Tikhale Ogwilizana Pamene Mapeto a Dzikoli Ayandikila
“Ndife ziwalo za thupi limodzi.”—AEF. 4:25.
1, 2. Kodi Mulungu amafuna kuti olambila ake onse, acinyamata ndi acikulile, azicita ciani?
KODI ndinu wacinyamata mumpingo? Ngati ndi conco, dziŵani kuti ndinu wofunika kwambili m’gulu la Yehova la padziko lonse. M’maiko oculuka, anthu ambili amene akubatizidwa ndi acinyamata. Ndithudi, n’zolimbikitsa kwambili kuona acinyamata ambili akusankha kutumikila Yehova.
2 Pokhala wacinyamata, kodi mumakonda kukhala ndi acinyamata anzanu? Sitikukaikila kuti mumatelo. Zimakhala zosangalatsa kuceza ndi anthu a msinkhu wathu. Komabe, kaya ndife acinyamata kapena acikulile, ndiponso mosasamala kanthu za kumene tinakulila, Mulungu amafuna kuti tizimulambila mogwilizana. Mtumwi Paulo analemba kuti colinga ca Mulungu n’cakuti “anthu kaya akhale a mtundu wotani apulumuke ndi kukhala odziŵa coonadi molondola.” (1 Tim. 2:3,4) Lemba la Chivumbulutso 7:9 limanena kuti olambila Mulungu ndi ocokela “m’dziko lililonse, fuko lililonse, mtundu uliwonse, ndi cinenelo ciliconse.”
3, 4. (a) Ndi mzimu wotani umene wafala pakati pa acinyamata masiku ano? (b) Ndi khalidwe liti limene limagwilizana ndi lemba la Aefeso 4:25?
3 Acinyamata amene amatumikila Yehova ndi osiyana kwambili ndi acinyamata a m’dzikoli. Acinyamata ambili amene satumikila Yehova ali ndi umoyo wodzikonda, ndipo amangocita zofuna zao. Ocita kafukufuku ena amanena kuti acinyamata a masiku ano ndi “M’badwo Wodzikonda.” Mwa zokamba zao ndi kavalidwe kao, acinyamatawa amasonyeza kuti salemekeza acikulile ndipo amawaona kuti ndi “otsalila.”
4 Mzimu umenewu ndi wofala kwambili. Conco, acinyamata amene akutumikila Yehova amaona kuti pamafunika khama kwambili kuti apewe mzimu umenewu n’kuyamba kuona zinthu mmene Mulungu amazionela. Ngakhale m’nthawi ya atumwi, Paulo analangiza Akristu anzake kuti apewe ‘kaganizidwe kamene kakugwila nchito mwa ana akusamvela’ kamene io “panthawi inayake” anali kuyendamo. (Ŵelengani Aefeso 2:1-3.) Tikuyamikila acinyamata onse amene amapewa mzimu wa dziko ndi kuyesetsa kutumikila Mulungu mogwilizana ndi abale ndi alongo onse. Khalidwe limeneli n’logwilizana ndi mau a Paulo akuti “ndife ziwalo za thupi limodzi.” (Aef. 4:25) Pamene mapeto a dzikoli akuyandikila, tifunika kucita zinthu mogwilizana kwambili kuposa ndi kale lonse. Tsopano tiyeni tikambilane zitsanzo zingapo za m’Baibulo zimene zingatithandize kuona kufunika kokhala ogwilizana.
ANACITA ZINTHU MOGWILIZANA
5, 6. Kodi nkhani ya Loti ndi ana ake aakazi ikutiphunzitsa ciani pankhani ya kukhala ogwilizana kwambili?
5 M’nthawi zakale, Yehova anali kuteteza anthu ake akamathandizana panthawi za mavuto. Atumiki a Mulungu amakono angaphunzilepo kanthu pa zitsanzo za m’Baibulo zimenezo. Cimodzi mwa zitsanzo zimenezo ndi ca Loti.
6 Loti ndi banja lake anali pangozi cifukwa mzinda wa Sodomu, umene io anali kukhalamo, unali pafupi kuonongedwa. Angelo a Mulungu analamula Loti kuti acoke mumzindawo ndi kukakhala ku dela la kumapili. Iwo anamuuza kuti: “Thawani mupulumutse moyo wanu!” (Gen. 19:12-22) Loti anamvela ndipo ana ake aakazi naonso anathawa mumzindawo pamodzi ndi iye. Koma n’zomvetsa cisoni kuti anansi ake sanathawe. Amuna amene anali kudzakwatila ana ake anaona ngati Loti anali ‘kunena zoceza.’ Pamapeto pake, io anaonongedwa. (Gen. 19:14) Loti yekha ndi ana ake aakazi amene anagwilizana naye kwambili ndi amene anapulumuka.
7. Kodi Yehova anathandiza bwanji anthu amene anacita zinthu mogwilizana panthawi imene Aisiraeli anali kucoka mu Iguputo?
7 Ganizilani citsanzo cinanso ici: Pamene Aisiraeli anali kutuluka mu Iguputo, io sanapange tumagulu n’kumayenda njila zosiyanasiyana. Ndiponso pamene Mose ‘anatambasula dzanja lake kuloza panyanja,’ Yehova anagaŵa nyanjayo. Koma Mose sanaoloke yekha kapena kuoloka ndi Aisiraeli ocepa cabe panyanjayo. Anaoloka nyanjayo onse pamodzi monga gulu motetezedwa ndi Yehova. (Eks.14:21, 22, 29, 30) Iwo anacita zinthu mogwilizana, ndipo “khamu la anthu a mitundu yosiyanasiyana” amene sanali Aisiraeli anapita nao limodzi. (Eks. 12:38) Kodi zikanakhala zanzelu ngati Aisiraeli ena, mwina acinyamata, akanapanga kagulu n’kuyamba kuyenda njila imene io akanaona kukhala yoyenela? Ai. Kucita zimenezo kukanapangitsa kuti Yehova asawateteze.—1 Akor. 10:1.
8. Kodi anthu a Mulungu anaonetsa bwanji kuti anali ogwilizana m’nthawi ya Yehosafati?
8 M’masiku a Mfumu Yehosafati, anthu a Mulungu anayang’anizana ndi “khamu lalikulu” la adani ocokela m’madela ozungulila. (2 Mbiri 20: 1, 2) N’zolimbikitsa kuti atumiki a Mulungu sanayese kulimbana ndi adani ao mwa mphamvu zao zokha. Koma anadalila Yehova. (Ŵelengani 2 Mbiri 20:3, 4.) Iwo anacita zinthu mogwilizana, ndipo palibe amene anali kucita za mumtima mwake. Baibulo limanena kuti: “Anthu onse a ku Yuda anali ataimilila pamaso pa Yehova, kuphatikizaponso akazi ao ndi ana ao, ngakhalenso ana ao ang’onoang’ono.” (2 Mbiri 20:13) Onse pamodzi, acicepele ndi acikulile, anakhulupilila Yehova ndi kutsatila malangizo ake, ndipo Yehova anawateteza kwa adani ao. (2 Mbiri 20:20-27) Ici ndi citsanzo cabwino kwambili kwa ife anthu a Mulungu coonetsa zimene tiyenela kucita tikakumana ndi mavuto.
9. Pa nkhani ya kukhala ogwilizana, kodi tikuphunzila ciani pa zocita za Akristu a m’nthawi ya atumwi?
9 Akristu a m’nthawi ya atumwi naonso anali kucita zinthu mogwilizana. Mwacitsanzo, Ayuda ambili ndi anthu ena otembenukila ku Ciyuda amene anakhala Akristu, anali kulabadila “zimene atumwiwo anali kuphunzitsa. Iwo anali kugaŵana zinthu, kudya cakudya komanso kupemphela.” (Mac. 2:42) Panthawi ya cinzunzo, mgwilizano wao unaonekela kwambili cifukwa panthawiyo ndi pamene anafunika kuthandizana kwambili. (Mac. 4:23, 24) Mwacionekele, inunso mungavomeleze kuti panthawi ya mavuto, kukhala ogwilizana n’kofunika kwambili.
KHALANI OGWILIZANA PAMENE TSIKU LA YEHOVA LIKUYANDIKILA
10. Kodi ndi liti pamene tidzafunika kukhala ogwilizana kwambili?
10 Posacedwapa, padzikoli padzacitika mavuto amene sanacitikepo n’kale lonse. Mneneli Yoweli ananena kuti nthawi imeneyo idzakhala “tsiku lamdima ndi lacisoni.” (Yow. 2:1, 2; Zef. 1:14) Panthawiyo, anthu a Mulungu adzafunika kukhala ogwilizana kwambili. Kumbukilani kuti Yesu anakamba kuti: “Ufumu uliwonse wogawanika umatha.”—Mat. 12:25.
11. Kodi mau a pa Salimo 122:3, 4 tingawagwilizanitse bwanji ndi anthu a Mulungu lelolino? (Onani cithunzi cili kuciyambi kwa nkhani ino.)
11 Panthawi ya mavuto imeneyo, tidzafunika kukhala ogwilizana kwambili. Mgwilizano umene tidzafunika kukhala nao pocita zinthu zakuuzimu tingauyelekezele ndi mmene nyumba za mumzinda wa Yerusalemu wakale zinamangidwila. Nyumbazo zinamangidwa moyandikana kwambili cakuti wamasalimo wina ananena kuti mzinda wa Yerusalemu “unamangidwa ngati cinthu cimodzi cogwilizana.” Conco, zinali zosavuta kuti anthu a mumzindawo azithandizana ndi kutetezana pakakhala mavuto. Komanso kuyandikana kwa nyumbazo kungaimilenso mgwilizano umene mtundu wonse wa Isiraeli unali nao pa kulambila. Mgwilizano wao unali kuonekela pamene ‘mafuko onse a Ya’ anali kukumana kuti alambile Mulungu. (Ŵelengani Salimo 122:3, 4.) Ifenso tiyenela kupitilizabe kukhala ngati “cinthu cimodzi cogwilizana” masiku ano ndiponso m’masiku ovuta amene akubwela mtsogolo.
12. N’ciani cidzatithandiza kupulumuka panthawi imene anthu a Mulungu adzaukilidwa?
12 N’cifukwa ciani tidzafunika kukhala ogwilizana kwambili panthawiyo? Lemba la Ezekieli caputala 38 linanenelatu kuti “Gogi wa kudziko la Magogi” adzaukila anthu a Mulungu. Panthawi imeneyo sitidzayenela kulola cina ciliconse kutigaŵanitsa. Sitidzafunikila kuika cidalilo cathu pa dziko kuti tipeze thandizo. M’malomwake, tidzafunika kugwilizana kwambili ndi abale athu. Koma sikuti tidzapulumuka cabe cifukwa cakuti tili m’gulu la Mulungu. Panthawi yovuta imeneyo, Yehova ndi Mwana wake adzapulumutsa anthu amene amaitana pa dzina lake. (Yow. 2:32; Mat. 28:20) Komabe anthu amene analeka kugwilizana ndi gulu la nkhosa la Mulungu, kapena kuti amene anadzilekanitsa ndi gulu, n’zokaikitsa kuti adzapulumuka.—Mika 2: 12.
13. Kodi acinyamata oopa Mulungu angaphunzile ciani pa zimene takambilanazi?
13 Motelo, n’zoonekelatu kuti si canzelu kutengela acinyamata amene amapatuka n’kuyamba kucita zinthu paokha. Posacedwapa, tonse, kaya ndife acinyamata kapena acikulile, tidzafunika kwambili thandizo la Akristu anzathu. Ino ndiyo nthawi yophunzila kucitila zinthu pamodzi, cifukwa mgwilizano wotelo udzafunika kwambili mtsogolo.
“ZIWALO ZA THUPI LIMODZI”
14, 15. (a) N’cifukwa ciani Yehova amaphunzitsa acinyamata ndi acikulile masiku ano? (b) Ndi malangizo otani amene Yehova amatipatsa otilimbikitsa kukhala ogwilizana?
14 Yehova akutithandiza kuti ‘tizimutumikila mogwilizana.’ (Zef. 3:8, 9) Iye akutiphunzitsa kuti tizicita zinthu mogwilizana ndi colinga cake camuyaya. Kodi colinga cimeneci n’ciani? Iye amafuna “kusonkhanitsanso zinthu zonse pamodzi mwa Khristu.” (Ŵelengani Aefeso 1:9, 10.) Mulungu amafuna kugwilizanitsa zolengedwa zonse zimene ndi zomvela m’cilengedwe conse, ndipo adzakwanilitsa colinga cake cimeneci. Kodi zimenezi sizikukuthandizani inuyo acinyamata kuona kuti mufunika kucita zinthu mogwilizana ndi gulu la Yehova?
15 Yehova akutiphunzitsa kukhala ogwilizana lelolino n’colinga cakuti tidzakhale ogwilizana kwamuyaya. Malemba amatilangiza mobwelezabweleza kuti ‘tizisamalilana mofanana,’ ‘tikhale ndi cikondi ceniceni,’ ‘tizitonthozana,’ ndi ‘kulimbikitsana.’ (1 Akor. 12:25; Aroma 12:10; 1 Ates. 4:18; 5:11) Yehova amadziŵa kuti Akristu tonse ndife opanda ungwilo, ndipo zimenezi zingapangitse kuti tizivutika kucita zinthu mogwilizana. Conco, tiyenela kuyesetsa ‘kukhululukilana ndi mtima wonse.’—Aef. 4:32.
16, 17. (a) Kodi colinga cimodzi ca misonkhano yathu n’ciani? (b) N’ciani cimene acinyamata angaphunzile pa zimene Yesu anali kucita ali wacinyamata?
16 Yehova amatithandiza kukhala ogwilizana kudzela m’misonkhano yacikristu. Takhala tikuŵelenga mobwelezabweleza malangizo opezeka pa lemba la Aheberi 10:24, 25. Cimodzi mwa zolinga za misonkhano yathu ndi kutithandiza ‘kuganizilana kuti tilimbikitsane pa cikondi ndi nchito zabwino.’ N’zosangalatsa kuti cimodzi mwa zolinga za misonkhano n’cakuti ‘tizilimbikitsana, ndipo tiwonjezele kucita zimenezi, makamaka pamene tikuona kuti tsikulo likuyandikila.’
17 Pamene anali wacinyamata, Yesu anapeleka citsanzo cabwino cifukwa anali kukonda misonkhano. Ali ndi zaka 12, iye anali pamodzi ndi makolo ake pa msonkhano waukulu. Panthawi ina, iye anasowa koma osati cifukwa cakuti anapita kukaseŵela ndi acinyamata anzake. M’malomwake, Yosefe ndi Mariya anamupeza akukambilana mau a Mulungu ndi aphunzitsi pa kacisi.—Luka 2:45-47.
18. Kodi mapemphelo athu angathandize bwanji kuti tikhale ogwilizana?
18 Kuonjezela pa kukulitsa cikondi pakati pathu ndi kupezeka pa misonkhano kuti tilimbitse mgwilizano wathu, tifunikanso kumapemphelelana. Popemphelela abale athu kwa Yehova, tifunika kuchula mwacindunji mavuto amene akukumana nao. Tikamatelo, timayamba kuwakonda kwambili. Koma sikuti ndi Akristu acikulile okha amene ayenela kucita zimenezi. Ngati ndinu wacinyamata, kodi mumayesetsa kupemphelela Akristu anzanu kuti mukhale nao pa ubwenzi wolimba monga abale ndi alongo anu acikristu? Kucita zimenezi kudzakuthandizani kuti musadzakhale mbali ya dzikoli pamene lidzaonongedwa.
TIZIONETSA KUTI “NDIFE ZIWALO ZA THUPI LIMODZI”
19-21. (a) N’ciani cofunika cimene timacita poonetsa kuti “ndife ziwalo za thupi limodzi”? Pelekani zitsanzo. (b) Kodi mukuphunzila ciani pa zimene abale ena anacita pamene kunacitika ngozi zacilengedwe?
19 Anthu a Yehova anayamba kale kucita zinthu motsatila mfundo ya pa Aroma 12:5. Lembali limati: “Aliyense payekha ndi ciwalo ca mnzake.” Timaona umboni wa zimenezi pakagwa tsoka. Mu December 2011, mvula yamkuntho inapangitsa kuti madzi asefukile pa cilumba ca Mindanao ku Philippines. Pa nthawi yocepa cabe, nyumba zoposa 40,000 zinadzala madzi, kuphatikizapo nyumba zambili za abale athu. Komabe, ofesi ya nthambi m’dzikolo inanena kuti “abale a m’madela ena anayamba kutumiza thandizo m’delalo ngakhale kuti makomiti oyang’anila za cithandizo anali asanapangidwe.”
20 Mofananamo, pamene kum’maŵa kwa dziko la Japan kunacitika civomezi camphamvu cimene cinapangitsa kuti kucitike tsunami, abale ndi alongo athu anavutika kwambili. Ena anatsala opanda ciliconse. Yoshiko anali kukhala pa mtunda wa makilomita pafupifupi 40 kucokela pa Nyumba ya Ufumu, ndipo nyumba yake inaonongeka. Iye anati: “Tinadabwa titamva kuti tsiku lotsatila pambuyo pa civomezi, woyang’anila dela ndi m’bale wina anapita kwathu kukatifunafuna.” Mwacimwemwe, iye anakambanso kuti: “Tinayamikila kwambili cifukwa cakuti tinalandila cakudya coculuka cakuuzimu kudzela mumpingo. Kuonjezela pamenepo, tinalandila zovala zamphepo, nsapato, zola [zikwama], ndi zovala zamkati.” M’bale wina wa m’komiti yoyang’anila za cithandizo anati: “Abale ocokela m’madela osiyanasiyana m’dziko la Japan anacita zinthu mogwilizana pothandiza abale athu. Abale ena anacokela ku dziko la United States, limene lili kutali ndi dziko la Japan, kuti akathandize abale athu. Pamene anafunsidwa kuti n’cifukwa ciani anayenda ulendo wautali conco, io anayankha kuti, ‘Ndife ogwilizana ndi abale athu a ku Japan, ndipo tifunika kuwathandiza.’” Kodi simunyadila kukhala m’gulu limene limasamalila kwambili anthu ake? Kunena zoona, Yehova amakondwela kwambili ndi mzimu wogwilizana umenewu.
21 Kukhala ndi mzimu wotelo kudzatithandiza kucita zinthu mogwilizana tikadzakumana ndi mavuto kapena tikadzaletsedwa kugwilizana ndi abale athu a m’maiko ena. Pamene dzikoli lili pafupi kuonongedwa, n’zosakaikitsa kuti tidzakumana ndi mavuto. Conco, tikamacita zinthu mogwilizana ndiye kuti tikuphunzila mmene tidzacitila tikadzakumana ndi mavuto mtsogolo. Fumiko, amene anapulumuka mphepo yamkuntho ku Japan, anati: “Mapeto ali pafupi kwambili. Motelo tifunika kupitilizabe kuthandiza Akristu anzathu pamene tikuyembekezela nthawi imene sikudzakhalanso ngozi zacilengedwe.”
22. Ndi phindu lokhalitsa liti limene tidzapeza tikakhalabe ogwilizana?
22 Acinyamata ndi acikulile akamayesetsa kulimbikitsa mgwilizano, ndiye kuti akukonzekela kudzapulumuka mapeto a dziko loipali lomwe mulibe mgwilizano. Monga mmene anacitila nthawi zakale, Mulungu adzapulumutsa anthu ake. (Yes. 52:9, 10) Nthawi zonse muzikumbukila kuti mufunika kupitilizabe kukhala m’gulu la anthu a Mulungu kuti mudzapulumuke. Cinthu cimodzi cimene cingakuthandizeni kucita zimenezo ndi kuyamikila madalitso amene takhala tikulandila. Nkhani yotsatila idzafotokoza zimenezi.