitsa na kucita zinthu mokoma mtima. Tikakhala okoma mtima na oganizila ena, ndiye kuti ‘tikutsanzila Mulungu, monga ana ake okondedwa.’—Aef. 5:1.
2. Kodi Yesu anaonetsa bwanji cikondi monga ca Atate wake?
2 Yesu anatengela kwambili Atate wake. Iye anati: “Bwelani kwa ine nonsenu ogwila nchito yolemetsa ndi olemedwa, ndipo ndidzakutsitsimutsani. . . , cifukwa ndine wofatsa ndi wodzicepetsa.” (Mat. 11:28, 29) Ngati titengela Khristu mwa ‘kucita zinthu moganizila anthu onyozeka,’ tidzayanjidwa na Atate wathu wakumwamba komanso tidzapeza cimwemwe coculuka. (Sal. 41:1) Lomba tiyeni tikambilane mmene tingaonetsele kuti timaganizila ena m’banja, mu mpingo, na mu ulaliki.
KHALANI OGANIZILA ENA M’BANJA
3. Kodi mwamuna angaonetse bwanji kuti amaganizila mkazi wake na kumumvetsetsa? (Onani pikica kuciyambi.)
3 Amuna ayenela kukhala citsanzo cabwino m’banja pa nkhani yoganizila ena. (Aef. 5:25; 6:4) Mwacitsanzo, iwo amalangizidwa kuti ayenela kukhala na akazi awo “mowadziŵa bwino.” Mau amenewa angamasulidwenso kuti “kuwaganizila kapena kuwamvetsetsa.” (1 Pet. 3:7) Kumvetsetsa munthu na kum’ganizila zimayendela pamodzi. Mwacitsanzo, mwamuna amene amamvetsetsa mkazi wake amadziŵa kuti mkaziyo, amene ni mnzake womuyenelela, ni wosiyana naye m’njila zambili. Koma samuona monga munthu wa pansi. (Gen. 2:18) Conco, amayesetsa kucita zinthu mom’ganizila, na kum’patsa ulemu. Pokamba za mwamuna wake, mlongo wina wa ku Canada anati: “Mwamuna wanga amakamba na kucita zinthu moniganizila nthawi zonse. Sakamba mau monga akuti, ‘Ni nkhaninso imeneyi, n’zocepa izi.’ Komanso, amamvetsela mwachelu pamene nikamba naye. Poniwongolela nikalakwitsa, amacita zinthu mokoma mtima.”
4. Pocita zinthu na akazi ena, kodi mwamuna angaonetse bwanji kuti amam’ganizila mkazi wake?
4 Cinanso, mwamuna woganizila mkazi wake amayesetsa kukhala wosamala pocita zinthu na akazi ena. Iye amapewa kuceza mokopana na akazi ena, kapena kucita zinthu zoonetsa kuti amawakhumbila. Amapewa kucita izi ngakhale pa mawebusaiti amene amapitapo, kapena poseŵenzetsa njila zocezela pa intaneti. (Yobu 31:1) Inde, iye amayesetsa kukhala wokhulupilika kwa mkazi wake, osati cabe cifukwa cokonda mkaziyo, koma cifukwanso cokonda Mulungu na kuzonda coipa.—Ŵelengani Salimo 19:14; 97:10.
5. Kodi mkazi angaonetse bwanji kuti amam’ganizila mwamuna wake?
5 Ngati mwamuna atengela citsanzo ca mutu wake, Yesu Khristu, mkazi amayamba ‘kumulemekeza kwambili.’ (Aef. 5:22-25, 33) Ndipo mkazi amene amalemekeza mwamuna wake, amayesetsa kucita naye zinthu mom’ganizila ndi mokoma mtima, maka-maka pamene mwamunayo ali na zambili zofunika kucita posamalila udindo wake mu mpingo, kapena ngati ni wopanikizika maganizo cifukwa ca mavuto. Mwamuna wina wa ku Britain anati: “Nthawi zina, mkazi wanga akangoona mmene nkhope yanga ikuonekela, amadziŵa kuti cinacake cikunivutitsa maganizo. Zikakhala conco, amaseŵenzetsa mfundo ya pa Miyambo 20:5. Ndipo nthawi zina, amayembekezela kwa nthawi yaitali ndithu, mpaka atapeza mpata wabwino wofunsa cimene cikunivutitsa maganizo. Ikakhala nkhani yakuti ningamuuze, nimam’fotokozela.”
6. Kodi tonse mumpingo tingalimbikitse bwanji ana kukhala oganizila ena? Nanga kukhala oganizila ena kungawapindulitse bwanji anawo?
6 Ngati makolo amacita zinthu moganizilana, amapeleka citsanzo cabwino kwa ana awo. Makolo ali na udindo waukulu wophunzitsa ana kukhala oganizila ena. Mwacitsanzo, angaphunzitse ana awo kuti asamathamange-thamange kapena kuseŵela m’Nyumba ya Ufumu. Komanso, pa maceza acikhristu, makolo angauze ana awo kuti apatse mpata acikulile wotenga cakudya iwo asanatenge. Aliyense mu mpingo angathandize makolo kuphunzitsa ana kukhala oganizila ena. Mwacitsanzo, ngati mwana waticitila zina zake zabwino, monga kutitsegulila citseko, tingacite bwino kumuyamikila. Kucita izi kungam’limbikitse, komanso kungakhomeleze mumtima mwake mfundo yakuti, “Kupatsa kumabweletsa cimwemwe coculuka kuposa kulandila.”—Mac. 20:35.
‘TIZILIMBIKITSANA’ MU MPINGO
7. Kodi Yesu anaonetsa bwanji kum’ganizila munthu amene anali wogontha? Nanga tiphunzilapo ciani pa citsanzo cimeneci ca Yesu?
7 Tsiku lina pamene Yesu anali ku Dekapole, anthu “anam’bweletsela munthu wogontha komanso wovutika kulankhula.” (Maliko 7:31-35) Yesu sanam’cilitsile pa gulu munthuyo. Koma ‘anam’tenga ndi kucoka naye pakhamu la anthulo.’ Kenako anam’cilitsa. N’cifukwa ciani anacita zimenezi? Zioneka kuti munthuyo sanali kukhala womasuka pa gulu cifukwa ca vuto lakelo. Pozindikila zimenezi, mwina n’cifukwa cake Yesu anamutengela pambali. Ise sitingathe kucilitsa anthu mozizwitsa. Koma tingathe kuganizila zosoŵa za Akhristu anzathu na kuwathandiza. Ndipo izi n’zimene tiyenela kucita. Mtumwi Paulo analemba kuti: “Tiyeni tiganizilane kuti tilimbikitsane pa cikondi ndi nchito zabwino.” (Aheb. 10:24) Yesu anadziŵa mmene munthu wogontha uja anali kumvelela, ndipo anacita zinthu mom’ganizila. Kodi ici si citsanzo cabwino kwa ise?
8, 9. Tingaonetse bwanji kuti timaganizila okalamba na odwala? Fotokozani zitsanzo.
8 Muzicita zinthu moganizila okalamba ndi odwala. Mpingo wacikhristu umadziŵika kwambili na cikondi, osati cabe mzimu wa cangu pa nchito. (Yoh. 13:34, 35) Cikondi cimeneci cimatilimbikitsa kuyesetsa kuthandiza acikulile na olemala kupezeka pa misonkhano na kulalikila uthenga wabwino wa Ufumu. Timacita izi olo kuti zimene iwo angacite mu ulaliki n’zocepa. (Mat. 13:23) M’bale wina wolemala, dzina lake Michael, amene amayendela pa kanjinga ka olemala, amayamikila kwambili thandizo limene amalandila kucokela kwa a m’banja lake, komanso abale a m’kagulu kake ka ulaliki. Iye anati: “Cifukwa ca thandizo lawo, nimakwanitsa kupezeka pa misonkhano na kulalikila mokhazikika. Ulaliki nimaukonda maningi, maka-maka wa poyela.”
9 Pa nyumba zambili za Beteli, pali abale na alongo okalamba na odwala. Abale oyang’anila acikondi amaonetsa kuti amaganizila Akhristu okhulupilika amenewa mwa kuwapangila makonzedwe ocita ulaliki wa makalata ndi wa pa foni. “Timayamikila kwambili mwayi wocita ulaliki wa makalata,” anatelo m’bale Bill wa zaka 86, amene amalalikila mwa kulembela makalata anthu okhala ku madela akutali. Mlongo Nancy, wa zaka 90 anati: “Siniona kulemba makalata monga nchito wamba. Koma nimaona kuti ni utumiki ndithu. Anthu afunika kuphunzila coonadi!” Mlongo Ethel, amene anabadwa mu 1921, anati: “Zoŵaŵa m’thupi mwanga sizikutha. Ndipo masiku ena, ngakhale kuvala zovala kumanivuta.” Ngakhale n’conco, mlongoyo amakonda kucita ulaliki wa pa foni, ndipo pali anthu acidwi amene amacitako ulendo wobwelelako. Nayenso Barbara, mlongo wa zaka 85 anati: “Cifukwa codwala-dwala, nthawi zambili zimanivuta kuyenda mu ulaliki. Koma ulaliki wa pa foni umanipatsa mwayi wouzako anthu uthenga wabwino. Nimam’yamikila ngako Yehova!” Kwa miyezi, gulu lina la Akhristu okalamba linathela maola 1,228 pa nchito yolalikila. Komanso analemba makalata 6,265, analalikila pafoni maulendo opitilila 2,000, na kugaŵila zofalitsa 6,315. Ndithudi, Yehova anakondwela kwambili poona kudzipeleka kwawo!—Miy. 27:11.
10. Tingawathandize bwanji abale athu kuti azipindula mokwanila na misonkhano?
10 Muziganizila ena pa misonkhano. Timafuna kuti abale athu azipindula mokwanila na misonkhano. Kuti izi zitheke, tiyenela kucita zinthu mowaganizila. Tingaonetse bwanji kuti timawaganizila? Njila imodzi ni kufika mofulumila pa msonkhano kuti tisawasokoneze pamene akumvetsela mapulogilamu. N’zoona kuti nthawi zina tingacedwe cifukwa ca zocitika zosayembekezeleka. Koma ngati tili na cizoloŵezi cocedwa, tiyenela kuwongolela kuti tionetse kuti timaganizila ena. Cinanso, tizikumbukila kuti Yehova na Yesu ndiwo amatiitana kuti tibwele kudzasonkhana. (Mat. 18:20) Tifunika kuwalemekeza mwa kufika mwamsanga pa misonkhano.
11. N’cifukwa ciani abale amene amakhala na mbali pa misonkhano ayenela kutsatila malangizo a pa 1 Akorinto 14:40?
11 Kuganizila abale athu kumaphatikizaponso kutsatila malangizo akuti: “Zinthu zonse zizicitika moyenela ndi mwadongosolo.” (1 Akor. 14:40) Abale amene ali na mbali pa msonkhano, angaonetse kuganizila ena mwa kusunga nthawi. Ngati m’bale asunga nthawi, amaonetsa kuti akuganizila mkambi wotsatila, komanso mpingo wonse. Mwacitsanzo, abale ena akakomboka amafunika kuyenda msenga wautali kubwelela ku nyumba. Ena amayenda pa mamotoka ocita kulipila. Ndipo enanso ali na mwamuna kapena mkazi wosakhulupilila, amene angakhumudwe ngati acedwa kufika pa nyumba.
12. N’cifukwa ciani akulu amene amatumikila mwakhama tiyenela ‘kuwapatsa ulemu waukulu mwacikondi’? (Onani bokosi yakuti, “ Muzicita Zinthu Moganizila Abale Amene Amatsogolela.”)
12 Abusa auzimu amene amatumikila modzipeleka mu mpingo komanso kutsogolela mwakhama pa nchito yolalikila, tiyenela kuwaganizila kwambili. (Ŵelengani 1 Atesalonika 5:12, 13.) Mwacionekele, mumayamikila zimene akulu amacita potisamalila mwauzimu. Conco, muziyesetsa kuonetsa kuyamikila kwanu mwa kuwamvela na kuwacilikiza. Tizikumbukila kuti ‘iwo amayang’anila miyoyo yathu monga anthu amene adzayankhe mlandu.’—Aheb. 13:7, 17.
MUZIGANIZILA ENA MU ULALIKI
13. Tiphunzilapo ciani tikaganizila mmene Yesu anali kucitila zinthu na anthu?
13 Pokamba za Yesu, Yesaya ananenelatu kuti: “Bango lophwanyika sadzalithyola, ndipo cingwe ca nyale comwe catsala pang’ono kuzima sadzacizimitsa.” (Yes. 42:3) Cikondi cinam’pangitsa Yesu kukhala munthu wacifundo. Anali kuwamvetsetsa anthu, amene mophiphilitsila anali monga bango lophwanyika, kapena ngati nyale imene yatsala pang’ono kuzima. Ndiye cifukwa cake iye anali kucita nawo zinthu moleza mtima, mokoma mtima, ndi mowaganizila. Ngakhale ana anali kumasuka naye. (Maliko 10:14) N’zoona kuti luso lathu la kuzindikila na kuphunzitsa silingafanane na limene Yesu anali nalo. Komabe, tingakwanitse kucita zinthu moganizila anthu a m’gawo lathu, ndipo izi n’zimene tiyenela kucita. Zimene zingaonetse kuti timawaganizila ni kakambidwe kathu powalalikila, nthawi imene timawafikila, na utali wa makambilano athu.
14. N’cifukwa ciani kukhala osamala pokamba na anthu n’kofunika?
14 Kodi tiyenela kukamba nawo bwanji anthu? Mat. 9:36) Zotulukapo zake n’zakuti anthu ambili amakonda kukayikila ena, ndipo alibe ciyembekezo. Conco, n’kofunika kwambili kuti zokamba zathu mu ulaliki komanso mmene timakambila zizionetsa kuti ndise okoma mtima ndi acifundo. Anthu ambili amakopeka na uthenga wathu, osati cabe cifukwa cakuti timadziŵa bwino Malemba na kuwafotokoza mwaluso. Koma amakopekanso cifukwa cakuti timawaonetsa cidwi na kuwaganizila.
Masiku ano, anthu mamiliyoni ambili-mbili ni “onyukanyuka ndi otayika” cifukwa copondelezedwa na atsogoleli acipembedzo, andale, komanso anthu azamalonda acinyengo ndi ankhanza. (15. Tingaonetse bwanji kuti timawaganizila anthu amene timawalalikila?
15 Pali njila zambili zimene tingaonetsele kuti timawaganizila anthu amene timakumana nawo mu ulaliki. Mwacitsanzo, kufunsa mafunso kumathandiza kwambili pophunzitsa. Koma tifunika kufunsa mokoma mtima ndi mwaulemu. M’gawo la mpainiya wina munali anthu ambili amanyazi komanso osamasuka. Mpainiyayo anazindikila kuti si bwino kufunsa mafunso amene angacititse munthu manyazi. Iye anali kupewa kufunsa mafunso amene munthu angalephele kuyankha, kapena amene angayankhe molakwika. Mwacitsanzo, anali kupewa kufunsa mafunso monga akuti, ‘Kodi mumalidziŵa dzina la Mulungu?’ kapena, ‘Kodi Ufumu wa Mulungu mumaudziŵa?’ M’malomwake, anali kukamba mau monga akuti, “Baibo imakamba kuti Mulungu ali na dzina. Kodi mungakonde kuti nikulongozeni dzinalo?” Zibadwa za anthu komanso zikhalidwe zawo zimasiyana-siyana. Conco, sitifunika kuika malamulo pa nkhani imeneyi. Komabe, nthawi zonse tiyenela kucita zinthu mwaulemu ndi moganizila ena. Kuti tikwanitse kucita izi, tifunika kuwadziŵa bwino anthu a m’dela lathu.
16, 17. Kodi kuganizila anthu kungatithandize bwanji (a) kusankha bwino nthawi yowafikila pa nyumba kukawalalikila? (b) kudziŵa utali wa nthawi imene tingakambilane nawo?
16 Ni nthawi yanji imene tiyenela kufikila anthu? Tikamalalikila ku nyumba na nyumba, timakhala alendo osayembekezeleka kwa eninyumba. Conco, ni bwino kufikila anthu pa nthawi imene angakhale omasuka kukambilana nase. (Mat. 7:12) Mwacitsanzo, kodi anthu m’gawo lanu amakonda kuuka mocedwa kumapeto kwa wiki? Ngati n’conco, mungayambe utumiki wanu mwa kucita ulaliki wa mumsewu, wapoyela, kapena kuyenda ku maulendo obwelelako kwa anthu amene mudziŵa kuti auka kale.
17 Kodi tiyenela kukamba nawo kwa nthawi yaitali bwanji anthu? Masiku yano, anthu ambili amakhala otangwanika kwambili. Conco, tingacite bwino kukambilana nawo kwa nthawi yocepa, maka-maka pa maulendo oyambilila. Makambilano athu ayenela kukhala aafupi, osati amtatakuya. (1 Akor. 9:20-23) Anthu akadziŵa kuti timawaganizila komanso timaona bize yawo, angatilole kuti tikakambilane nawonso nthawi ina. Inde, tikakhala mu ulaliki, tiyenela kuonetsa makhalidwe amene mzimu wa Mulungu umabala. Tikatelo, timakhaladi “anchito anzake a Mulungu,” ndipo iye angatiseŵenzetse pokoka munthu wina kuti akhale mtumiki wake.—1 Akor. 3:6, 7, 9.
18. Kodi tidzalandila madalitso anji tikakhala oganizila ena?
18 Conco, tiyeni tiyesetse mmene tingathele kukhala oganizila ena m’banja, mu mpingo, na mu ulaliki. Tikatelo, tidzalandila madalitso ambili pali pano komanso m’tsogolo. Salimo 41:1, 2 imati: “Wodala ndi munthu amene amacita zinthu moganizila munthu wonyozeka. Pa tsiku la tsoka, Yehova adzamupulumutsa. . . . Adzachedwa wodala padziko lapansi.”