Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Muzitsanzila Mulungu Amene Watilonjeza Moyo Wosatha

Muzitsanzila Mulungu Amene Watilonjeza Moyo Wosatha

“Muzitsanzila Mulungu, monga ana ake okondedwa.” —AEF. 5:1.

1. Ndi nzelu zotani zimene Yehova watipatsa zimene zingatithandize kuti timutsanzile?

YEHOVA anatipatsa nzelu zotithandiza kuganizila mmene ena akumvela. Nthawi zina, tingathe kumvetsa mavuto a ena ngakhale kuti sitinakumanepo nao. (Ŵelengani Aefeso 5:1, 2.) Kodi mphatso imeneyi ingatithandize bwanji kutsanzila Yehova? Nanga n’cifukwa ciani tifunika kuigwilitsila nchito mosamala?

2. Kodi Yehova amamva bwanji tikamavutika?

2 Mosakaikila, timasangalala kuti Mulungu walonjeza moyo wosafa wakumwamba kwa odzozedwa okhulupilika ndiponso moyo wosatha padziko lapansi kwa “nkhosa zina” za Yesu zokhulupilika. (Yoh. 10:16; 17:3; 1 Akor. 15:53) Kaya tili ndi ciyembekezo ca moyo wa kumwamba kapena padziko lapansi, panthawiyo sitidzakumana ndi mavuto amene alipo masiku ano. Yehova adziŵa mavuto amene tikukumana nao, monga mmene anacitila ndi Aisraeli pamene anali kuvutika mu ukapolo ku Iguputo. Malemba amati: “Pamene io anali kuvutika m’masautso ao onse, iyenso anali kuvutika.” (Yes. 63:9) Patapita zaka zambili, Ayuda anali ndi mantha kuti amange kacisi cifukwa adani ao anali kuwaopseza, koma Mulungu anati: “Amene akukukhudzani, akukhudza mwana wa diso langa.” (Zek. 2:8) Monga mmene mayi amakondela mwana wake, Yehova nayenso amathandiza anthu ake mwacikondi. (Yes. 49:15) Yehova amadziŵa mmene ena akumvela, ndipo nafenso watipatsa nzelu zotithandiza kuganizila mmene ena akumvela.—Sal. 103:13, 14

MMENE YESU ANAONETSELA CIKONDI CA MULUNGU

3. N’ciani cikuonetsa kuti Yesu anali wacifundo?

3 Yesu anali kumvetsa mavuto a ena, ngakhale amene iye sanakumanepo nao. Mwacitsanzo, anthu anali kukhala mwamantha cifukwa coopa atsogoleli acipembedzo amene anali kuwanamiza ndi kupanga malamulo ambili olemetsa. (Mat. 23:4; Maliko 7:1-5; Yoh. 7:13) Yesu sanaope kapena kunamizidwa, koma anacitila cifundo anthuwo ngakhale kuti sanakumanepo ndi vutolo. Conco, “poona cikhamu ca anthu, iye anawamvela cisoni, cifukwa anali onyukanyuka ndi otayika ngati nkhosa zopanda m’busa.” (Mat. 9:36) Mofanana ndi Atate ake, Yesu anali wacikondi ndi wacifundo.—Sal. 103:8.

4. Kodi Yesu anali kucita ciani cifukwa comvela cifundo ena?

4 Yesu akaona anthu akuvutika, anali kuwathandiza mwacikondi. Mwanjila imeneyi, iye anaonetsa cikondi cimene Atate ake ali naco. Atalalikila m’madela ambili, Yesu ndi atumwi ake anaganiza zopita kwaokha kuti akapume. Koma cifukwa comvela cifundo anthu amene anali kumuyembekezela, anayamba “kuwaphunzitsa zinthu zambili.”—Maliko 6:30, 31, 34.

TINGATSANZILE BWANJI CIKONDI CA YEHOVA?

5, 6. Kuti titsanzile cikondi ca Mulungu, kodi tiyenela kucita zinthu motani ndi anzathu? Pelekani citsanzo. (Onani cithunzi kuciyambi kwa nkhaniyi.)

5 Mmene timacitila zinthu ndi ena zimaonetsa ngati timatsanzila cikondi ca Mulungu kapena ayi. Yelekezelani kuti Mkristu wacinyamata, dzina lake Alan, akuganizila za m’bale wina wacikulile amene amavutika kuŵelenga kaamba ka vuto la maso. Cifukwa ca ukalamba sakwanitsanso kulalikila kunyumba ndi nyumba. Alan akukumbukila mau a Yesu akuti: “Zimene mukufuna kuti anthu akucitileni, inuyo muwacitile zomwezo.” (Luka 6:31) Ndiyeno, Alan adzifunsa kuti, ‘Kodi ndimafuna kuti anthu azindicitila ciani?’ Ndipo adziyankha kuti, ‘Ndimafuna kuti azichaya nane bola.’ Koma m’bale wacikulileyo sangachaye bola. Malinga ndi mau a Yesu, tiyenela kudzifunsa kuti, ‘Ngati ndakumana ndi mavuto amene mnzanga akukumana nao, kodi ndingafune kuti ena andicitile ciani?’

6 Alan ndi wacinyamata, koma angakwanitse kuganizila mavuto amene sanakumanepo nao. Iye akuona mavuto amene m’bale wacikulileyo akukumana nao ndipo akumumvetsela mokoma mtima. Pang’onopang’ono, Alan akumvetsa mmene m’bale wacikulileyo amamvelela cifukwa colephela kuŵelenga Baibulo kapena kulalikila kunyumba ndi nyumba. Alan ataganizila mavuto a m’baleyo, akuzindikila zimene angacite kuti amuthandize, ndipo akufunitsitsa kucitapo kanthu. Nafenso tingacite cimodzimodzi. Kuti titsanzile cikondi ca Mulungu tiyenela kuganizila mmene ena akumvelela.—1 Akor. 12:26.

Muzitsanzila Yehova mwa kusonyeza cikondi (Onani ndime 7)

7. Tingacite bwanji kuti timvetse mmene anthu amene akukumana ndi mavuto akumvelela?

7 Nthawi zina zimavuta kumvetsa mavuto amene ena akukumana nao. Anthu ambili amakumana ndi mavuto amene sitinakumanepo nao. Abale athu ena akuvutika cifukwa ca matenda, ukalamba kapena cifukwa cakuti anavulala. Ena akuvutika ndi matenda a maganizo kapena cifukwa cakuti anthu ena anawacitila nkhanza. Enanso akuvutika cifukwa cosiyana cipembedzo ndi anthu a m’banja lao kapena cifukwa cokhala m’banja la kholo limodzi. Aliyense amakumana ndi mavuto osiyanasiyana amene mwina ife sitinakumanepo nao. Tingatsanzile bwanji cikondi ca Mulungu pocita zinthu ndi anthu otelo? Tiyenela kumvetsela mwachelu pamene akutifotokozela mavuto ao. Kucita zimenezi kudzatilimbikitsa kutsanzila cikondi ca Yehova mwa kuwathandiza. Mavuto amene anthu amakumana nao amasiyanasiyana, koma tingathe kuwalimbikitsa mwakuuzimu kapena kuwapatsa thandizo lina.—Ŵelengani Aroma 12:15; 1 Petulo 3:8.

TSANZILANI KUKOMA MTIMA KWA YEHOVA

8. N’ciani cinathandiza Yesu kucita zinthu mokoma mtima?

8 Mwana wa Mulungu anati: “Wam’mwambamwamba,  . . ndi wacifundo kwa osayamika ndi kwa oipa.” (Luka 6:35) Yesu anali kutsanzila kukoma mtima kwa Mulungu. N’ciani cinathandiza Yesu kucita zimenezo? Iye anali kuganizila mmene zokamba ndi zocita zake zingakhudzile ena. Mwacitsanzo, mayi wina amene anali wodziŵika kuti ndi wocimwa anafika kwa Yesu, ndipo anayamba kulila cakuti ananyowetsa mapazi ake ndi misozi. Yesu anazindikila kuti mayiyo analapa, ndipo anadziŵanso mmene akanamvelela akanamukalipila. Conco, anamuyamikila ndi kumukhululukila. Komanso pamene Mfarisi anakhumudwa ndi zimene zinacitika, Yesu anakamba naye mokoma mtima.—Luka 7:36-48.

9. N’ciani cingatithandize kutsanzila kukoma mtima kwa Mulungu? Pelekani citsanzo.

9 Kodi tingatsanzile bwanji kukoma mtima kwa Mulungu? Mtumwi Paulo analemba kuti: “Kapolo wa Ambuye sayenela kukangana ndi anthu, koma ayenela kukhala wodekha kwa onse.” (2 Tim. 2:24) Anthu odekha amakhala osamala pocita zinthu ndi ena kuti apewe kuwakhumudwitsa. Kodi mungasonyeze bwanji kudekha pa zocitika izi? Tiyelekezele kuti muli ku nchito, ndiyeno woyang’anila sakugwila bwino nchito yake. Kodi mungacite ciani? Tinenenso kuti m’bale wabwela kumisonkhano pambuyo pa miyezi yambili. Kodi mungakambe naye bwanji? Kapena muli mu utumiki, ndipo mwininyumba wakuuzani kuti, “Ndine wotangwanika.” Kodi mudzacita zinthu momuganizila? Tinenenso kuti mnzanu wa muukwati wakufunsani kuti, “N’cifukwa ciani simunandiuze zimene munakonza kudzacita pa Ciŵelu?” Kodi mudzayankha modekha? Kuganizila mmene ena akumvela ndi mmene mau athu angawakhudzile, kudzatithandiza kutsanzila kukoma mtima kwa Yehova pokamba ndi pocita nao zinthu.—Ŵelengani Miyambo 15:28.

TSANZILANI NZELU ZA MULUNGU

10, 11. N’ciani cingatithandize kutsanzila nzelu za Mulungu? Pelekani citsanzo

10 Kuganizila zinthu zimene sizinaticikilepo kungatithandizenso kutsanzila nzelu za Yehova ndi kudziŵa zotulukapo za zocita zathu. Nzelu ndi limodzi mwa makhalidwe akuluakulu a Yehova, ndipo iye akafuna amaonelatu zinthu zamtsogolo. Ifeyo sitingathe kuonelatu zamtsogolo, koma timafunika kuganizila zotulukapo za zinthu zimene tifuna kucita. Aisiraeli sanaganizile za mavuto amene angabwele cifukwa cosamvela Mulungu. Mosasamala kanthu ndi zimene Mulungu anawacitila, Mose anadziŵa kuti io adzacita zoipa. Iye anakamba kuti: “Pakuti iwo ndi mtundu wopanda nzelu, ndipo ndi osazindikila. Akanakhala anzelu, akanaganizila mozama zimenezi. Akanalingalila kuti ziwathela bwanji.”—Deut. 31:29, 30; 32:28, 29.

11 Kuti titsanzile nzelu za Mulungu, tiyenela kuganizila mwakuya mavuto amene angabwele cifukwa ca zocita zathu. Mwacitsanzo, ngati muli pa cibwenzi muyenela kukumbukila kuti cilakolako cakugonana ndi camphamvu kwambili. Musacite kapena kuganizila zinthu zimene zingasokoneze ubwenzi wanu wamtengo wapatali ndi Yehova. M’malomwake, muyenela kutsatila Mau a Mulungu amene amati: “Wocenjela ndi amene amati akaona tsoka amabisala, koma anthu osadziŵa zinthu amangopitabe ndipo amalangidwa.”—Miy. 22:3.

PEWANI MAGANIZO OLAKWIKA

12. Kodi kuganizila zoipa kungativulaze bwanji?

12 Munthu wanzelu amadziŵa kuti maganizo ali ngati moto. Moto tikaugwilitsila nchito bwino umakhala wothandidza. Mwacitsanzo, tingaugwilitsile nchito kuphikila cakudya. Koma ngati taugwilitsila nchito molakwika, ungatenthe nyumba ndi kupha anthu. Mofananamo, maganizo abwino amatithandiza kutsanzila Yehova. Komabe, kuganizila zinthu zoipa kungativulaze. Mwacitsanzo, ngati timakonda kulakalaka zaciwelewele, tingacite zimene tikulakalazo mpata ukapezeka. Ndithudi, kulakalaka zaciwelewele kungaononge ubwenzi wathu ndi Yehova.—Ŵelengani Yakobo 1:14, 15.

13. Kodi Hava anali kuganiza kuti adzakhala ndi umoyo wotani?

13 Tiyeni tione zimene zinacitika kuti mkazi woyamba, Hava, ayambe kulakalaka kudya cipatso coletsedwa ca “mtengo wodziŵitsa cabwino ndi coipa.” (Gen. 2:16, 17) Njoka inamuuza kuti: “Kufa simudzafa ayi. Mulungutu akudziŵa kuti tsiku limene mudzadye cipatso ca mtengo umenewu, maso anu adzatseguka ndithu, ndipo mudzafanana ndi Mulungu. Mudzadziŵa zabwino ndi zoipa.” Hava “anayamba kuona kuti zipatso za mtengowo n’zokoma kudya, zokhumbilika ndi zosililika.” Kodi zotsatilapo zake zinali zotani? “Anathyola cipatso ca mtengowo n’kudya. Pambuyo pake, anapatsako mwamuna wake pamene anali limodzi, ndipo nayenso anadya.” (Gen. 3:1-6) Hava anaona kuti zimene Satana anamuuza zinali zabwino. Mwina iye anaganiza kuti, ‘M’malo moti wina azindiuza kuti cabwino ndi ici, coipa ndi ici, ndizisankha ndekha.’ Maganizo amenewa anali olakwika kwambili. Zotsatilapo zake n’zakuti ‘ucimo unaloŵa m’dziko kudzela mwa munthu mmodzi, ndi imfa kudzela mwa ucimo.’—Aroma 5:12.

14. Ndi macenjezo otani okhudza ciwelewele amene Baibulo limapeleka?

14 Chimo limene Hava anacita m’munda wa Edeni silinali cigololo. Ngakhale n’conco, Yesu anaticenjeza kuti tiyenela kupewa maganizo aciwelewele. Iye anati: “Aliyense woyang’anitsitsa mkazi mpaka kumulakalaka, wacita naye kale cigololo mumtima mwake.” (Mat. 5:28) Komanso, Paulo anaticenjeza kuti: “Musamakonzekele kucita zilakolako za thupi.”—Aroma 13:14.

15. Ndi cuma cotani cimene tifunika kudziunjikila? Ndipo n’cifukwa ciani?

15 Baibulo limanenanso kuti tiyenela kupewa maganizo ofunitsitsa kulemela. M’malomwake, tiyenela kuyesetsa kukondweletsa Yehova. Malemba amati cuma ca munthu wolemela ‘m’maganizo mwake cili ngati mpanda woteteza.’ (Miy. 18:11) Yesu ananena fanizo losonyeza zimene zimacitikila “munthu amene wadziunjikila yekha cuma, koma amene sali wolemela kwa Mulungu.” (Luka 12:16-21) Yehova amakondwela ngati timacita zinthu zomusangalatsa. (Miy. 27:11) Tikamaunjika ‘cuma cathu kumwamba,’ timakhala osangalala podziŵa kuti tacita zimene iye amafuna. (Mat. 6:20) Kunena zoona, ubwenzi wathu ndi Yehova ndiye cinthu camtengo wapatali kuposa zonse zimene tingakhale nazo.

MUSAMADE NKHAWA

16. N’ciani cingatithandize kucepetsa nkhawa?

16 Tikamadziunjikila “cuma padziko lapansi,” timakhala ndi nkhawa kwambili. (Mat. 6:19) Yesu ananenanso fanizo losonyeza mmene “nkhawa za moyo wa m’nthawi ino ndiponso cinyengo camphamvu ca cuma” zimalepheletsela coonadi ca Ufumu kukula. (Mat. 13:18, 19, 22) Anthu ena amakhala ndi nkhawa nthawi zonse cifukwa cofunafuna ndalama kapena zinthu zina. Komabe, kukhala ndi nkhawa kwambili kumayambitsa matenda ndipo kungaticititse kusiya kukhulupilila Yehova. Conco, tiyeni nthawi zonse tizikhulupilila Yehova ndi kukumbukila kuti “nkhawa mumtima mwa munthu ndi imene imauwelamitsa, koma mau abwino ndi amene amausangalatsa.” (Miy. 12:25) Ngati muli ndi nkhawa, muyenela kuuzako mtumiki wa Yehova amene amakumvetsetsani. Makolo anu, bwenzi lanu, kapena mnzanu wa m’cikwati angakuthandizeni kucepetsa nkhawa ndi kukhulupilila Yehova.

17. Kodi Yehova amatithandiza bwanji kucepetsa nkhawa?

17 Yehova ndi amene amamvetsa nkhawa zathu kuposa wina aliyense. N’cifukwa cake Paulo analemba kuti: “Musamade nkhawa ndi kanthu kalikonse, koma pa ciliconse, mwa pemphelo ndi pembedzelo, pamodzi ndi ciyamiko, zopempha zanu zidziŵike kwa Mulungu. Mukatelo, mtendele wa Mulungu umene umaposa kuganiza mozama kulikonse, udzateteza mitima yanu ndi maganizo anu mwa Khristu Yesu.” (Afil. 4:6, 7) Conco, mukakhala ndi nkhawa ganizilani thandizo limene Yehova amapeleka kuti atithandize kulimbitsa ubwenzi wathu ndi iye. Amatithandiza kupitila mwa abale athu, akulu, kapolo wokhulupilika, angelo, ndi Yesu.

18. Kodi maganizo abwino angatithandize bwanji?

18 Monga mmene taphunzilila, maganizo abwino angatithandize kutsanzila makhalidwe a Yehova monga cikondi. (1 Tim. 1:11; 1 Yoh. 4:8) Kuti tikhale osangalala, tiyenela kuonetsa cikondi ceniceni kwa anzathu, kuganizila zotulukapo za zocita zathu, ndi kupewa nkhawa. Conco, tiyeni tiziganizila madalitso amtsogolo amene Yehova watilonjeza ndi kuyesetsa kutsanzila makhalidwe ake monga cikondi, kukoma mtima, nzelu, ndi cimwemwe.—Aroma 12:12