Khalani ndi Cikhulupililo Cosagwedela mu Ufumu
“Cikhulupililo ndico ciyembekezo cotsimikizilika ca zinthu zoyembekezeledwa.”—AHEB. 11:1.
1, 2. N’ciani cidzatithandiza kulimbitsa cikhulupililo cathu cakuti Ufumu wa Mesiya udzakwanilitsa cifunilo ca Mulungu ponena za anthu? (b) Malinga ndi Aefeso 2:12, kodi mapangano amatilimbikitsa motani? (Onani cithunzi pamwamba.)
POKHALA Mboni za Yehova, timalalikila kuti Ufumu wa Mulungu ndiwo wokha umene udzathetsa mavuto athu onse. Mofunitsitsa timauzako anthu coonadi cimeneci ca m’Malemba. Ndiponso, ciyembekezo ca Ufumu cimatitonthoza. Komabe, kodi timakhulupililadi kuti Ufumu ndi weniweni ndi kuti udzakwanilitsa cifunilo ca Mulungu? Nanga n’ciani cingatithandize kukhala ndi cikhulupililo cosagwedela mu Ufumu wa Mulungu?—Aheb. 11:1.
2 Ufumu wa Mesiya ndiwo makonzedwe a Wamphamvuyonse amene adzakwanilitsa cifunilo cake ponena za cilengedwe. Maziko a Ufumu umenewu ali monga thanthwe cifukwa cakuti Yehova ndiye woyenelela kulamulila. Koma pali zambili zofunika monga, amene adzakhala mfumu, amene adzalamulila naye, ndi mmene ulamulilo wao udzakhalila. Kupyolela m’mapangano, zinthu zonse zimenezi zinakhazikitsidwa moyenelela. Mapangano amenewa akhazikitsidwa moyenela kapena mwalamulo, ndipo amene ali mbali yake ndi Mulungu kapena Mwana wake, Yesu Kristu. Kuganizila kwambili mapangano amenewa kudzatithandiza kumvetsetsa mmene cifunilo ca Mulungu cidzakwanilitsidwila. Kudzatithandizanso kuona kudalilika kwa Ufumu wa Mesiya.—Ŵelengani Aefeso 2:12.
3. Tikambilana ciani m’nkhani ino ndi m’nkhani yotsatila?
3 Baibulo limafotokoza mapangano 6 ogwilizana ndi Ufumu wa Mesiya, amene wolamulila wake ndi Kristu Yesu. Mapangano amenewa ndi (1) pangano la Abulahamu, (2) pangano la Cilamulo, (3) pangano la Davide, (4) pangano la wansembe monga Melekizedeki, (5) pangano latsopano, ndi (6) pangano la Ufumu. Tiyeni tikambilane mmene pangano lililonse limagwilizanilana ndi Ufumu, ndi mmene limagwilila nchito ponena za cifunilo ca Mulungu ca dziko lapansi ndi anthu.—Onani kamutu kakuti, “ Mmene Mulungu Adzakwanilitsila Cifunilo Cake.”
PANGANO LIONETSA MMENE CIFUNILO CA MULUNGU CIDZAKWANILITSIDWILA
4. Malinga ndi lemba la Genesis, Yehova anachula zinthu zitatu ziti ponena za anthu?
4 Yehova analenga dziko lapansi kuti anthu akhalemo. Ndiyeno, iye anachula zinthu zitatu ponena za anthu kuti (1) Mulungu adzalenga munthu m’cifanizilo cake, (2) anthu adzafutukula Paladaiso padziko lapansi ndipo lidzadzaza ndi anthu olungama, ndi (3) anthu adzaletsedwa kudya zipatso za mtengo wodziŵitsa cabwino ndi coipa. (Gen. 1:26, 28; 2:16, 17) Zinthu zitatu zimenezi n’zimene zinali zofunika kuti cifunilo ca Mulungu kwa anthu ndi dziko lapansi cikwanilitsike. Komabe, n’ciani cinacitika kuti mapangano akhale ofunika?
5, 6. (a) N’ciani cimene Satana anacita kuti alepheletse cifunilo ca Mulungu? (b) Nanga Yehova anacitanji ndi zimene Satana anatsutsa mu Edeni?
5 Pofuna kulepheletsa cifunilo ca Mulungu, Satana Mdyelekezi anasonkhezela anthu kuti apanduke. Iye anacita zimenezi mwa kupeputsa lamulo limene anthu anafunikila kumvela. Iye anacititsa mkazi woyamba, Hava, kusamvela lamulo lakuti asadye zipatso za mtengo wodziŵitsa cabwino ndi coipa. (Gen. 3:1-5; Chiv. 12:9) Mwa kucita zimenezo, Satana anatsutsa kuti Mulungu ndiye woyenela kulamulila cilengedwe cake. Pambuyo pake, Satana anacititsanso atumiki okhulupilika a Mulungu kukhala ndi maganizo odzikonda.—Yobu 1:9-11; 2:4, 5.
6 Nanga Yehova anacitanji ndi zimene Satana anatsutsa mu Edeni? Iye anali ndi mphamvu zowapha nthawi imeneyo. Koma zimenezo zikanacititsa kuti cifunilo ca Mulungu cakuti ‘dziko lidzaze’ ndi ana omvela a Adamu ndi Hava cisakwanilitsike. M’malo mwakupha opandukawo nthawi imeneyo, Mlengi wanzelu anakhazikitsa pangano la mu Edeni. Anacita zimenezi kuti mau ake akwanilitsike.—Ŵelengani Genesis 3:15.
7. Kodi pangano la mu Edeni limatitsimikizila ciani ponena za njoka ndi mbeu yake?
7 Kupyolela m’pangano la mu Edeni, Yehova anapeleka ciweluzo kwa njoka ndi mbeu yake. Njoka ndi mbeu yake zikuimila Satana Mdyelekezi ndi onse amene ali kumbali yake potsutsa ulamulilo wa Mulungu. Mulungu woona anapatsa mbeu ya mkazi wakumwamba mphamvu yoononga Satana. Conco, pangano la mu Edeni silimangokamba za amene anasonkhezela kupanduka mu Edeni ndi mmene zotsatilapo za kupanduka zidzathetsedwela. Koma limafotokozanso njila yothetsela kupanduka kumeneko.
8. Tingakambe ciani ponena za mmene timadziŵila mkazi ndi mbeu yake?
8 Nanga ndani amene anali kudzakhala mbeu imeneyo? Popeza mbeu imeneyo idzaphwanya mutu wa njoka, kapena kuti ‘kuononga’ colengedwa cauzimu, Satana Mdyelekezi, ndiye kuti mbeu imeneyo iyenela kukhala colengedwa cauzimu. (Aheb. 2:14) Conco, mkazi amene akubeleka mbeu ayenelanso kukhala colengedwa cauzimu. Yehova atakhazikitsa pangano la mu Edeni, mbeu imeneyi ndiponso mkazi sinadziŵike kwa zaka pafupifupi 4 sauzande. Komabe, Yehova anapanga mapangano angapo otithandiza kudziŵa mbeu imeneyo. Mapangano amenewo amathandizanso atumiki ake kudziŵa kuti mbeu imeneyi ndiyo njila yokha yothetsela mavuto amene Satana anabweletsa pa mtundu wa anthu.
PANGANO LIDZIŴIKITSA MBEU
9. Ndi liti pamene pangano la Yehova ndi Abulahamu linayamba kugwila nchito?
9 Zaka 2 sauzande kucokela pamene Yehova anapeleka ciweluzo kwa Satana, iye analamula kholo lakale Abulahamu kuti acoke mumzinda wa Uri wa ku Mesopotamiya, ndi kupita kudziko la Kanani. (Mac. 7:2, 3) Pamene Abulahamu anali ku Harana, paulendo wake wopita ku Kanani, Yehova anamuuza kuti: “Tuluka m’dziko lako, pakati pa abale ako, ndi kusiya nyumba ya bambo ako. Upite kudziko limene ndidzakusonyeza. Ine ndidzatulutsa mtundu waukulu mwa iwe. Ndidzakudalitsa ndi kukudza dzina lako, ndipo iwe ukhale dalitso kwa ena. Odalitsa iwe ndidzawadalitsa, ndipo otembelela iwe ndidzawatembelela. Mabanja onse a padziko lapansi adzapeza madalitso cifukwa ca iwe.” (Gen. 12:1-3) Imeneyi ndiyo nkhani yoyamba kulembedwa yonena za pangano la Abulahamu, pangano limene Yehova Mulungu anapanga ndi Abulahamu. Komabe, umboni uonetsa kuti zimene Yehova anauza Abulahamu ku Harana anangobweleza zimene anamuuza poyamba ku Uri. Nthawi yeniyeni imene Yehova anakhazikitsa pangano ndi Abulahamu sidziŵika. Koma panganoli linayamba kugwila nchito mu 1943 B.C.E., pamene Abulahamu anali ndi zaka 75, anacoka ku Uri ku Mesopotamiya, ndi kuoloka Mtsinje wa Firate.
10. (a) Abulahamu anaonetsa bwanji kuti anali ndi cikhulupililo cosagwedela m’malonjezo a Mulungu? (b) Kodi Yehova pang’onopang’ono anaulula ciani ponena za mbeu ya mkazi?
10 Yehova anauza Abulahamu za lonjezo lake mobwelezabweleza. Ndipo nthawi iliyonse imene anakamba naye anali kuonjezapo mfundo zina. (Gen. 13:15-17; 17:1-8, 16) Abulahamu anali ndi cikhulupililo cosagwedela m’malonjezo a Mulungu cakuti anali wofunitsitsa kupeleka nsembe mwana wake wobadwa yekha. Conco, Yehova analimbitsa pangano limenelo mwa kupeleka lonjezo lotsimikizilika. (Ŵelengani Genesis 22:15-18; Aheberi 11:17.) Patapita zaka zoposa 30 pangano la Abulahamu litayamba kugwila nchito, pang’onopang’ono Yehova anaulula mbali yofunika ponena za mbeu ya mkazi. Anachula kuti mbeu imeneyo idzacokela m’mbadwa za Abulahamu. Anachulanso kuti idzaculuka, idzakhala mafumu olamulila, idzaononga adani onse, ndi kuti mitundu yonse idzadalitsidwa kupyolela mwa mbeu imeneyo.
11, 12. Kodi Malemba amaonetsa bwanji kuti pangano la Abulahamu lidzakwanilitsidwa kwakukulu mtsogolo? Nanga zimenezo zimatikhudza bwanji?
11 Pangano la Abulahamu linakwanilitsidwa koyamba kwa mbadwa zake, pamene zinaloŵa m’Dziko Lolonjezedwa. Komabe, Malemba amaonetsa kuti mbali ina ya pangano limeneli ili ndi kukwanilitsidwa kwa kuuzimu. (Agal. 4:22-25) Komabe, pa kukwanilitsidwa kwakukulu kwa ulosi umenewu, monga mmene mtumwi Paulo anafotokozela mouzilidwa, mbali yoyamba ya mbeu ya Abulahamu ndi Kristu. Ndipo mbali yaciŵili ndi Akristu a 144,000 odzozedwa ndi mzimu. (Agal. 3:16, 29; Chiv. 5:9, 10; 14:1, 4) Mkazi amene akubeleka mbeu ndi “Yerusalemu wam’mwamba,” amene ndi mbali ya kumwamba ya gulu la Mulungu lopangidwa ndi zolengedwa zauzimu zokhulupilika. (Agal. 4:26, 31) Malinga ndi pangano la Abulahamu, mbeu ya mkazi idzabweletsa madalitso pa mtundu wa anthu.
12 Pangano la Abulahamu limatsimikizila kuti Ufumu wa kumwamba ndi weniweni, ndi kuti udzapeleka mwai kwa Mfumu ndi olamulila anzake kuti aloŵe Ufumuwo. (Aheb. 6:13-18) Nanga pangano limeneli lidzagwila nchito kwa utali wotani? Lemba la Genesis 17:7 limanena kuti lidzakhala “pangano mpaka kalekale.” Lidzapitilizabe kugwila nchito mpaka Ufumu wa Mesiya utaononga adani a Mulungu, kuphatikizapo “njoka,” kufikila mabanja onse padziko lapansi atadalitsidwa. (1 Akor. 15:23-26) Ndithudi, aja amene adzakhala padziko lapansi adzapindula kwamuyaya. Ndipo pangano limene Mulungu anacita ndi Abulahamu lionetsa kuti Yehova ndi wofunitsitsa kukwanilitsa cifunilo cake cakuti anthu olungama ‘adzaze dziko lapansi.’—Gen. 1:28.
PANGANO LITSIMIKIZILA KUTI UFUMU UDZAKHALA KOSATHA
13, 14. Pangano la Davide limatitsimikizila ciani ponena za ulamulilo wa Mesiya?
13 Pangano la mu Edeni ndiponso pangano la Abulahamu limatiphunzitsa kuti nthawi zonse ulamulilo wa Yehova ndi wozikidwa zolimba pa miyezo yake yolungama. (Sal. 89:14) Kodi boma la Mesiya limeneli lidzaipitsidwa ndi kucotsedwapo? Pangano lina likutsimikizila kuti zimenezo n’zosatheka.
14 Ganizilani zimene Yehova analonjeza Davide, Mfumu ya Isiraeli wakale kupyolela mu pangano la Davide. (Ŵelengani 2 Samueli 7:12, 16.) Iye anacita pangano ndi Davide pamene anali Mfumu ku Yerusalemu. Ndipo anam’lonjeza kuti Mesiya adzacokela m’banja lake. (Luka 1:30-33) Yehova anapeleka malangizo acindunji onena za mzele wobadwila Mesiya. Iye anakamba kuti mbeu imeneyi ya Davide idzakhala ‘yoyenelela mwalamulo’ kukhala Mfumu ya Ufumu wa Mesiya. (Ezek. 21:25-27) Kupyolela mwa Yesu Mesiya, ucifumu wa Davide ‘udzakhazikika mpaka kalekale.’ Ndithudi, mbeu ya Davide “idzakhala mpaka kalekale, ndipo mpando wake wacifumu udzakhala ngati dzuŵa.” (Sal. 89:34-37) Zoonadi, ulamulilo wa Mesiya sudzaipitsidwa, ndipo zimene udzacita zidzakhala kwamuyaya!
PANGANO LINAKWANILITSA NCHITO YA UNSEMBE
15-17. Malinga ndi pangano la wansembe monga Melekizedeki, kodi mbeu idzacitanso utumiki wina uti? Ndipo n’cifukwa ciani?
15 Ngakhale kuti pangano la Abulahamu ndi pangano la Davide limatitsimikizila kuti mbeu ya mkazi idzakhala mfumu, zimenezo sizokwanila kuti mitundu yonse ya anthu idalitsidwe. Kuti io adalitsidwedi, ayenela kumasulidwa ku ucimo ndi kuwabweletsa m’banja la Yehova. Koma kuti zimenezi zitheke, mbeu inafunikilanso kutumikila pa udindo waunsembe. Conco, Mlengi wanzelu anapanga makonzedwe ena kupyolela mu pangano la wansembe monga Melekizedeki.
16 Kupyolela mwa Mfumu Davide, Yehova anaulula kuti adzacita pangano ndi Yesu lokhala ndi zolinga ziŵili: Coyamba, kuti ‘akhale kudzanja lamanja [la Mulungu]’ kufikila atagonjetsa adani ake. Caciŵili, kuti akhale “wansembe mpaka kalekale monga mwa unsembe wa Melekizedeki.” (Ŵelengani Salimo 110:1, 2, 4.) N’cifukwa ninji amuyelekezela ndi “unsembe wa Melekizedeki”? Cifukwa cakuti kukali zaka zambili kuti mbadwa za Abulahamu ziloŵe M’dziko Lolonjezedwa, Melekizedeki, mfumu ya ku Salemu, analinso “wansembe wa Mulungu Wam’mwambamwamba.” (Aheb. 7:1-3) Iye anaikidwa mwacindunji ndi Yehova kuti acite nchito yaunsembe. Malemba a Ciheberi amaonetsa kuti ndiye yekha amene anatumikila monga mfumu komanso wansembe. Ndiponso, popeza kuti sanaloŵe m’malo mwa winawake kapena kuloŵedwa m’malo, iye achedwa “wansembe wamuyaya.”
17 Yesu anaikidwa mwacindunji kuti akhale wansembe kupitila mu pangano limene Yehova anacita ndi iye. Ndipo iye adzakhalabe “wansembe mpaka muyaya monga mwa unsembe wa Melekizedeki.” (Aheb. 5:4-6) Zimenezi zionetsa kuti Yehova iye mwini adzagwilitsila nchito Ufumu wa Mesiya kudalitsa mitundu yonse, ndi kukwanilitsa cifunilo cake coyambilila ca dziko lapansi cokhudza anthu.
MAPANGANO AKHALA MAZIKO OYENELELA A UFUMU
18, 19. (a) Kodi mapangano amene takambilana atsimikizila ciani ponena za Ufumu? (b) Ndi funso liti limene lidzayankhidwa m’nkhani yotsatila?
18 Kucokela pa mapangano amene takambilana, taona mmene amagwilizanilana ndi Ufumu wa Mesiya. Taonanso kuti Ufumu umenewu ndi wozikika zolimba mwalamulo. Pangano la mu Edeni litsimikizila kuti Yehova kupyolela mwa mbeu ya mkazi, adzakwanilitsa cifunilo cake ponena za dziko lapansi ndi anthu. Ndani amene anali kudzakhala mbeu? Nanga inali kudzatumikila pa udindo uti? Pangano la Abulahamu linayala maziko a zonsezi.
19 Pangano la Davide linapeleka malangizo oonjezeleka ponena za mzele wobadwila wa Mesiya. Pangano limenelo linacititsanso Yesu kukhala ndi mphamvu zolamulila padziko lapansi kwamuyaya. Ndipo pangano la wansembe monga Melekizedeki, litsimikizila kuti mbeuyo idzatumikila monga wansembe. Komabe, Yesu sadzakhala yekha pothandiza anthu kuti akhale angwilo. Palinso ena amene adzozedwa kuti atumikile monga mafumu ndi ansembe. Kodi io acokela kuti? Funso limeneli lidzayankhidwa m’nkhani yotsatila.