Kodi Kukwatiwa “Mwa Ambuye” N’kofunikabe?
“Sindikupeza munthu woti ndingakwatilane naye mumpingo, ndipo ndikuopa kuti ndingakalambe ndili mbeta.”
“Amuna ena m’dzikoli ndi okoma mtima, acikondi ndi acifundo. Sadana ndi cipembedzo canga, ndipo amandisangalatsa kuposa abale ena.”
Atumiki ena a Mulungu alankhulapo mau ngati amenewa pankhani yopeza munthu wokwatilana naye. Ngakhale ndi conco, io amadziwa bwino malangizo a mtumwi Paulo okhudza kukwatiwa “mwa Ambuye.” Ndipo Akristu onse ayenela kutsatila malangizo amenewa. (1 Akor. 7:39) Nanga n’cifukwa ciani angalankhule zofanana ndi zili pamwambazi?
ZIMENE ZIMACITITSA ENA KUKAIKILA
Amene amakamba mau ngati amenewo amaona kuti pali alongo ambili kuposa abale. Ndipo izi zilidi conco m’maiko ambili. Ganizilani zitsanzo ziŵili izi: Ku Korea, pa Mboni 100 zomwe ndi mbeta, 57 ndi alongo, ndipo 43 ndi abale. Ku Colombia nakonso pa avaleji, 66 pelesenti ya Mboni ndi alongo ndipo 34 pelesenti ndi abale.
M’madela ena, cinthu cimene cimavuta n’cakuti makolo amene si Mboni amafuna ndalama zambili za malowolo, moti abale osauka zimawavuta kukwatila. Poganizila zimenezi, mlongo angaone kuti n’zosatheka kukwatiwa “mwa Ambuye.” Motelo, angadzifunse kuti, “Kodi n’kwanzelu kuganizila kuti ndingapeze munthu wondikwatila mumpingo?” *
KUDALILA YEHOVA NDI KOFUNIKA
Ngati munakhalapo ndi maganizo amenewa, dziŵani kuti Yehova amadziŵa za vuto lanulo ndi mmene mukumvelela.—2 Mbiri 6:29, 30.
Ngakhale zili conco, Yehova waika malangizo m’Mau ake okhudza kukwatiwa kokha mwa Ambuye. N’cifukwa ciani? Cifukwa cakuti iye amadziŵa bwino zimene anthu ake amafunikila. Sikuti iye amangofuna cabe kuteteza atumiki ake ku mavuto amene angakumane nao cifukwa cosankha zinthu mopanda Neh. 13:23-26) Conco, pofuna kuti atumiki ake zinthu ziziwayendela bwino, Mulungu watipatsa malangizo akuti tiyenela kukwatila olambila oona. (Sal. 19:7-10; Yes. 48:17, 18) Timayamikila kwambili kuti Mulungu amatipatsa malangizo acikondi ndi odalilika. Tikamamvela Yehova monga Wolamulila wathu, timaonetsa kuti iye ndi woyenela kutiuza zimene tiyenela kucita.—Miy. 1:5.
nzelu, koma amafunanso kuti tikhale osangalala. M’nthawi ya Nehemiya, Ayuda ambili anali kukwatila akazi omwe sanali kulambila Yehova. Iye anachula za citsanzo coipa ca Solomo. Nehemiya anati Solomo “anakondedwa ndi Mulungu wake, mwakuti Mulungu anamuika kukhala mfumu ya Isiraeli yense. Koma akazi acilendo anamucimwitsa.” (Mosakaikila, inu simufuna “kumangidwa m’goli” ndi munthu amene angakucititseni kusiya kutumikila Mulungu. (2 Akor. 6:14) Malangizo a Mulungu amakhala othandiza nthawi zonse, ndipo Akristu ambili masiku ano asankha kumvela Yehova. Koma ena asankha zosiyana ndi zimenezi.
NDI KOFUNIKABE
Maggy * mlongo wa ku Australia, anafotokoza zimene zinali kucitika pamene anayamba cibwenzi ndi munthu wosakhulupilila. Iye anati: “Ndinali kuphonya misonkhano yambili pofuna kuceza ndi cibwenzi cangaci. Ndinafooka mwakuuzimu.” Ratana wa ku India anayamba cibwenzi ndi mnyamata amene anali naye kalasi imodzi yemwenso anali atayamba kuphunzila Baibulo. Colinga cimene mnyamatayo anayambila kuphunzila Baibulo cinali cakuti akhale pacibwenzi ndi Ratana. M’kupita kwa nthawi Ratana anasiya kutumikila Yehova, ndipo anayamba kupita ku cipembedzo cina n’colinga cofuna kukwatilana ndi mnyamatayo.
Citsanzo cina ndi ca Ndenguè wa ku Cameroon. Iye anakwatiwa ali ndi zaka 19. Mwamuna amene anam’funsila cikwati anam’lonjeza kuti sadzamuletsa kupita ku cipembedzo cake. Koma patapita milungu iŵili pambuyo pokwatilana, mwamuna wake anamuletsa kupita ku misonkhano yacikristu. Iye anati: “Ndinakhala wosungulumwa ndipo ndinali kungokhalila kulila. Ndinazindikila kuti ndinalibe ufulu wocita zinthu pandekha, moti ndimangokhalila kudziimba mlandu.”
N’zoona kuti Akristu ena anakwatiwa kwa anthu amene satumikila Yehova, omwe ndi okoma mtima komanso ololela. Ngakhale kuti mungakwatiwe kwa munthu wokoma mtima amene satumikila Yehova, kodi ubwenzi wanu ndi Yehova ungakhudzidwe bwanji? Nanga mungamamve bwanji mukaganizila kuti simunamvele malangizo opindulitsa amene Mulungu anakupatsani? Koposa zonse, kodi Yehova angamve bwanji pa zimene mungasankhe kucita?—Miy. 1:33.
Abale ndi alongo padziko lonse amavomeleza mfundo yakuti kukwatiwa “mwa Ambuye” ndi kwabwino. Abale ndi alongo omwe ndi mbeta ndi otsimikiza mtima kukondweletsa Yehova, ndipo amafuna kukwatilana ndi munthu amene amalambila Mulungu. Mlongo wina wa ku Japan, wochedwa Michiko, anakakamizidwa ndi acibale ake kukwatiwa ndi munthu wosakhulupilila. Kuonjezela pa kulimbana ndi ciyeso cimeneco, zinali kum’pweteka kuona anzake ena akukwatiwa mumpingo iye n’kukhalabe mbeta. Iye anati: “Kuganizila kuti Yehova ndi ‘Mulungu wacimwemwe,’ kunandithandiza kuona kuti aliyense akhoza kukhala ndi cimwemwe kaya ali m’cikwati kapena ai. Ndipo ndimakhulupililanso kuti iye amatipatsa zokhumba zathu. Conco, ngati sitikupezabe munthu wokwatilana naye, ndi bwino kuyembekeza ngakhale kuti tikufunitsitsa kukwatiwa.” (1 Tim. 1:11) M’kupita kwa nthawi, Michiko anakwatiwa ndi m’bale wabwino, ndipo amakondwela kuti anayembekezela.
Abale ena nawonso akhala akuyembekezela kuti apeza munthu woyenelela wokwatilana naye. Mmodzi wa abale amenewa ndi Bill wa ku Australia. Iye ananena kuti nthawi zina anali kukopeka ndi akazi amene sanali a Mboni. Komabe, iye anali kupewa kukhala nao pacibwenzi. Cifukwa? Cifukwa cakuti iye sanafune ‘kumangidwa m’goli’ ndi wosakhulupilila. Kwa zaka zambili, iye anali kukopeka ndi alongo ena koma io sanali kum’konda. Bill anayembekezela zaka 30 kuti apeze mlongo womuyenelela. Iye anati: “Sindikudandaula kuti ndinayembekezela kwa zaka zambili.” Iye anapitiliza kuti: “Ndimaona kuti ndine wodalitsidwa cifukwa ine ndi mkazi wanga timapitila
limodzi mu ulaliki, kuphunzila pamodzi, ndi kulambila pamodzi. Ndine wokondwela kudziŵana ndi kuyanjana ndi anzake a mkazi wanga cifukwa onse amalambila Yehova. Cikwati cathu n’colimba cifukwa timagwilitsila nchito mfundo za m’Baibulo.”ZIMENE MUNGACITE POYEMBEKEZELA YEHOVA
N’ciani cimene mungacite poyembekezela kuti Yehova akuthandizeni? Muyenela kuganizila cifukwa cake mukali mbeta. Ngati mukuona kuti cifukwa cacikulu n’coti mukutsatila malangizo a m’Baibulo okhudza kukwatiwa “mwa Ambuye,” ndiye kuti mukucita bwino cifukwa mukulemekeza lamulo la Mulungu. Dziŵani kuti Yehova amakondwela mukamamvela Mau ake. (1 Sam. 15:22; Miy. 27:11) Pitilizani ‘kukhutula za mumtima mwanu’ kwa Mulungu mpemphelo. (Sal. 62:8) Mapemphelo anu angakhale atanthauzo kwambili pamene mupitiliza kum’pempha mocokela pansi pa mtima. Ubale wanu ndi Yehova udzalimba kwambili pamene mupitiliza kupilila mosasamala kanthu za ziyeso zimene mungakumane nazo tsiku lililonse. Dziŵani kuti Yehova amakudelani nkhawa cifukwa ndinu amtengo wapatali kwa iye. Iye samalonjeza aliyense kuti adzam’patsa mnzake wa m’cikwati. Koma ngati mukufunadi munthu wokwatilana naye, Mulungu amadziŵa bwino mmene angakhutilitsile zokhumba zanu.—Sal. 145:16; Mat. 6:32.
Nthawi zina mungamve monga mmene wamasalimo anamvela pamene anati: “Fulumilani, ndiyankheni inu Yehova. Mphamvu zanga zatha. Musandibisile nkhope yanu.” (Sal. 143:5-7, 10) Pa nthawi ngati zimenezo, mungafunike kuyembekezela Atate wanu wakumwamba kuti akuonetseni cimene cili cifunilo cake kwa inu. Mungacite zimenezi mwa kupeza nthawi yoŵelenga Mau ake ndi kusinkhasinkha pa zimene mukuŵelenga. Mudzamvetsa malamulo ake ndi kuona mmene anacitila zinthu ndi anthu ake akale. Mwa kutelo, cikhulupililo canu cidzakhala colimba mwa Mulungu.
N’cianinso cingakuthandizeni kukhala osangalala ndi kupindula pamene mukali mbeta? Mungagwilitsile nchito nthawiyo kukulitsa mzimu wozindikila, wopatsa, wogwila nchito mwakhama, ubwino, kudzipeleka kwa Mulungu ndi kukhala ndi mbili yabwino. Makhalidwe amenewa ndi ofunika kuti mudzakhale ndi banja lacimwemwe. (Gen. 24:16-21; Rute 1:16, 17; 2:6, 7, 11; Miy. 31:10-27) Funani Ufumu coyamba mwa kutengako mbali mokwanila m’nchito yolalikila ndi zocita zina zacikristu, ndipo kucita zimenezi kudzakutetezani. Ponena za nthawi imene iye anali mbeta, Bill amene tam’chula poyamba anati: “Zakazo zinadutsa mofulumila cifukwa ndinagwilitsila nchito nthawiyo kutumikila Yehova monga mpainiya.”
Ndithudi, kukwatiwa “mwa Ambuye” n’kofunikabe. Kutsatila malangizo amenewa kudzakuthandizani kulemekeza Yehova ndipo mudzakhala acimwemwe. Baibulo limati: “Wodala ndi munthu woopa Yehova, munthu amene amasangalala kwambili ndi malamulo ake. Zinthu zamtengo wapatali ndiponso cuma zili m’nyumba yake, ndipo cilungamo cake cidzakhalapo kwamuyaya.” (Sal. 112:1, 3) Conco, khalani otsimikiza mtima kutsatila lamulo la Mulungu lokhudza kukwatiwa “mwa ambuye.”