Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

 ZA M’NKHOKWE YATHU

Kuwala kwa Coonadi Kufika m’Dziko la Japan

Kuwala kwa Coonadi Kufika m’Dziko la Japan

Tumapepala toitanila anthu ku nkhani ya onse tunagwilitsidwa nchito ku Tokyo, ndipo tunamwazidwa ndi ndeke m’tauni ya Osaka

PA September 6, 1926, woyang’anila woyendela wina anabwelela kwao ku Japan monga mmishonale kucokela ku United States. M’dzikoli munali cabe munthu mmodzi amene anali kulandilako magazini a The Watch Tower. Munthu ameneyu anali atayambitsa kagulu ka ophunzila Baibulo mumzinda wa Kobe, ndipo ameneyu ndiye analandila mmishonaleyo. Ndipo mu mzinda umenewu, Ophunzila Baibulo anacita msonkhano wao waukulu woyamba pa January 2, 1927. Anthu 36 anapezeka pamsonkhano umenewu, ndipo anthu 8 anabatizika. Ndithudi, msonkhano umenewu unali ndi ciyambi cabwino. Koma kodi gulu locepa limeneli likanakwanitsa bwanji kufikila anthu 60 miliyoni a m’dzikolo, amene anafunikila kuona kuwala kwa coonadi ca m’Baibulo?

Mu May 1927, Ophunzila Baibulo okangalika analalikila poyela kuti aitanile anthu ku nkhani za m’Baibulo. Pankhani yoyamba imene inali kudzakambidwa mu mzinda wa Osaka, abale anaika zikwangwani m’madela onse a mzinda kuti aitanile anthu. Anatumiza tumapepala toitanila anthu tokwanila 3,000 kwa anthu olemekezeka. Anagaŵilanso tumapepala tokwanila 150,000. Ciitano cimeneco cinalembedwanso m’manyuzipepala, ndi pa matikiti a sitima okwanila 400,000. Ndipo pa tsiku la nkhani, ndeke ziŵili zinamwaza tumapepala toitanila anthu m’dela lonse tokwanila 100,000. Anthu 2,300 anadzaza holo yaikulu ya Osaka Asahi kuti amvetsele nkhani yakuti, “Ufumu wa Mulungu Wayandikila.” Koma anthu ena pafupifupi 1,000 anauzidwa kubwelela cifukwa cosoŵa malo okhala. Pambuyo pa nkhani, anthu oposa 600 anatsalila kuti amvetsele mbali ya mafunso ndi mayankho. Ndiyeno, m’miyezi yotsatila nkhani za m’Baibulo zinali kupelekedwa m’tauni ya Kyoto ndi m’matauni ena a kumadzulo kwa Japan.

Mu October 1927, Ophunzila Baibulo anakonza zakuti nkhani za m’Baibulo zizipelekedwa m’tauni ya Tokyo. Conco, io anaitananso anthu olemekezeka, kuphatikizapo nduna yaikulu ya boma, aphungu a nyumba ya malamulo, abusa a zipembedzo, ndi akuluakulu a asilikali. Anagwilitsila nchito zikwangwani, manyuzipepala, ndi tumapepala toitanila anthu tokwanila 710,000. Ndipo anthu 4,800 anapezeka pa nkhani zitatu za m’Baibulo zimene zinakambidwa mumzinda waukulu wa Japan.

AKOPOTALA OKANGALIKA

Katsuo ndi Hagino Miura

Akopotala (apainiya) anagwila nchito yofunika kwambili yolalikila uthenga wa Ufumu ku nyumba ndi nyumba. Matsue Ishii ndi mwamuna wake Jizo, amodzi mwa akopotala oyamba ku Japan, analalikila pafupifupi dziko lonse, kuyambila ndi dela la Sapporo mpaka ku Sendai, Tokyo, Yokohama, Nagoya, Osaka, Kyoto, Okayama, ndi Tokushima. Mlongo Ishii ndi mlongo wina wacikulile dzina lake Sakiko Tanaka, anali kuvala zovala zaulemu zooneka ngati khoti kuti akalalikile kwa akuluakulu a boma. Ndipo mmodzi wa io anapempha makope 300 a buku lakuti The Harp of God ndi lakuti Deliverance, kuti awaike mu laibulale ya m’ndende.

Mwamuna wina dzina lake Katsuo Miura ndi mkazi wake Hagino, anapatsidwa mabuku ndi Mlongo Ishii.  Ataŵelenga mabukuwo, io mwamsanga anazindikila kuti apeza coonadi. Anabatizika mu 1931, ndipo anakhala akopotala. Munthu winanso dzina lake Haruichi ndi mkazi wake Tane Yamada, pamodzi ndi acibale ao ambili, analandila coonadi caka ca 1930 cisanafike. Banja limeneli linayamba nchito ya ukopotala, ndipo mwana wao wamkazi, Yukiko, anapita kukatumikila pa Beteli ku Tokyo.

MA “YEHU”—AAKULU NDI AANG’ONO

Yehu wamkulu amene munali kugona apainiya 6

Kale kwambili, magalimoto anali odula ku Japan ndipo miseu inali yoipa. Conco, Kazumi Minoura ndi akopotala ena anali kugwilitsila nchito makalavani opanda injini. Iwo anali kuchula makalavani amenewo kuti Yehu, potengela dzina la Yehu, woyendetsa galeta amene anadzakhala mfumu mu Isiraeli. (2 Maf. 10:15, 16) Ma Yehu Aakulu atatu amenewo, kapena kuti makalavani anali a mamita 2.2 m’litali, 1.9 m’lifupi, ndi 1.9 kutalika kwake, ndipo kalavani lililonse munali kugona apainiya 6. Kuonjezela apo, panalinso ma Yehu aang’ono 11 amene munali kugona anthu aŵili, ndipo anali kukokedwa ndi njinga. Ma Yehu amenewa anapangidwa ku nthambi ya ku Japan. Kiichi Iwasaki, amene anathandiza kupanga ma Yehu amenewo, anati: “Yehu iliyonse inali ndi tenti ndi batili ya galimoto kuti aziyatsila malaiti.” Akopotala anali kuwala monga zounikila za coonadi m’dziko lonse la Japan. Iwo anali kupita ndi makalavani ao m’madela a mapili ndi m’zigwa, kuyambila ca kumpoto kwa Hokkaido mpaka kum’mwela kwa Kyushu.

Yehu wamng’ono amene munali kugona anthu aŵili

Kopotala wina dzina lake Ikumatsu Ota, anati: “Tikangofika m’tauni, tinali kuimika kalavani yathu m’mbali mwa mtsinje kapena pamalo oonekela bwino. Coyamba, tinali kupita kukaonana ndi anthu apamwamba monga meya wa mzinda. Ndiyeno, tinali kupita kunyumba ndi nyumba kukagaŵila mabuku athu. Tikatsiliza kulalikila m’gawo lonse, tinali kupita m’tauni ina.”

Ophunzila Baibulo anali cabe 36 pamene anacita msonkhano wao waukulu woyamba m’tauni ya Kobe. (Zek. 4:10) Koma mu 1932, patangopita zaka zisanu, akopotala 103 ndi ofalitsa ena ku Japan anagwila nchito yolalikila, ndipo anagaŵila mabuku oposa 14,000. Masiku ano, ulaliki wa poyela ukucitika m’madela ambili ku Japan, ndipo ofalitsa pafupifupi 220,000 akuwalitsa coonadi m’dziko la Japan.—Za m’nkhokwe yathu ku Japan.

Cithunzi colembedwa ndi Kiichi Iwasaki, amene anapanga ma Yehu ku Beteli ya ku Japan