Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

“Ngati Zimenezi Mukuzidziŵa, Ndinu Odala Mukamazicita”

“Ngati Zimenezi Mukuzidziŵa, Ndinu Odala Mukamazicita”

“Cakudya canga ndico kucita cifunilo ca amene anandituma ndi kutsiliza nchito yake.”—YOH. 4:34.

NYIMBO: 80, 35

1. Kodi mzimu wodzikonda wa m’dzikoli ungatilepheletse bwanji kukhala odzicepetsa?

N’CIFUKWA ciani nthawi zambili cimakhala covuta kucita zimene timaphunzila m’Mau a Mulungu? Cifukwa cimodzi n’cakuti, kuti munthu acite coyenela amafunika kukhala wodzicepetsa. Koma kukhala odzicepetsa n’kovuta masiku ano. Tikukhala ‘m’masiku otsiliza’, ndipo anthu ambili ni “odzikonda, okonda ndalama, odzimva, odzikweza,” komanso “osadziletsa.” (2 Tim. 3:1-3) Monga atumiki a Mulungu, timadziŵa kuti makhalidwe amenewa ni oipa. Koma nthawi zina tingayambe kucita nsanje mu mtima mwathu tikaona kuti anthu amene amacita makhalidwe amenewa zinthu zikuwayendela bwino, ndipo akukhala mosangalala. (Sal. 37:1; 73:3) Tingafike pokayikila ngati kuika zofuna za ena patsogolo kulidi kwa phindu. Komanso tingayambe kuona kuti tikakhala odzicepetsa, anthu ena adzaleka kutilemekeza. (Luka 9:48) Kutengela mzimu wodzikonda wa m’dzikoli kungawononge ubale umene tili nawo mu mpingo, komanso mbili yathu monga Akhristu oona. Koma zinthu zingatiyendele bwino ngati tiphunzila za atumiki okhulupilika ochulidwa m’Baibo na kutengela citsanzo cawo.

2. Tingaphunzile ciani kwa atumiki a Mulungu okhulupilika akale?

2 Kuti tikwanitse kutengela atumiki a Mulungu okhulupilika akale, tifunika kuphunzila zimene anacita kuti zinthu ziwayendele bwino mu umoyo wawo. Kodi anacita ciani kuti akhale pa ubwenzi na Mulungu komanso kuti iye apitilize kuwayanja? Nanga anapeza kuti mphamvu zowathandiza kucita cifunilo cake? Kuphunzila zinthu monga zimenezi ni mbali yofunika kwambili ya cakudya cathu cauzimu.

KUDYA CAKUDYA CAUZIMU SIKUTANTHAUZA KUNGOPHUNZILA CABE

3, 4. Kodi timalandila bwanji malangizo ocokela kwa Mulungu? (b) N’cifukwa ciani tingakambe kuti kudya cakudya cauzimu sikutanthauza cabe kuphunzila zinthu?

3 Timalandila malangizo othandiza kupitila m’Baibo, zofalitsa zathu, webusaiti yathu ya jw.org, JW Broadcasting, komanso ku misonkhano yampingo na ikulu-ikulu. Koma malinga n’zimene Yesu anakamba pa Yohane 4:34, kudya cakudya cauzimu kumaphatikizapo zambili osati cabe kuphunzila. Kodi kumaphatikizaponso ciani? Yesu anati: “Cakudya canga ndico kucita cifunilo ca amene anandituma ndi kutsiliza nchito yake.”

4 Kwa Yesu, kudya cakudya cauzimu kunali kuphatikizapo kucita zimene Mulungu anamulamula. Kodi kucita zimenezi kuli ngati kudya cakudya m’njila yotani? Monga mmene kudya cakudya cabwino cakuthupi kumatithandizila kukhala osangalala komanso athanzi, kucita cifunilo ca Mulungu kumatithandiza kukhala na cikhulupililo colimba kuti tikapeze moyo wosatha. Kodi sizinacitikepo kwa imwe kuti pamene munali kunyamuka kupita mu ulaliki munali olema, koma munabwelako mutatsitsimulidwa komanso muli na mphamvu?

5. Kodi kucita zinthu mwanzelu kuli na phindu lanji?

5 Kucita zinthu mogwilizana na malangizo a Mulungu ndiyo nzelu. (Sal. 107:43) Ngati tiyesetsa kucita zinthu mwanzelu, tidzapeza mapindu ambili. Baibo imati: “Zonse zimene umakonda sizingafanane nazo. . . . Zidzakhala ngati mtengo wa moyo kwa iye, ndipo ozigwilitsitsa adzachedwa odala.” (Miy. 3:13-18) Yesu anati: “Ngati zimenezi mukuzidziŵa, ndinu odala mukamazicita.” (Yoh. 13:17) Ophunzila a Yesu anafunika kupitiliza kucita zimene Yesu anawalamula kuti akhalebe acimwemwe kapena kuti odala. Mu umoyo wawo wonse, iwo anafunika kupitiliza kucita zimene Yesu anawaphunzitsa, komanso kutengela citsanzo cake.

6. N’cifukwa ciani tifunika kupitiliza kucita zimene timaphunzila?

6 Kupitiliza kucita zinthu mogwilizana na coonadi cimene timaphunzila n’kofunikanso kwambili masiku ano. Tiyelekezele motele: Makanika amakhala na zida komanso amakhala wodziŵa zambili. Koma ngati zinthu zimenezi sazigwilitsila nchito, sangapeze phindu lililonse. Ngati anaseŵenzako nchito ya umakanika m’mbuyomo na kufika poidziŵa bwino, afunika kupitiliza kugwilitsila nchito zimene anaphunzila kuti akhalebe makanika waluso. N’cimodzimodzi na ise. Pamene tinayamba kuŵelenga Baibo na kuseŵenzetsa zimene tinali kuphunzila, mwacionekele tinayamba kukhala na umoyo wacimwemwe. Komabe, kuti tikhale na cimwemwe cokhalitsa, tiyenela kupitiliza kuseŵenzetsa malangizo a Yehova tsiku lililonse mu umoyo wathu.

7. Kuti tikhale anzelu, kodi tiyenela kucita ciani tikaphunzila za atumiki a Mulungu okhulupilika akale?

7 Kudzicepetsa kwathu kungayesedwa m’mbali zingapo. Lomba tiyeni tikambilane zina mwa mbali zimenezo. Komanso, tidzakambilana mmene atumiki a Yehova okhulupilika akale anaonetsela kudzicepetsa pa mbali ngati zimenezo. Kumbukilani kuti kuphunzila pakokha sikungatithandize kukhala na cikhulupililo colimba. Koma tifunika kuganizila mmene ise patekha tingaseŵenzetsele zimene taphunzila, na kuyamba kucita zimenezo nthawi yomweyo.

MUSAMADZIONE NGATI APAMWAMBA KUPOSA ENA

8, 9. Kodi zocitika zolembedwa pa Machitidwe 14:8-15 zionetsa bwanji kuti Paulo anali wodzicepetsa? (Onani pikica kuciyambi.)

8 Cifunilo ca Mulungu n’cakuti “anthu, kaya akhale a mtundu wotani, apulumuke ndi kukhala odziŵa coonadi molondola.” (1 Tim. 2:4) Kodi imwe mumawaona bwanji anthu a mitundu yosiyana-siyana amene sanaphunzile coonadi? Mtumwi Paulo anali kulalikila m’masunagoge kwa Ayuda amene anali kum’dziŵa kale Mulungu woona. Koma anali kulalikilanso kwa anthu a mitundu ina amene anali kulambila mafano. Pa nthawi ina, zimene anthu a mitundu ina anacita atawalalikila zinayesa kudzicepetsa kwake.

9 Mwacitsanzo, paulendo woyamba wa Paulo wa umishonale, anthu a ku Lusitara anayamba kuona Paulo na Baranaba monga milungu imene inasanduka anthu. Anayamba kuwachula na maina a milungu yawo yonama, Zeu na Heme. Kodi Paulo na Baranaba ananyadila cifukwa cotamandidwa mwanjila imeneyi? Kodi anaona kuti anali kulandila madalitso pambuyo pozunzidwa m’mizinda iŵili imene analalikilako asanafike ku Lusitara? Kodi anaganiza kuti kuchuka kwawo kudzathandiza kupititsa patsogolo nchito yofalitsa uthenga wabwino? Kutalitali! Poonetsa kusagwilizana na zimene anthuwo anali kucita, mwamsanga Paulo na Baranaba anang’amba zovala zawo, na kuthamanga kukaloŵa m’khamu la anthulo akufuula kuti: “Anthu inu, mukucitilanji zimenezi? Ifenso ndife anthu okhala ndi zofooka ngati inu nomwe.”—Mac. 14:8-15.

10. Kodi Paulo na Baranaba anali kudziona olingana na anthu a ku Lusitara okamba Cilukaoniya m’njila yotani?

10 Pamene Paulo na Baranaba anakamba kuti nawonso anali opanda ungwilo, sanatanthauze kuti kulambila kwawo kunali kolingana ndi kwa anthu a ku Lusitara olambila mafano. Paulo na Baranaba anali amishonale amene anapatsidwa utumiki wapadela. (Mac. 13:2) Komanso anali atadzozedwa na mzimu woyela na kupatsidwa ciyembekezo caulemelelo. Komabe, Paulo na Baranaba anazindikila kuti anthu a ku Lusitara okamba Cilukaoniya akanalabadila uthenga wabwino, sembe nawonso anapatsidwa mwayi wofanana na umene iwo anapatsidwa.

11. Pamene tilalikila, tingatengele bwanji citsanzo ca Paulo ca kudzicepetsa?

11 Kodi tingatengele bwanji citsanzo ca Paulo ca kudzicepetsa? Coyamba, sitiyenela kuyembekezela kapena kulolela kuti ena azititamanda kapena kutilemekeza kwambili cifukwa ca zinthu zimene tacita mwa mphamvu za Yehova. Aliyense wa ise angacite bwino kudzifunsa kuti: ‘Kodi nimawaona bwanji anthu amene nimawalalikila? Kodi nimaonetsa tsankho kwa anthu ena a m’dela langa?’ Padziko lonse lapansi, Mboni za Yehova zakhala zikufufuza mosamala m’magawo awo, kuti zione ngati mukali anthu ena amene angamvetsele uthenga wabwino. Kuti acite izi, nthawi zina amafunika kuphunzila citundu kapena cikhalidwe ca anthu amene amasalidwa m’dela lawo. Akhristu amene amalalikila kwa anthu aconco afunika kupewelatu mzimu wodziona monga apamwamba. Koma ayenela kuyesetsa kuwadziŵa bwino anthuwo kuti awafike pa mtima na uthenga wa Ufumu.

MUZIPEMPHELELAKO ENA N’KUWACHULA MAINA

12. Kodi Epafura anaonetsa bwanji kuti anali na mtima woganizila ena kwambili?

12 Njila ina imene tingaonetsele kuti timamvela malangizo a Mulungu modzicepetsa, ni kupemphelela anthu amene anapeza kale “cikhulupililo cofanana ndi cathu.” (2 Pet. 1:1) N’zimene Epafura anali kucita. Baibo imamuchula katatu cabe. Ndipo katatu konseko amachulidwa m’makalata ouzilidwa a Paulo. Pamene Paulo anali mkaidi wosacoka pa nyumba ku Roma, analembela kalata Akhristu a ku Kolose. M’kalatayo, iye anauza Akhristuwo kuti Epafura anali ‘kuwapemphelela mwakhama nthawi zonse.” (Akol. 4:12) Epafura anali kuwadziŵa bwino abale a ku Kolose, komanso anali kuwakonda kwambili. Olo kuti iye anali “mkaidi mnzake” wa Paulo, sanaleke kuganizila zosoŵa zauzimu za Akhristu anzake. (Filim. 23, NWT) Ndipo anacitapo kanthu kuti awathandize. Anawapemphelela. Iye anali na mtima woganizila ena kwambili. Ifenso tingacite bwino kumapemphelela Akhristu anzathu na kuwachula maina powapemphelela. Mapemphelo aconco amagwila nchito mwamphamvu kwambili.—2 Akor. 1:11; Yak. 5:16.

13. Mungatengele bwanji citsanzo ca Epafura pa mapemphelo amene mumapeleka?

13 Kodi n’ndani amene mungawapemphelele mwa kuwachula maina? Mofanana na Epafura, abale na alongo athu ambili amapemphelela Akhristu a mu mpingo mwawo, kapena mabanja amene akusamalila maudindo aakulu. Amapemphelelanso Akhristu amene afuna kupanga zosankha zazikulu, kapenanso amene akukumana na ziyeso. Enanso ambili amapemphelela Akhristu amene maina awo amapezeka pa jw.org, pa nkhani yakuti “A Mboni za Yehova Akumangidwa Cifukwa Cotsatila Zimene Amakhulupilila.” (Pitani ku Chichewa na kuona mbali yakuti MALO A NKHANI > ZOKHUDZANA NDI MALAMULO.) Kuwonjezela apo, sitiyenela kuiŵala kupemphelela abale na alongo amene anafeledwa, amene akhudzidwa na tsoka la zacilengedwe kapena nkhondo, komanso amene akukumana na mavuto a zacuma. Kukamba zoona, pali abale na alongo ambili amene tifunika kumawapemphelela, ndipo angapindule na mapemphelo athu. Tikamawapemphelela, timaonetsa kuti sitiganizila zofuna zathu zokha koma timaganizilanso zofuna za ena. (Afil. 2:4) Ndipo Yehova amamvetsela mapemphelo aconco.

KHALANI “WOFULUMILA KUMVA”

14. Kodi Yehova amapeleka citsanzo cabwanji pankhani yomvetsela zokamba za ena?

14 Njila inanso imene tingaonetsele kuti ndise odzicepetsadi ni kukhala okonzeka kumvetsela ena akamakamba nase. Yakobo 1:19 imakamba kuti tiyenela kukhala “ofulumila kumva.” Yehova amapeleka citsanzo cabwino ngako pa mbaliyi. (Gen. 18:32; Yos. 10:14) Ganizilani makambilano amene anali pakati pa Mose na Yehova, malinga n’zimene zinalembedwa pa Ekisodo 32:11-14. (Ŵelengani.) Olo kuti Yehova anali kudziŵa kale zocita, anapatsa Mose mpata wofotokozako maganizo ake. Kodi imwe mungamvetsele moleza mtima kwa munthu amene amacita zinthu mosaganiza bwino, kenako n’kutsatila malingalilo amene angapeleke? Zaconco n’zimene Yehova amacita. Iye amamvetsela moleza mtima zokamba za anthu onse amene amapemphela kwa iye ali na cikhulupililo.

15. Tingatengele bwanji citsanzo ca Yehova pa nkhani yolemekeza ena?

15 Aliyense wa ise angacite bwino kudzifunsa kuti: ‘Ngati Yehova amadzicepetsa mpaka kumvetsela zokamba za anthu, monga anacitila kwa Abulahamu, Rakele, Mose, Yoswa, Manowa, Eliya, na Hezekiya, kodi ine siniyenela kucita zoposa pamenepo? Kodi sinifunika kulemekeza kwambili abale anga, kumvetsela malingalilo awo, komanso ngakhale kucita zinthu mogwilizana na malingalilo awo abwino? Kodi palipano mu mpingo mwathu kapena m’banja lathu muli winawake amene afunika thandizo langa? Kodi ningamuthandize bwanji?’—Gen. 30:6; Ower. 13:9; 1 Maf. 17:22; 2 Mbiri 30:20.

“MWINA YEHOVA AONA” MASAUTSO ANGA

Davide anati: “Musiyeni anyoze. . . . !” Kodi mukanakhala imwe, sembe munacita ciani? (Onani palagilafu 16, 17)

16. Kodi Mfumu Davide anacita ciani pamene Simeyi anacita zinthu zom’khumudwitsa?

16 Kudzicepetsa kumatithandiza kukhala odziletsa ngati wina watikhumudwitsa. (Aef. 4:2) Citsanzo cabwino pa nkhani imeneyi cipezeka pa 2 Samueli 16:5-13. (Ŵelengani.) Tsiku lina, Simeyi, wacibululu wa Mfumu Sauli, ananyoza na kucitila cipongwe Davide na atumiki ake popanda cifukwa. Davide anapilila zinthu zopanda cilungamo zimenezo, olo kuti akanatha kumulanga Simeyi. N’ciani cinathandiza Davide kuugwila mtima? Yankho tingalipeze tikapenda zimene Salimo 3 imakamba.

17. N’ciani cinathandiza Davide kuugwila mtima pamene Simeyi anacita zinthu zom’khumudwitsa? Nanga tingatengele bwanji citsanzo cake?

17 Tumau twapamwamba pa Salimo 3 tuonetsa kuti salimoyi inalembedwa pamene Davide “anali kuthawa mwana wake Abisalomu.” Zimene vesi 1 na 2 ikamba zigwilizana na zocitika zofotokozedwa pa 2 Samueli caputa 16. Ndipo Salimo 3:4 ionetsa bwino cidalilo cimene Davide anali naco mwa Mulungu. Iye anati: “Ndidzafuulila Yehova mokweza, ndipo iye adzandiyankha m’phili lake loyela.” Na ise tiyenela kupemphela ngati anthu ena acita zinthu zotikhumudwitsa. Tikatelo, Yehova adzatipatsa mzimu wake woyela, umene ungatithandize kupilila. Conco, yesetsani kukhala odziletsa kwambili komanso wokonzeka kukhululuka pamene wina wakulakwilani. Kodi muli na cikhulupililo cakuti Yehova adzaona masautso anu na kukudalitsani?

“NZELU NDIYO CINTHU COFUNIKA KWAMBILI”

18. Kodi tidzapindula bwanji ngati tipitiliza kuseŵenzetsa malangizo a Mulungu?

18 Kucita zinthu zimene tidziŵa kuti n’zoyenela kumabweletsa madalitso oculuka. N’cifukwa cake Miyambo 4:7 imati “Nzelu ndiyo cinthu cofunika kwambili.” N’zoona kuti maziko a nzelu ni kukhala na cidziŵitso. Koma kukhala cabe na cidziŵitso si kokwanila. Nzelu imaonekela kwambili mwa zosankha zimene timapanga. Ngakhale nyelele zimaonetsa kuti zili na nzelu, mwa kusonkhanitsilatu cakudya cawo m’malanga. (Miy. 30:24, 25) Khristu, amene ndiye “nzelu za Mulungu,” nthawi zonse amacita zinthu zokondweletsa Atate wake. (1 Akor. 1:24; Yoh. 8:29) Na ise Mulungu adzatidalitsa ngati tikhalabe odzicepetsa, komanso ngati tionetsa nzelu mwa kucita zinthu zimene tidziŵa kuti ndiye zoyenela. (Ŵelengani Mateyu 7:21-23.) Conco, yesetsani kucita zinthu zimene zingathandize kuti aliyense mu mpingo azitumikila Yehova modzicepetsa. Kucita zinthu mogwilizana na coonadi cimene timaphunzila kumafuna nthawi na kuleza mtima. Koma tikamacita zimenezi, timaonetsa kuti ndise odzicepetsa, ndipo kudzicepetsa kudzatithandiza kukhala acimwemwe tsopano mpaka muyaya.