Kodi Nthawi Ili Bwanji?
MUKAFUNA kudziŵa nthawi, kodi mumacita ciani? Mosakayikila mumayang’ana pa nkholoko yanu. Ngati mnzanu wakufunsani nthawi, kodi mungamuyankhe bwanji? Pali njila zosiyana-siyana zochulila nthawi. Kodi njila zimenezo n’ziti?
Cabwino, tikambe kuti papita ola limodzi na maminetsi 30 kucokela pa 12:00hrs masana. Mnzanuyo mungamuuze kuti nthawi ili 1:30. Koma potengela dela limene mumakhala komanso zimene anthu anazoloŵela kwanuko, mwina mungakambe kuti nthawi ili 13:30. Kachulidwe kameneka ka nthawi n’kotengela nkholoko yoonetsa maola 24 pa tsiku. Komanso kuli madela ena kumene anthu amachula nthawi imeneyi kuti “hafu 1,” kutanthauza kuti papita maminetsi 30 kucokela pamene 1 koloko yakwana.
Monga munthu amene amaŵelenga Baibo, mwina mumafuna kudziŵa kuti anthu m’nthawi yakale anali kuchula bwanji nthawi. Panali njila zosiyana-siyana zochulila nthawi. Malemba Aciheberi amachula nthawi monga “m’maŵa kwambili,” “m’maŵa,” “masana,” na ‘madzulo.’ (Gen. 8:11; 19:27; 1 Maf. 18:26) Komabe, nthawi zina iwo anali kuchula nthawi mwacindunji kwambili kuposa pamenepa.
M’nthawi yakale, kaŵili-kaŵili kunali kukhala alonda, maka-maka usiku. Zaka mahadiledi ambili Yesu asanabadwe, Aisiraeli anali kugaŵa usiku m’zigawo zitatu, zimene anali kuzicha maulonda. (Sal. 63:6, ftn.) Oweruza 7:19 imakamba za “ulonda wapakati pa usiku.” Pofika m’nthawi ya Yesu, Ayuda anali atatengela kaŵelengedwe ka Agiriki na Aroma, kokhala na zigawo zinayi za maulonda a usiku.
Kangapo konse, mabuku a Uthenga Wabwino amachulako za maulonda amenewa. Mwacitsanzo, Mateyu anakamba kuti inali nthawi ya “ulonda wacinayi” pamene Yesu anali kuyenda pamwamba pa madzi, kuyandikila ngalawa imene munali ophunzila ake. (Mat. 14:25) Komanso m’fanizo lina, Yesu anati: “Odala ndi akapolo amene mbuye wawo pofika adzawapeza akudikila! . . . Iwo ndi odala ndithu ngati atawapeza akudikilabe ngakhale atafika pa ulonda waciwili kapenanso wacitatu!”—Luka 12:37, 38.
Yesu anachula maulonda onse anayi pamene anauza ophunzila ake kuti: “Conco khalani maso, pakuti simukudziŵa nthawi yobwela mwininyumba. Simukudziŵa ngati adzabwele madzulo, pakati pa usiku, atambala akulila, kapena m’mawa.” (Maliko 13:35) Ulonda woyamba pa maulonda amenewo, wa “madzulo,” unali kuyamba dzuŵa likaloŵa, mpaka ca m’ma 21:00hrs madzulo. Ulonda waciŵili, wa “pakati pa usiku,” unali kuyamba ca m’ma 21:00hrs mpaka pakati pa usiku. Ulonda wacitatu, wa pa nthawi imene “atambala akulila,” unali kuyamba pakati pa usiku, mpaka ca m’ma 03:00hrs usiku. Zioneka kuti ni nthawi ya ulonda umenewu pamene tambala analila, pa usiku umene Yesu anagwidwa na adani ake. (Maliko 14:72) Ulonda wacinayi, wa “m’maŵa,” unali kuyamba ca m’ma 03:00hrs, mpaka m’maŵa pa nthawi ya kutuluka dzuŵa.
Conco, olo kuti m’nthawi yakale anthu analibe nkholoko, anali na njila yodziŵila nthawi, ya masana komanso ya usiku.