Muzikumbukila Amene Ali mu Utumiki Wanthawi Zonse
“Timakumbukila nthawi zonse nchito zanu zacikhulupililo, ndi nchito zanu zacikondi.”—1 ATES. 1:3.
1. Kodi Paulo anawaona bwanji aja amene analikutumikila Yehova mwakhama?
MTUMWI Paulo anakumbukila aja amene anagwila nchito yolalikila uthenga wabwino mwakhama. Iye analemba kuti: “Timakumbukila nthawi zonse nchito zanu zacikhulupililo, ndi nchito zanu zacikondi. Timatelonso pokumbukila mmene munapililila cifukwa ca ciyembekezo canu mwa Ambuye wathu Yesu Kristu, pamaso pa Mulungu wathu ndi Atate.” (1 Ates. 1:3) Yehova nayenso amakumbukila nchito zacikondi za aja amene amamutumikila mokhulupilika, kaya acite zambili kapena zocepa.—Aheb. 6:10.
2. Tikambilana ciani m’nkhani ino?
2 Atumiki ambili akale ndi amakono, adzimana zinthu zambili kuti atumikile Yehova mu utumiki wanthawi zonse. M’nkhani ino, tikambilana zimene ena m’nthawi ya atumwi anacita kuti atumikile Yehova. Tidzaphunzilanso zimene atumiki anthawi zonse amacita masiku ano, ndi mmene tingawathandizile.
AKRISTU A M’NTHAWI YA ATUMWI
3, 4. (a) M’nthawi ya atumwi, ndi m’njila ziti zimene abale ndi alongo anatumikila Yehova? (b) Nanga zosoŵa zao zakuthupi zinasamalilidwa motani?
3 Yesu atangobatizika, anayamba nchito imene inali kudzafalikila padziko lonse lapansi. (Luka 3:21-23; 4:14, 15, 43) Pambuyo pa imfa yake, atumwi ake anapititsa patsogolo nchito yolalikila imeneyi. (Mac. 5:42; 6:7) Akristu ena, monga Filipo, anagwila nchito yaumishonale ku Palestine. (Mac. 8:5, 40; 21:8) Paulo ndi ena anapita kukatumikila kumadela akutali. (Mac. 13:2-4; 14:26; 2 Akor. 1:19) Mwacitsanzo, ena monga Silivano (Sila), Maliko, ndi Luka anatumikilanso monga alembi. (1 Pet. 5:12) Alongo ena anacilikiza abale okhulupilika amenewa. (Mac. 18:26; Aroma. 16:1, 2) Nkhani zao zocititsa cidwi za zimacititsa m’Malemba Acikristu Acigiriki kukhala okondweletsa poŵelenga. Ndipozimatikumbutsa kuti Yehova amayamikila nchito imene atumiki ake amacita.
4 Nanga atumiki akale anthawi zonse anali kupeza bwanji zosoŵa zao? Nthawi zina, abale anzao anali kuwapatsa zofunikila, koma io sanali kukakamiza abale kuti awathandize. (1 Akor. 9:11-15) Mipingo ndi anthu ena anali kuwathandiza modzifunila. (Ŵelengani Macitidwe 16:14, 15; Afilipi 4:15-18.) Paulo ndi Sila anali kugwilako tu nchito twina kuti azidzithandiza.
ATUMIKI ANTHAWI ZONSE MASIKU ANO
5. Kodi banja lina linakamba ciani za umoyo wao mu utumiki wanthawi zonse?
5 Ngakhale masiku ano, ambili amagwila nchito mwakhama mwakucita mautumiki anthawi zonse osiyanasiyana. (Onani bokosi lakuti, “ Mautumiki Anthawi Zonse.”) Kodi io amaiona bwanji nchito imene anasankha? Mungacite bwino kuwafunsa, ndipo mudzalimbikitsidwa ndi mayankho ao. Mwacitsanzo: M’bale amene watumikila monga mpainiya wanthawi zonse, mpainiya wapadela, mmishonale, ndipo pa nthawi ino akutumikila pa Beteli ku dziko lina anati: “Ndaona kuti kuyamba utumiki wanthawi zonse ndi cosankha cabwino koposa cimene ndinapanga. Pamene ndinafika zaka 18, zinandivuta kusankha kuti ndipite ku univesite, ndiloŵe nchito, kapena kucita upainiya. Ndaona kuti Yehova saiŵala kudzipeleka kwanga mu utumiki wanthawi zonse. Ndagwilitsila nchito maluso anga amene Yehova anandipatsa mwanjila imene sindikanatelo ndikanasankha nchito yakuthupi.” Mkazi wake naye anati: “Utumiki uliwonse wandithandiza kupita patsogolo. Taona mmene Yehova watitetezela, ndi kutitsogolela mobwelezabweleza mwa njila imene sizikanacitika tikanasankha umoyo wa wofuwofu. Tsiku lililonse ndimayamikila Yehova cifukwa cokhala mu utumiki wanthawi zonse.” Kodi inunso, simungakonde kukhala ndi umoyo wofanana ndi umenewu?
6. Kodi Yehova amauona bwanji utumiki wathu kwa iye?
6 N’zoona kuti ena palipano mikhalidwe siwalola kucita utumiki wanthawi zonse. Tidziŵa kuti Yehova amayamikila kwambili zonse zimene amacita mocokela pansi pamtima. Mwacitsanzo, pa Filimoni 1-3, Paulo anatumiza moni kwa abale onse mumpingo wa ku Kolose, ndipo ena anawachula maina. (Ŵelengani.) Paulo anawayamikila, ndipo nayenso Yehova anawayamikila. Mofananamo, Atate wathu wakumwamba amayamikila utumiki wanu. Nanga mungathandize bwanji aja amene ali mu utumiki wanthawi zonse?
KUTHANDIZA APAINIYA
7, 8. Kodi upainiya umaphatikizapo kucita ciani? Nanga ena mumpingo angawathandize motani apainiya?
7 Mofanana ndi alaliki a m’nthawi ya atumwi, apainiya acangu amalimbikitsa mpingo. Ambili amayesetsa kuthela maola 70 mu ulaliki mwezi uliwonse. Kodi mungawathandize motani?
8 Mlongo wina dzina lake Shari amene ndi mpainiya anakamba kuti: “Apainiya amaoneka olimba cifukwa nthawi zonse amakhala mu ulaliki. Koma ngakhale n’conco, io amafunikila kuwalimbikitsa.” (Aroma 1:11, 12) Ponena za apainiya a pa mpingo wake, mlongo wina amene anali mpainiya kwa zaka zambili anati: “Apainiya amalimbikila kugwila nchito mwakhama. Iwo amayamikila ngati ena awatengako pa galimoto kupita nao mu ulaliki, kuwaitana ku cakudya, kuwapatsako kandalama ka mafuta a galimoto kapena kowathandiza kugula zinthu zina. Zimenezi zimaonetsa kuti mumawakonda.”
9, 10. N’ciani cimene ena amacita kuti athandize apainiya mumpingo wao?
9 Njila ina imene tingathandizile apainiya ndi mwa kugwila nao nchito mu ulaliki. Mpainiya wina dzina lake Bobbi, anacondelela kuti: “Mkati mwa mlungu timafuna anthu ambili olalikila nao.” Mpainiya wina mu mpingo umenewo anati: “Timavutika kupeza wogwila naye nchito masana.” Mlongo wina amene tsopano akutumikila pa Beteli ku Brooklyn, anakumbukila thandizo limene analandila pamene anali kucita upainiya. Iye anati: “Mlongo wina amene anali ndi galimoto anandiuza kuti, ‘Nthawi iliyonse mukasoŵa wolalikila naye muzinditumila foni kuti tipite limodzi.’ Mlongo ameneyu anandithandiza kwambili kuti ndipitilize upainiya.” Mlongo wina dzina lake Shari anati: “Kaŵilikaŵili apainiya amene sali pa banja akacoka mu ulaliki amakhala okha. Zingakhale bwino nthawi zina kuitanako abale kapena alongo osakwatila kuti mukhale nao pa kulambila kwa pabanja. Mungawaitaneko pa zocitika zina, ndipo zimenezi zidzawalimbikitsa.”
10 Ponena za thandizo limene iye ndi alongo ena osakwatila analandila, mlongo wina amene wakhala mu utumiki wanthawi zonse kwa zaka pafupifupi 50, anati: “Pakapita miyezi ingapo, akulu a mpingo wathu anali kuwacezela apainiya. Anali kutifunsa za umoyo wathu ndi nchito imene tinali kugwila. Ndipo anali kutifunsanso ngati pali zovuta zilizonse. Pocita zimenezi io anali kutiganiziladi. Iwo anali kufika kunyumba kwathu kuti aone ngati pali zina zimene tifunikila.” Akulu amenewa ndi ena amatsatila citsanzo ca Onesiforo. Iye anali kusamalila banja lake, koma anapelekanso thandizo lofunikila kwa Paulo.—2 Tim. 1:18.
11. Kutumikila monga mpainiya wapadela kumaphatikizapo ciani?
11 Mipingo ina yapindula kukhala ndi apainiya apadela. Apainiya apadela ambili amathela maola 130 mu ulaliki mwezi uliwonse. Cifukwa ca kuculuka kwa nthawi imene amathela mu ulaliki ndi kuthandiza m’njila zina, io alibe nthawi yambili yakuti aseŵenze. Conco, ofesi ya nthambi imawapatsa alawansi yocepa mwezi ndi mwezi, kuwathandiza kuti apitilize utumiki.
12. Kodi akulu ndi ofalitsa ena angathandize motani apainiya apadela?
12 Tingacitenji kuti tithandize apainiya apadela? Mkulu wina amene akutumikila pa ofesi ya nthambi ndipo amalankhula ndi apainiya apadela ambili anati: “Akulu ayenela kulankhula nao, kudziŵa mmene zinthu zilili paumoyo wao, ndi kuona mmene angawathandizile. Abale ena amaganiza kuti apainiya apadela sasoŵa kanthu cifukwa cakuti amapatsidwa alawansi.” Mofanana ndi apainiya anthawi zonse, apainiya apadela amafuna olalikila nao. Kodi inu mungalalikile nao?
MMENE TINGATHANDIZILE OYANG’ANILA DELA
13, 14. (a) Tiyenela kukumbukila ciani ponena za oyang’anila dela? (b) Nanga mungacite ciani kuti muzithandiza oyang’anila dela?
13 Oyang’anila dela ndi akazi ao amaoneka kuti ndi anthu olimba kuuzimu ndi kuti sangagonje pamayeselo. Zimenezo n’zoona, koma naonso amafunikila kuwalimbikitsa, kulalikila nao, ndi kuwaitanako ku zosangulutsa zina. Nanga bwanji ngati woyang’anila dela kapena mkazi wake, ndi wodwala ku cipatala ndipo mwina afunikila opaleshoni? Iwo amalimbikitsidwa kwambili ngati abale ndi alongo awathandiza pa zosoŵa zao ndi kuonetsa kuti amawakonda. Luka, “dokotala wokondedwa,” anasamalila zosoŵa za Paulo ndi ena amene anapita kukatumikila mipingo yosiyanasiyana.—Akol. 4:14; Mac. 20:5–21:18.
14 Oyang’anila dela ndi akazi ao amafuna cikondi ndi cilimbikitso cocokela kwa mabwenzi apamtima. Woyang’anila dela wina analemba kuti: “Anzanga amadziŵa pamene ndifunikila thandizo. Amandifunsa mafunso anzelu ndipo zimenezi zandithandiza kuwafotokozela nkhawa zanga. Kungokhala amvetseli abwino kwakhala kothandiza kwambili.” Oyang’anila dela amayamikila kwambili ngati abale ndi alongo amawakonda kucokela pansi pa mtima, ndi kukhala mabwenzi ao enieni.
THANDIZANI ATUMIKI A PA BETELI
15, 16. Kodi atumiki a pa Beteli ndi atumiki a pa Nyumba za Misonkhano amacita utumiki wotani? Ndipo tingawathandize motani?
15 Aja amene akutumikila pa Beteli ndi Nyumba za Misonkhano, amacita nchito yofunika yolalikila uthenga wabwino. Ngati muli ndi atumiki a pa Beteli mumpingo wanu kapena m’dela lanu, mungacitenji kuti muwathandize?
16 Akangofika pa Beteli, io angayambe kuyewa kunyumba cifukwa cokhala kutali ndi banja lao ndi mabwenzi. Atumiki a pa Beteli atsopanowa, amayamikila pamene abale anzao a pa Beteli ndi mumpingo wao akhala nao pa ubwenzi. (Maliko 10:29, 30) Utumiki wao pa Beteli umawapatsa mpata wosonkhana ndi kutengako mbali mu ulaliki mlungu uliwonse. Komabe, nthawi zina io amakhala ndi nchito zina zoonjezeleka. Zimapindulitsa onse ngati abale mumpingo adziŵa bwinobwino zimenezi, ndi kuyamikila atumiki a pa Beteli ndi nchito yao.—Ŵelengani 1 Atesalonika 2:9.
THANDIZANI ATUMIKI ANTHAWI ZONSE AMENE ATUMIKILA KU MAIKO ENA
17, 18. Ndi mautumiki otani amene atumiki anthawi zonse amene akutumikila m’maiko ena amacita?
17 Abale amene asankha kukatumikila ku maiko ena amavutika ndi zakudya zacilendo, cinenelo, miyambo, ndi zikhalidwe zosiyana ndi zimene anazoloŵela. N’cifukwa ciani amasankha kukatumikila m’mikhalidwe ya conco?
18 Ena ndi amishonale ndipo amathela nthawi yao yoculuka mu ulaliki. Iwo ndi alaliki komanso aphunzitsi aluso ndipo amauzako ena mumpingo zimene anaphunzila. Ofesi ya nthambi imalinganiza nyumba yabwino koma osati yodula kwambili. Ndipo amapatsidwa alawansi yocepa imene imawathandiza pa zosoŵa zao. Ena amatumikila pa ofesi ya nthambi. Ndipo ena amathandiza kumanga maofesi a nthambi, maofesi omasulila mabuku, Nyumba za Misonkhano, kapena Nyumba za Ufumu. Amawakonzela zakudya, malo ogona ndi zina zofunikila. Mofanana ndi atumiki a pa Beteli, naonso amasonkhana nthawi zonse ndi kutengako mbali mu nchito yolalikila. Mpingo umapindula kwambili kukhala ndi abale ndi alongo amenewa.
19. Tingathandize bwanji atumiki anthawi zonse amene akutumikila m’dziko lathu?
19 Mungathandize bwanji atumiki anthawi zonse amene akutumikila m’dziko lanu? Muyenela kudziŵa kuti zakudya zimene anali kudya kwao n’zosiyana ndi zimene inu mumadya. Conco, mukawaitana ku cakudya muziwafunsa ngati angakonde kulaŵa zakudya zanu, kapena ngati pali zakudya zina zimene sangakonde. Khalani odekha makamaka pamene io akuphunzila cinenelo ndi cikhalidwe canu. Zimatenga nthawi kuphunzila bwinobwino cinenelo, koma muyenela kuwathandiza mwacikondi mmene angachulile bwinobwino mau. Iwo amafunitsitsa kuphunzila.
20. Ndi njila yabwino iti imene tingathandizile atumiki anthawi zonse ndi makolo ao?
20 Atumiki anthawi zonse amakalamba, cimodzimodzinso makolo ao. Ngati makolo ao ndi Mboni, mwacionekele amafunitsitsa kuti ana ao apitilize ndi utumiki wao wanthawi zonse. (3 Yohane 4) Ngakhale n’conco, atumiki anthawi zonse amacita zimene angathe ngati makolo ao afunikila cisamalilo. Ndipo nthawi ndi nthawi amayesetsa kuwacezela. Koma ao amene amakhala pafupi ndi makolo angathandize amene ali mu utumiki wanthawi zonse. Iwo angadzipeleke kuthandiza makolowo ngati angafunikile thandizo. Tisaiŵale kuti atumiki anthawi zonse ndi otangwanika kwambili ndi nchito yolalikila, imene ndi yofunika kwambili padziko lonse masiku ano. (Mat. 28:19, 20) Kodi inu ndi mpingo wanu mungathandize makolo a atumiki anthawi zonse amene angafunikile thandizo?
21. Kodi atumiki anthawi zonse amaona bwanji thandizo ndi cilimbikitso cimene ena amapeleka?
21 Ambili amene amayamba utumiki wanthawi zonse sacita zimenezo kuti apeze phindu. Koma amatelo cifukwa afuna kutumikila Yehova ndi ena. Iwo amayamikila thandizo lililonse limene mungapeleke. Mlongo wina amene ali mu utumiki wanthawi zonse, ndipo anasamukila kudziko lina anati: “Kungolandila ka khadi kosonyeza kuyamikila zimaonetsa kuti ena amakuganizila, ndipo amakondwela ndi utumiki wako.”
22. Kodi mumauona bwanji utumiki wanthawi zonse?
22 Anthu amene ali mu utumiki wanthawi zonse anasankha nchito yokondweletsa ndi yopindulitsa kwambili. Atumiki anthawi zonse aphunzila makhalidwe ndi maluso amene ndi ofunika tsopano ndiponso m’dziko latsopano. Posacedwapa atumiki a Yehova adzagwila nchito yopindulitsa kwambili tsiku lililonse. Conco, tiyeni tipitilize kukumbukila ‘nchito zacikhulupililo ndi zacikondi’ za atumiki anthawi zonse.—1 Ates. 1:3.